MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | ACHINYAMATA
Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha
VUTO LIMENE LIMAKHALAPO
-
Bambo anu auzidwa kuti azikagwira ntchito kwina ndipo banja lanu lonse likufunika kusamuka.
-
Mnzanu wapamtima akusamuka.
-
M’bale wanu wamkulu wapanga ukwati ndipo wasamuka.
Kodi mungatani zimenezi zitakuchitikirani?
Mtengo womwe umawerama mphepo ikamaomba sungatchoke msanga kukakhala mphepo ya mkuntho. Nanunso mukhoza kuphunzira kuti musamavutike kuzolowera zinthu zikasintha. Tisanakambirane mmene mungaphunzirire, tiyeni tikambirane zinthu zingapo zimene muyenera kudziwa zokhudza kusintha kwa zinthu.
ZIMENE MUYENERA KUDZIWA
Zinthu zimasintha pa moyo wa munthu wina aliyense. Baibulo limafotokoza mfundo yosatsutsika yokhudza anthufe. Limati: “Zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.” (Mlaliki 9:11) Nanunso zinthu zosayembekezereka zingakuchitikireni koma si kuti zonse zimakhala zoipa. Ndipotu nthawi zina zinthu zikasintha, zimaoneka ngati zoipa koma pamapeto pake mumaona kuti kusinthako kwakuthandizani. Komabe, anthu ambiri safuna kuti zinthu zisinthe pamoyo wawo ndipo amakhumudwa zikasintha.
Achinyamata ndi amene amavutika kwambiri zinthu zikasintha. N’chifukwa chiyani zili choncho? Mnyamata wina dzina lake Alex * ananena kuti: “Pa nthawiyi, zinthu zimakhala kuti zikusintha m’thupi mwathu ndiye zinanso zikasintha zimangowonjezera mavuto.”
Chifukwa chinanso n’chakuti: Akuluakulu savutika kwambiri zinthu zikasintha chifukwa amakhala atazolowera. Iwo savutika kudziwa zoyenera kuchita potengera zomwe zinawachitikirapo m’mbuyomo. Koma zimakhala zovuta kwa achinyamata chifukwa amakhala kuti sanakumane ndi zambiri.
N’zotheka kuzolowera zinthu zikasintha. Achinyamata ena amaphunzira kupirira zinthu zikasintha kapena akakumana ndi mavuto ndipo zimenezi zimawathandiza kudziwa zambiri. Achinyamata oterewa samwa mowa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo chifukwa chokhumudwa zinthu zikasintha.
ZIMENE MUNGACHITE
Zinthu zikasintha muzivomereza. N’zosakayikitsa kuti mumafuna kuti zinthu zizichitika mmene mukufunira pamoyo wanu. Komatu zimenezi n’zosatheka chifukwa anzanu akhoza kusamuka kapena kulowa m’banja. Abale anu adzakula n’kumakakhala paokha, banja lanu lingasamuke pa zifukwa zina ndipo zingapangitse kuti musiyane ndi anzanu komanso zinthu zomwe munazolowera. Zoterezi zikakuchitikirani ndi bwino kuvomereza m’malo momangodandaula.—Lemba lothandiza: Mlaliki 7:10.
Muziganizira zakutsogolo. Munthu yemwe amangoganizira zakumbuyo amafanana ndi dalaivala yemwe amangoyang’ana pagalasi loonera zinthu zakumbuyo akamayendetsa galimoto. Sikulakwa kuyang’ana pagalasili kwa nthawi yochepa, koma dalaivala wabwino amayang’ana kwambiri kutsogolo. Choncho, zinthu zikasintha pamoyo wanu, muziyang’ana zakutsogolo osati zakumbuyo. (Miyambo 4:25) Kuti zimenezi zitheke mungachite bwino kukhala ndi zolinga zoti muzikwaniritse pakadutsa mwezi umodzi kapena 6.
Muziganizira zinthu zabwino. Mtsikana wina dzina lake Laura ananena kuti: “Munthu akamaganizira zinthu zabwino zimene zachitika chifukwa cha kusintha kwa zinthu, sadandaula kwambiri ndi kusinthako.” Kodi mungalembe chinthu chabwino chimene chachitika chifukwa cha kusintha kwa zinthu pa moyo wanu?—Lemba lothandiza: Mlaliki 6:9.
Mtsikana wina dzina lake Victoria ali mwana, anzake apamtima onse anasamuka. Iye ananena kuti: “Pa nthawiyi, ndinkasowa wocheza naye ndipo ndinkangolakalaka zinthu zikanapanda kusintha. Koma panopa, ndimaona kuti kusinthaku kunandithandiza kwambiri. Ndinazindikira kuti kusintha kwa zinthu kumathandiza kuti munthu akule. Ndinkaonanso kuti zinali zotheka kupeza anzanga ena omwe ndinayandikana nawo.”—Lemba lothandiza: Miyambo 27:10.
Munthu yemwe amangoganizira zakumbuyo amafanana ndi dalaivala yemwe amangoyang’ana pagalasi loonera zinthu zakumbuyo akamayendetsa galimoto
Muzithandiza ena. Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” (Afilipi 2:4) Munthu akamathandiza anthu ena, samangokhalira kudandaula za mavuto ake. Mtsikana wina wazaka 17 dzina lake Anna ananena kuti: “Nditakula ndinazindikira kuti ndikamathandiza munthu amene akukumana ndi mavuto ofanana ndi anga kapena aakulu, ndinkakhala wosangalala.”
^ ndime 11 Tasintha maina ena m’nkhaniyi.