Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ali Ndi Makhalidwe Otani?

Kodi Mulungu Ali Ndi Makhalidwe Otani?

Tikazindikira makhalidwe abwino amene munthu ali nawo, timayamba kumudziwa bwino ndipo zikatero tingayambe kugwirizana naye kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Tikaphunzira za makhalidwe ake, timayamba kumudziwa bwino ndipo tingayambe kumuona kuti ndi mnzathu wapamtima. Yehova ali ndi makhalidwe abwino ambiri. Koma makhalidwe ake akuluakulu ndi mphamvu, nzeru, chilungamo ndi chikondi.

MULUNGU NDI WAMPHAMVU

“Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Inuyo ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu yanu.”​—YEREMIYA 32:17.

Umboni woti Mulungu ndi wamphamvu umaoneka m’zinthu zimene analenga. Mwachitsanzo, kodi mumamva bwanji mukaima panja nthawi yotentha, kunja kuli dzuwa? N’zosachita kufunsa kuti mumamva kutentha kwa dzuwa. Kutentha kwa dzuwa ndi zotsatira za zinthu zamphamvu zimene Mulungu analenga. Kodi dzuwa ndi lotentha bwanji? Asayansi amati pakatikati pa dzuwa ndi potentha madigiri seshasi 15,000,000. Pa sekondi iliyonse, dzuwa limatulutsa mphamvu zofanana ndi mphamvu za mabomba anyukiliya mamiliyoni ambirimbiri.

Komatu dzuwa ndi laling’ono poyerekezera ndi nyenyezi zina mamiliyoni ambirimbiri zomwe zili m’chilengedwechi. Asayansi amanena kuti nyenyezi ina yotchedwa UY Scuti, yomwe ndi imodzi mwa nyenyezi zikuluzikulu, ndi yaikulu kuposa dzuwa maulendo pafupifupi 1,700. Nyenyezi imeneyi itati iikidwe pamene pali dzuwa, ingaphimbe dziko lapansi lonseli mpaka kukafika pamene pali pulaneti yotchedwa Jupiter. Mwina zimenezi zikutithandiza kumvetsa bwino mawu a Yeremiya aja, akuti Yehova Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu.

Kodi timapindula bwanji ndi mphamvu za Mulungu? Kuti tikhale ndi moyo timadalira zinthu zimene Mulungu analenga monga dzuwa komanso zinthu zina za padzikoli. Komanso Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza aliyense payekha. Kodi amachita bwanji zimenezi? Yesu ali padzikoli, Mulungu anam’patsa mphamvu kuti athe kuchita zinthu zosiyanasiyana zodabwitsa monga kuchiritsa akhungu, olumala, akhate, ogontha komanso kuukitsa akufa. (Mateyu 11:5) Nanga bwanji masiku ano? Baibulo limati Yehova “amapereka mphamvu kwa munthu wotopa.” Limanenanso kuti: “Anthu odalira Yehova adzapezanso mphamvu.” (Yesaya 40:29, 31) Komanso Mulungu angathe kutipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tithe kupirira kapena kuthana ndi mavuto komanso mayesero amene tingakumane nawo. (2 Akorinto 4:7) Kodi inuyo simungafune kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ameneyu, amene amagwiritsa ntchito mphamvu zake zopanda malire mwachikondi pofuna kutithandiza?

MULUNGU NDI WANZERU

“Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! Zonsezo munazipanga mwanzeru.”​—SALIMO 104:24.

Tikaphunzira zambiri zokhudza zinthu zimene Mulungu analenga, m’pamenenso timayamba kumulemekeza kwambiri chifukwa chogoma ndi nzeru zake. Ndipotu asayansi ena amaphunzira zokhudza zinthu zina zimene Mulungu analenga n’cholinga choti abere luso loti azigwiritsa ntchito popanga zinthu. Kuchokera m’zinthu za m’chilengedwe, asayansi amabera luso lopanga zinthu zosiyanasiyana, kuyambira zazing’ono monga mazipi ochita kumata, mpaka zinthu zikuluzikulu ngati ndege.

Diso la munthu linapangidwa modabwitsa kwambiri

Chitsanzo chogometsa kwambiri cha zinthu zimene Mulungu analenga ndi thupi la munthu. Mwachitsanzo, taganizirani mmene mwana amayambira. Mwana amayamba kupangika kuchokera ku selo limodzi lokhala ndi malangizo onse okhudza mmene munthu adzakhalire. Seloli limagawikana n’kupanga maselo ambirimbiri ofanana. Koma pa nthawi yoyenera maselowa akamagawikana amapanga maselo osiyanasiyana ogwira ntchito zambirimbiri. Ena mwa maselo amenewa amakhala maselo a magazi, a mitsempha komanso a mafupa. Pasanapite nthawi, ziwalo zimapangika ndipo zimayamba kugwira ntchito. Pakangotha miyezi 9 kuchokera pamene selo loyamba lija linayamba kugawikana, mwana amakhala atapangika ndipo amakhala kuti ali ndi maselo mabiliyoni ambirimbiri. Zimachita kuonekeratu kuti amene anakonza zimenezi ndi wanzeru kwambiri. Anthu ambiri akaganizira zimenezi, amagwirizana ndi wolemba Baibulo wina amene anati: “Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.”​—Salimo 139:14.

Kodi timapindula bwanji ndi nzeru za Mulungu? Mlengi wathu amadziwa zimene timafunikira kuti tikhale osangalala. Popeza ndi wanzeru komanso amadziwa zambiri, amatipatsa malangizo othandiza kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Mwachitsanzo, amatiuza kuti: “Pitirizani . . . kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akolose 3:13) Kodi malangizo amenewa ndi anzeru? Inde. Madokotala anapeza kuti kukhululuka kumathandiza kuti munthu azigona tulo tabwino ndiponso kuti magazi ake aziyenda bwino. Kungathandizenso kuti munthu asadwale matenda ovutika maganizo kapena matenda ena. Mulungu ali ngati mnzathu amene amatikonda yemwe satopa kutipatsa malangizo othandiza. (2 Timoteyo 3:16, 17) Kodi inuyo simungasangalale kukhala ndi mnzanu wotereyu?

MULUNGU NDI WACHILUNGAMO

“Yehova amakonda chilungamo.”​—SALIMO 37:28.

Nthawi zonse Yehova amachita zinthu zabwino. “Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo.” (Yobu 34:10) Nthawi zonse chigamulo chake chimakhala choyenera, ngati mmene wamasalimo ananenera kuti: “Mudzaweruza anthu molungama.” (Salimo 67:4) Popeza “Yehova amaona mmene mtima ulili,” sangapusitsidwe ndi chinyengo. Iye amadziwa zoona ndipo amapereka chigamulo choyenera. (1 Samueli 16:7) Komanso Mulungu amadziwa chinthu chilichonse chopanda chilungamo komanso chachinyengo chomwe chikuchitika padzikoli ndipo analonjeza kuti posachedwapa “oipa adzachotsedwa padziko lapansi.”​—Miyambo 2:22.

Komabe Mulungu si woweruza wankhanza amene amangoganizira zopereka chilango. Iye amasonyeza chifundo akaona kuti pakufunika kutero. Baibulo limati: “Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo.” Iye amasonyeza makhalidwe amenewa ngakhalenso kwa anthu oipa, ngati alapa kuchokera pansi pa mtima. Kodi chilungamo chenicheni si chimenechi?​—Salimo 103:8; 2 Petulo 3:9.

Kodi timapindula bwanji ndi chilungamo cha Mulungu? Mtumwi Petulo anati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Timapindula ndi chilungamo cha Mulungu chifukwa iye alibe tsankho komanso sakondera. Tonse Mulungu angalole kuti tizimulambira mosatengera kuti ndife a dziko liti, mtundu uti komanso ndife ophunzira kapena osaphunzira, olemera kapena osauka.

Mulungu alibe tsankho ndipo timapindula ndi kupanda tsankho kwake mosatengera za mtundu wathu kapena zoti ndife olemera kapena osauka

Popeza Mulungu amafuna kuti tipindule ndi chilungamo chake, anatipatsa chikumbumtima. Baibulo limati chikumbumtima chili ngati lamulo ‘lolembedwa mumtima mwathu’ limene ‘limatichitira umboni’ kuti zimene tachita ndi zabwino kapena zoipa. (Aroma 2:15) Kodi chikumbumtima chimatithandiza bwanji? Ngati chikumbumtima chathu tachiphunzitsa bwino, chingatithandize kuti tisachite zinthu zoipa kapena zopanda chilungamo. Ndipo tikalakwitsa zinazake, chingatichititse kuti tilape n’kusiya zoipazo. Kumvetsa bwino maganizo a Mulungu pa nkhani ya chabwino ndi choipa, kumatithandiza kuti timuyandikire.

MULUNGU NDIYE CHIKONDI

“Mulungu ndiye chikondi.”​—1 YOHANE 4:8.

Mulungu amasonyeza kuti ndi wamphamvu, wanzeru komanso wachilungamo. Koma Baibulo silinena kuti Mulungu ndiye mphamvu, nzeru kapena chilungamo. Limati Mulungu ndiye chikondi. N’chifukwa chiyani? Chifukwa choti mphamvu zake zimamuthandiza kuti akwanitse kuchita zinthu ndipo chilungamo ndi nzeru zake zimamuthandiza kudziwa njira imene angachitire zinthuzo. Koma chikondi ndi chimene chimamupangitsa kuti achite zinthuzo. Choncho, zonse zimene Yehova amachita amazichita chifukwa cha chikondi.

Ngakhale kuti Yehova sankasowa chilichonse, chikondi chinamupangitsa kuti alenge angelo komanso anthu amene angapindule komanso kusangalala ndi chikondi chakecho. Iye anakonza dzikoli kuti likhale malo abwino oti anthu azikhalapo. Komanso amasonyeza chikondi kwa anthu onse chifukwa “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”​—Mateyu 5:45.

Kuwonjezera pamenepo, “Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Amasonyeza chikondi kwa anthu amene amafunitsitsa ndi mtima wonse kumudziwa komanso kukhala naye pa ubwenzi. Yehova amaona anthu oterewa aliyense payekha. Ndipotu inuyo “amakuderani nkhawa.”​—1 Petulo 5:7.

Kodi timapindula bwanji ndi chikondi cha Mulungu? Timasangalala ndi kukongola kwa dzuwa likamalowa. Zimatisangalatsanso tikamva mwana akuseka. Komanso timasangalala wachibale wathu akasonyeza kuti amatikonda. Zinthu zimenezi zingaoneke ngati zazing’ono, koma ndi zothandiza kwambiri pa moyo wathu.

Pali njira inanso imene timapindulira ndi chikondi cha Mulungu, ndipo njira yake ndi pemphero. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” Mofanana ndi mmene bambo wachikondi amachitira, Yehova amafuna kuti tikakhala ndi vuto tizimufotokozera momasuka kuti atithandize. Amatilonjeza kuti tikachita zimenezi adzatipatsa “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”​—Afilipi 4:6, 7.

Mu nkhaniyi takambirana mwachidule makhalidwe akuluakulu a Mulungu, omwe ndi mphamvu, nzeru, chilungamo ndi chikondi. Kodi zimenezi zakuthandizani kumudziwa bwino Mulungu kuposoyamba? Kuti mudziwenso zinthu zina zokhudza Mulungu, tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zotsatira kuti mudziwe zimene iye wachita komanso zimene adzakuchitireni m’tsogolo.

KODI MULUNGU ALI NDI MAKHALIDWE OTANI? Mulungu ndi wamphamvu, wanzeru komanso wachilungamo kuposa aliyense. Koma khalidwe lake losangalatsa kwambiri ndi chikondi