Mungathe Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
ANTHU ENA AMAONA KUTI . . .
Zimenezi n’zosatheka chifukwa Mulungu alibe nafe chidwi, ndi wapamwamba, ndi woyera kwambiri komanso si waubwenzi.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.
“[Mutulireni] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.”—1 Petulo 5:7.
KODI TINGATANI KUTI TIKHALE PA UBWENZI NDI MULUNGU?
Muzilankhula naye.—Salimo 145:18, 19.
Muzimumvetsera.—Salimo 32:8.
Muzitsatira malangizo ake.—Miyambo 3:5, 6.
Musataye mtima.—Mateyu 7:7, 8.