Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Anu?

Kodi Mulungu Amamva Mapemphero Anu?

Mukamapemphera, kodi mumaganiza kuti Mulungu akumvadi?

KODI BAIBULO LIMANENA ZOTANI?

  • Mulungu akumvetsera. Baibulo limanena kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi . . . Adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo.”​—Salimo 145:18, 19.

  • Mulungu amafuna kuti muzipemphera kwa iye. Baibulo limatiuza kuti: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”​—Afilipi 4:6.

  • Mulungu amakuganizirani. Mulungu amadziwa nkhawa zanu zonse ndipo amafuna kukuthandizani. Baibulo limanena kuti: ‘Muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7.