Matenda Ovutika Maganizo Ndi Vuto la Padziko Lonse
“Nthawi zonse ndimangopezeka kuti ndili ndi nkhawa ngakhale pamene ndangokhala ndekhandekha m’chipinda changa.”
“Ndikakhala kuti ndikumva bwino kwambiri, m’pamene ndimachita mantha kwambiri. Potengera zimene zakhala zikundichitikira, ndimadziwa kuti ndikasangalala kwambiri, sipamatenganso nthawi kuti ndikhumudwe.”
“Ndimayesetsa kuti ndiziganizira zinthu zokhazo zomwe zandichitikira patsikulo, koma mwadzidzidzi, nthawi zina ndimapezeka kuti ndayamba kuda nkhawa ndi zinthu zinanso zambiri.”
Zimenezi ndi zimene anthu ena omwe ali ndi matendawa ananena. Kodi inuyo kapena munthu amene mumamukonda mukukumananso ndi mavuto amenewa?
Dziwani kuti si inu nokha. Masiku ano, pali anthu ambiri amene akukhudzidwa ndi matenda amaganizo, ena mwa iwo kapenanso achibale awo akudwala matendawa.
N’zosachita kufunsa kuti tikukhala ‘munthawi yapadera komanso yovuta’ zomwe zikuchititsa kuti anthu azikhala ndi nkhawa zosiyanasiyana. (2 Timoteyo 3:1) Kafukufuku wina anasonyeza kuti padziko lonse lapansi, pafupifupi munthu mmodzi pa anthu 8 aliwonse akulimbana ndi matenda ovutika maganizo. Chifukwa cha mliri wa COVID-19, mu 2020, chiwerengero cha anthu amene anali ndi nkhawa chinawonjezereka kufika pa 26 peresenti poyerekeza ndi mu 2019, ndipo chiwerengero cha anthu amene anali ndi matenda aakulu ovutika maganizo chinawonjezereka pafupifupi ndi 28 peresenti.
N’zoona kuti timafunika kudziwa chiwerengero cha anthu amene ali ndi nkhawa komanso anthu amene akudwala matenda ovutika maganizo. Komabe, chofunika kwambiri ndi kudziwa mmene inuyo ndi achibale anu mukumvera komanso mmene thanzi lanu lilili.
Zimene munthu woganiza bwino amachita
Munthu amene alibe matenda ovutika maganizo nthawi zambiri amachita zinthu bwinobwino ndiponso sasokonezeka maganizo. Iye amakwanitsa kulimbana ndi nkhawa, amagwira ntchito bwinobwino ndiponso amakhala wokhutira ndi moyo wake.
Kukhala ndi matenda ovutika maganizo . . .
-
SIKUTANTHAUZA kuti ndiwe munthu wofooka.
-
NDI chizindikiro cha matenda amene amapangitsa munthu kuti azikhala ndi nkhawa, asamaganize bwinobwino komanso kuti azilephera kudziletsa.
-
Vutoli lingachititse munthu kuti azilephera kugwirizana ndi anthu ena komanso kuti asamachite bwinobwino zinthu zina za tsiku ndi tsiku.
-
Matendawa angakhudze anthu osiyanasiyana posatengera msinkhu, chikhalidwe, chipembedzo, maphunziro, mtundu wawo, kapenanso kuchuluka kwa ndalama zimene ali nazo.
Kumene mungapeze thandizo ngati muli ndi vuto la maganizo
Ngati munthu amene mumamukonda kapena inuyo mwayamba kuchita zinthu mosiyana ndi mmene munkachitira poyamba, monga kusowa tulo kapena kugona kwambiri, kuvutika kudya kapena kudya kwambiri komanso kuvutika kwambiri ndi nkhawa, mungafunike kupeza thandizo lachipatala kuti mudziwe chimene chikuyambitsa vutolo komanso kuti muthandizidwe moyenerera. Koma kodi mungapeze kuti thandizo?
Munthu wanzeru kwambiri kuposa anthu onse amene anakhalako padzikoli, Yesu Khristu, ananena kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.” (Mateyu 9:12) Anthu omwe akulimbana ndi mavuto okhudza thanzi lawo akalandira mankhwala komanso thandizo loyenerera lachipatala, akhoza kuchepetsa mavutowo komanso angathandizidwe kuti ayambe kukhala ndi moyo wosangalala. Choncho ndi nzeru kuti tisamazengereze kukalandira thandizo ngati tayamba kuona kuti zizindikiro za matendawa zikupitirirabe. a
Ngakhale kuti Baibulo si buku lofotokoza malangizo azachipatala, komabe lili ndi mfundo zimene zingakuthandizeni ngati muli ndi vuto la maganizo. Tikukulimbikitsani kuti muwerenge nkhani zotsatirazi zomwe zikufotokoza mmene Baibulo lingatithandizire kulimbana ndi vuto la maganizo.
a Magazini ya Nsanja ya Olonda sisankhira anthu thandizo la mankhwala limene ayenera kulandira. Munthu aliyense payekha ayenera kufufuza mosamala thandizo limene akufuna kulandira asanasankhe zochita.