Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sankhani Kukhala Kumbali ya Ufumu wa Mulungu Panopa

Sankhani Kukhala Kumbali ya Ufumu wa Mulungu Panopa

Tiyerekeze kuti kudera lanu kukubwera chimphepo chamkuntho. Boma likuchenjeza anthu kuti: “FULUMIRANI! THAWIRANI KUMALO OTETEZEKA!” Kodi pamenepa muyenera kuchita chiyani? N’zosachita kufunsa kuti muyenera kuthawira komwe mungatetezeke.

Panopa zili ngati tonse tikukhala kumalo omwe kukubwera chimphepo chamkuntho chimene Yesu ananena kuti ndi “chisautso chachikulu.” (Mateyu 24:21) Kulibe malo omwe tingathawireko koma pali zinthu zina zomwe tingachite kuti tidzatetezeke pachisautsochi. Kodi zinthu zake ndi ziti?

Pa ulaliki wake wapaphiri, Yesu Khristu anapereka malangizo akuti: “Pitirizani kufunafuna ufumu [wa Mulungu] choyamba ndi chilungamo chake.” (Mateyu 6:33) Kodi tingachite bwanji zimenezi?

Tizifunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba. Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kumaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kuposa chilichonse. (Mateyu 6:25, 32, 33) Tikutero chifukwa chakuti anthu sangakwanitse kuthetsa mavuto amene timakumana nawo. Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungachite zimenezi.

Tizifunafuna chilungamo chake. Tiziyesetsa kutsatira malamulo komanso mfundo zolungama za Mulungu. Tiyenera kuchita zimenezi chifukwa tikamasankha tokha zoyenera ndi zosayenera, zotsatira zake zimakhala zoipa. (Miyambo 16:25) Koma tikamatsatira mfundo za Mulungu, timamusangalatsa komanso zinthu zimatiyendera bwino.​—Yesaya 48:17, 18.

Pitirizani kufunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba ndi chilungamo chake. Yesu anachenjeza kuti ena akhoza kusokonezedwa n’kumaganiza kuti angakhale otetezeka ngati atapeza ndalama zambiri. Pamene ena akhoza kumatanganidwa kwambiri ndi nkhawa za moyo mpaka kumasowa nthawi yofunafuna Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 6:19-21, 25-32.

Koma Yesu analonjeza kuti anthu amene ali kumbali ya Ufumu wa Mulungu, azipeza zimene amafunikira panopa ndipo m’tsogolomu adzapeza madalitso osatha.​—Mateyu 6:33.

Ngakhale kuti ophunzira a Yesu ankafunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba ndi chilungamo chake, sanaone kutha kwa mavuto a anthu mu nthawi yawo. Komabe ankakhala motetezeka. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji?

Iwo ankatsatira mfundo zolungama za Mulungu ndipo zimenezi zinkawateteza kuti asakumane ndi mavuto omwe anthu osamvera Mulungu ankakumana nawo. Popeza ankakhulupirira kwambiri kuti Ufumu wa Mulungu udzabwera, ankatha kupirira ngakhale mavuto aakulu kwambiri. Ndipo Mulungu anawapatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti akwanitse kupirira.​—2 Akorinto 4:7-9.

KODI INUYO MUZIFUNAFUNA UFUMU CHOYAMBA?

Akhristu a m’nthawi ya atumwi anamvera lamulo la Yesu loti tizifunafuna Ufumu choyamba. Iwo ankalalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’madera onse omwe ankakhala. (Akolose 1:23) Kodi masiku ano aliponso amene akugwira ntchito imeneyi?

Inde. A Mboni za Yehova amadziwa kuti posachedwapa, Ufumu wa Mulungu uchotsa zoipa zonse padzikoli. Choncho amayesetsa kutsatira mawu a Yesu akuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—Mateyu 24:14.

Ndiye kodi inuyo muzitani mukamva uthenga wabwino? Tikukulimbikitsani kuti muzichita zimene anthu akale amumzinda wa Bereya ku Makedoniya anachita. Paulo atawauza uthenga wabwino wa Ufumu, iwo “analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri.” Kenako anayamba “kufufuza Malemba mosamala” kuti atsimikizire ngati zomwe anamvazo zinalidi zoona. Ndiyeno anatsatira zimene anaphunzirazo.​—Machitidwe 17:11, 12.

Inunso mukhoza kuchita zimenezi. Mukamafunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba ndi chilungamo chake mudzakhala otetezeka panopa komanso mudzapeza mtendere wosatha m’tsogolo.