Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Anthu ambiri amapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Koma kodi munadzifunsapo kuti, Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani komanso udzachita zotani?
TAONANI ZIMENE BAIBULO LIMANENA:
Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?
Ndi boma lakumwamba ndipo Yesu Khristu ndi Mfumu yake.—Yesaya 9:6, 7; Mateyu 5:3; Luka 1:31-33.
Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani?
Udzathetsa zoipa zonse ndipo udzabweretsa mtendere wosatha padzikoli.—Danieli 2:44; Mateyu 6:10.
Kodi kufunafuna Ufumu choyamba n’kutani?
Ndi kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu komanso kukhulupirira kuti ndi Ufumu wokhawu umene udzakonze zinthu padzikoli kuti zikhale mmene Mulungu amafunira.—Mateyu 6:33; 13:44.