Dziko Latsopano Lili Pafupi
Mulungu analenga dziko lapansi kuti anthu olungama azikhalamo mpaka kalekale. (Salimo 37:29) Anaika banja loyambirira Adamu ndi Hava, m’munda wokongola wa Edeni n’kuwapatsa udindo woti azilima ndi kusamalira mundawo limodzi ndi ana awo.—Genesis 1:28; 2:15.
Koma masiku ano dzikoli sililinso Paradaiso amene Mulungu ankafuna. Komabe, maganizo a Mulungu sanasinthe. Ndiye kodi adzachita chiyani kuti dzikoli likhalenso Paradaiso? Monga mmene taonera m’nkhani zapitazi, Mulungu sadzawononga dziko lenilenili. M’malomwake adzalipereka kwa anthu okhulupirika kuti azikhalamo. Ndiye kodi zinthu zidzakhala bwanji dzikoli likadzakhalanso Paradaiso?
Boma limene lidzalamulire dziko lonse
Posachedwapa Ufumu wa Mulungu ukayamba kulamulira anthu, dzikoli lidzakhala malo osangalatsa kwambiri. Anthu azidzakhala mogwirizana komanso azidzasangalala ndi ntchito yomwe agwira. Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti adzalamulire dziko lapansi. Masiku ano olamulira ambiri saganizira anthu awo. Koma Yesu ndi wosiyana kwambiri ndi anthu amenewa chifukwa azidzachita zinthu mokomera anthu onse. Iye adzakhala Mfumu yachikondi, yokoma mtima, yachifundo ndiponso yachilungamo.—Yesaya 11:4.
Anthu onse azidzakhala mogwirizana
Anthu omwe adzakhale m’dziko latsopano sadzakhala ogawikana chifukwa chosiyana mayiko kapena mitundu. Anthu onse adzakhala ogwirizana. (Chivumbulutso 7:9, 10) Anthu onse padzikoli azidzakonda Mulungu komanso anzawo ndipo azidzachita zinthu mogwirizana kuti akwaniritse cholinga chimene Mulungu anali nacho poyamba choti azisamalira dzikoli.—Salimo 115:16.
Zinthu zizidzayenda bwino m’chilengedwechi
Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira dzikoli, Mulungu adzachititsa kuti nyengo isamadzasokonekere. (Salimo 24:1, 2) Yesu ali padziko lapansi anagwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa poletsa chimphepo choopsa chimene chinachitika panyanja. (Maliko 4:39, 41) Khristu akamadzalamulira, anthu sazidzaopanso ngozi zam’chilengedwe. Pa nthawiyo, anthu azidzakhala mwamtendere ndi zinyama ndipo sadzawononganso zinthu zam’chilengedwe.—Hoseya 2:18.
Anthu adzakhala athanzi komanso adzakhala ndi chakudya chochuluka
Anthu onse sadzadwala, kukalamba kapena kufa. (Yesaya 35:5, 6) Anthu adzasangalala kukhala m’dziko lokongola komanso labwino ngati munda wa Edeni umene Adamu ndi Hava ankakhalamo. M’dziko latsopano, anthu onse adzakhala ndi chakudya chochuluka ngati mmene zinalili m’munda wa Edeni. (Genesis 2:9) Mofanana ndi Aisiraeli akale, aliyense m’Paradaiso ‘azidzadya mkate wake ndi kukhuta.’—Levitiko 26:4, 5.
Anthu azidzakhala mwamtendere komanso motetezeka
Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dzikoli, anthu azidzakhala mwamtendere komanso azidzachitirana zinthu mokoma mtima ndiponso mwachilungamo. Sikudzakhalanso nkhondo, anthu sazidzagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika ndiponso aliyense sadzavutika kupeza zinthu zofunika pa moyo. Baibulo limatilonjeza kuti: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.”—Mika 4:3, 4.
Aliyense adzakhala ndi nyumba yabwino komanso azidzasangalala ndi ntchito yomwe wagwira
Aliyense adzakhala ndi nyumba yabwino ndipo palibe amene azidzasowa pokhala. Anthu onse azidzasangalala ndi ntchito yomwe agwira. Baibulo limanena kuti m’dziko latsopano anthu “sadzagwira ntchito pachabe.”—Yesaya 65:21-23.
Maphunziro abwino kwambiri
Baibulo limati: “Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yesaya 11:9) Anthu amene azidzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu adzaphunzira zinthu zochuluka zokhudza Mlengi wathu Yehova ndiponso zinthu zokongola zimene analenga. Anthuwa sadzagwiritsa ntchito nzeru zawozo popanga zida zoopsa kapena kupweteka anzawo. (Yesaya 2:4) M’malomwake, azidzakhala mwamtendere n’kumasamalira dziko.—Salimo 37:11.
Anthu adzakhala ndi moyo mpaka kalekale
Polenga dzikoli, Mulungu anachita zonse zofunikira kuti anthu azikhalamo mosangalala. Iye ankafuna kuti anthu akhale ndi moyo padzikoli mpaka kalekale. (Salimo 37:29; Yesaya 45:18) Kuti cholinga chimenechi chidzatheke, Mulungu “adzameza imfa kwamuyaya.” (Yesaya 25:8) Baibulo limati: “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) Mulungu akamadzawononga dziko loipali adzapulumutsa anthu ena. Kenako adzaukitsa anthu ambiri amene anamwalira. Anthu onsewa adzakhala ndi mwayi wokhala m’dziko latsopano mpaka kalekale.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Fufuzani kuti mudziwe zimene mungachite kuti mudzapulumuke dziko loipali likamadzawonongedwa n’kukhala m’dziko latsopano lomwe layandikira. Pemphani kuti wa Mboni za Yehova azikuphunzitsani Baibulo kwaulere.