Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale M’dziko Latsopano?
Nkhani zapitazi zafotokoza kuti posachedwapa Mulungu awononga maboma a anthu ndi kuthetsa mavuto onse padzikoli. N’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti zimenezi zidzachitikadi? N’chifukwa chakuti Mawu a Mulungu omwe ndi Baibulo analonjeza kuti:
“Dziko likupita.”—1 YOHANE 2:17.
Sitikukayikiranso kuti padzakhala opulumuka chifukwa vesi lili pamtundali limanenanso kuti:
“Wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”
Choncho, tiyenera kuchita zimene Mulungu amafuna ngati tikufuna kudzapulumuka. Kuti tidziwe zimene Mulungu amafuna, choyamba tiyenera kumudziwa bwino.
“KUDZIWA MULUNGU” KUNGATITHANDIZE KUTI TIDZAPULUMUKE
Yesu ananena kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona.” (Yohane 17:3) Tifunika “kudziwa” Mulungu kuti tidzapulumuke mapeto a dzikoli n’kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Zimenezi zimaphatikizapo zambiri kuposa kungodziwa kuti Mulungu aliko komanso kudziwa zinthu zochepa zokhudza iyeyo. Timafunika kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Ngati tikufuna kuti munthu winawake akhale mnzathu wapamtima tifunika kupeza nthawi yocheza naye. N’zimenenso tiyenera kuchita kuti Mulungu akhale mnzathu wapamtima. Tiyeni tione mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.
MUZIWERENGA MAWU A MULUNGU TSIKU LILILONSE
Kuti tikhale ndi moyo timafunikira kudya tsiku lililonse. Koma Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.”—Mateyu 4:4.
Masiku ano mawu amene Yehova ananena timawapeza m’Baibulo. Mukamawerenga buku lopatulikali mudziwa zimene Mulungu anachita kale, zimene akuchita panopa ndiponso zimene adzachite m’tsogolo.
MUZIPEMPHERA KWA MULUNGU KUTI AZIKUTHANDIZANI
Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukufuna kumvera Mulungu koma zikukuvutani kusiya makhalidwe amene iye amadana nawo? Ngati ndi choncho, mungachite bwino kuyesetsa kumudziwa bwino Mulungu.
Taganizirani za mayi wina yemwe tangomutchula kuti Sakura, amene poyamba ankakonda kuchita zachiwerewere. Atayamba kuphunzira Baibulo anaphunzira lamulo la Mulungu lakuti “thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Sakura anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize ndipo anakwanitsa kusiya khalidwe loipali. Komabe panopa akuyesetsa kuti asayambirenso khalidwe loipali. Iye akuti: “Ndikayamba kuganizira zinthu zachiwerewere ndimapemphera kwa Yehova moona mtima chifukwa ndimadziwa kuti pandekha sindingakwanitse kulimbana ndi vutoli. Pemphero landithandiza kwambiri kuti ndiyandikire Yehova.” Mofanana ndi Sakura, anthu mamiliyoni ambiri akuphunzira Baibulo n’cholinga choti amudziwe bwino Mulungu. Mulungu amawapatsa mphamvu zowathandiza kusintha n’kumachita zimene iye amafuna.—Afilipi 4:13.
Mukamudziwa bwino Mulungu m’pamene amayamba kukukondani ndipo mumakhala mnzake wapamtima. (Agalatiya 4:9; Salimo 25:14) Mukatero mudzapulumuka n’kukhala m’dziko latsopano la Mulungu. Koma kodi moyo udzakhala wotani m’dziko latsopano? Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.
^ ndime 15 Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.