Tikufunikira Dziko Labwino
A António Guterres omwe ndi mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations ananena kuti: “Tikukhala m’dziko lodzaza ndi mavuto.” Kodi inunso mukuona choncho?
Nkhani zimene timamvetsera, kuonera ndi kuwerenga, zimakhala ndi zinthu zambiri zodetsa nkhawa monga:
Matenda ndi miliri
Ngozi za m’chilengedwe
Umphawi ndi njala
Kuonongeka kwa mpweya ndi madzi komanso kutentha kwa dziko
Kuphwanya malamulo, zachiwawa ndiponso zachinyengo
Nkhondo
Mpake kuti tikufunikira dziko labwino. Dziko limene mudzakhale
Anthu athanzi labwino
Chitetezo
Chakudya chokwanira
Mpweya ndi madzi abwino
Chilungamo chenicheni
Mtendere wochuluka
Kodi tikamanena kuti dziko labwino tikutanthauza chiyani?
Kodi n’chiyani chimene chidzachitikire dziko limene tikukhalamoli?
Kodi tingatani kuti tidzakhale m’dziko labwino?
Magaziniyi ifotokoza mayankho otonthoza ochokera m’Baibulo a mafunso amenewa ndi enanso.