Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Ananena

Kodi Mapeto Adzafika Liti? Zimene Yesu Ananena

Malinga ndi mmene taonera munkhani yapitayi, Baibulo likamanena za mapeto a dziko silitanthauza kuti limene lidzathe ndi dziko lapansili kapena anthu. M’malomwake limatanthauza kuti maboma oipa a anthu amene alipowa komanso anthu amene ali kumbali ya mabomawa ndi amene adzathe. Koma kodi Baibulo limanena kuti maboma oipawa adzatha liti?

TAONANI MFUNDO ZIWIRI ZIMENE YESU ANANENA ZOKHUDZA MAPETO:

“Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—MATEYU 25:13.

“Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.”​—MALIKO 13:33.

Choncho palibe munthu amene akudziwa nthawi yeniyeni pamene mapeto a dzikoli adzafike. Komabe Mulungu anakhazikitsa “nthawi yoikidwiratu” kutanthauza ‘tsiku ndi ola’ lenileni limene mapeto adzafike. (Mateyu 24:36) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitingadziwiretu kuti mapeto ali pafupi? Ayi ndithu. Yesu anauza ophunzira ake zinthu zosiyanasiyana zimene zingawathandize kuzindikira kuti mapeto ali pafupi.

CHIZINDIKIRO

Zinthu zosiyanasiyana zimene Yesu ananenazi zikuimira “chizindikiro cha mapeto a nthawi ino.” Iye anati: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.” (Mateyu 24:3, 7) Yesu ananenanso kuti kudzakhala “miliri” kutanthauza matenda ofalikira mwamsanga. (Luka 21:11) Kodi zinthu zimene Yesu analoserazi mukuona kuti zikuchitika?

Masiku ano anthu akuvutika kwambiri ndi nkhondo, njala, zivomezi komanso matenda osiyanasiyana. Mwachitsanzo mu 2004, chivomezi champhamvu chimene chinachitika panyanja ya Indian Ocean chinachititsa kuti kuchitike tsunami yomwe inapha anthu pafupifupi 225,000. Kwa nthawi yopitirira chaka chimodzi, mliri wa COVID-19 wapha anthu pafupifupi 2.6 miliyoni padziko lonse lapansi. Yesu ananena kuti zinthu ngati zimenezi zidzakhala zizindikiro zosonyeza kuti mapeto a dzikoli ali pafupi.

“MASIKU OTSIRIZA”

Baibulo limafotokoza kuti nthawi imene mapeto adzatsale pang’ono kufika imatchedwa “masiku otsiriza.” (2 Petulo 3:3, 4) Lemba la 2 Timoteyo 3:1-5, limanena kuti m’masiku otsiriza anthu azidzachita makhalidwe ambiri oipa. (Onani bokosi lakuti, “ Zomwe Zikuchitika Pamene Dziko Latsala Pang’ono Kutha.”) Kodi masiku ano mumaona anthu amene ali ndi makhalidwe monga kudzikonda, dyera, chiwawa ndi kusakonda ena? Umenewu ndi umboni winanso wosonyeza kuti tikukhala kumapeto kwenikweni kwa dziko loipali.

Kodi masiku otsiriza adzatenga nthawi yaitali bwanji? Baibulo limanena kuti adzakhala “kanthawi kochepa.” Kenako Mulungu adzawononga “amene akuwononga dziko lapansi.”​—Chivumbulutso 11:15-18; 12:12.

DZIKO LATSOPANO LAYANDIKIRA

Mulungu anaikiratu tsiku komanso nthawi imene adzawononge dziko loipa lomwe lilipoli. (Mateyu 24:36) Koma palinso nkhani yabwino. Nkhani yake ndi yakuti Mulungu “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe.” (2 Petulo 3:9) Choncho akupereka mwayi kwa anthu kuti aphunzire za iye, n’kumachita zimene iye amafuna. Akuchita zimenezi chifukwa akufuna kuti tidzapulumuke dziko loipali likamadzawonongedwa komanso kuti tidzakhale ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi.

Mulungu akuphunzitsa anthu amitundu yonse kuti adziwe zoyenera kuchita n’cholinga choti adzapulumuke n’kukhala m’dziko latsopano lomwe lidzalamuliridwe ndi Ufumu wake. Yesu ananena kuti uthenga wabwino wokhudza Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:14) Mu 2019, a Mboni za Yehova padziko lonse anathera maola opitirira 2 biliyoni polalikira ndi kuphunzitsa anthu uthenga wa m’Baibulo wopatsa chiyembekezo. Yesu ananena kuti ntchito imeneyi idzagwiridwa padziko lonse mapeto asanafike.

Posachedwapa, maulamuliro onse a anthu athetsedwa. Koma nkhani yabwino ndi yoti mukhoza kudzapulumuka dzikoli likamadzawonongedwa n’kulowa m’dziko lapansi la paradaiso limene Mulungu walonjeza. Nkhani yotsatira ifotokoza zimene mungachite kuti mudzakhale m’dziko latsopano.

Zimene Yesu ananena zokhudza “masiku otsiriza” zimatipatsa chiyembekezo