Anapatsa Agalu Anga Mabisiketi
NICK, yemwe amakhala mumzinda wa Oregon ku U.S.A., analemba kuti: “Kumayambiriro kwa chaka cha 2014, ndinayamba kumazungulira ndi tiagalu tanga m’tauni yomwe ndinkakhala. Nthawi zina a Mboni ankakhala pamalo ena azamalonda ndi timashelefu tawo tamabuku. Iwo ankavala bwino kwambiri ndipo ankapereka moni wamsangala kwa anthu odutsa.
“Sikuti a Mboniwo ankangokomera mtima anthu okha, koma ankakomeranso mtima agalu anga. Tsiku lina, Elaine, yemwe anaima pafupi ndi kashelefu anapatsa tiagalu tanga mabisiketi. Ndiye nthawi zonse tikamayenda, agalu angawo ankandikokera komwe kunali kashelefuko kuti a Mboniwo akawapatsenso mabisiketi.
“Panapita miyezi ingapo zimenezi zikuchitika. Tiagaluto tinkasangalala kudya mabisiketi, pomwe ine ndinkasangalala kukambirana mwachidule mfundo zina ndi a Mboniwo. Koma sindinkafuna kuzolowerana nawo kwambiri. Ndinali ndi zaka zoposa 70 ndipo sindinkadziwa kuti a Mboni amakhulupirira zotani. Popeza kuti ndinakhumudwa ndi matchalitchi a Chikhristu, ndinaona kuti bola ndizingophunzira Baibulo pandekha.
“Pa nthawiyi ndinkaonanso a Mboni ena ataima ndi mashelefu awo m’malo osiyanasiyana mumzindawo. Nawonso nthawi zonse ankakhala amsangala. Iwo ankayankha mafunso anga pogwiritsa ntchito Baibulo ndipo zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kuwakhulupirira kwambiri.
“Tsiku lina Elaine anandifunsa kuti, ‘Kodi mumakhulupirira kuti zinyama ndi mphatso yochokera kwa Mulungu?’ Ndinayankha kuti, ‘Inde, ndimakhulupirira kwambiri.’ Kenako anandiwerengera Yesaya 11:6-9. Kungoyambira pa nthawiyi, ndiyamba kufuna kuphunzira Baibulo, koma sindinkafuna kulandira buku lililonse la Mboniwo.
“M’masiku otsatira, ndinkasangalala kukambira mwachidule mfundo zochititsa chidwi ndi Elaine limodzi ndi mwamuna wake Brent. Anandiuza kuti ndiwerenge buku la Mateyu mpaka Machitidwe kuti ndimvetse zimene kukhala Mkhristu weniweni kumatanthauza. Ndinawerengadi, ndipo pasanapite nthawi ndinavomera kuti iwo azindiphunzitsa Baibulo. Mmenemu munali mkatikati mwa chaka cha 2016.
“Ndinkayembekezera mwachidwi mlungu uliwonse kuphunzira Baibulo komanso kukapezeka kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Ndinkasangalala kwambiri ndipo ndinkaona kuti ndi madalitso kuphunzira zimene Baibulo limanena. Patangotha chaka ndinabatizidwa. Panopa ndili ndi zaka 79, ndipo ndimadziwa kuti ndinapeza chipembedzo choona. Yehova wandidalitsa pondilola kukhala m’banja lake la atumiki odzipereka.”