Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 36

Anthu a Yehova Amakonda Chilungamo

Anthu a Yehova Amakonda Chilungamo

“Odala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo.”​—MAT. 5:6.

NYIMBO NA. 9 Yehova Ndi Mfumu Yathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yosefe anakumana ndi mayesero otani, nanga anachita chiyani?

 YOSEFE mwana wa Yakobo anakumana ndi mayesero ovuta kwambiri. Mayi wina anamuuza kuti, “Ugone nane.” Mayiyu anali mkazi wa Potifara yemwe anali mbuye wake. Koma Yosefe anakana zimene mayiyo ankafuna. Mwina wina angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yosefe anakana mayesero amenewa?’ Potifara anali atachokapo. Kuwonjezera pamenepo, Yosefe anali kapolo ndipo mayiyo akanachititsa kuti moyo wake ukhale wovuta chifukwa chakuti anakana zimene ankafuna. Komabe Yosefe anapitiriza kukana ngakhale kuti mayiyo ankamukakamiza mobwerezabwereza. Chifukwa chiyani? Iye anati: “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”​—Gen. 39:7-12.

2. Kodi Yosefe anadziwa bwanji kuti kuchita chigololo n’kuchimwira Mulungu?

2 Kodi Yosefe anadziwa bwanji kuti Mulungu wake amaona kuti chigololo ndi “choipa chachikulu”? Lamulo la m’Chilamulo cha Mose lakuti, “Usachite chigololo,” linalembedwa patapita zaka 200 kuchokera pa nthawiyo. (Eks. 20:14) Komabe Yosefe ankadziwa bwino Yehova ndipo anazindikira mmene angamvere ngati iye atachita chiwerewere. Mwachitsanzo, n’zosakayikitsa kuti Yosefe ankadziwa zimene Yehova anakonza pa nkhani ya ukwati kuti mwamuna azikhala ndi mkazi mmodzi. Ayeneranso kuti anamva mmene Yehova kawiri konse anatetezera agogo ake a Sara, pamene anakumana ndi zinthu zomwe zikanachititsa kuti asakhale wokhulupirika kwa mwamuna wawo. Mulungu anachitanso chimodzimodzi poteteza Rabeka mkazi wa Isaki. (Gen. 2:24; 12:14-20; 20:2-7; 26:6-11) Kuganizira nkhani zimenezi kunathandiza Yosefe kuzindikira zoyenera ndi zosayenera pamaso pa Mulungu. Chifukwa chakuti Yosefe ankakonda Mulungu, ankakondanso mfundo zake zolungama ndipo anatsimikiza mtima kuzitsatira.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Kodi mumakonda chilungamo? N’zosachita kufunsa. Komabe tonsefe si angwiro ndipo ngati sitingasamale, tingasokonezedwe ndi mmene dzikoli limaonera nkhani ya chilungamo. (Yes. 5:20; Aroma 12:2) Choncho tikambirana kuti chilungamo n’chiyani komanso mmene timapindulira chifukwa chokonda chilungamo. Kenako tikambirananso zinthu zitatu zimene zingatithandize kuti tizikonda kwambiri mfundo za Yehova.

KODI CHILUNGAMO N’CHIYANI?

4. Kodi ndi maganizo olakwika ati amene anthu ambiri amakhala nawo pa nkhani ya chilungamo?

4 Anthu ambiri amaganiza kuti munthu wolungama ndi munthu amene ndi wonyada, wokonda kuweruza ena kapenanso amene amadziona kuti ndi wabwino kuposa ena. Komatu Mulungu sasangalala ndi makhalidwe amenewa ngakhale pang’ono. Yesu ali padzikoli anadzudzula mwamphamvu atsogoleri achipembedzo a mu nthawi yake, chifukwa chokhazikitsa mfundo zawozawo pa nkhani ya chilungamo. (Mlal. 7:16; Luka 16:15) Munthu wachilungamo samaganiza kuti ndi wabwino kuposa ena.

5. Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, kodi chilungamo n’chiyani? Perekani zitsanzo.

5 Chilungamo ndi khalidwe labwino kwambiri. Mwachidule, chilungamo chimatanthauza kuchita zimene Yehova amaona kuti n’zoyenera. M’Baibulo, mawu akuti “chilungamo” amanena za kutsatira mfundo za Yehova, zomwe ndi zapamwamba kwambiri. Mwachitsanzo, Yehova analamula amalonda kuti azigwiritsa ntchito ‘muyezo woyenera.’ (Deut. 25:15) Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “woyenera” angamasuliridwenso kuti “wolungama.” Choncho Mkhristu amene akufuna kukhala wolungama pamaso pa Mulungu amachita zinthu zonse moona mtima pa nkhani za malonda. Munthu amene amakonda chilungamo, amadana ndi kuona wina akuchitiridwa zopanda chilungamo. Ndipo ‘pofuna kuti azikondweretsa [Yehova] pa chilichonse,’ munthu wolungama amaganizira mmene Yehovayo amaonera zimene amasankha.​—Akol. 1:10.

6. N’chifukwa chiyani sitikayikira mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa? (Yesaya 55:8, 9)

6 Baibulo limafotokoza kuti Yehova ndi mwiniwake wa chilungamo. Pa chifukwa chimenechi iye amatchedwa “malo okhalamo chilungamo.” (Yer. 50:7) Monga Mlengi, ndi Yehova yekha amene angathe kukhazikitsa mfundo zokhudza chabwino ndi choipa. Popeza iye ndi wangwiro, maganizo ake pa nkhani yokhudza chabwino ndi choipa ndi apamwamba kwambiri kuposa maganizo athu, omwe nthawi zambiri amasokonezedwa chifukwa choti ndife ochimwa. (Miy. 14:12; werengani Yesaya 55:8, 9.) Komabe popeza tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, timakwanitsa kuyendera mfundo zake zachilungamo. (Gen. 1:27) Ndipo timasangalala tikamachita zimenezi. Kukonda Atate wathu kumatichititsa kuti tizimutsanzira mmene tingathere.​—Aef. 5:1

7. N’chifukwa chiyani timafunikira mfundo zodalirika? Fotokozani.

7 Timapindula chifukwa chotsatira mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa. Kodi mukudziwa chifukwa chake tikutero? Taganizirani zimene zikanachitika ngati banki iliyonse ikanakhala ndi mfundo zakezake zokhudza mphamvu ya ndalama kapenanso ngati kampani iliyonse ya zomangamanga ikanakhala ndi mfundo zakezake pa nkhani ya miyezo. Bwenzitu kuli chisokonezo. Ndipo ngati azachipatala atalephera kutsatira mfundo zoyenera posamalira odwala, zingachititse kuti odwala ena amwalire. Choncho kutsatira mfundo zodalirika kumateteza. Mofanana ndi zimenezi, mfundo za Mulungu pa nkhani ya chabwino ndi choipa zimatiteteza.

8. Kodi anthu amene amachita chilungamo akuyembekezera madalitso otani?

8 Yehova amadalitsa anthu amene amayesetsa kutsatira mfundo zake. Iye amalonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:29) Taganizirani mmene anthu onse adzakhalire ogwirizana, amtendere komanso osangalala akamadzatsatira mfundo za Yehova. Yehova amafuna kuti mudzasangalale ndi moyo ngati umenewu. Kunena zoona, tonsefe tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kuti tizikonda chilungamo. Ndiye tingatani kuti tizikonda kwambiri khalidweli? Tiyeni tione zinthu zitatu zimene tiyenera kuchita.

MUZIKONDA KWAMBIRI MFUNDO ZA YEHOVA

9. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikonda chilungamo?

9 1: Tizikonda Mwini wake wa mfundozo. Kuti tizikonda chilungamo tiyenera kumakonda kwambiri yemwe anakhazikitsa mfundo zokhudza chabwino ndi choipa. Tikamakonda kwambiri Yehova m’pamenenso timafunitsitsa kutsatira mfundo zake zolungama. Mwachitsanzo, Adamu ndi Hava akanakhala kuti ankakonda Yehova akanamvera lamulo lake lolungama.​—Gen. 3:1-6, 16-19.

10. Kodi Abulahamu anatani kuti adziwe bwino maganizo a Yehova?

10 Ifeyo sitifuna kulakwitsa ngati mmene Adamu ndi Hava anachitira. Tingapewe zimenezi ngati titapitiriza kuphunzira zokhudza Yehova, kuyamikira makhalidwe ake komanso kuyesetsa kuti tizimvetsa mmene amaganizira. Tikatero tidzayamba kumukonda kwambiri. Taganizirani za Abulahamu. Iye ankakonda kwambiri Yehova. Ngakhale pamene zinkamuvuta kumvetsa zimene Yehova wasankha, iye ankamumverabe ndipo ankayesetsa kuti amudziwe bwino. Mwachitsanzo, atadziwa kuti Yehova akufuna kuwononga Sodomu ndi Gomora, poyamba Abulahamu ankaopa kuti mwina “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” awononga oipa pamodzi ndi wolungama omwe. Abulahamu ankaona kuti zimenezi ndi zosayenera choncho modzichepetsa anafunsa Yehova mafunso angapo. Yehova anamuyankha moleza mtima. Pamapeto pake Abulahamu anazindikira kuti Yehova amafufuza mtima wa munthu aliyense ndiponso kuti sapereka chilango kwa anthu oipa limodzi ndi osalakwa omwe.​—Gen. 18:20-32.

11. Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakonda komanso kukhulupirira Yehova?

11 Zimene Abulahamu anakambirana ndi Yehova zokhudza mizinda ya Sodomu ndi Gomora, zinamuthandiza kwambiri. N’zosakayikitsa kuti iye anayamba kukonda komanso kulemekeza kwambiri Atate ake kuposa kale. Patapita zaka, kukhulupirira kwake Yehova kunayesedwa kwambiri. Yehova anamuuza kuti apereke nsembe mwana wake wokondedwa Isaki. Koma popeza kuti Abulahamu anali atamudziwa bwino Mulungu, pa nthawiyi sanamufunse mafunso. Abulahamu anangokonzeka n’kukachita zimene Yehova anamuuza kuti achite. Komabe taganizirani ululu umene ankamva pokonzekera kukachita zimene Mulungu anamuuzazo. Abulahamu ayenera kuti ankaganizira kwambiri zimene anaphunzira zokhudza Yehova. Iye ankadziwa kuti Yehova sangachite chilichonse mopanda chilungamo kapena mopanda chikondi. Mogwirizana ndi zimene mtumwi Paulo ananena, Abulahamu ankakhulupirira kuti Yehova aukitsa mwana wake Isaki. (Aheb. 11:17-19) Ndipotu Yehova anali atalonjeza kuti Isaki adzakhala tate wa mtundu waukulu, koma pa nthawiyi iye analibe ana. Abulahamu ankakonda Yehova choncho ankakhulupirira kuti Atate ake nthawi zonse amachita zinthu mwachilungamo. Mwachikhulupiriro, iye anamvera ngakhale kuti zinali zovuta.​—Gen. 22:1-12.

12. Kodi tingatsanzire bwanji Abulahamu? (Salimo 73:28)

12 Kodi tingatsanzire bwanji Abulahamu? Mofanana ndi iye, tiyenera kupitiriza kuphunzira za Yehova. Tikamachita zimenezi tidzakhala naye pa ubwenzi ndipo tidzayamba kumukonda kwambiri. (Werengani Salimo 73:28.) Tidzaphunzitsa chikumbumtima chathu kuti chizitithandiza kuganiza ngati mmene Mulungu amaganizira. (Aheb. 5:14) Zotsatira zake n’zakuti tidzakana munthu wina akatiyesa kuti tichite zoipa. Sitidzalola kuchita chilichonse chimene chingakhumudwitse Atate wathu kapena kuwononga ubwenzi wathu ndi iye. Koma kodi ndi njira inanso iti imene tingasonyezere kuti timakonda chilungamo?

13. Kodi tingatani kuti tizichita chilungamo? (Miyambo 15:9)

13 2: Tsiku ndi tsiku muziyesetsa kuti muzikonda kwambiri chilungamo. Kuti tikhale ndi thupi lamphamvu timafunika kuchita khama kuti tizichita masewera olimbitsa thupi tsiku lililonse. Mofanana ndi zimenezi, timafunikanso khama kuti tizikonda mfundo za Yehova zolungama. Zimenezi si zovuta kuti tizizichita tsiku ndi tsiku. Yehova ndi wololera ndipo sayembekezera kuti tizichita zoposa zomwe tingathe. (Sal. 103:14) Iye amatitsimikizira kuti “amakonda munthu wochita chilungamo.” (Werengani Miyambo 15:9.) Tikamayesetsa kuti tikwaniritse cholinga china chake potumikira Yehova, pamafunika kuchita khama kuti tichikwaniritse. Zimenezi ndi zimenenso zimafunika tikamafuna kuchita chilungamo. Ndipo Yehova adzatithandiza moleza mtima kuti n’kupita kwa nthawi tizichita bwino pa nkhaniyi.​—Sal. 84:5, 7.

14. Kodi “chodzitetezera pachifuwa cha chilungamo” n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani chili chofunika?

14 Mwachikondi, Yehova amatikumbutsa kuti kuchita chilungamo si mtolo wolemetsa. (1 Yoh. 5:3) M’malomwake ndi chitetezo chomwe timafunikira tsiku lililonse. Kumbukirani zida zankhondo zimene mtumwi Paulo anafotokoza. (Aef. 6:14-18) Kodi ndi chida chiti chimene chinkateteza mtima wa msilikali? Chinali “chodzitetezera pachifuwa chachilungamo,” chomwe chimaimira mfundo zolungama za Yehova. Mofanana ndi chodzitetezera pachifuwa chomwe chimateteza mtima, mfundo zolungama za Yehova zimateteza mtima wathu wophiphiritsa, womwe ndi umunthu wathu wamkati. Choncho nthawi zonse muzionetsetsa kuti pa zida zanu za nkhondo, palinso chodzitetezera pachifuwa cha chilungamo.​—Miy. 4:23.

15. Kodi tingavale bwanji chodzitetezera pachifuwa cha chilungamo?

15 Kodi tingavale bwanji chodzitetezera pachifuwa cha chilungamo? Tingachite zimenezi poganizira mfundo za Mulungu tikamasankha zochita tsiku lililonse. Tikamasankha nkhani zoti tilankhule, nyimbo zoti timvetsere, zosangalatsa zoti tionere kapenanso mabuku oti tiwerenge, choyamba tizidzifunsa kuti: ‘Kodi ndikhala ndikulowetsa zotani mumtima mwanga? Kodi Yehova amavomereza zimenezi? Kapena kodi zimalimbikitsa chiwerewere, chiwawa, dyera komanso kudzikonda, omwe ndi makhalidwe amene Yehova amaona kuti ndi kupanda chilungamo?’ (Afil. 4:8) Ngati zimene mumasankha zili zogwirizana ndi zomwe Yehova amafuna, mumakhala mukulola kuti mfundo zake zolungama ziteteze mtima wanu.

Chilungamo chanu chingakhale “ngati mafunde a m’nyanja” (Onani ndime 16-17)

16-17. Kodi lemba la Yesaya 48:18, limatitsimikizira bwanji kuti tingathe kupitiriza kutsatira mfundo za Yehova?

16 Kodi kapena mumada nkhawa kuti mwina simungapitirize kutsatira mfundo za Yehova zachilungamo tsiku ndi tsiku komanso chaka chilichonse? Taganizirani chitsanzo chomwe Yehova anagwiritsa ntchito chomwe chili pa Yesaya 48:18. (Werengani.) Yehova amatitsimikizira kuti chilungamo chathu “chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.” Tayerekezani kuti mwaima mphepete mwa nyanja yaikulu ndipo mukuona mafunde akubwera mosalekeza. Kodi mungamadere nkhawa kuti mwina tsiku lina mafundewo adzasiya? Ayi. Chifukwa mukudziwa kuti mafundewo akhala akuchitika panyanjapo kwa zaka zambiri ndipo apitirizabe.

17 Chilungamo chanu chingafanane ndi mafunde a nyanjayo. Mukafuna kusankha zochita pa nkhani ina yake, choyamba muziganizira kaye zimene Yehova angafune kuti muchite. Ndiyeno muzichita zimenezo. Kaya zimene mukufunika kusankha zitakhala zovuta bwanji, nthawi zonse Atate wanu yemwe ndi wachikondi adzakuthandizani kuti musatekeseke komanso kuti tsiku lililonse muzichita zinthu zogwirizana ndi mfundo zake zolungama.​—Yes. 40:29-31.

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuweruza ena potengera mfundo zathu?

18 3: Muzisiya nkhani yoweruza m’manja mwa Yehova. Pamene tikuyesetsa kuti tizitsatira mfundo za Yehova zolungama, tiyenera kupewa kuweruza anzathu kapenanso kumadziona kuti ndife olungama kuposa anthu ena. M’malo momayerekezera zimene tikuchita ndi zimene ena akuchita n’kumaona kuti ife tikuchita bwino kwambiri, ngati kuti tili ndi ufulu wowaweruza potengera mfundo zathu, timakumbukira kuti Yehova ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi.” (Gen. 18:25) Yehova sanatipatse udindo umenewo. Ndipotu Yesu analamula kuti: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.”​—Mat. 7:1. *

19. Kodi Yosefe anasonyeza bwanji kuti ankaona kuti Yehova ndiye woyenera kuweruza?

19 Tiyeni tiganizirenso chitsanzo cha Yosefe, yemwe anali munthu wolungama. Iye anapewa kuweruza ena ngakhalenso amene anamuchitira zoipa. Azichimwene ake enieni anamuzunza, kumugulitsa ku ukapolo ndipo anatsimikizira bambo awo kuti anali ataphedwa. Patapita zaka, Yosefe anakumananso ndi anthu a m’banja lake. Popeza kuti pa nthawiyi anali wolamulira wamphamvu, iye akanatha kuweruza abale ake mwankhanza komanso kuwabwezera. Abale akewo ankaopa kuti mwina zimenezi ndi zimene angachite ngakhale kuti ankadzimvera chisoni chifukwa cha zimene anamuchitira. Koma Yosefe analankhula mowalimbikitsa kuti: “Musaope ayi. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu?” (Gen. 37:18-20, 27, 28, 31-35; 50:15-21) Modzichepetsa Yosefe anazindikira kuti ndi Yehova yekha, yemwe anali ndi udindo woweruza abale akewo.

20-21. Kodi tingatani kuti tisamadzione kuti ndife abwino kuposa ena?

20 Mofanana ndi Yosefe, timasiya nkhani yoweruza m’manja mwa Yehova. Timapewa kuonetsa ngati tikudziwiratu zimene zachititsa abale ndi alongo athu kuchita zina zake. Sitidziwa za mumtima mwa munthu koma Yehova yekha ndi amene “amafufuza zolinga zake.” (Miy. 16:2) Iye amakonda anthu onse posatengera chikhalidwe chawo kapena mmene anakulira. Ndipotu Yehova amatilimbikitsa kuti ‘tifutukule mtima wathu.’ (2 Akor. 6:13) Ifenso timafunitsitsa kuti tizikonda abale ndi alongo athu onse osati kuwaweruza.

21 Zimenezi zikutanthauzanso kuti sitiyenera kuweruza anthu amene si abale ndi alongo. (1 Tim. 2:3, 4) Kodi inuyo mungaweruze wachibale wanu yemwe si wa Mboni kuti, “Ameneyu sangayambe choonadi”? Ayi. Kuchita zimenezi kungakhale kudzikuza ndiponso kudziona kuti ndinu wabwino kuposa iyeyo. Yehova akupitirizabe kupereka mwayi kwa “anthu kwina kulikonse” woti alape. (Mac. 17:30) Nthawi zonse muzikumbukira kuti si chilungamo kumadziona kuti ndinu wolungama kwambiri kuposa ena.

22. N’chifukwa chiyani mwatsimikiza mtima kuti muzikonda chilungamo?

22 Tikamakonda mfundo za Yehova zachilungamo, timakhala osangalala ndipo timalimbikitsa ena kuti azitikonda komanso azikonda Mulungu wathu. Tiyeni tisasiye kukhala ndi “njala ndi ludzu la chilungamo.” (Mat. 5:6) Tisamakaikire kuti Yehova amaona khama lathu ndipo nthawi zonse amasangalala kutiona tikupitirizabe kuchita zinthu zoyenera. Pamene zinthu zopanda chilungamo zikuwonjezereka m’dzikoli, tisamade nkhawa. Nthawi zonse tizikumbukira kuti “Yehova amakonda anthu olungama.”​—Sal. 146:8.

NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

^ M’dziko loipali, n’zovuta kupeza anthu achilungamo. Komabe pali mamiliyoni a anthu omwe amachita zinthu mwachilungamo. N’zosakayikitsa kuti inuyo muli m’gulu la anthu amenewo. Mumayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo chifukwa mumakonda Yehova ndipo iye amakonda chilungamo. Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri chilungamo? Nkhaniyi itithandiza kudziwa kuti chilungamo n’chiyani komanso mmene timapindulira tikamachita zinthu mwachilungamo. Tikambirananso zimene tingachite kuti tizikonda kwambiri khalidweli.

^ Nthawi zina akulu amafunika kuweruza nkhani zina zomwe zikukhudza machimo akuluakulu komanso kulapa. (1 Akor. 5:11; 6:5; Yak. 5:14, 15) Komabe modzichepetsa, amakumbukira kuti sangadziwe za mumtima ndiponso kuti amaweruzira Yehova. (Yerekezani ndi 2 Mbiri 19:6.) Ndipo mosamala amaweruza potsatira mfundo za Mulungu zomwe ndi zogwirizana ndi chifundo komanso chilungamo chake.