Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Baibulo limanena kuti pamafunika mboni zosachepera ziwiri kuti nkhani inayake itsimikiziridwe kuti ndi yoona. (Num. 35:30; Deut. 17:6; 19:15; Mat. 18:16; 1 Tim. 5:19) Koma Chilamulo chinkanena kuti ngati mwamuna anagwirira mtsikana wolonjezedwa kukwatiwa ali “kuthengo” ndipo anakuwa, mtsikanayo sankaimbidwa mlandu wochita chigololo koma mwamunayo ankaimbidwa mlandu. Popeza panalibe mboni zimene zinaona akugwiriridwa, n’chifukwa chiyani mtsikanayo analibe mlandu koma mwamuna yekhayo?
Lamulo la pa Deuteronomo 22:25-27 silinali lokhudza kutsimikizira ngati mwamunayo ali ndi mlandu kapena ayi chifukwa zinali zitatsimikiziridwa kale. Koma lamuloli linkafotokoza zimene zingathandize kudziwa ngati mkaziyo ali ndi mlandu kapena ayi. Tingaone zimenezi m’mavesi ena am’chaputala chomwecho.
Mavesi ena amafotokoza za mwamuna amene anagonana ndi mkazi wolonjezedwa kukwatiwa ali “mumzinda.” Mwamunayo anali ndi mlandu wa chigololo chifukwa mkazi wolonjezedwa kukwatiwayo ankaonedwa ngati wakwatiwa kale. Nanga n’chiyani chinkachitikira mkaziyo? Mavesiwo amanena kuti iye “sanakuwe mumzindawo.” Ngati akanakuwa, anthu ena akanamva ndipo akanamuthandiza kuti asagwiriridwe. Koma popeza sanakuwe, mkaziyo ankakhala kuti wachitanso chigololo ndipo onse awiri ankaimbidwa mlandu.—Deut. 22:23, 24.
Pambuyo pa mavesiwa, Chilamulo chimafotokoza zinthu zina zimene zingachitike. Chimanena kuti: “Koma ngati mwamunayo wapeza mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo kuthengo ndipo wamugwira ndi kugona naye, mwamunayo afe yekha. Mtsikanayo musam’chite chilichonse. Iye sanachite tchimo loyenera imfa, chifukwa mlanduwu ukufanana ndi wa munthu amene waukira mnzake ndi kumupha, kuchotsa moyo wake. Popeza kuti anam’peza kuthengo, mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo anakuwa, koma panalibe womulanditsa.”—Deut. 22:25-27.
Zikakhala chonchi, oweruza ankakhulupirira mkaziyo. Zinali choncho chifukwa chakuti oweruza ankaona kuti mkaziyo “anakuwa koma panalibe womulanditsa.” Choncho ankakhala kuti sanachite chigololo. Koma mwamunayo anali ndi mlandu wochita chigololo chifukwa ‘chogwira mkazi wolonjezedwa kukwatiwayo ndi kugona naye.’
Choncho ngakhale kuti cholinga cha lamuloli chinali kusonyeza kuti mkaziyo analibe mlandu, zimene nkhaniyi imanena zakuti mwamunayo anali ndi mlandu wogwirira komanso wa chigololo n’zolondola. Sitiyenera kukayikira kuti oweruza ‘ankafufuza n’kutsimikizira’ nkhaniyo kuti asankhe zochita mogwirizana ndi mfundo zimene Mulungu anawauza momveka bwino komanso mobwerezabwereza.—Deut. 13:14; 17:4; Eks. 20:14.