NKHANI YOPHUNZIRA 6
“Mutu wa Mkazi ndi Mwamuna”
“Mutu wa mkazi ndi mwamuna.”—1 AKOR. 11:3.
NYIMBO NA. 13 Khristu Ndi Chitsanzo Chathu
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi mlongo angachite bwino kudzifunsa mafunso ati akamaganizira za munthu amene akufuna kudzakhala naye pabanja?
AKHRISTU onse amatsogoleredwa ndi Yesu yemwe ndi wangwiro. Komabe mkazi wa Chikhristu akakwatiwa, amatsogoleredwa ndi mwamuna yemwe si wangwiro. Zimenezitu sizikhala zophweka nthawi zonse. Choncho akamaganizira za mwamuna yemwe akufuna kudzakhala naye pabanja, mkazi angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘N’chiyani chikusonyeza kuti m’baleyu adzakhala mutu wa banja wabwino? Kodi amaona kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri pa moyo wake? Ngati si choncho, n’chiyani chikundipangitsa kuganiza kuti iye adzathandiza banja lathu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova?’ Mlongoyo angachitenso bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndili ndi makhalidwe ati amene angathandize kuti ndidzakhale ndi banja labwino? Kodi ndine woleza mtima komanso wopatsa? Kodi ndili pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?’ (Mlal. 4:9, 12) Zimene mkazi angasankhe asanakwatiwe, zingachititse kuti adzakhale ndi banja labwino komanso losangalala.
2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Alongo ambiri a Chikhristu ndi zitsanzo zabwino pa nkhani yogonjera amuna awo. Timawayamikira kwambiri chifukwa cha zimenezi. Ndipo timasangalala kutumikira Yehova Iimodzi ndi alongo okhulupirikawa. Munkhaniyi tikambirana mayankho a mafunso atatu awa: (1) Kodi ndi mavuto ena ati amene alongo okwatiwa amakumana nawo? (2) N’chifukwa chiyani mkazi amasankha kugonjera mwamuna wake? (3) Kodi amuna a Chikhristu ndi akazi awo angaphunzire chiyani pa nkhani yogonjera pa chitsanzo cha Yesu, Abigayeli ndi Mariya mkazi wa Yosefe, yemwenso ndi mayi ake a Yesu?
KODI NDI MAVUTO ATI AMENE AKAZI OKWATIWA AMAKUMANA NAWO?
3. N’chifukwa chiyani mabanja onse amakumana ndi mavuto?
3 Ukwati ndi mphatso yangwiro yochokera kwa Mulungu, koma anthufe si angwiro. (1 Yoh. 1:8) N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amachenjeza anthu amene ali pabanja kuti adzakumana ndi mavuto, omwe amafotokozedwa kuti ndi “nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) Tiyeni tione mavuto ena omwe mkazi amene ali pabanja angakumane nawo.
4. N’chifukwa chiyani nthawi zina mkazi akhoza kumaona ngati ndi wotsika akamagonjera mwamuna wake?
4 Nthawi zina chifukwa cha kumene anakulira, mkazi akhoza kumaona ngati ndi wotsika akamagonjera mwamuna wake. Marisol yemwe amakhala ku United States ananena kuti: “Kumene ndinakulira, nthawi zambiri akazi ankauzidwa kuti palibe kusiyana pakati pa amuna ndi akazi ndipo ayenera kuchita zinthu zofanana. Ndimadziwa kuti Yehova anakonza zoti mwamuna azitsogolera monga mutu ndiponso kuti mkazi ayenera kumumvera, komabe ngakhale ndi choncho mkaziyo ayenera kupatsidwa ulemu. Koma chifukwa cha zimene anthu m’dzikoli amanena, nthawi zina zimandivuta kuti ndizilemekeza udindo wa mwamuna wanga monga mutu.”
5. Kodi ndi maganizo olakwika ati amene amuna ena amakhala nawo okhudza akazi?
5 Nthawi zina mkazi akhoza kukwatiwa ndi mwamuna amene amaona kuti akazi ndi otsika poyerekeza ndi amuna. Mlongo wina dzina lake Ivon, yemwe amakhala ku South America, ananena kuti: “Kumene ndimakhala amuna ndi amene amayambirira kudya chakudya ndipo akazi amadya pambuyo pake. Ana aakazi amauzidwa kuti ndi amene ayenera kuphika komanso kugwira ntchito zonse za pakhomo, koma ana aamuna amachitiridwa zinthu zonse ndi amayi awo komanso azichemwali awo ndipo amauzidwa kuti ndi ‘mafumu a m’nyumbamo.’” Mlongo wina dzina lake Yingling, yemwe amakhala ku Asia, ananena kuti: “Muchilankhulo chathu muli mwambi wina umene umanena kuti akazi sayenera kukhala anzeru kapena kukhala ndi luso linalake. Udindo wawo ndi kugwira ntchito za pakhomo ndipo saloledwa kufotokoza maganizo awo kwa amuna awo.” Mwamuna amene amayendera maganizo amenewa alibe chikondi ndipo satsatira mfundo za m’Baibulo. Iye amachititsa kuti mkazi wake asamasangalale komanso amalephera kutsanzira Yesu ndipo sasangalatsa Yehova.—Aef. 5:28, 29; 1 Pet. 3:7.
6. Kodi akazi okwatiwa ayenera kuchita chiyani kuti akhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?
6 Monga mmene tinaonera munkhani yapitayi, Yehova amayembekezera amuna a Chikhristu kuti azipezera anthu a m’banja lawo zinthu zofunika pa moyo, kuwathandiza kuti aziona kuti ndi otetezeka komanso kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Iye. (1 Tim. 5:8) Komabe alongo amene ali pabanja, tsiku lililonse amayenera kupeza nthawi yowerenga mawu a Mulungu, kuganizira mozama zimene awerengazo komanso kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima. Nthawi zina kuchita zimenezi kungakhale kovuta. Akazi amatanganidwa kwambiri, choncho akhoza kumaona ngati alibe nthawi komanso mphamvu yochitira zonsezi, komabe iwo ayenera kuona kuti kupeza nthawi yochita zimenezi n’kofunika kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova amafuna kuti aliyense payekha apitirizebe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi iye.—Mac. 17:27.
7. Kodi n’chiyani chingathandize kuti mkazi azimvera komanso kulemekeza mwamuna wake?
7 Kunena zoona, mkazi ayenera kuchita khama kuti azigonjera mwamuna wake yemwe si wangwiro. Komabe iye angakwanitse udindo umene Yehova anamupatsa akamvetsa komanso kuvomereza chifukwa chake Baibulo limanena kuti akazi ayenera kugonjera amuna awo.
N’CHIFUKWA CHIYANI AKAZI AMASANKHA KUGONJERA AMUNA AWO?
8. Mogwirizana ndi Aefeso 5:22-24, n’chifukwa chiyani mkazi wa Chikhristu amasankha kugonjera mwamuna wake?
8 Mkazi wa Chikhristu amasankha kugonjera mwamuna wake chifukwa ndi zimene Yehova amafuna kuti azichita. (Werengani Aefeso 5:22-24.) Iye amakhulupirira Atate wake wakumwamba ndipo amadziwa kuti amamukonda komanso amamuuza kuti achite zinthu zimene ndi zothandiza kwa iye.—Deut. 6:24; 1 Yoh. 5:3.
9. Kodi chimachitika n’chiyani ngati mkazi wa Chikhristu amalemekeza udindo wa mwamuna wake?
Sal. 119:165) Zimenezi zimachititsa kuti anthu onse m’banjamo kuphatikizapo iyeyo, mwamuna wake ndi ana ake azisangalala.
9 Dzikoli limalimbikitsa kuti akazi azinyalanyaza mfundo za Yehova komanso kuti aziona kuti kugonjera kumawachititsa kuoneka ngati otsika. Komatu anthu amene amalimbikitsa maganizo amenewa, sadziwa Mulungu wathu wachikondi. Yehova sangapereke kwa ana ake aakazi omwe ndi a mtengo wapatali, lamulo limene lingachititse kuti azioneka otsika. Mlongo amene amayesetsa kukwaniritsa udindo umene Yehova wamupatsa, amathandiza kuti m’banja lake mukhale mtendere. (10. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Carol ananena?
10 Mkazi amene amagonjera mwamuna wake yemwe si wangwiro amasonyeza kuti amakonda ndiponso amalemekeza Yehova, yemwe anakonza zoti ena azitsogolera monga mutu. Carol, yemwe amakhala ku South America, ananena kuti: “Ndimadziwa kuti mwamuna wanga amalakwitsa zinthu zina. Ndimadziwanso kuti zimene ndimachita akalakwitsa zimasonyeza kuti ndimaona ubwenzi wanga ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali. Choncho ndimapitirizabe kumugonjera chifukwa ndimafuna kusangalatsa Atate wanga wakumwamba.”
11. Kodi n’chiyani chimathandiza mlongo wina dzina lake Aneese kuti azikhululuka, nanga tingaphunzire chiyani pa zimene ananena?
11 Nthawi zina zingakhale zovuta kuti mkazi azilemekeza komanso kugonjera mwamuna wake, makamaka ngati amaona kuti mwamuna wakeyo samuganizira kapena kumudera nkhawa. Koma taonani zimene mlongo wina wokwatiwa dzina lake Aneese amachita akakumana ndi zoterezi. Iye anati: “Ndimayesetsa kuti ndisakwiye kwambiri. Ndimakumbukira kuti tonsefe timalakwitsa zinthu zina. Ndiye ndimayesetsa kuti ndizikhululuka ndi mtima wonse ngati mmene Yehova amachitira. Ndikakhululuka ndimaona kuti ndimapeza mtendere wa mumtima.” (Sal. 86:5) Choncho mkazi akamakhululukira mwamuna wake zimakhala zosavuta kuti azimugonjera.
KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI PA ZITSANZO ZA ANTHU A M’BAIBULO?
12. Kodi m’Baibulo muli zitsanzo zotani?
12 Anthu ena amaona kuti munthu amene amagonjera ena ndi wofooka. Komatu zimenezi si zoona ngakhale pang’ono. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anali ogonjera koma anali
olimba mtima. Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Yesu, Abigayeli komanso Mariya.13. N’chifukwa chiyani Yesu amagonjera Yehova? Fotokozani.
13 Yesu amagonjera Yehova, koma si kuti amachita zimenezi chifukwa chakuti alibe nzeru kapena luso. Ndipotu ndi munthu wanzeru zambiri yekha amene angaphunzitse zomveka komanso zosavuta kumva ngati mmene Yesu ankachitira. (Yoh. 7:45, 46) Yehova ankadziwa luso limene Yesu anali nalo, moti analola kugwira naye ntchito pamene ankalenga zinthu zonse. (Miy. 8:30; Aheb. 1:2-4) Ndipo Yesu ataukitsidwa, Yehova anamupatsa ‘ulamuliro wonse, kumwamba ndi padziko lapansi.’ (Mat. 28:18) Ngakhale kuti Yesu ali ndi luso komanso nzeru, iye amadalirabe Yehova kuti azimutsogolera. N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Amachita zimenezi chifukwa chakuti iye amakonda Atate.—Yoh. 14:31.
14. Kodi amuna angaphunzire chiyani (a) pa nkhani ya mmene Yehova amaonera akazi? (b) pa mfundo yopezeka mu Miyambo 31?
14 Zimene amuna okwatira angaphunzirepo. Yehova sanakonze zoti akazi azigonjera amuna awo chifukwa chakuti amawaona kuti ndi otsika poyerekeza ndi amuna. Umboni wa zimenezi ndi wakuti iye anasankha akazi ena kuti akalamulire limodzi ndi Yesu kumwamba. (Agal. 3:26-29) Yehova anasonyeza kuti amadalira Mwana wake pomupatsa ulamuliro. Mofanana ndi zimenezi, mwamuna wanzeru amapatsa mkazi wake mphamvu yotha kuchita zinthu zina. Baibulo limafotokoza zimene mkazi waluso angachite. Mwachitsanzo, iye angathe kuyang’anira ntchito zonse zapakhomo, kugula kapena kugulitsa malo komanso kuchita bizinezi. (Werengani Miyambo 31:15, 16, 18.) Iye si kapolo amene alibe ufulu wofotokoza maganizo ake. M’malomwake, mwamuna wake amamudalira ndipo amamumvetsera akamafotokoza maganizo akewo. (Werengani Miyambo 31:11, 26, 27.) Mwamuna akamalemekeza mkazi wake mwa njira imeneyi, zimachititsa kuti mkaziyo azimugonjera mosangalala.
15. Kodi akazi okwatiwa angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yesu?
15 Zimene akazi okwatiwa angaphunzirepo. Ngakhale kuti Yesu anachita zinthu zazikulu, iye samaona kuti angaoneke wotsika akamagonjera Yehova ngati mutu wake. (1 Akor. 15:28; Afil. 2:5, 6) Mofanana ndi zimenezi, mkazi wabwino amene amatengera chitsanzo cha Yesu, samaona kuti aoneka wotsika akamagonjera mwamuna wake. N’zoona kuti amathandiza mwamuna wake chifukwa choti amamukonda, koma chifukwa chachikulu chimene amachitira zimenezi n’chakuti amakonda komanso kulemekeza Yehova.
16. Mogwirizana ndi 1 Samueli 25:3, 23-28, kodi Abigayeli anakumana ndi mavuto otani? (Onani chithunzi chapachikuto.)
16 Abigayeli anali pabanja ndi Nabala. Nabala anali wodzikonda, wonyada komanso wosayamika. Ngakhale zinali choncho, Abigayeli sanayese kupeza njira yachidule yothetsera banja lake. Iye akanatha kusankha kukhala chete n’kulola kuti Davide ndi amuna amene anali nawo adzaphe mwamuna wake. Koma iye anachita zonse zimene akanatha kuti ateteze Nabala ndi anthu onse a m’banja lake. Taganizirani mmene Abigayeli anachitira zinthu molimba mtima pokakumana ndi amuna 400 onyamula zida komanso polankhula mwaulemu ndi Davide. Ndipotu iye anali wokonzeka kupepesa chifukwa cha zimene mwamuna wake anachita. (Werengani 1 Samueli 25:3, 23-28.) Davide anazindikira kuti Yehova anagwiritsa ntchito mayi wolimba mtimayu kuti amupatse malangizo n’cholinga choti asapalamule mlandu waukulu.
17. Kodi amuna akuphunzira chiyani pa nkhani ya Davide ndi Abigayeli?
17 Zimene amuna okwatira angaphunzirepo. Abigayeli anali mkazi wanzeru. Davide anachita zinthu mwanzeru chifukwa chomvetsera malangizo ake. Chifukwa cha zimenezi iye anapewa kuchita zinthu zimene zikanachititsa kuti akhale ndi mlandu wamagazi. Mofanana ndi Davide, mwamuna wanzeru amaganizira mofatsa zimene mkazi wake akunena asanasankhe zochita pa nkhani zofunika
kwambiri. N’kutheka kuti maganizo a mkazi wake angamuthandize kuti asasankhe zinthu mopanda nzeru.18. Kodi akazi akuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Abigayeli?
18 Zimene akazi okwatiwa angaphunzirepo. Mkazi amene amakonda komanso kulemekeza Yehova angathandize kwambiri banja lake ngakhale kuti mwamuna wake satumikira Yehova kapena kutsatira mfundo zake. Iye sayesa kuthetsa banja lake popanda zifukwa za m’Malemba. M’malomwake pokhalabe waulemu komanso wogonjera, amayesa kuthandiza mwamuna wake kuti aphunzire za Yehova. (1 Pet. 3:1, 2) Ngakhale kuti mwina mwamunayo sangatengere chitsanzo chabwino cha mkaziyo, Yehova amayamikira ngati mkaziyo apitirizabe kukhala wogonjera kwa mwamuna wake n’kupitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Yehovayo.
19. Kodi ndi pa nthawi iti pamene mkazi sayenera kumvera mwamuna wake?
19 Mkazi wa Chikhristu amene amagonjera mwamuna wake sangalole kuchita zimene mwamuna wake wamupempha, ngati zinthuzo zikusemphana ndi malamulo kapena mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, mlongo amene mwamuna wake si wa Mboni sangalole ngati mwamunayo atamuuza kuti aname, abe kapena achite zinthu zina zimene Yehova amadana nazo. Akhristu onse kuphatikizapo alongo amene ali pabanja amaona kuti chofunika kwambiri ndi kumvera Yehova Mulungu kuposa anthu. Choncho ngati mlongo atauzidwa kuti achite zinthu zimene ndi zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo, ayenera kukana n’kufotokoza mwaulemu koma molimba mtima chifukwa chimene sangachitire zinthuzo.—Mac. 5:29.
20. Kodi tikudziwa bwanji kuti Mariya anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?
20 Mariya anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. N’zodziwikiratu kuti iye ankadziwa bwino Malemba. Tikutero chifukwa pamene ankacheza ndi Elizabeti, yemwe ndi mayi ake a Yohane m’batizi, iye anatchula mfundo zopezeka m’Malemba a Chiheberi maulendo oposa 20. (Luka 1:46-55) Ndipo taganizirani izi: Ngakhale kuti Mariya anali pachibwenzi ndi Yosefe, mngelo wa Yehova sanayambe kukaonekera kwa Yosefeyo. M’malomwake anayamba kuonekera kwa Mariya n’kumuuza zoti adzabereka Mwana wa Mulungu. (Luka 1:26-33) Yehova ankamudziwa bwino Mariya ndipo sankakayikira kuti azidzamukonda Mwana wakeyo komanso kumusamalira. Ndipo sitikukayikira kuti Mariya anapitirizabe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ngakhale pambuyo poti Yesu waphedwa n’kuukitsidwa kupita kumwamba.—Mac. 1:14.
21. Kodi amuna angaphunzire chiyani pa zimene Baibulo limanena zokhudza Mariya?
21 Zimene amuna okwatira angaphunzirepo. Mwamuna wanzeru amasangalala akaona kuti mkazi wake amadziwa bwino Malemba. Iye samakhumudwa kapena kuganiza kuti mkazi wakeyo amulanda udindo wotsogolera m’banja mwawo. Amadziwanso kuti mkazi amene amadziwa bwino Baibulo ndi mfundo zake ndi amene angathandize kwambiri banja lake. Ndipotu ngakhale kuti mkazi angakhale wophunzira kuposa mwamuna wake, ndi udindo wa mwamunayo kutsogolera banja lake pa kulambira kwa pabanja komanso pa zinthu zina zokhudza kulambira.—Aef. 6:4.
22. Kodi akazi okwatiwa angaphunzire chiyani kwa Mariya?
22 Zimene akazi okwatiwa angaphunzirepo. Mkazi ayenera kugonjera mwamuna wake, koma ayenera kudziwa kuti ndi udindo wake kulimbitsa chikhulupiriro chake. (Agal. 6:5) Kuti zimenezi zitheke, iye ayenera kupeza nthawi yophunzira mawu a Mulungu payekha komanso kuganizira mozama zimene waphunzirazo. Zimenezi zingamuthandize kuti azikonda komanso kulemekeza Yehova ndiponso kuti azigonjera mwamuna wake mosangalala.
23. Kodi akazi akamagonjera amuna awo zimathandiza bwanji iwowo, anthu a m’banja lawo komanso anthu a mumpingo?
23 Akazi amene amagonjera amuna awo chifukwa chakuti amakonda Yehova, amakhala osangalala komanso okhutira kusiyana ndi akazi amene amakana kutsatira zimene Yehova anakonza zoti mwamuna azitsogolera m’banja. Akazi ogonjerawa, amaperekanso chitsanzo chabwino kwa anyamata ndi atsikana. Amathandizanso kuti anthu m’banja komanso mumpingo azikondana ndiponso azikhala mwa mtendere. (Tito 2:3-5) Masiku ano, chiwerengero chachikulu cha atumiki a Yehova ndi akazi. (Sal. 68:11) Tonsefe, kaya ndife amuna kapena akazi, tingathandize kwambiri kuti aliyense mumpingo azisangalala. Munkhani yotsatira tidzakambirana mmene aliyense angachitire zimenezi.
NYIMBO NA. 131 “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”
^ ndime 5 Yehova anakonza zoti mkazi wokwatiwa azigonjera mwamuna wake. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Amuna a Chikhristu ndi akazi awo, angaphunzire zambiri pa nkhani yokhala ogonjera pa chitsanzo cha Yesu komanso akazi ena omwe nkhani zawo zinalembedwa m’Baibulo.
^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pamene ankacheza ndi Elizabeti, yemwe ndi mayi ake a Yohane M’batizi, Mariya anatchula mfundo zopezeka m’Malemba a Chiheberi omwe analoweza pamtima.
^ ndime 70 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Nayenso mkazi wa Chikhristu yemwe ali pabanja amayesetsa kupeza nthawi yophunzira Baibulo n’cholinga choti alimbitse ubwenzi wake ndi Yehova.