Zonsezi N’chifukwa Cha Kumwetulira Basi
TSIKU lina atsikana awiri amayenda kumalo a zamalonda mumzinda wa Baguio ku Philippines. Iwo anaona a Mboni akulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu koma sanafike pamalopo. Mlongo amene anali pashelefupo dzina lake Helen, anawamwetulira. Atsikanawo anapitiriza ulendo wawo koma sanaiwale zimene Helen anachita powamwetulira.
Kenako atsikanawo ali m’basi pobwerera kwawo, anaona chikwangwani chachikulu cha jw.org pa Nyumba ya Ufumu. Iwo anakumbukira kuti zilembo zimenezi ndi zomwe anazionanso pakashelefu kaja. Ndiye anatsika basi n’kupita pageti la Nyumba ya Ufumuyo kukaona nthawi imene misonkhano imachitikira pa nyumbayo.
Atsikanawo anadzachita nawo msonkhano wotsatira pa Nyumba ya Ufumuyo. Iwo atalowa m’Nyumba ya Ufumuyo anadabwa kwambiri kuona Helen. Nthawi yomweyo anamuzindikira kuti ndi munthu amene anawamwetulira uja. Helen anati: “Pamene atsikanawo ankabwera pamene ndinali ndinayamba kuchita timantha. Ndinkaganiza kuti mwina pali zinazake zimene ndalakwitsa.” Koma atsikanawo anafotokozera Helen kuti anamuona ataima pakashelefu.
Atsikanawo anasangalala kuchita nawo msonkhanowo komanso kucheza ndi abale ndi alongo. Ataona anthu ena akukonza m’Nyumba ya Ufumuyo pambuyo pamsonkhanowo, anafunsa ngati angagwire nawo ntchitoyo. Mmodzi wa atsikanawo anachoka m’dzikolo koma winayo anayamba kusonkhana ndipo akuphunzira Baibulo. Zonsezi n’chifukwa cha kumwetulira basi.