NKHANI YOPHUNZIRA 6
NYIMBO NA. 10 Tamandani Yehova Mulungu Wathu
“Tamandani Dzina la Yehova”
“Inu atumiki a Yehova, mutamandeni, tamandani dzina la Yehova.”—SAL. 113:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona zimene zingatilimbikitse kuti tizitamanda dzina loyera la Yehova pa mpata uliwonse.
1-2. Kodi n’chiyani chingatithandize kumvetsa mmene Yehova amamvera chifukwa cha bodza lomwe anamunenera?
TAYEREKEZERANI kuti mnzanu akukunenerani zoipa. Mukudziwa kuti ndi zabodza, koma anthu ena akukhulupirira zimenezo. Kuwonjezera pamenepo, anthu akupitiriza kunenabe zabodzazo ndipo anthu enanso ambiri akukhulupirira. Kodi mungamve bwanji? Ngati mumaganizira anthu komanso mbiri yanu, n’zosachita kufunsa kuti bodza limeneli lingakupwetekeni kwambiri.—Miy. 22:1.
2 Chitsanzo chimenechi chingatithandize kumvetsa mmene Yehova anamvera mbiri yake itaipitsidwa. Mmodzi wa ana ake auzimu ananena bodza lokhudza iyeyo kwa Hava, ndipo Hava anakhulupirira bodzalo. Bodzalo linachititsa kuti makolo athu oyambawo asamvere Yehova. Zotsatira zake n’zakuti anthu onse anachimwa ndipo amafa. (Gen. 3:1-6; Aroma 5:12) Mavuto onse omwe timaona m’dzikoli monga imfa, nkhondo ndi zinthu zina zomvetsa chisoni, zinayamba chifukwa cha bodza lomwe Satana anayamba kufalitsa m’munda wa Edeni. Kodi Yehova anamva kupweteka chifukwa cha bodzali ndi zotsatirapo zake? Mosakayikira zinamupweteka. Komabe Yehova sanapse mtima kapena kusunga chakukhosi. Ndipotu iye nthawi zonse ndi “Mulungu wachimwemwe.”—1 Tim. 1:11.
3. Kodi tili ndi mwayi wochita chiyani?
3 Tili ndi mwayi wothandiza nawo kuyeretsa dzina la Yehova pomvera lamulo losavuta ili lakuti: “Tamandani dzina la Yehova.” (Sal. 113:1) Tingachite zimenezi pouza ena zabwino zokhudza Mwiniwake wa dzinali. Kodi ndinu wokonzeka kuchita zimenezi? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zomwe zingatilimbikitse kuti tizitamanda dzina la Mulungu ndi mtima wonse.
TIMASANGALATSA YEHOVA TIKAMATANDA DZINA LAKE
4. N’chifukwa chiyani Yehova amasangalala tikamamutamanda? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.)
4 Timasangalatsa Atate wathu wakumwamba tikamatamanda dzina lake. (Sal. 119:108) Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu Wamphamvuyonse ali ngati anthu omwe si angwiro, amene amafuna kutamandidwa chifukwa chofuna kuti azidziona kuti ndi ofunika? Ayi. Taganizirani chitsanzo ichi. Mwachikondi, kamtsikana kakukoleka dzanja lake m’khosi mwa bambo ake n’kuwauza kuti, “Ndinu bambo wabwino kwambiri padziko lonse.” Zimene mwanayo wachita zikuwakhudza kwambiri bambo akewo ndipo akusangalala kwambiri. Chifukwa chiyani? Kodi tinganene kuti bamboyo amafunika kulimbikitsidwa kapena kutamandidwa ndi mwana wakeyo kuti azidziona kuti ndi wofunika? Ayi. M’malomwake, chifukwa chakuti amakonda mwana wakeyo, bamboyo akusangalala kuti mwanayo wamusonyeza chikondi ndipo wamuyamikira. Iye akudziwa kuti makhalidwe amenewa adzathandiza mwanayo kukhala wosangalala akamakula. Mofanana ndi zimenezi, Yehova yemwe ndi Bambo wathu wamkulu amasangalala tikamamutamanda.
5. Kodi timathandiza kutsutsa bodza liti tikamatamanda dzina la Mulungu?
5 Tikamatamanda Atate wathu wakumwamba timathandiza kutsutsa bodza lomwe Satana ananena, limene limakhudzanso munthu aliyense. Satana amanena kuti palibe munthu amene angakhale wokhulupirika atakumana ndi mayesero pothandiza kuti dzina la Mulungu lisadetsedwe. Iye amanena kuti tingasiye kutumikira Mulungu ngati titaona kuti kuchita zimenezo kungachititse kuti tikumane ndi mavuto. (Yobu 1:9-11; 2:4) Koma Yobu anakhalabe wokhulupirika ndipo anasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Nanga bwanji inuyo? Aliyense wa ife ali ndi mwayi wothandiza kuti dzina la Atate wathu lisadetsedwe komanso kumusangalatsa popitirizabe kumutumikira mokhulupirika. (Miy. 27:11) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri.
6. Kodi tingatsanzire bwanji Mfumu Davide ndi Alevi? (Nehemiya 9:5)
6 Kukonda Mulungu kumachititsa anthu okhulupirika kuti azitamanda dzina lake ndi mtima wonse. Mfumu Davide analemba kuti: “Moyo wanga utamande Yehova. Chilichonse cha mkati mwanga, chitamande dzina lake.” (Sal. 103:1) Davide ankadziwa kuti kutamanda dzina la Yehova kumatanthauza kutamanda Yehovayo. Choncho tikamva dzinali timaganizira makhalidwe ake abwino komanso ntchito zake zodabwitsa. Davide ankafuna aziona kuti dzina la Atate wake ndi loyera komanso kumalitamanda. Iye ankafuna azichita zimenezo ndi “chilichonse cha mkati [mwake]” kapena kuti ndi mtima wonse. Mofanana ndi Davide, Alevi nawonso ankatsogolera potamanda Yehova. Modzichepetsa, iwo anavomereza kuti mawu awo sakanatha kufotokoza mokwanira ulemerero umene dzina loyera la Yehova liyenera kulandira. (Werengani Nehemiya 9:5.) Mosakayikira, Yehova anasangalala ndi kudzichepetsa komanso kumutamanda kochokera pansi pamtima kumeneku.
7. Kodi tingatamande bwanji Yehova tikamalalikira komanso m’zochita zathu za tsiku ndi tsiku?
7 Masiku ano tingasangalatse Yehova, polankhula za iye mosonyeza kuti timayamikira komanso kumukonda. Tikamalalikira, timakumbukira kuti cholinga chathu chachikulu ndi kuthandiza anthu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuwathandiza kuti nawonso azimuona kuti ndi Atate wawo wachikondi. (Yak. 4:8) Timasangalala kusonyeza anthu zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Yehova kuti ndi wachikondi, chilungamo, nzeru, mphamvu komanso ali ndi makhalidwe ena abwino. Timatamandanso Yehova ndi kumusangalatsa tikamayesetsa kumutsanzira. (Aef. 5:1) Tikamachita zimenezi, timakhala osiyana kwambiri ndi anthu a m’dziko loipali. Ena angamaone kuti ndife osiyana ndipo angamadabwe chifukwa chake zili choncho. (Mat. 5:14-16) Ndiyeno tikamachita nawo zinthu za tsiku ndi tsiku, tingathe kuwafotokozera chifukwa chake timachita zinthu mosiyana ndi iwowo. Zotsatira zake n’zakuti anthu amtima wabwino amayamba kukopeka ndi Mulungu wathu. Tikamatamanda Yehova m’njira zimenezi, timasangalatsa mtima wake.—1 Tim. 2:3, 4.
TIMASANGALATSA YESU TIKAMATAMANDA DZINA LA YEHOVA
8. N’chifukwa chiyani Yesu ali chitsanzo chabwino pa nkhani yotamanda dzina la Yehova?
8 Pa zolengedwa zonse zanzeru kumwamba ndi padzikoli, palibe amene amadziwa bwino Atate kuposa Mwana. (Mat. 11:27) Yesu amakonda Atate wake ndipo ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yotamanda dzina la Yehova. (Yoh. 14:31) Popemphera kwa Atate wake pa usiku wake womaliza, anafotokoza chinthu chofunika kwambiri chimene anachita pautumiki wake wapadzikoli, ponena kuti: “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu.” (Yoh. 17:26) Kodi ankatanthauza chiyani pamenepa?
9. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito fanizo liti pofotokoza momveka bwino mmene Atate wake alili?
9 Yesu anachita zambiri kuposa kungodziwitsa anthu kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Ayuda omwe ankawaphunzitsa, ankadziwa kale dzina la Mulungu. Koma Yesu anapereka chitsanzo chabwino chifukwa “ndi amene anafotokoza za Mulungu.” (Yoh. 1:17, 18) Mwachitsanzo, Malemba a Chiheberi amasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima. (Eks. 34:5-7) Yesu anamveketsa bwino mfundo ya choonadi imeneyi pamene anafotokoza fanizo la mwana wolowerera ndi bambo ake. Tikamawerenga zimene bamboyu anachita ataona mwana wake wolapayo “ali chapatali ndithu,” n’kumuthamangira, kumukumbatira komanso kumukhululukira ndi mtima wonse, timamvetsa bwino chifundo komanso kukoma mtima kwa Yehova. (Luka 15:11-32) Apa Yesu anathandiza anthu kumvetsa zoona zenizeni zokhudza mmene Atate wake alili.
10. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu ankagwiritsa ntchito dzina lenileni la Atate wake ndipo ankafunanso kuti ena azichita zomwezo? (Maliko 5:19) (Onaninso chithunzi.) (b) Kodi Yesu amafuna kuti ifeyo tizichita chiyani masiku ano?
10 Kodi Yesu amafuna kuti enanso azigwiritsa ntchito dzina lenileni la Atate wake? Inde. Atsogoleri ena achipembedzo pa nthawiyo, ankakhulupirira kuti dzina la Mulungu ndi lopatulika kwambiri ndipo si ulemu kumalitchula. Koma Yesu sanalole kuti miyambo yosagwirizana ndi Malembayi imulepheretse kulemekeza dzina la Atate wake. Taganizirani zimene zinachitika atachiritsa munthu wina wogwidwa ndi ziwanda, m’dera la Agerasa. Anthu akumeneko anachita mantha ndipo anapempha Yesu kuti achoke m’deralo, ndipo anachokadi. (Maliko 5:16, 17) Komabe, Yesu ankafuna kuti anthu akumeneko adziwe dzina la Yehova. Choncho analamula munthu amene anamuchiritsayo kuti aziuza anthu, osati zimene Yesu anamuchitira, koma zimene Yehova anamuchitira. (Werengani Maliko 5:19.) a Masiku anonso, iye amafuna kuti tizidziwitsa anthu padziko lonse dzina la Atate wake. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Tikamachita zimenezi, timasangalatsa Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu.
11. Kodi Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipempherera chiyani, nanga n’chifukwa chiyani zili zofunika? (Ezekieli 36:23)
11 Yesu ankadziwa kuti cholinga cha Yehova ndi kuyeretsa dzina lake komanso kutsutsa mabodza onse amene ananenedwa okhudza iye. N’chifukwa chake Mbuye wathu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Yesu ankamvetsa kuti kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu, ndi nkhani yaikulu yokhudza zolengedwa zonse. (Werengani Ezekieli 36:23.) Palibe aliyense, kumwamba kapena padziko lapansi, amene anayeretsa kwambiri dzina la Yehova kuposa Yesu. Koma kodi pamene Yesu ankamangidwa, adani ake ankamuimba mlandu wotani? Ankanena kuti ankanyoza Mulungu. Mosakayikira, Yesu ankadziwa kuti kunyoza dzina loyera la Atate wake ndi tchimo lalikulu kwambiri. Choncho anakhumudwa kwambiri poona kuti akuimbidwa mlandu umenewu. N’kutheka kuti zimenezi ndi zomwe zinachititsa Yesu kuti ‘azunzike koopsa mumtima mwake,’ kutatsala maola ochepa kuti agwidwe.—Luka 22:41-44.
12. Kodi Yesu anayeretsa dzina la Atate wake m’njira yaikulu iti?
12 Kuti ayeretse dzina la Atate wake, Yesu anapirira kuzunzidwa, kunyozedwa komanso mabodza omwe ankanenedwa okhudza iye. Iye ankadziwa kuti anali atamvera Atate wake mu zonse ndipo panalibe chifukwa choti achitire manyazi. (Aheb. 12:2) Ankadziwanso kuti Satana ndi amene ankachititsa zonse zomwe ankakumana nazo pa nthawi yovutayi. (Luka 22:2-4; 23:33, 34) Satana ankafunitsitsa kuti amulepheretse Yesu kukhala wokhulupirika, koma analephera mochititsa manyazi. Apa Yesu anasonyeza kuti Satana ndi wabodza komanso kuti Yehova ali ndi atumiki ake okhulupirika omwe amapitirizabe kumutumikira mokhulupirika ngakhale atakumana ndi mayesero aakulu.
13. Kodi tingatani kuti tizisangalatsa Yesu yemwe ndi Mfumu yathu?
13 Kodi inuyo mukufunitsitsa kusangalatsa Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu yanu? Ngati ndi choncho, pitirizani kutamanda dzina la Yehova komanso kuthandiza anthu ena kuti adziwe makhalidwe amene ali nawo. Mukamachita zimenezi ndiye kuti mukutsanzira Yesu. (1 Pet. 2:21) Mofanana ndi Yesu, mudzasangalatsa Yehova komanso kusonyeza kuti Satana yemwe ndi mdani wake, ndi wabodza lankunkhuniza.
TIMAPULUMUTSA ANTHU TIKAMATAMANDA DZINA LA YEHOVA
14-15. Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zomwe zimachitika tikamaphunzitsa anthu zokhudza Yehova?
14 Tikamatamanda dzina la Yehova, timathandiza anthu kuti adzapulumuke. Kodi timachita bwanji zimenezi? Satana “wachititsa khungu maganizo” a anthu osakhulupirira. (2 Akor. 4:4) Zotsatira zake n’zakuti anthuwo amakhulupirira mabodza ake, monga akuti: Kulibe Mulungu, Mulungu ali kutali kwambiri ndipo sasamala za anthu, Mulungu ndi wankhanza ndipo amazunza anthu mpaka kalekale. Mabodza onsewa cholinga chake n’chakuti aipitse dzina la Yehova komanso mbiri yake kuti anthu asamafunenso kukhala naye pa ubwenzi. Koma ntchito yathu imalepheretsa cholinga cha Satanachi. Timaphunzitsa anthu choonadi chokhudza Atate wathu ndipo timatamanda dzina lake loyera. Ndiye kodi zotsatirapo zake zimakhala zotani?
15 Choonadi cha Mawu a Mulungu ndi champhamvu kwambiri. Tikamaphunzitsa anthu zoona zokhudza Yehova komanso mmene alili, pamachitika chinthu china chodabwitsa. Khungu limene Satana amachititsa m’maganizo mwa anthu aja limayamba kuchoka ndipo amayamba kuona makhalidwe abwino a Atate athu okondedwa, ngati mmene ifeyo timachitira. Iwo amagoma ndi mphamvu zake zopanda malire. (Yes. 40:26) Amayamba kumukhulupirira chifukwa amaona kuti ndi wachilungamo. (Deut. 32:4) Amaphunzira zambiri zokhudza nzeru zake zapamwamba. (Yes. 55:9; Aroma 11:33) Amalimbikitsidwanso kudziwa kuti iyeyo ndi chikondi. (1 Yoh. 4:8) Akayamba kukhala naye pa ubwenzi, chiyembekezo chawo chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale monga ana ake, chimakhala chotsimikizika. Tilitu ndi mwayi waukulu kwambiri wothandiza anthu kuti akhale pa ubwenzi ndi Atate wawo. Tikamachita zimenezi, Yehova amationa kuti ndife “antchito anzake.”—1 Akor. 3:5, 9.
16. Kodi anthu ena anamva bwanji atadziwa dzina la Mulungu? Perekani zitsanzo.
16 Poyambirira tingaphunzitse munthu kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Zimenezi zingamufike pamtima kwambiri munthu wamaganizo abwino. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Aaliyah b anakulira m’banja lomwe silinali la Chikhristu. Koma iye sankakhutira ndi chipembedzo chake ndipo sanali pa ubwenzi ndi Mulungu. Zimenezi zinasintha atangoyamba kuphunzira ndi a Mboni. Anayamba kumuona Mulungu ngati mnzake. Anadabwa ataphunzira kuti m’Mabaibulo ambiri anachotsamo dzina la Mulungu n’kuikamo mayina audindo monga, Ambuye. Kudziwa dzina la Mulungu kunasintha kwambiri moyo wake. Mosangalala iye anati: “Mnzanga wapamtima ali ndi dzina.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Aaliyah anati: “Tsopano ndili ndi mtendere wamumtima. Ndimaona kuti ndinachita mwayi.” Mwamuna wina dzina lake Steve yemwe anali woimba, analeredwa m’chipembedzo cha Chiyuda. Iye anasiya kupita kuchipembedzo chilichonse chifukwa ankaona zachinyengo zambiri zomwe zinkachitika. Koma pa nthawi inayake amayi ake atamwalira, anavomera kukhala nawo pa phunziro la Baibulo limene wa Mboni wina ankachititsa. Iye anasangalala kwambiri atadziwa dzina la Mulungu. Steve anati: “Ndinali ndisakudziwa dzina la Mulungu.” Anawonjezeranso kuti: “Kwa nthawi yoyamba ndinamvetsa kuti Mulungu alipo ndipo ndi weniweni. Nthawi yomweyo ndinadziwa kuti ndapeza mnzanga.”
17. N’chifukwa chiyani mukufunitsitsa kupitiriza kutamanda dzina la Yehova? (Onaninso chithunzi.)
17 Mukamagwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu, kodi mumawadziwitsa dzina lopatulika la Yehova? Kodi mumawathandiza kudziwa zoona zokhudza Mulungu wathu? Mukamachita zimenezi, mumakhala mukutamanda dzina lake. Pitirizani kutamanda dzina loyera la Yehova, pothandiza anthu kuti adziwe zenizeni zokhudza Mwiniwake wa dzinali. Mukatero mudzawathandiza kuti apulumuke. Mudzakhalanso mukutsatira Mfumu yanu Khristu Yesu. Ndipo koposa zonse, mudzasangalatsa Atate wanu wachikondi, Yehova. Pitirizani ‘kutamanda dzina lake kwamuyaya.’—Sal. 145:2.
KODI KUTAMANDA DZINA LA MULUNGU . . .
-
kumasangalatsa bwanji Yehova?
-
kumasangalatsa bwanji Khristu Yesu?
-
kumathandiza bwanji kuti anthu adzapulumuke?
NYIMBO NA. 2 Dzina Lanu Ndinu Yehova