Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

A Burnett, a Simone, Eston ndi Caleb

Anadzipereka Ndi Mtima Wonse ku Oceania

Anadzipereka Ndi Mtima Wonse ku Oceania

A RENEÉ a ku Australia azaka za m’ma 30, anakulira m’banja limene anthu ake ankakonda kwambiri kulalikira. Mlongoyu ananena kuti: “Nthawi zambiri tinkasamukira kumadera amene kukufunika ofalitsa ambiri. Makolo anga ankayesetsa kuti tizikhala osangalala. Nditakula n’kukhala ndi ana awiri, ndinkafuna kuti nawonso azikhala ndi moyo wosangalala.”

Amuna awo a Reneé ndi a Shane ndipo ali ndi zaka za m’ma 30. Nawonso anali ndi maganizo ngati a akazi awo ndipo anati: “Mwana wathu wachiwiri atangobadwa, tinawerenga nkhani ina mu Nsanja ya Olonda yomwe inafotokoza za banja lomwe linapita pa boti kukalalikira kuzilumba za Tonga zomwe zili kum’mwera chakumadzulo kwa nyanja ya Pacific. * Nkhaniyi inatilimbikitsa moti tinalemba kalata ku ofesi ya nthambi ya ku Australia ndi ya ku New Zealand, yopempha kuti atiuze kumene kukufunika ofalitsa ambiri. * N’zochititsa chidwi kuti anatiuza kuti tipite kuzilumba za Tonga, kumene kunapita banja lomwe linatchulidwa mu Nsanja ya Olonda ija.

Jacob, a Reneé, Skye ndi a Shane

A Shane ndi akazi awo komanso ana awo awiri Jacob ndi Skye, anakhala ku Tonga pafupifupi chaka chimodzi. Koma chifukwa cha zipolowe zomwe zinkachitika ku Tonga, anabwerera ku Australia. Komabe sanasinthe cholinga chawo chofuna kuchita zambiri. Choncho mu 2011, anasamukira pachilumba cha Norfolk chomwe chili pa mtunda wa makilomita 1,500 chakum’mawa kwa dziko la Australia. Kodi zinthu zinawayendera bwanji kumeneko? Mwana wawo Jacob, yemwe pano ali ndi zaka 14, ananena kuti: “Yehova watisamalira komanso watithandiza kuti tizisangalala ndi ntchito yolalikira.”

MABANJA AMENE ANADZIPEREKA KUKATUMIKIRA KUMADERA ENA

Mofanana ndi banja la a Shane, mabanja ena ambiri adzipereka kuti akatumikire kumadera ena. N’chifukwa chiyani anaganiza zochita zimenezi?

“Popeza anthu ambiri a kuno amamvetsera, tinkafuna kuti akhale ndi mwayi wophunzira Baibulo mlungu uliwonse.”​—A Burnett

A Burnett ndi akazi awo a Simone ali ndi zaka za m’ma 30 ndipo ali ndi ana awiri, Eston wazaka 12 ndi Caleb wazaka 9. Banjali linasamukira kutauni ina ya ku Queensland m’dziko la Australia. A Burnett anati: “Abale ndi alongo amangolalikira kudera lino pakatha zaka zitatu kapena 4 zilizonse. Koma popeza anthu ambiri akuno amamvetsera, tinkafuna kuti akhale ndi mwayi wophunzira Baibulo mlungu uliwonse.”

Jim, Jack, a Mark ndi a Karen

A Mark ndi akazi awo a Karen, omwe ali ndi zaka za m’ma 50, anatumikirapo m’mipingo ingapo ya kufupi ndi mzinda wa Sydney, ku Australia. Kenako anasamukira kutauni ina yakumpoto kwa Australia limodzi ndi ana awo atatu, Jessica, Jim ndi Jack. A Mark anati: “Ndimakonda kwambiri anthu, choncho ndinkafuna kukakhala kumene ndingathandize anthu ambiri mumpingo ndiponso mu utumiki.” Poyamba akazi awo sankafuna kusamuka koma anati: “Amuna anga ndiponso anthu ena atandilimbikitsa, ndinavomera kuti tisamuke. Panopa ndimaona kuti tinachita bwino kusamuka.”

A Ben, Jade, Bria ndi a Carolyn

A Ben ndi akazi awo a Carolyn a ku Queensland ku Australia, nthawi ina anatumikirapo ngati apainiya apadera pachilumba cha Timor ku Timor-Leste m’dziko la Indonesia. Koma patapita nthawi anabwerera ku Queensland. A Ben anafotokoza zimene zinkachitika pamene anali ku Timor-Leste. Iwo anati: “Ntchito yolalikira inkayenda bwino kwambiri ndipo abale ankatithandiza moti zinali zovuta kwambiri kuti tichokeko. Ngakhale kuti tinachoka, tinkafunitsitsabe titabwererako moti ana athu atabadwa, tinangowadikira kuti akule.” Choncho mu 2011, iwo ndi ana awo aang’ono Jade ndi Bria, anabwerera ku Timor-Leste. A Carolyn anati: “Tinkafuna kuti ana athu azitumikira Yehova mosangalala pocheza ndi amishonale, anthu a ku Beteli komanso apainiya apadera.”

ZIMENE ANACHITA POKONZEKERA

Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge?” (Luka 14:28) N’chimodzimodzinso ngati banja laganiza zosamukira kudera lina. Limafunika kukonzekera bwino. Koma kodi ndi zinthu ziti zimene liyenera kuganizira pokonzekera?

UBWENZI WAWO NDI YEHOVA: A Ben anati: “Tinkafuna kukathandiza anthu ena osati kuyembekezera kuti iwowo azikatithandiza. Choncho tisanasamuke tinkayesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova komanso kuchita zambiri mu utumiki ndiponso mumpingo.”

Jacob yemwe tamutchula kale uja anati: “Tisanasamuke, tinkawerenga nkhani zambiri za mu Nsanja ya Olonda ndiponso mu Galamukani! zokhudza mabanja amene anasamukira kumadera ofunika ofalitsa ambiri. Tinkakambirana mavuto amene mabanjawo ankakumana nawo ndiponso zimene Yehova anachita powathandiza.” Mchemwali wake Skye amene ali ndi zaka 11 anati: “Ndinkapemphera pafupipafupi ndikakhala ndekha komanso ndi makolo anga.”

KUKONZEKERETSA MAGANIZO: A Reneé anati: “Tinkakhala m’dera limene ndinkalikonda kwambiri komanso pafupi ndi achibale ndiponso anzathu. Koma ndinkayesetsa kuganizira madalitso amene tingapeze tikasamuka m’malo moganizira kwambiri zinthu zimene tingazisiye.”

CHIKHALIDWE CHA KUMENEKO: Mabanja ambiri amafufuza kuti adziwe mmene zinthu zilili kudera limene akusamukira. Mwachitsanzo, a Mark anati: “Tinawerenga nkhani zambiri zokhudza tauni yomwe tinkasamukira. Komanso abale akutauniyi ankatitumizira nyuzipepala za kumeneko. Izi zinatithandiza kudziwa chikhalidwe cha anthu am’tauniyi.”

A Shane aja anati: “Tisanasamuke, ndinkayesetsa kutsanzira kwambiri makhalidwe a Khristu. Ndinkadziwa kuti ndikakhala wokhulupirika, wofatsa, woona mtima ndiponso wakhama, ndingathe kukhala bwino ndi anthu kulikonse.”

ZIMENE AMACHITA AKAKUMANA NDI MAVUTO

Anthu ambiri amene amasamukira kudera lina amati zimawayendera bwino ngati amakhala ololera, amaona zinthu moyenera komanso amapewa kudandaula kwambiri akakumana ndi mavuto.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi a Reneé. Iwo anati: “Ndaphunzira kuchita zinthu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo pachilumba cha Norfolk, sitima zikalephera kubwera chifukwa choti nyanja sili bwino, zakudya zimasowa ndipo zimadula. Choncho ndaphunzira kugwiritsa ntchito bwino zinthu zochepa zomwe tili nazo.” Amuna awo anati: “Tinakonzanso bajeti ndipo timayesetsa kuitsatira nthawi zonse.”

Mwana wawo, Jacob, anafotokoza vuto lina limene amakumana nalo. Anati: “Ndinalibe mnzanga wamsinkhu wanga chifukwa mumpingo wathu munali banja lathu ndi anthu ena 7 basi, omwenso anali akuluakulu okhaokha. Komabe popeza ndinkayenda nawo mu utumiki, tinayamba kugwirizana ndipo anakhala anzanga.”

Jim, yemwe panopa ali ndi zaka 21, ankakumananso ndi vuto ngati lomweli. Anati: “Mpingo wapafupi ndi wathu uli pa mtunda wa makilomita 725. Choncho sitikhala ndi mpata wocheza ndi anthu a m’mipingo ina. Koma timayembekezera kwambiri nthawi ya misonkhano ikuluikulu. Pa nthawiyi timayesetsa kufika msanga kuti tikhale ndi nthawi yambiri yocheza ndi abale ndi alongo athu.”

“TINACHITA BWINO KUBWERA KUNO”

Baibulo limati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa.” (Miy. 10:22) Padziko lonse, abale ndi alongo amene akutumikira kumadera kumene kulibe ofalitsa ambiri amaona kuti mawu amenewa ndi oona.

A Mark anati: “Tikuona kuti kukatumikira kudera lina kwathandiza kwambiri ana athu, ndipo amenewa ndi madalitso aakulu. Panopa ana athu achinyamata amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova aziwasamalira akamaika za Ufumu pamalo oyamba. Sakanakhala ndi chikhulupiriro chimenechi zikanakhala kuti sitinasamuke.”

A Shane anati: “Panopa ndimagwirizana kwambiri ndi mkazi wanga ndiponso ana anga. Akamafotokoza zimene Yehova wawachitira, ndimasangalala kwambiri.” Mwana wawo, Jacob, ananena kuti: “Ndikusangalala kwambiri ndipo ndikuona kuti tinachita bwino kubwera kuno.”

^ ndime 3 Onani nkhani yakuti, “Mabwenzi a Mulungu pa Zisumbu za Tonga” mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 2004, tsamba 8 mpaka 11.

^ ndime 3 Mu 2012, ofesi ya nthambi ya ku Australia ndi ya ku New Zealand anaziphatikiza n’kukhala nthambi imodzi yomwe tsopano imadziwika kuti Australasia.