“Tipita Nanu Limodzi”
“Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—ZEK. 8:23.
NYIMBO: 65, 122
1, 2. (a) Kodi Yehova ananeneratu kuti m’nthawi yathu ino kudzachitika zinthu zotani? (b) Kodi m’nkhaniyi tikambirana mafunso ati? (Onani chithunzi pamwambapa.)
PONENA za nthawi yathu ino, Yehova analosera kuti: “Amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu amitundu ina adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zek. 8:23) Mofanana ndi amuna 10 otchulidwa mulembali, anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi ‘agwira chovala cha munthu amene ndi Myuda.’ Iwo amasangalala kwambiri kuchita zinthu mogwirizana ndi “Isiraeli wa Mulungu,” kapena kuti odzozedwa, podziwa kuti Yehova akudalitsa anthuwa.—Agal. 6:16.
2 Nayenso Yesu anasonyeza kuti anthu a Mulungu azidzachita zinthu mogwirizana kwambiri. Ananena kuti otsatira ake omwe adzapite kumwamba, ndi “kagulu ka nkhosa” ndipo odzakhala padzikoli ndi “nkhosa zina.” Koma anati onse adzakhala ‘m’gulu limodzi’ ndipo adzakhala “ndi m’busa mmodzi.” (Luka 12:32; Yoh. 10:16) Komabe mwina tingafunse kuti: (1) Kodi amene akuyembekeza kudzakhala padzikoli ayenera kudziwa mayina a odzozedwa onse amene alipo masiku ano? (2) Kodi Akhristu odzozedwa ayenera kudziona bwanji? (3) Munthu wina wamumpingo mwathu akayamba kudya zizindikiro pa Chikumbutso, kodi tiyenera kutani? (4) Kodi tiyenera kudandaula ngati chiwerengero cha anthu amene anadya zizindikiro chakwera? Tiyeni tikambirane mafunso amenewa.
KODI TIYENERA KUDZIWA MAYINA A ODZOZEDWA ONSE OMWE ALIPO?
3. N’chifukwa chiyani n’zosatheka kudziwa anthu amene adzakhale m’gulu la 144,000?
3 Kodi a nkhosa zina ayenera kudziwa mayina a odzozedwa onse a masiku ano? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti munthu amene wadzozedwa amakhala kuti wangosankhidwa koma sizinatsimikizike kuti adzalandiradi mphoto yake. Satana amadziwanso zimenezi ndipo n’chifukwa chake amagwiritsa ntchito “aneneri onyenga” kuti ‘asocheretse osankhidwawo.’ (Mat. 24:24) Akhristu odzozedwa sadziwa ngati adzalandiredi mphoto yawo, mpaka pamene Yehova wawadinda chidindo chomaliza posonyeza kuti ndi oyenera kulandira mphotoyo. Yehova amachita zimenezi wodzozedwa wokhulupirika asanamwalire. Koma kwa odzozedwa amene angakhalebe ndi moyo, Yehova adzawadinda chidindochi “chisautso chachikulu” chitangotsala pang’ono kuyamba. (Chiv. 2:10; 7:3, 14) Choncho panopa n’zosatheka kudziwa anthu amene adzakhale m’gulu la 144,000. [1]
4. Popeza n’zosatheka kudziwa mayina a odzozedwa onse amene ali padzikoli, kodi a nkhosa zina ‘angapite nawo’ bwanji?
4 Popeza panopa n’zosatheka kudziwa mayina a odzozedwa onse, kodi a nkhosa zina ‘angapite nawo limodzi’ bwanji? Ulosi wa Zekariya uja umanena kuti anthu 10 “adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” Ngakhale kuti lembali latchula “Myuda,” limasonyeza kuti mawuwa sakuimira munthu mmodzi koma gulu la odzozedwa. A nkhosa zina akudziwa zimenezi ndipo amatumikira Yehova limodzi ndi gululi. Sikuti amafunika kudziwa munthu aliyense m’gululi n’kumamutsatira. Yesu ndiye Mtsogoleri wathu ndipo Baibulo limati tiyenera kutsatira iye yekha basi.—Mat. 23:10.
KODI AKHRISTU ODZOZEDWA AYENERA KUDZIONA BWANJI?
5. Kodi odzozedwa ayenera kuganizira kwambiri mawu ati a Paulo, ndipo n’chifukwa chiyani?
5 Anthu amene amadya zizindikiro pa Chikumbutso ayenera kuganizira kwambiri zimene lemba la 1 Akorinto 11:27-29 limanena. (Werengani.) Kodi palembali Paulo ankatanthauza chiyani? Ankatanthauza kuti ngati wodzozedwa sakutumikira Mulungu mokhulupirika, ndiye kuti amadya zizindikiro “mosayenerera.” (Aheb. 6:4-6; 10:26-29) Lembali limathandizanso odzozedwa kukumbukira kuti ayenera kukhalabe okhulupirika kuti adzalandire mphoto yawo. Ayenera kuchita zimenezi mpaka ‘adzapeze mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba, chodzera mwa Khristu Yesu.’—Afil. 3:13-16.
6. Kodi Akhristu odzozedwa ayenera kumadziona bwanji?
6 Paulo anauza Akhristu odzozedwa kuti ‘aziyenda moyenera.’ Kodi angachite bwanji zimenezi? Iye anati: “Muziyenda modzichepetsa nthawi zonse, mofatsa, moleza mtima, ndiponso mololerana m’chikondi. Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa.” (Aef. 4:1-3) Mzimu wa Mulungu umathandiza munthu kuti akhale wodzichepetsa osati wonyada. (Akol. 3:12) Akhristu odzozedwa saganiza kuti mzimu woyera umawathandiza kwambiri kuposa a nkhosa zina. Sanenanso kuti amadziwa zinthu zina zapadera kapena ndi abwino kuposa ena. Iwo salimbikitsanso anthu ena kuti ayambe kudya zizindikiro chifukwa amadziwa kuti Yehova ndi amene amasankha odzozedwa.
7, 8. Kodi Akhristu odzozedwa sayembekezera chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
7 Ngakhale kuti Akhristu odzozedwa amadziwa kuti ali ndi mwayi waukulu, safuna kuti anthu aziwapatsa ulemu wapadera. (Aef. 1:18, 19; werengani Afilipi 2:2, 3.) Mzimu wa Mulungu umawathandiza kudziwa kuti adzozedwa, koma sudziwitsa anthu onse za zimenezi. Choncho sadabwa ngati anthu ena zingawavute kukhulupirira kuti iwowo adzozedwa. Amadziwanso kuti Baibulo limalangiza Akhristu kuti asamangokhulupirira aliyense amene amati wapatsidwa udindo wapadera ndi Mulungu. (Chiv. 2:2) Odzozedwa akakumana ndi munthu, sanena kuti iwo ndi odzozedwa ngati njira yodzidziwikitsira. Popeza kuti safuna kupatsidwa ulemu wapadera, sakonda kuuza anthu zoti ndi odzozedwa kapena kukamba za mphoto yomwe adzalandire kumwamba.—1 Akor. 1:28, 29; werengani 1 Akorinto 4:6-8.
8 Komanso Akhristu odzozedwa sadziona kuti ali m’gulu lapadera kwambiri. Safufuzanso anthu ena amene ndi odzozedwa n’cholinga choti azicheza okhaokha kapena kuphunzira limodzi Baibulo. (Agal. 1:15-17) Amadziwa kuti izi n’zosagwirizana ndi mzimu woyera umene umathandiza kuti anthu onse a Mulungu azikhala mwamtendere komanso mogwirizana.—Werengani Aroma 16:17, 18.
KODI TIZICHITA BWANJI ZINTHU NDI ODZOZEDWA?
9. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala pochita zinthu ndi odzozedwa? (Onani bokosi lakuti, “ Chikondi ‘Sichichita Zosayenera.’”)
9 Kodi tizichita bwanji zinthu ndi anthu odzozedwa? Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Nonsenu ndinu abale.” Ananenanso kuti: “Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.” (Mat. 23:8-12) Choncho sitiyenera kupereka ulemu wapadera kwa anthu ena, ngakhale kwa abale odzozedwa a Khristu. Baibulo limatiuza kuti tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha anthu amene akutitsogolera, koma silinena kuti tiyenera kulemekeza munthu wina ngati kuti ndi mtsogoleri wathu. (Aheb. 13:7) N’zoona kuti Baibulo limanena kuti anthu ena ayenera kupatsidwa “ulemu waukulu.” Komabe anthuwo ayenera kupatsidwa ulemu osati chifukwa choti ndi odzozedwa koma chifukwa ‘amatsogolera bwino’ komanso “amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” (1 Tim. 5:17) Choncho odzozedwa akhoza kuchita manyazi abale ndi alongo akamawalemekeza kwambiri kuposa anthu ena. Komanso odzozedwa akamapatsidwa ulemu wapadera, mwina zingawavute kuti akhalebe odzichepetsa. (Aroma 12:3) Palibe Mkhristu amene angafune kuchita zinthu zimene zingapangitse kuti m’bale wina wa Yesu akhale wosakhulupirika.—Luka 17:2.
10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza odzozedwa?
10 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza odzozedwa? Tizipewa kulowerera nkhani zimene sizikutikhudza. (1 Ates. 4:11; 2 Ates. 3:11) Mwachitsanzo, si bwino kuwafunsa mafunso monga lakuti, ‘Kodi munadziwa bwanji kuti mwadzozedwa?’ Tisamaganizenso kuti makolo, achibale komanso mwamuna kapena mkazi wa munthu wodzozedwa nayenso ndi wodzozedwa. Munthu sadzozedwa potengera banja limene wachokera. (1 Ates. 2:12) Tizipewanso kufunsa mwamuna kapena mkazi wa munthu wodzozedwa mafunso okhudza mmene amamvera akaganizira kuti sadzakhala limodzi ndi mnzakeyo m’Paradaiso. M’malo mowafunsa mafunso amene angawakhumudwitse, tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova ‘adzatambasula dzanja lake ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.’—Sal. 145:16.
11. Kodi tikamachita zinthu moyenera ndi odzozedwa tingapewe mavuto otani?
11 Tikamachita zinthu moyenera ndi odzozedwa timapewanso mavuto ena. Baibulo limanena kuti nthawi zina mumpingo mukhoza kupezeka “abale onyenga.” (Agal. 2:4, 5; 1 Yoh. 2:19) Abale onyengawa akhoza kunena kuti ndi odzozedwa. Komanso Akhristu ena odzozedwa angasiye kukhala okhulupirika. (Mat. 25:10-12; 2 Pet. 2:20, 21) Tikamapewa ‘kutamanda anthu’ sitidzakhumudwa kwambiri kapena kubwerera m’mbuyo ngati m’bale wodziwika bwino kapena amene wakhala Mkhristu kwa zaka zambiri wasiya kutumikira Yehova.—Yuda 16.
KODI TIZIDANDAULA CHIWERENGERO CHA ANTHU AMENE ANADYA ZIZINDIKIRO CHIKAKWERA?
12, 13. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudandaula ngati chiwerengero cha anthu amene anadya zizindikiro pa Chikumbutso chikukwera?
12 Kwa zaka zambiri m’mbuyomu, chiwerengero cha anthu amene ankadya zizindikiro pa Chikumbutso chinkatsika. Koma pa zaka zingapo zapitazi, taona kuti chiwerengerochi chayambanso kukwera. Kodi tiyenera kudandaula ndi zimenezi? Ayi. Tiyeni tione zifukwa zake.
13 “Yehova amadziwa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Abale amene amawerenga anthu omwe adya zizindikiro pa Chikumbutso, sangadziwe amene ndi wodzozedwadi. Pa gulu la anthu amene adya zizindikirowo pamakhalanso ena amene sayenera kudya. Ena amene amadya zizindikiro, pakapita nthawi amasiya. Palinso ena amene saganiza bwino chifukwa cha matenda ndipo amadya zizindikiro poganiza kuti adzozedwa. Choncho sitikudziwa chiwerengero cholondola cha odzozedwa enieni amene atsala padzikoli.
14. Kodi Baibulo limati chiyani zokhudza chiwerengero cha odzozedwa amene adzakhale padzikoli chisautso chachikulu chikamadzayamba?
Mat. 24:31) N’zoona kuti Malemba amanena kuti m’masiku otsiriza padzikoli padzakhala odzozedwa ochepa. (Chiv. 12:17) Komabe sanena kuti adzakhalapo angati chisautso chachikulu chikamadzayamba.
14 Odzozedwa azidzapezekabe m’madera ambiri padzikoli pa nthawi imene Yesu adzabwere kudzawatenga. Baibulo limati pa nthawiyo Yesu “adzatumiza angelo ake ndi kulira kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera kumphepo zinayi, kuchokera kumalekezero a m’mlengalenga mpaka kumalekezero ena.” (15, 16. Kodi tiyenera kukumbukira zotani zokhudza anthu amene Mulungu amawasankha kukhala m’gulu la 144,000?
15 Yehova amadzoza anthu pa nthawi imene waona kuti ndi yoyenera. (Aroma 8:28-30) Iye anayamba kusankha odzozedwa Yesu ataukitsidwa ndipo zikuoneka kuti Akhristu onse a m’nthawi ya atumwi anali odzozedwa. Kuchokera nthawi imeneyo kudzafika kumayambiriro kwa masiku otsiriza, anthu ambiri amene ankati ndi otsatira a Yesu anali Akhristu onyenga. Yesu ananena kuti anthuwa anali ngati “namsongole.” Komabe pa nthawiyo, Yehova anapitiriza kudzoza anthu ena ndipo Yesu anati amenewa anali ngati “tirigu.” (Mat. 13:24-30) M’masiku otsiriza ano, Yehova wakhalanso akusankha anthu oti akhale m’gulu la 144,000. [2] Ngati Mulungu wasankha kudzoza anthu ena m’masiku otsiriza kapena kumapeto kwake, tiyenera kungovomereza podziwa kuti nthawi zonse amachita zinthu mwanzeru. (Yes. 45:9; Dan. 4:35; werengani Aroma 9:11, 16.) [3] Tiyenera kusamala kuti tisakhale ngati antchito amene anayamba kudandaula chifukwa cha malipiro amene mbuye wawo anawapatsa. Anthuwo anadandaula chifukwa analandira malipiro ofanana ndi a anthu amene anayamba ntchito mochedwa.—Werengani Mateyu 20:8-15.
16 Sikuti onse amene akuyembekezera kudzapita kumwamba ali m’gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) M’nthawi ya atumwi, Yehova ndi Yesu ankadyetsa anthu kudzera mwa anthu ochepa. Paja Akhristu odzozedwa ochepa okha ndi amene analemba nawo Malemba Achigiriki. Masiku anonso Akhristu odzozedwa ochepa ndi amene asankhidwa kuti azipereka chakudya chauzimu “pa nthawi yoyenera.”
17. Fotokozani mwachidule zimene taphunzira m’nkhaniyi.
17 Kodi taphunzira chiyani m’nkhaniyi? Taona kuti Yehova wasankha kuti pakhale magulu awiri a atumiki ake. Akhristu odzozedwa omwe ali ngati “Myuda” adzakhala ndi moyo kumwamba. Pomwe amene ali ngati “amuna 10” adzakhala ndi moyo padziko lapansi. Komabe Yehova amapereka malamulo ofanana kwa anthu a m’magulu awiri onsewa ndipo amafuna kuti onse akhale okhulupirika, odzichepetsa komanso ogwirizana. Onse ayenera kuchita zimene angathe kuti mumpingo muzikhala mtendere. Pamene mapeto akuyandikira, tiyeni tonse tipitirize kutsatira Khristu ndiponso kutumikira Yehova mogwirizana.
^ [1] (ndime 3) Lemba la Salimo 87:5, 6 limasonyeza kuti mwina m’tsogolo mayina a anthu onse amene azidzalamulira ndi Yesu kumwamba adzadziwika.—Aroma 8:19.
^ [2] (ndime 15) Ngakhale kuti lemba la Machitidwe 2:33 limasonyeza kuti Yehova amagwiritsa ntchito Yesu podzoza anthu, Yehova ndi amene amasankha anthuwo.
^ [3] (ndime 15) Kuti mudziwe zambiri, werengani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2007, tsamba 30 mpaka 31.