Kudzichepetsa N’kofunika Kwambiri
“Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.”—MIY. 11:2.
NYIMBO: 38, 69
1, 2. N’chifukwa chiyani Mulungu anasiya kukonda Sauli? (Onani chithunzi pamwambapa.)
SAULI, yemwe anali mfumu ya Isiraeli, poyamba anali munthu wabwino komanso wodzichepetsa. (1 Sam. 9:1, 2, 21; 10:20-24) Koma pasanapite nthawi anayamba kudzikuza. Mwachitsanzo, pa nthawi ina iye ankayembekezera mneneri Samueli kuti adzapereke nsembe ku Giligala. Koma Samueliyo anachedwa. Afilisiti anali atatsala pang’ono kufika kuti adzamenyane ndi Aisiraeli ndipo Aisiraeli ena anayamba kubalalika. Choncho Sauli analephera kudikira moleza mtima ndipo anapereka nsembe kwa Mulungu ngakhale kuti sunali udindo wake kuchita zimenezi. Yehova sanasangalale ndi zimene Sauli anachitazi.—1 Sam. 13:5-9.
2 Samueli atafika anadzudzula Sauli. Koma m’malo movomereza kulakwa kwake iye anayamba kudziikira kumbuyo, kuimba mlandu anthu ena komanso kuchepetsa tchimo lake. (1 Sam. 13:10-14) Kungoyambira nthawi imeneyi, Sauli anayamba kuchita zinthu zambiri zoipa. Izi zinachititsa kuti ufumu uchotsedwe kubanja lake komanso kuti Yehova asiye kumukonda. (1 Sam. 15:22, 23) Choncho zinthu sizinamuthere bwino ngakhale kuti anayamba bwino kwambiri.—1 Sam. 31:1-6.
3. (a) Kodi anthu ambiri ali ndi maganizo otani pa nkhani ya kudzichepetsa? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
3 Masiku ano anthu ambiri amaganiza kuti kukhala odzichepetsa kungachititse kuti asatchuke komanso kuti zinthu zisamawayendere bwino. Choncho safuna n’komwe kukhala odzichepetsa. Mwachitsanzo, wochita zisudzo wina wotchuka, yemwenso ndi wandale, ananena kuti: “Ine sindiyerekeza n’komwe kukhala wodzichepetsa. Ndipo ndimakhulupirira kuti sindidzachita zimenezo.” Koma kodi n’chifukwa chiyani kudzichepetsa n’kofunikabe masiku ano? Kodi munthu wodzichepetsa amatani? Nanga tingatani kuti nthawi zonse tizikhala odzichepetsa? M’nkhaniyi tikambirana mafunso awiri oyambawa, ndipo lachitatuli tidzakambirana m’nkhani yotsatira.
N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZICHEPETSA N’KOFUNIKA?
4. Kodi munthu wodzikuza amatani?
4 Baibulo limasonyeza kuti munthu wodzikuza amakumana ndi mavuto koma wodzichepetsa zinthu zimamuyendera bwino. (Werengani Miyambo 11:2.) Ndiyetu mpake kuti Davide anapempha Yehova kuti: “Mundiletse kuchita modzikuza, ine mtumiki wanu.” (Sal. 19:13) Kodi munthu ‘wodzikuza’ amatani? Amachita zinthu zomwe si udindo wake ndipo nthawi zambiri amachita zimenezi chifukwa cha kunyada kapena chifukwa cholephera kuleza mtima. Popeza ndife ochimwa, tonsefe pa nthawi ina tinachitapo zinthu modzikuza. Koma chitsanzo cha Mfumu Sauli chikusonyeza kuti tikalola zimenezi kukhala chizolowezi, tingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Lemba la Salimo 119:21 limati Yehova ‘amadzudzula odzikuza.’ N’chifukwa chiyani zili choncho?
5. N’chifukwa chiyani tingati kukhala wodzikuza n’koopsa?
5 Kukhala ndi chizolowezi chochita zinthu modzikuza n’koopsa. Tikutero pa zifukwa zitatu. Choyamba tikamachita zinthu modzikuza timasonyeza kuti sitilemekeza Yehova yemwe ndi Wolamulira wathu. Chachiwiri, tikamachita zinthu zomwe si udindo wathu, anthu ena sangasangalale ndipo tingathe kuyambana nawo. (Miy. 13:10) Chachitatu, zikadziwika kuti tachita zinthu modzikuza, tingachite manyazi. (Luka 14:8, 9) Apatu zikusonyezeratu kuti kudzikuza si kwabwino. Mpake kuti Malemba amatilimbikitsa kuti tikhale odzichepetsa.
KODI MUNTHU WODZICHEPETSA AMATANI?
6, 7. Kodi munthu wodzichepetsa amatani?
6 M’Baibulo mawu akuti kudzichepetsa amatanthauza kukhala wosanyada komanso wosadzikuza. (Afil. 2:3) Munthu wodzichepetsa amazindikira zimene sayenera kuchita ndipo akalakwitsa amavomereza kulakwa kwake. Iye amamvetsera maganizo a ena ndipo amaphunzirapo kanthu. Choncho munthu wodzichepetsa amasangalatsa kwambiri Yehova.
7 Munthu wodzichepetsa amazindikiranso kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse kuchita. Iye amadziwanso zinthu zimene si udindo wake kuchita. Zimenezi zimamuthandiza kuti azilemekeza ena komanso aziwachitira zinthu mokoma mtima.
8. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasonyeze kuti tayamba kuchita zinthu modzikuza?
8 Koma mosazindikira munthu angayambe kuganiza kapena kuchita zinthu modzikuza. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Mwina tingayambe Aroma 12:16) Kapena tingayambe kuchita zinthu modzitama kuti anthu atione. (1 Tim. 2:9, 10) Mwinanso tingayambe kugwiritsa ntchito udindo wathu, kapena zinthu zina pofuna kuti anthu aziyendera maganizo athu.—1 Akor. 4:6.
kudziona kuti ndife ofunika kuposa ena chifukwa choti tili ndi udindo winawake. (9. Kodi n’chiyani chimachititsa ena kuyamba kudzikuza? Perekani zitsanzo za m’Baibulo.
9 Tonsefe tingayambe kuchita zinthu modzikuza ngati titalola kuti zilakolako za thupi zizititsogolera. Anthu ambiri amayamba kudzikuza chifukwa cha nsanje, kufuna udindo komanso chifukwa chosaugwira mtima. Anthu ena a m’Baibulo monga Abisalomu, Uziya komanso Nebukadinezara anayamba kudzikuza chifukwa chotsatira “ntchito za thupi” ndipo Yehova anawachititsa manyazi.—2 Sam. 15:1-6; 18:9-17; 2 Mbiri 26:16-21; Dan. 5:18-21.
10. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuweruza ena? Perekani zitsanzo za m’Baibulo.
10 Koma palinso zifukwa zina zimene zingapangitse munthu kuti achite zinthu zooneka ngati si wodzichepetsa. Mwachitsanzo, taganizirani za Abimeleki ndi Petulo. (Gen. 20:2-7; Mat. 26:31-35) Kodi anthu amenewa tingati anali odzikuza? Kapena vuto ndi loti sankadziwa zonse kapena anachita zinthu asanaganize kaye? Popeza sitidziwa za mumtima mwa munthu, si bwino kuthamangira kuweruza ena.—Werengani Yakobo 4:12.
TIZIKHUTIRA NDI MALO ATHU M’GULU LA YEHOVA
11. Kodi munthu wodzichepetsa amazindikira chiyani?
11 Munthu wodzichepetsa amazindikira malo ake m’gulu la Yehova. Popeza Yehova ndi Mulungu wadongosolo, amapatsa aliyense zochita m’gulu lake. Zochitazi sizikhala zofanana koma tonse ndife ofunika kwambiri. Yehova ndi wokoma mtima ndipo anatipatsa mphatso zosiyanasiyana, luso komanso zinthu zina zimene tingagwiritse ntchito pomutumikira komanso pothandiza ena. (Aroma 12:4-8) Yehova amaona kuti tonsefe tili ngati oyang’anira ndipo izi zimasonyeza kuti amatilemekeza, kutidalira komanso amayembekezera kuti tikwaniritse udindo wathu.—Werengani 1 Petulo 4:10.
12, 13. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa ngati utumiki wathu wasintha?
12 Koma zimene tikuchita m’gulu la Yehova zikhoza kusintha nthawi iliyonse. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yesu. Poyamba anali awiriwiri ndi Yehova m’chilengedwe chonsechi. (Miy. 8:22) Koma kenako anathandiza nawo polenga angelo, zinthu zakumwamba ndi zapadziko lapansi komanso anthu. (Akol. 1:16) Patapita nthawi, anasinthanso n’kubwera padzikoli. Poyamba anali kamwana ndipo kenako anakhala munthu wamkulu. (Afil. 2:7) Iye atafa anaukitsidwa n’kubwerera kumwamba ndipo mu 1914 anakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Aheb. 2:9) Komatu amenewa si mapeto a kusintha kwa utumiki wake. Pambuyo pa ulamuliro wake wa zaka 1,000, iye adzapereka Ufumu kwa Yehova kuti “Mulungu akhale zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akor. 15:28.
13 Nafenso utumiki wathu ukhoza kusintha mwina chifukwa cha zinthu zina zimene zachitika pa moyo wathu. Mwachitsanzo, zimene munkachita muli nokha zikhoza kusintha mukakhala pa banja kapena mukakhala ndi ana. Komanso achikulire ena angaone kuti maudindo awo achepa ndipo angathe Aheb. 6:10.
kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Mwachidule tingati zinthu zikasintha pa moyo wathu, utumiki komanso udindo wathu umasinthanso. Tikhoza kupezeka kuti tayamba kuchita zambiri kapena zochepa. Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, timadwaladwala kapena ayi, Yehova amatiganizira ndipo amadziwa zimene aliyense angachite bwino pomutumikira. Iye sayembekezera zimene sitingakwanitse ndipo amayamikira zimene timayesetsa kumuchitira.—14. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kuti tizikhutira ndi zimene tikuchita komanso kuti tizisangalala?
14 Yesu ankasangalala ndi utumiki uliwonse umene anapatsidwa ndipo ifenso tikhoza kumasangalala ndi utumiki wathu. (Miy. 8:30, 31) Munthu wodzichepetsa amakhutira ndi utumiki kapena udindo umene ali nawo mumpingo. Iye sadandaula kuti sanapatsidwe utumiki winawake kapena kuti anzake apatsidwa udindo wina. M’malomwake amasangalala ndi utumiki umene ali nawo n’kumauchita mwakhama podziwa kuti wachokera kwa Yehova. Komanso amalemekeza anthu amene apatsidwa udindo ndipo amawathandiza podziwa kuti udindo wawowo wachokeranso kwa Yehova.—Aroma 12:10.
KHALANI NDI MAGANIZO OYENERA PA NKHANI YA KUDZICHEPETSA
15. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Gidiyoni?
15 Gidiyoni ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kudzichepetsa. Mngelo wa Yehova atabwera kwa iye, Gidiyoni anavomereza modzichepetsa kuti anali munthu wamba. Ower. 6:15) Yehova atamupatsa ntchito yoti achite, iye anaonetsetsa kuti wamvetsa zoyenera kuchita ndipo anadalira Yehova kuti amutsogolere. (Ower. 6:36-40) Gidiyoni anali munthu wolimba mtima. Komabe ankachita zinthu mwanzeru ndiponso mosamala. (Ower. 6:11, 27) Komanso iye sanagwiritse ntchito udindo wake ngati mwayi woti atchuke. M’malomwake atangomaliza ntchito imene Yehova anamupatsa, anabwerera kwawo.—Ower. 8:22, 23, 29.
(16, 17. Kodi munthu wodzichepetsa amadzifunsa mafunso ati akapatsidwa utumiki watsopano?
16 Kukhala odzichepetsa sikutanthauza kuti tisamayesetse kuti tiyenerere udindo winawake kapena tizikana udindo popanda chifukwa. Paja Malemba amatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kupita patsogolo. (1 Tim. 4:13-15) Koma kodi nthawi zonse timafunika kupatsidwa utumiki wina kuti zioneke kuti tikupita patsogolo? Ayi. Yehova angatidalitse ndipo tingathe kumapita patsogolo ngakhale kuti sitinasinthe utumiki. Tingathenso kumasonyeza kwambiri makhalidwe abwino n’kumayesetsanso kuti tizichita bwino utumiki umene tili nawo panopa.
17 Munthu wodzichepetsa akapatsidwa utumiki amayamba wafufuza zoyenera kuchita pa utumikiwo. Kenako amaganizira bwino nkhaniyo kuti aone ngati angakwanitse. Mwachitsanzo, amadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikayamba utumikiwu ndizipeza nthawi yochitanso zinthu zina zofunika kwambiri? Ngati nthawi sizipezeka, kodi n’zotheka kupatsa ena ntchito zina kuti ndizipeza nthawi yochita utumiki watsopanowu?’ Ngati yankho pa mafunso awiriwa ndi loti ayi, ndiye kuti ndi bwino kupempha kuti apatse ena utumiki watsopanowo. Kupemphera komanso kudzifufuza moona mtima kungathandize kuti tisamavomere zinthu zimene sitingakwanitse.
18. (a) Kodi munthu wodzichepetsa amatani akapatsidwa utumiki watsopano? (b) Kodi munthu wodzichepetsa amatsatira bwanji lemba la Aroma 12:3?
18 Nkhani ya Gidiyoni ikhoza kutithandizanso tikapatsidwa utumiki watsopano. Imatikumbutsa mfundo yoti sitingachite bwino utumiki uliwonse popanda kutsogoleredwa komanso kudalitsidwa ndi Yehova. Paja timalangizidwa kuti: “Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (Mika 6:8) Choncho tikapatsidwa utumiki tizipemphera kwa Yehova. Ndiyeno kuti tidziwe zochita, tizifufuza m’Mawu ake komanso m’malangizo amene gulu lake lapereka. Tikatero timasonyeza kuti tikuzindikira zoti nzeru zathu n’zoperewera poyerekezera ndi za Yehova. Tisamaiwalenso kuti ‘kudzichepetsa kwa Yehova n’kumene kumatikweza’ osati luso lathu. (Sal. 18:35) Tikamayenda modzichepetsa ndi Mulungu tidzapewa kudziona ngati apamwamba kapena ngati osanunkha kanthu.—Werengani Aroma 12:3.
19. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala odzichepetsa?
19 Munthu wodzichepetsa amapereka ulemerero kwa Yehova podziwa kuti iye ndi Mlengi komanso Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. (Chiv. 4:11) Amakhalanso wokhutira ndi zimene akuchita ndipo amakhala wakhama. Amalemekeza maganizo a ena ndipo izi zimalimbikitsa mgwirizano. Iye samadziona kuti ndi wofunika kuposa ena ndipo amakhala wosamala pochita zinthu. Izi zimathandiza kuti asamalakwitselakwitse. Pa zifukwa zimenezi, tikhoza kunena kuti kudzichepetsa n’kofunika kwambiri kwa anthu onse a Mulungu ndipo Yehova amakonda kwambiri anthu odzichepetsa. Koma kodi tingatani kuti tizikhala odzichepetsa nthawi zonse? Tidzaona m’nkhani yotsatira.