Nkhani Yophunzira 3
Yehova Amaona Kuti Ndinu Amtengo Wapatali
“Anatikumbukira pamene [tinali okhumudwa].”—SAL. 136:23.
NYIMBO NA. 33 Umutulire Yehova Nkhawa Zako
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. Kodi atumiki a Yehova ambiri amakumana ndi mavuto otani, nanga zimenezi zimawakhudza bwanji?
TAGANIZIRANI zitsanzo izi: M’bale wachinyamata amupeza ndi matenda oopsa. M’bale wina wachotsedwa ntchito ndipo sakupeza ina ngakhale kuti akufufuza mwakhama. Mlongo akulephera kuchita zambiri potumikira Yehova chifukwa cha uchikulire.
2 Ngati mukukumana ndi mavuto ngati amene tatchulawa, mwina mungamaone kuti ndinu wopanda ntchito. Zimenezi zingachititse kuti musamasangalale, muzidziona kuti ndinu wosafunika komanso mungamavutike kugwirizana ndi anthu ena.
3. Kodi Satana komanso anthu amene amamutsanzira amaona bwanji moyo?
3 Anthu am’dzikoli amatengera maganizo a Satana pa nkhani ya moyo wa anthu. Satana amachitira anthu zinthu ngati kuti ndi osafunika. Iye anasonyeza kuipa mtima pouza Hava kuti adzakhala pa ufulu akapanda kumvera Mulungu, chonsecho akudziwa kuti adzafa. Satana ndi amene amalamulira zinthu zamalonda, zandale komanso zachipembedzo m’dzikoli. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amalonda, andale komanso atsogoleri azipembedzo amatengera maganizo ake osalemekeza moyo komanso anthu.
4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
4 Koma Yehova amafuna tizidziona kuti ndife amtengo wapatali ndipo amatithandiza tikakumana ndi zinthu zimene Sal. 136:23; Aroma 12:3) Munkhaniyi, tiona mmene Yehova amatithandizira (1) tikamadwala, (2) tikakumana ndi mavuto azachuma komanso (3) tikamaona kuti palibe zimene tingachite potumikira Yehova chifukwa cha uchikulire. Koma choyamba, tiyeni tikambirane zimene zingatitsimikizire kuti Yehova amaona kuti ndife amtengo wapatali.
zingatichititse kumva kuti ndife achabechabe. (YEHOVA AMAONA KUTI NDIFE AMTENGO WAPATALI
5. N’chiyani chimakutsimikizirani inuyo kuti anthufe ndi amtengo wapatali kwa Yehova?
5 N’zoona kuti tinapangidwa kuchokera ku fumbi, koma anthufe ndi amtengo wapatali. (Gen. 2:7) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ndife amtengo wapatali kwa Yehova? Iye analenga anthu m’njira yoti azitha kutengera makhalidwe ake. (Gen. 1:27) Apatu anatilemekeza kuposa zinthu zina zonse zapadzikoli ndipo anatipatsa udindo woyang’anira dziko lapansi komanso nyama.—Sal. 8:4-8.
6. Kodi pali umboni wina wotani wosonyeza kuti Yehova amationabe kuti ndife amtengo wapatali ngakhale kuti ndife ochimwa?
6 Mulungu sanasiye kulemekeza anthu ngakhale Adamu atachimwa. Iye amatiwerengera kwambiri moti anapereka Mwana wake wokondedwa kuti akhale dipo lotiwombola. (1 Yoh. 4:9, 10) Chifukwa cha dipoli, Yehova adzatha kuukitsa anthu “olungama ndi osalungama” amene anafa chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa Adamu. (Mac. 24:15) Mawu ake amasonyeza kuti iye amationa kuti ndife amtengo wapatali mosaganizira za thanzi lathu, chuma chathu kapena msinkhu wathu.—Mac. 10:34, 35.
7. Perekani zifukwa zina zosonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri atumiki ake.
7 Pali zifukwa zinanso zosonyeza kuti ndife amtengo wapatali kwa Yehova. Iye anatikokera m’gulu lake ndipo anasangalala ataona zimene tinachita titamva uthenga wabwino. (Yoh. 6:44) Titayamba kuyandikira kwa iye, nayenso anatiyandikira. (Yak. 4:8) Yehova amayesetsanso kutiphunzitsa ndipo izi zimatitsimikizira kuti amatikonda kwambiri. Iye amadziwa mmene tilili panopa komanso mmene tingadzakhalire m’tsogolo. Ndipo amatipatsa malangizo chifukwa chotikonda. (Miy. 3:11, 12) Wonsewutu ndi umboni wakuti ndife amtengo wapatali kwa Yehova.
8. Kodi mawu a pa Salimo 18:27-29 angatithandize bwanji pamene takumana ndi mavuto?
8 Mfumu Davide ankadziwa kuti Yehova amamukonda komanso kumuthandiza ngakhale kuti anthu ena ankamuona kuti ndi wachabechabe. Kudziwa zimenezi kunathandiza Davide kuti apirire mavuto ake. (2 Sam. 16:5-7) Ifenso tikakhumudwa kapena kukumana ndi mavuto enaake, Yehova akhoza kutithandiza kuti tikhale ndi maganizo oyenera n’kulimbana ndi vuto lililonse. (Werengani Salimo 18:27-29.) Yehova akamatithandiza, palibe chilichonse chimene chingatilepheretse kumutumikira mosangalala. (Aroma 8:31) Tiyeni tsopano tikambirane mavuto atatu aja komanso zimene zingatithandize kukumbukira kuti Yehova amatikondabe tikamakumana ndi mavutowo.
PAMENE TIKUDWALA
9. Kodi tingamve bwanji pamene tikudwala?
9 Tikadwala tikhoza kukhumudwa n’kumaona kuti sitingachite chilichonse potumikira Yehova. Tikhozanso kuchita manyazi anthu ena akaona kuti tikulephera kuchita zinthu zina kapena tikudalira anzathu kuti azitithandiza. Ngakhale pamene ena sadziwa za matenda athu, tikhoza kuchita manyazi chifukwa choti sitingakwanitse kuchita zinthu zina. Koma Yehova amatilimbikitsa pa nthawi
yovuta ngati imeneyi. Kodi amatilimbikitsa bwanji?10. Malinga ndi Miyambo 12:25, n’chiyani chingatithandize tikamadwala?
10 Tikamadwala “mawu abwino” angatilimbikitse kwambiri. (Werengani Miyambo 12:25.) M’Baibulo muli mawu abwino ambiri amene amatikumbutsa kuti Yehova amatikonda ngakhale kuti tikudwala. (Sal. 31:19; 41:3) Tikamawerenga mobwerezabwereza Mawu ake, Yehova adzatithandiza kuti tisamadzione ngati achabechabe tikamadwala.
11. Kodi Yehova anathandiza bwanji m’bale wina?
11 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Jorge. Ali mnyamata, anayamba kudwala ndipo matenda ake ankakula mwamsanga. Iye anayamba kuganiza kuti ndi wachabechabe. Jorge anati: “Sindinkayembekezera kuti matenda anga angandichititse manyazi chonchi kapena kuchititsa kuti anthu ambiri azindidabwa. Pamene matenda anga ankakula ndinkaona kuti moyo wanga usinthiratu. Ndinakhumudwa kwambiri ndipo ndinachonderera Yehova kuti andithandize.” Kodi Yehova anamuthandiza bwanji? Jorge ananena kuti: “Ndinkavutika kuika maganizo pa zimene ndinkawerenga. Choncho anthu ena anandiuza kuti ndiziwerenga malemba ochepa a m’buku la Masalimo omwe amasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri atumiki ake. Ndinkawerenga malembawo tsiku lililonse ndipo ankandilimbikitsa. Kenako anthu ena anaona kuti ndayamba kumwetulira kwambiri. Iwo ananenanso kuti ndinkawalimbikitsa chifukwa chokhala wosangalala. Ndinazindikira kuti Yehova anayankha mapemphero anga ndipo anandithandiza kusintha mmene ndinkadzionera. Ndinayamba kuganizira kwambiri zimene Mawu ake amanena zosonyeza kuti iye amandikonda ngakhale kuti ndikudwala.”
12. Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji mukamadwala?
12 Ngati mukuvutika ndi matenda enaake, dziwani kuti Yehova amamvetsa mavuto anu. Choncho muzimupempha kuti azikuthandizani kukhala ndi maganizo oyenera. Muziwerenganso mawu abwino amene Yehova wakusungirani m’Baibulo. Muziganizira kwambiri malemba amene amasonyeza kuti Yehova amakonda atumiki ake. Mukamachita zimenezi, mudzaona kuti Yehova amakomera mtima anthu onse amene amamutumikira mokhulupirika.—MAVUTO AZACHUMA
13. Kodi munthu amene ndi mutu wa banja angamve bwanji ngati wachotsedwa ntchito?
13 Munthu aliyense amene ndi mutu wa banja amafuna kupezera banja lake zinthu zofunika pa moyo. Koma tiyerekeze kuti m’bale wachotsedwa ntchito ngakhale kuti sanalakwitse chilichonse. Iye akuyesetsa kufufuza ntchito ina koma sikupezeka. Zimenezi zingamuchititse kuti azidziona ngati wachabechabe. Kodi kuganizira malonjezo a Yehova kungamuthandize bwanji?
14. N’chifukwa chiyani Yehova amakwaniritsa malonjezo ake?
14 Yehova nthawi zonse amakwaniritsa zimene walonjeza. (Yos. 21:45; 23:14) Iye amachita zimenezi pa zifukwa zingapo. Choyamba ndi chakuti zimakhudza dzina lake. Yehova analonjeza kuti azisamalira atumiki ake okhulupirika ndipo amaona kuti ali ndi udindo wokwaniritsa lonjezoli. (Sal. 31:1-3) Chachiwiri, Yehova amadziwa kuti tikhoza kukhumudwa kwambiri ngati atapanda kusamalira ana ake. Iye analonjeza kuti adzatipatsa zofunika pa moyo komanso kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi ndipo palibe chimene chingamulepheretse kukwaniritsa lonjezoli.—Mat. 6:30-33; 24:45.
15. (a) Kodi Akhristu oyambirira anakumana ndi vuto lotani? (b) Kodi lemba la Salimo 37:18, 19 limatilimbikitsa bwanji?
15 Tikamakumbukira chifukwa chake Yehova amakwaniritsa malonjezo ake, sitidzakayikira kuti adzatithandiza tikakumana ndi mavuto azachuma. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira Akhristu oyambirira. Atayamba kuzunzidwa ku Yerusalemu, ‘onse anabalalika kupatulapo atumwi okha.’ (Mac. 8:1) Apa n’zosachita kufunsa kuti anakumana ndi mavuto azachuma. Ambiri ayenera kuti anasiya nyumba ndi mabizinezi awo. Koma Yehova sanawasiye ndipo ankakhalabe osangalala. (Mac. 8:4; Aheb. 13:5, 6; Yak. 1:2, 3) Ngati Yehova anathandiza Akhristu okhulupirikawa, ndiye kuti ifenso angatithandize.—Werengani Salimo 37:18, 19.
TIKAMAVUTIKA CHIFUKWA CHA UCHIKULIRE
16. Kodi ndi vuto liti limene lingatichititse kuganiza kuti si ife ofunika kwa Yehova?
16 Anthufe tikamakula tingayambe kuona kuti sitingachite zambiri potumikira Yehova. Mwina Mfumu Davide ankavutika ndi maganizo amenewa atayamba kukalamba. (Sal. 71:9) Ndiye kodi Yehova angatithandize bwanji?
17. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mlongo wina?
17 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Jheri. Iye anapemphedwa kuti akaphunzire kasamalidwe ka Nyumba ya Ufumu koma sankafuna kupita. Mlongoyu anati: “Ndine wokalamba, wamasiye komanso ndilibe luso lililonse limene Yehova angaligwiritse ntchito. Ndine wachabechabe.” Usiku woti maphunzirowo ali mawa lake, mlongoyu anapemphera kwa Yehova kuchokera mumtima.
Kutacha anapita ku Nyumba ya Ufumu koma ankadzikayikirabe ngati anali woyenera kupezekako. Pa nthawi ya maphunzirowo, m’bale wina ananena kuti luso lofunika kwambiri ndi mtima wofuna kuphunzitsidwa ndi Yehova. Jheri anati: “Ndinaganiza kuti, ‘Luso limeneli ndili nalo!’ Ndinazindikira kuti Yehova akuyankha pemphero langa moti ndinayamba kulira. Ankanditsimikizira kuti ndili ndi chinthu chamtengo wapatali chimene ndingamupatse ndipo ankafuna kundiphunzitsa.” Poganizira zimene zinachitikazo, Jheri anati: “Ndinapita ndikuchita mantha, nditakhumudwa komanso ndikudzikayikira kwambiri. Koma ndinachokako nditalimbikitsidwa, ndili wokonzeka kugwira ntchito komanso ndikudziona kuti ndine wamtengo wapatali.”18. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amayamikira utumiki wathu ngakhale titakalamba?
18 Pamene tikukula, tisamakayikire kuti padakali zinthu zina zimene Yehova amafuna kuti tichite. (Sal. 92:12-15) Yesu anasonyeza kuti Yehova amayamikira zilizonse zimene tingachite pomutumikira ngakhale zitaoneka zochepa kwambiri. (Luka 21:2-4) Choncho muziganizira kwambiri zimene mungakwanitse kuchita. Mwachitsanzo, mukhoza kuuza anthu za Yehova, kupempherera abale anu komanso kulimbikitsa anthu ena kuti akhalebe okhulupirika. Yehova amaona kuti ndinu wantchito mnzake ngati muli ndi mtima womumvera osati chifukwa chochita zinthu zambiri pomutumikira.—1 Akor. 3:5-9.
19. Kodi lemba la Aroma 8:38, 39 limatilimbikitsa bwanji?
19 Timayamikira kwambiri kutumikira Yehova Mulungu, yemwe amaona kuti atumiki ake ndi amtengo wapatali. Iye anatilenga kuti tizichita zimene amafuna ndipo tikamamulambira timakhala osangalala. (Chiv. 4:11) M’dzikoli, tikhoza kumaoneka ngati osanunkha kanthu koma Yehova sachita nafe manyazi. (Aheb. 11:16, 38) Mwina tingafooke chifukwa cha matenda, mavuto azachuma kapena ukalamba. Koma tizikumbukira kuti palibe chimene chingatilekanitse ndi chikondi cha Atate wathu wakumwamba.—Werengani Aroma 8:38, 39.
^ ndime 5 Kodi munakumanapo ndi mavuto amene anakupangitsani kumva kuti ndinu wachabechabe? Nkhaniyi ikuthandizani kukumbukira kuti Yehova amaona kuti ndinu amtengo wapatali kwambiri. Ifotokoza zimene mungachite kuti musamadzione kuti ndinu wachabechabe ngakhale mutakumana ndi zinthu zokhumudwitsa.
NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa