NKHANI YOPHUNZIRA 30
Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Amene Sakonda Zachipembedzo?
“Ndakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana, kuti mulimonse mmene zingakhalire ndipulumutseko ena.”—1 AKOR. 9:22.
NYIMBO NA. 82 “Onetsani Kuwala Kwanu”
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi m’mayiko ena zinthu zasintha bwanji pa nkhani ya chipembedzo?
KWA zaka masauzande angapo, anthu ambiri padzikoli akhala akukonda zachipembedzo. Koma panopa zinthu zasintha kwambiri pa nkhaniyi. Masiku ano, chiwerengero cha anthu amene sali m’chipembedzo chilichonse chikuwonjezeka. Ndipo m’mayiko ena anthu ambiri amanena kuti alibe chipembedzo. *—Mat. 24:12.
2. N’chiyani chingachititse anthu kuti asiye kukonda zachipembedzo?
2 N’chifukwa chiyani anthu ambiri masiku ano sakonda zachipembedzo? * Anthu ena amangoganizira za zosangalatsa kapena mavuto awo. (Luka 8:14) Pomwe ena asiya kukhulupirira zoti kuli Mulungu. Ndiye pali enanso amene amakhulupirira Mulungu koma amaganiza kuti zachipembedzo ndi zachikale komanso zosathandiza. Amaganizanso kuti zachipembedzo n’zosemphana ndi sayansi ndipo munthu woganiza bwino sangazitsatire. Mwina iwo amamva anzawo, aphunzitsi awo kapena akatswiri ena akunena kuti zamoyo sizinachite kulengedwa. Koma samva anthu akufotokoza zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira kuti kuli Mulungu. Palinso ena amene sakonda zachipembedzo chifukwa choti atsogoleri a zipembedzo amangofuna ndalama komanso udindo. Kumayiko ena, boma limaletsa zinthu zokhudza chipembedzo.
3. Kodi cholinga cha nkhaniyi n’chiyani?
3 Yesu amafuna kuti ‘tiziphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mat. 28:19) Ndiye kodi tingathandize bwanji anthu amene sakonda zachipembedzo kuti ayambe kukonda Mulungu komanso kukhala ophunzira a Khristu? Tiyenera kuzindikira kuti zimene munthu angachite atamva uthenga wathu zingadalire kumene anakulira. Mwachitsanzo, anthu amene amachokera ku Europe akhoza kuchita zinthu mosiyana ndi anthu a ku Asia. Tikutero chifukwa chakuti ku Europe, anthu ambiri anamvapo zinthu zina zokhudza Baibulo komanso mfundo yoti Mulungu analenga zinthu zonse. Koma ku Asia, anthu ambiri sadziwa za Baibulo komanso sakhulupirira kuti kuli Mlengi. Cholinga cha nkhaniyi ndi kutithandiza kuti tizitha kufika pamtima anthu onse, mosaganizira kumene achokera.
TIZIKHALA NDI MAGANIZO OYENERA
4. N’chiyani chingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera?
4 Tizikhala ndi maganizo oyenera. Chaka ndi chaka, anthu amene sanali m’chipembedzo chilichonse amakhala a Mboni za Yehova. Ambiri mwa anthuwa amakhala kuti anali kale ndi makhalidwe abwino komanso ankanyansidwa ndi chinyengo cha m’zipembedzo. Pomwe ena anali ndi makhalidwe oipa ndipo ankafunika kusintha. Sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatithandiza kupeza anthu omwe ali ndi ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48; 1 Tim. 2:3, 4.
5. Kodi n’chiyani chimathandiza anthu kuti azimvetsera uthenga wathu?
5 Tizikhala okoma mtima komanso aulemu. Nthawi zambiri anthu amamvetsera uthenga wathu chifukwa cha mmene timawalankhulira osati chifukwa cha zimene timanena. Anthuwo amayamikira tikamawalankhula mokoma mtima, mwaulemu komanso mowaganizira. Sitiyenera kukakamiza anthu kuti azitimvetsera. Koma tiziyesetsa kumvetsa maganizo awo pa nkhani ya zipembedzo. Mwachitsanzo, anthu ena sakonda kulankhula nkhani zachipembedzo ndi anthu omwe sakuwadziwa. Ena amaganiza kuti si ulemu kufunsa munthu maganizo ake pa nkhani ya Mulungu. Pomwe ena amachita manyazi kuti anthu ena aziwaona akuwerenga Baibulo, makamaka ndi Mboni za Yehova. Mulimonse mmene zilili, tiyenera kulemekeza maganizo a munthu aliyense.—2 Tim. 2:24.
6. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankatha kusintha polankhula ndi anthu, nanga tingamutsanzire bwanji?
6 Kodi tingatani tikaona kuti munthu wina sakusangalala tikamatchula mawu monga akuti “Baibulo,” “zinthu zimene zinalengedwa,” “Mulungu” kapena “chipembedzo”? Tikhoza kutsanzira mtumwi Paulo n’kusintha zimene tikunena. Paulo akamalankhula ndi Ayuda ankagwiritsa ntchito Malemba. Koma polankhula ndi akatswiri a nzeru zachigiriki ku Areopagi, sanatchule za Baibulo. (Mac. 17:2, 3, 22-31) Kodi tingamutsanzire bwanji? Tikakumana ndi munthu amene sakhulupirira Baibulo, tikhoza kukambirana naye popanda kutchula za Baibulolo. Mukaona kuti munthu wina angachite manyazi anthu ena akamuona akuwerenga nanu Baibulo, mungamusonyeze malemba m’njira yosaonekera, mwina pogwiritsa ntchito chipangizo.
7. Kodi mwina tingafunike kuchita chiyani kuti titsatire chitsanzo cha Paulo pa 1 Akorinto 9:20-23?
7 Tizikhala omvetsa komanso tizimvetsera. Tiziyesetsa kumvetsa chifukwa chake anthu amakhala ndi maganizo enaake. (Miy. 20:5) Paulo anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye anakulira m’dera la Ayuda. Choncho anayenera kusintha polalikira anthu amitundu ina chifukwa iwo sankadziwa za Yehova komanso Malemba. Kuti nafenso tizitha kusintha, tingafunike kufufuza kapena kufunsa maganizo a anthu amumpingo wathu n’cholinga choti timvetse bwino anthu am’gawo lathu.—Werengani 1 Akorinto 9:20-23.
8. Tchulani njira ina imene mungagwiritse ntchito kuti muyambe kukambirana ndi anthu.
8 Cholinga chathu ndi kufufuza anthu ‘oyenerera.’ (Mat. 10:11) Kuti tichite zimenezi, tiyenera kupempha anthu kuti afotokoze maganizo awo ndipo tizimvetsera mwachidwi. M’bale wina wa ku England amakonda kufunsa anthu maganizo awo pa nkhani ya mmene tingakhalire ndi banja losangalala, kulera bwino ana kapena kupirira zinthu zopanda chilungamo. Iye akamva maganizo awo, amanena kuti, “Kodi maganizo anu ndi otani pa malangizo awa omwe analembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo?” Kenako amawasonyeza malemba ena pafoni yake popanda kutchula Baibulo.
TIZIFIKA ANTHU PAMTIMA
9. Kodi tingathandize bwanji anthu amene sakonda kulankhula za Mulungu?
9 Tikhoza kufika pamtima anthu amene sakonda kulankhula za Mulungu tikamakambirana nawo zinthu zimene amachita nazo chidwi. Mwachitsanzo, anthu ambiri amachita chidwi ndi zinthu za m’chilengedwe. Choncho tikhoza kukambirana nawo kuti: “Mwina mukudziwa kuti asayansi apanga zinthu zambiri zatsopano potengera zimene aona m’chilengedwe. Mwachitsanzo, popanga maikolofoni anatengera makutu ndipo popanga makamera anatengera maso. Nanga inuyo mumaganiza kuti zinthu za m’chilengedwe zinakhalako bwanji? Kodi mukuona kuti zinakhalapo chifukwa cha mphamvu inayake yodabwitsa, munthu winawake kapena chinachitika n’chiyani?” Tikamva maganizo awo, tikhoza kunena kuti: “Popeza akatswiri aphunzira zinthu poona mmene makutu kapena maso alili, tingadzifunse kuti, Kodi iwo amakhala akuphunzira kwa ndani? Ineyo ndinachita chidwi ndi zimene wandakatulo wakale analemba. Iye analemba kuti: ‘Kodi amene anakupatsani makutu, sangamve? Kapena amene anapanga maso, sangaone?’ Ndipo pomaliza ananena kuti iye ndi ‘amene amaphunzitsa anthu kuti akhale ozindikira.’ Pali asayansi ena amene amagwirizananso ndi mawu amenewa.” (Sal. 94:9, 10) Kenako tingawaonetse vidiyo ina ya pa jw.org® ya m’gulu la mavidiyo akuti “Mmene Moyo Unayambira” omwe amapezeka pa “Zochitika pa Moyo wa Anthu Ena.” (Pitani pamene alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO.) Apo ayi, tikhoza kuwapatsa kabuku kakuti Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? kapena kakuti Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri.
10. Kodi tingayambe bwanji kukambirana ndi munthu amene sakonda kulankhula za Mulungu?
10 Anthu ambiri amafuna kukhala ndi tsogolo labwino. Koma ambiri amaopa kuti dzikoli likhoza kuwonongedwa kapena kufika poti anthu sangakhalemonso. Woyang’anira dera wina wa ku Norway ananena kuti anthu amene sakonda kukambirana za Mulungu nthawi zambiri amalolera kukambirana za mavuto am’dzikoli. Sal. 37:29; Mlal. 1:4.
Choncho iye akapereka moni kwa anthu, amawafunsa kuti: “Kodi inuyo mumaganiza kuti n’chiyani chingathandize kuti tsogolo lathu likhale labwino? Kodi amene angatithandize ndi andale, asayansi kapena munthu wina?” Akamva maganizo awo, amawerenga kapena kungotchula lemba limene limasonyeza kuti m’tsogolomu zinthu zidzakhala bwino. Ena amasangalala kumva lonjezo la m’Baibulo lakuti dzikoli silidzatha ndipo anthu abwino adzakhalamo mpaka kalekale.—11. N’chifukwa chiyani tiyenera kusintha njira zolalikirira, nanga tingatengere bwanji chitsanzo cha Paulo pa Aroma 1:14-16?
11 Tiyenera kusintha njira zolalikirira mogwirizana ndi anthu amene takumana nawo. Tikutero chifukwa chakuti munthu aliyense amakhala wosiyana ndi mnzake. Chimene chingasangalatse munthu wina chikhoza kumunyansa wina. Ena sadandaula kungoyamba kukambirana za Mulungu kapena Baibulo, pomwe ena amafuna kuti muyambe kaye n’kukambirana nkhani zina. Kaya zinthu zili bwanji, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tilalikire kwa anthu a mitundu yonse. (Werengani Aroma 1:14-16.) Koma tizikumbukiranso mfundo yakuti Yehova ndi amene amakulitsa mbewu za choonadi m’mitima ya anthu oyenerera.—1 Akor. 3:6, 7.
KODI TINGATHANDIZE BWANJI ANTHU A KU ASIA?
12. Kodi tingathandize bwanji anthu am’mayiko a ku Asia omwe sanaganizirepo za Mlengi?
12 Padziko lonse, abale ndi alongo amakumana ndi anthu ochokera m’mayiko a ku Asia ndipo ena ndi ochokera m’mayiko amene boma linaletsa ntchito yathu. Anthu ambiri am’mayiko a ku Asia sanaganizirepo za Mlengi. Ena amachita chidwi ndipo amavomera kuphunzira Baibulo koma ena amakayikira mfundo zilizonse zachilendo. Ndiye kodi tingawathandize bwanji? Ofalitsa ena aluso zimawayendera bwino akayamba n’kucheza nawo nkhani zina. Ofalitsawo amachita zinthu mowaganizira ndipo mpata ukapezeka amawafotokozera mmene kutsatira mfundo ina ya m’Baibulo kunawathandizira.
13. Kodi anthu ambiri amachita chidwi ndi chiyani? (Onani chithunzi patsamba loyamba la magaziniyi.)
13 Anthu ambiri amachita chidwi ndi mfundo zothandiza za m’Baibulo. (Mlal. 7:12) Chitsanzo ndi zimene mlongo wina wa ku New York ananena. Iye amalalikira kwa anthu olankhula Chitchainizi ndipo anati: “Ndimayesetsa kusonyeza chidwi kwa anthu ndipo ndimamvetsera maganizo awo. Ndikamva kuti angofika kumene kuchokera kudziko lina, ndimawafunsa kuti: ‘Panopa zikukuyenderani bwanji kunoko? Mwapeza kale ntchito? Kaya mukukhala bwanji ndi anthu akuno?’” Nthawi zina zimenezi zimathandiza mlongoyu kuti ayambe kukambirana nawo mfundo za m’Baibulo. Mwina angawafunse kuti: “Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingatithandize kugwirizana ndi anthu ena? Kodi mungakonde kuti ndikusonyezeni mwambi wina wa m’Baibulo? Umanena kuti: ‘Chiyambi cha mkangano chili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo. Choncho mkangano usanabuke, chokapo.’ Kodi mukuganiza kuti malangizo amenewa angatithandize kuti tizikhala bwino ndi anzathu?” (Miy. 17:14) Kucheza ndi anthu m’njira ngati imeneyi kungatithandize kuzindikira anthu amene angafune kuphunzira zambiri.
14. Kodi m’bale wina wa ku Asia amathandiza bwanji anthu amene amanena kuti sakhulupirira Mulungu?
14 Nanga tingathandize bwanji anthu amene amanena kuti sakhulupirira zoti kuli Mulungu? M’bale wina amene ali ndi luso lolalikira kwa anthu oterewa kudziko lina la ku Asia ananena kuti: “Nthawi zambiri munthu akanena kuti sakhulupirira Mulungu amatanthauza kuti sagwirizana ndi kulambira milungu imene anthu ambiri amalambira. Choncho ndimagwirizana naye n’kunena kuti milungu yambiri ndi yopangidwa ndi anthu ndipo si yeniyeni. Ndimakonda kuwerenga lemba la Yeremiya 16:20 lomwe limati: ‘Kodi munthu wochokera kufumbi angapange milungu? Zimene munthu amapangazo si milungu yeniyeni.’ Kenako ndimafunsa kuti: ‘Kodi tingasiyanitse bwanji Mulungu weniweni ndi milungu imene anthu amapangayi?’ Ndimamvetsera bwino zimene angayankhe, kenako ndimawerenga lemba la Yesaya 41:23 lomwe limati: ‘Nenani zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, kuti tidziwe kuti inu ndinu milungu.’ Kenako ndimamupatsa chitsanzo cha zinthu zimene Yehova ananeneratu.”
15. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha m’bale wina wa ku Asia?
15 Chitsanzo china ndi zimene m’bale wina wa ku Asia amachita pa ulendo wobwereza. Iye anati: “Ndimasonyeza anthu nzeru zothandiza za m’Baibulo, maulosi amene anakwaniritsidwa komanso malamulo amene zinthu za m’chilengedwe zimayendera. Kenako ndimawathandiza kuzindikira kuti umenewu ndi umboni wakuti pali Mlengi wanzeru. Munthu akayamba kuvomereza zoti mwina Mulungu alikodi, ndimamusonyeza zimene Baibulo limanena zokhudza Yehova.”
16. Malinga ndi Aheberi 11:6, n’chifukwa chiyani anthu amene timaphunzira nawo amafunika kukhulupirira Mulungu komanso Baibulo, nanga tingawathandize bwanji pa nkhaniyi?
16 Tikamaphunzira ndi anthu amene sakonda zachipembedzo tiyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti azikhulupirira zoti kuli Mulungu. (Werengani Aheberi 11:6.) Tiziwathandizanso kuti azikhulupirira Baibulo. Mwina tingafunike kubwereza mfundo zina maulendo angapo. Mwina ulendo uliwonse umene tikuphunzira tiyenera kukambirana nawo umboni wakuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, tingakambirane nawo maulosi amene anakwaniritsidwa. Tingawasonyezenso umboni wakuti Baibulo ndi lolondola pa nkhani za sayansi komanso mbiri yakale kapena umboni wakuti lili ndi mfundo zothandiza pa moyo wathu.
17. Kodi kukonda anthu n’kothandiza bwanji?
17 Kuti tithandize anthu kukhala ophunzira a Khristu, tiyenera kuwasonyeza chikondi mosaganizira kuti ali ndi chipembedzo kapena ayi. (1 Akor. 13:1) Cholinga chathu pophunzira nawo chizikhala chowathandiza kudziwa kuti Mulungu amatikonda ndipo amafuna kuti ifenso tizimukonda. Chaka chilichonse, anthu ambirimbiri amene sankakonda zopembedza amabatizidwa chifukwa choti ayamba kukonda Mulungu. Choncho tiyeni tizikhala ndi maganizo oyenera ndipo tizisonyeza chikondi kwa anthu a mitundu yonse. Tizimvetsera zimene akulankhula n’kumvetsa maganizo awo. Tiziwapatsanso chitsanzo chabwino chimene chingawathandize kukhala ophunzira a Khristu.
NYIMBO NA. 76 Kodi Mumamva Bwanji?
^ ndime 5 Masiku ano, timakumana ndi anthu ambiri omwe sali m’chipembedzo chilichonse. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tiwalalikire komanso kuwathandiza kuti ayambe kukhulupirira Yehova Mulungu ndiponso Baibulo.
^ ndime 1 Kafukufuku wina anasonyeza kuti ena mwa mayikowa ndi Albania, Australia, Austria, Azerbaijan, Canada, China, Czech Republic, Denmark, France, Germany, Hong Kong, Ireland, Israel, Japan, Korea, Netherlands, Norway, South Korea, Spain, Sweden, Switzerland, United Kingdom ndi Vietnam.
^ ndime 2 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Munkhaniyi, mawu oti anthu amene sakonda zachipembedzo akunena za anthu amene sali m’chipembedzo chilichonse kapena amene sakhulupirira zoti kuli Mulungu.
^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akulalikira munthu amene amagwira naye ntchito kuchipatala ndipo kenako munthuyo akuona webusaiti yathu ya jw.org.