NKHANI YOPHUNZIRA 28
Muzipewa Kuyambitsa Mpikisano Koma Muzilimbikitsa Mtendere
“Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.”—AGAL. 5:26.
NYIMBO NA. 101 Tizigwira Ntchito Mogwirizana
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi chimachitika n’chiyani anthu akakhala ndi mtima wampikisano?
MASIKU ano anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda ndipo amalimbikitsa mtima wampikisano. Mwachitsanzo munthu wina wabizinezi angalolere kuchita zinthu zoipa n’cholinga choti bizinezi yake iziyenda bwino kuposa anzake. Wochita masewera angavulaze dala mnzake wa timu ina n’cholinga choti timu yake ipambane. Komanso mtima wampikisano ungalimbikitse mwana wasukulu kuti abere mayeso n’cholinga choti apeze malo ku yunivesite ina yotchuka. Monga Akhristu, timadziwa kuti zimenezi ndi zolakwika ndipo ndi “ntchito za thupi.” (Agal. 5:19-21) Komabe, kodi n’zotheka kuti mosadziwa mtumiki wa Yehova azilimbikitsa mtima wampikisano mumpingo? Limenelitu ndi funso lofunika chifukwa mtima umenewu ungachititse kuti abale ndi alongo asamagwirizane.
2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
2 Munkhaniyi tikambirana makhalidwe oipa amene tiyenera kupewa kuti tisamalimbikitse mtima wampikisano pakati pa abale athu. Tikambirananso zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo amene anapewa mtima wampikisano. Koma choyamba tiyeni tikambirane zimene tingachite kuti tizifufuza zolinga zathu.
MUZIFUFUZA ZOLINGA ZANU
3. Kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kudzifunsa?
3 Nthawi ndi nthawi tingachite bwino kumafufuza zolinga zathu. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimamva bwino mumtima pokhapokha ndikaona kuti ndimaposa anthu ena pa zinthu zinazake?
Kodi ndimachita khama mumpingo n’cholinga choti anthu andione kuti ndine wabwino kwambiri kuposa m’bale kapena mlongo winawake? Kapena ndimachita khama chifukwa chofuna kusangalatsa Yehova?’ N’chifukwa chiyani tiyenera kudzifunsa mafunso amenewa? Tiyeni tione zimene Mawu a Mulungu amanena.4. Mogwirizana ndi Agalatiya 6:3, 4, n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kumadziyerekezera ndi ena?
4 Baibulo limatiuza kuti tisamadziyerekezere ndi ena. (Werengani Agalatiya 6:3, 4.) Chifukwa chiyani? Chifukwa tikayamba kuganiza kuti timaposa m’bale wathu tingayambe kunyada. Ndipo chifukwa china n’chakuti tikamadziona kuti ndife osafunika chifukwa choti ena akutiposa, tingafooke. Kaya tikudziyerekezera motani, kuchita zimenezi kungasonyeze kuti sitikuganiza bwino. (Aroma 12:3) Mlongo wina yemwe amakhala ku Greece, dzina lake Katerina, * ananena kuti: “Ndinkakonda kudziyerekezera ndi alongo ena omwe ankaoneka okongola, aluso akakhala mu utumiki komanso amene sankavutika kupeza anzawo. Ndikatero ndinkadziona ngati wachabechabe.” Tizikumbukira kuti Yehova anatikokera kwa iye, osati chifukwa choti ndife okongola, odziwa kulankhula kapena ndife otchuka, koma chifukwa choti timafunitsitsa kumukonda komanso kumvera Mwana wake.—Yoh. 6:44; 1 Akor. 1:26-31.
5. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Hyun?
5 Funso lina limene tiyenera kumadzifunsa ndi lakuti, ‘Kodi anthu ena amandidziwa monga munthu amene amakonda mtendere kapena amene amakonda kukangana ndi ena?’ Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina wa ku South Korea dzina lake Hyun. Panthawi ina iye ankaona abale ena audindo mumpingo ngati anthu opikisana nawo. Iye anati: “Sindinkagwirizana nawo abalewa moti nthawi zambiri ndinkatsutsa zimene anena.” Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iye ananena kuti: “Khalidwe langa linachititsa kuti anthu asamagwirizane mumpingo.” Anzake ena a Hyun anamuthandiza kuti azindikire za vuto lake. Iye anasintha ndipo panopa ndi mkulu wabwino kwambiri. Tikazindikira kuti tili ndi mtima woyambitsa mpikisano, osati wolimbikitsa mtendere tiyenera kusintha mwamsanga.
TIZIPEWA KUDZIKUZA KOMANSO NSANJE
6. Mogwirizana ndi Agalatiya 5:26, kodi ndi makhalidwe oipa ati amene amachititsa kuti munthu akhale ndi mtima wampikisano?
6 Werengani Agalatiya 5:26. Kodi ndi makhalidwe oipa ati amene angachititse kuti tiyambe kukhala ndi mtima wampikisano? Loyamba ndi kudzikuza. Munthu wodzikuza amakhala wonyada komanso wodzikonda. Khalidwe lina loipa ndi nsanje. Sikuti munthu wansanje amangosirira zimene ena ali nazo koma amalakalakanso atazitenga kuti zikhale zake. Choncho munthu amene ali ndi nsanje amadana kwambiri ndi munthu amene akumuchitira nsanjeyo. Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tipewe makhalidwe amenewa, ngati mmene tingapewere mlili uliwonse woopsa.
7. Kodi ndi chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuipa kwa nsanje komanso kudzikuza?
7 Tingayerekezere kudzikuza komanso nsanje ndi tizitsotso timene tili m’mafuta a ndege. Ndegeyo ikhoza kunyamuka koma tizitsotsoto tikhoza kutseka mapaipi amene mumadutsa mafutawo, zomwe zingachititse kuti injini isiye kugwira bwino ntchito ndipo ndegeyo ingagwe. Mofanana ndi zimenezi, munthu akhoza kutumikira Yehova kwa kanthawi ndithu koma ngati ali wodzikuza komanso wansanje, sangapite patali. (Miy. 16:18) Akhoza kusiya kutumikira Yehova ndipo zimenezi zingavulaze iyeyo komanso anthu ena. Ndiye kodi tingatani kuti tizipewa nsanje komanso mtima wodzikuza?
8. Kodi tingapewe bwanji mtima wodzikuza?
8 Tingathe kupewa kudzikuza potsatira malangizo a Paulo amene analembera Afilipi akuti: Afil. 2:3) Ngati timaona ena kukhala otiposa sitidzayamba kuchita mpikisano ndi anthu amene amatha kuchita bwino zinthu zina, kapena ali ndi luso kuposa ifeyo. M’malomwake, tidzayamba kusangalala ndi zimene amakwanitsa kuchita. Ndipo tidzatero makamaka akamagwiritsa ntchito luso lawo potumikira Yehova ndi kumutamanda. Ndipo ngati abalewo amatsatira malangizo a Paulo, nawonso adzayamba kuona makhalidwe abwino amene tili nawo. Pamapeto pake tonse tidzalimbikitsa mtendere komanso mgwirizano mumpingo.
“Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.” (9. Kodi tingatani kuti tipewe chizolowezi chochitira ena nsanje?
9 Tingapewe chizolowezi chochitira ena nsanje pokhala odzichepetsa, kapena kuti kuzindikira zimene tingakwanitse kuchita ndi zimene sitingakwanitse. Ngati tili odzichepetsa sitingayambe kudzionetsera kuti tili ndi luso kapena timachita bwino zinthu kuposa wina aliyense. M’malomwake, tidzayamba kuganizira zimene tingaphunzire kwa ena amene ali ndi luso kuposa ifeyo. Tiyerekeze kuti mumpingo muli m’bale wina amene amakamba bwino nkhani, tingamufunse kuti amatani kuti akonzekere bwino nkhani. Ngati mlongo wina amaphika bwino chakudya, tingamufunse kuti atithandize kudziwa zimene tingachite kuti ifenso tiziphika bwino. Ngati Mkhristu wachinyamata amavutika kupeza anzake ocheza nawo, angapemphe malangizo kwa wina amene savutika kuchita zimenezi. Tikamatero, tingapewe nsanje ndiponso tikhoza kuphunzira zambiri.
ZIMENE TINGAPHUNZIRE KWA ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO
10. Kodi Gidiyoni anakumana ndi vuto lotani?
10 Taganizirani zimene zinachitika pakati pa Gidiyoni, yemwe anali wa fuko la Manase, ndi amuna a fuko la Efuraimu. Gidiyoni ndi amuna 300 omwe anali nawo anali atapambana pankhondo mothandizidwa ndi Yehova ndipo akanatha kuyamba kunyada chifukwa cha zimenezi. Amuna a ku Efuraimu anapita kukakumana ndi Gidiyoni, osati chifukwa chofuna kukamuyamikira, koma kukakangana naye. Zikuoneka kuti iwo anakwiya chifukwa Gidiyoni sanawaitane Ower. 8:1.
kuti akamenye nawo nkhondo yolimbana ndi adani a Mulungu. Iwo ankaganizira kwambiri za kulemekezedwa kwa fuko lawo ndipo analephera kuona kufunika kwa zimene Gidiyoni anachita, zomwe ndi kulemekeza dzina la Yehova komanso kuteteza anthu ake.—11. Kodi Gidiyoni anawayankha bwanji amuna a ku Efuraimu?
11 Modzichepetsa Gidiyoni anafunsa amuna a ku Efuraimu kuti: “Kodi ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu?” Kenako iye anawapatsa chitsanzo chosonyeza mmene Yehova anawadalitsira. Pamapeto pake “mkwiyo wawo unaphwa.” (Ower. 8:2, 3) Gidiyoni anadzichepetsa n’cholinga choti alimbikitse mtendere pakati pa anthu a Mulungu.
12. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Gidiyoni komanso amuna a ku Efuraimu?
12 Kodi tikuphunzirapo chiyani pankhani imeneyi? Pa zimene amuna a ku Efuraimu anachita tikuphunzirapo kuti sitiyenera kuganizira kwambiri za kulemekezedwa kwathu koma kulemekezedwa kwa Yehova. Mitu ya mabanja komanso akulu angapeze phunziro labwino pa chitsanzo cha Gidiyoni. Ngati munthu wina wakhumudwa chifukwa cha zimene ife tachita tiziyesetsa kumvetsa chimene chachititsa kuti munthuyo akhumudwe. Tikhoza kumuyamikira chifukwa cha zimene amachita bwino. Ndipotu tingafunike kuchita zinthu modzichepetsa makamaka ngati zikuchita kuonekeratu kuti munthu winayo analakwitsa. Komanso kulimbikitsa mtendere n’kofunika kwambiri kuposa kusonyeza ena kuti ifeyo sitinalakwitse chilichonse.
13. Kodi ndi vuto lotani limene Hana anakumana nalo, nanga anachita chiyani?
13 Taganiziraninso chitsanzo cha Hana. Iye anakwatiwa ndi Mlevi wina dzina lake Elikana, yemwe ankamukonda kwambiri. Elikana anali ndi mkazi wina dzina lake Penina. Iye ankakonda kwambiri Hana kuposa Penina. Komabe, “Penina anabereka ana koma Hana analibe ana.” Chifukwa cha zimenezi, Penina ankanyoza Hana ndipo “anali kum’sautsa kwambiri n’cholinga choti amukhumudwitse.” Hana ankakhumudwa kwambiri chifukwa cha zimenezi, moti “anali kulira ndiponso sankadya.” (1 Sam. 1:2, 6, 7) Koma palibe paliponse m’Baibulo pamene timawerenga kuti Hana anabwezera zimene Penina ankachita. M’malomwake, iye anafotokozera Yehova mmene ankamvera ndipo ankakhulupirira kuti achitapo kanthu. Kodi Penina anasiya kumuvutitsa Hana? Baibulo silifotokoza. Koma chomwe timadziwa n’chakuti Hana anapezanso mtendere wa mumtima ndipo “sanakhalenso ndi nkhawa.”—1 Sam. 1:10, 18.
14. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Hana?
14 Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Hana? Ngati munthu wina akufuna kuti muzipikisana, muzikumbukira kuti inuyo mukhoza kupewa zimenezi. Musamalole kuti muzikangana. M’malo mobwezera choipa muziyesetsa kukhala naye pa mtendere. (Aroma 12:17-21) Ngakhale zitaoneka kuti munthu winayo sakufuna kuti mukhazikitse mtendere, inuyo mungakhale ndi mtendere wamumtima.
15. Kodi Apolo ndi Paulo anali ofanana pa zinthu ziti?
15 Pomaliza tiyeni tione zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Apolo ndi mtumwi Paulo. Anthu awiri onsewa ankadziwa bwino Malemba. Onse anali aphunzitsi abwino komanso odziwika. Ndiponso onse anali atathandiza anthu ambiri kukhala ophunzira. Koma palibe amene ankaona mnzake ngati wopikisana naye.
16. Kodi mungafotokoze kuti Apolo anali munthu wotani?
16 Apolo anali “mbadwa ya ku Alekizandiriya,” komwe kunkadziwika kwambiri pa nkhani ya maphunziro m’nthawi ya atumwi. Iye anali ndi luso la kulankhula ndipo “analinso kuwadziwa bwino Malemba.” (Mac. 18:24) Panthawi imene anali ku Korinto, ena mumpingo anasonyeza kuti ankamukonda kwambiri kuposa abale ena kuphatikizapo mtumwi Paulo. (1 Akor. 1:12, 13) Kodi Apolo analimbikitsa maganizo ogawanitsa amenewa? Sitikuganiza kuti anatero. Ndipotu patapita nthawi Apolo atachoka ku Korinto, Paulo anamulimbikitsa kuti abwererekonso. (1 Akor. 16:12) Paulo sakanachita zimenezi akanaona kuti Apolo amagawanitsa mpingo. N’zoonekeratu kuti Apolo ankagwiritsa bwino ntchito luso lake polalikira uthenga wabwino komanso kulimbikitsa abale. Tingathenso kunena motsimikiza kuti Apolo anali wodzichepetsa. Mwachitsanzo, palibe paliponse m’Baibulo pamene pamasonyeza kuti iye anakhumudwa pamene Akula ndi Purisikila anamutenga ndi “kumufotokozera njira ya Mulungu molondola.”—Mac. 18:24-28.
17. Kodi Paulo analimbikitsa bwanji mtendere?
17 Mtumwi Paulo ankadziwa ntchito yabwino imene Apolo ankagwira. Koma iye sankadera nkhawa kuti anthu ena aziona kuti Apolo akumuposa. Malangizo amene Paulo anapereka kumpingo wa ku Korinto anasonyeza kuti iye anali wodzichepetsa komanso woganiza bwino. M’malo motengeka ndi zimene ena ankanena kuti, “Ine ndine wa Paulo,” iye anathandiza anthu onse kuti azilemekeza Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu.—18. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 4:6, 7, kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Apolo ndi Paulo?
18 Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Apolo komanso Paulo? Tikhoza kumachita khama kutumikira Yehova komanso tingathandize anthu ambiri kuti afike pobatizidwa. Koma timazindikira kuti zimenezi zimatheka chifukwa chakuti Yehova akutithandiza. Pa chitsanzo cha Apolo komanso Paulo tikupezapo phunziro lina lakuti ngati tili ndi maudindo mumpingo tingachitenso zambiri polimbikitsa mtendere. Timayamikira kwambiri abale audindo akamalimbikitsa mtendere komanso mgwirizano. Iwo amachita zimenezi popereka malangizo a m’Mawu a Mulungu komanso pothandiza onse kuti asamaganizire kwambiri za iwowo, koma za Yesu Khristu yemwe ndi chitsanzo chathu.—Werengani 1 Akorinto 4:6, 7.
19. Kodi aliyense wa ife ayenera kuchita chiyani? (Onaninso bokosi lakuti “ Muzipewa Kuyambitsa Mpikisano.”)
19 Aliyense ali ndi mphatso kapena luso limene Mulungu anamupatsa. Tingathe kugwiritsa ntchito mphatso zimenezi “potumikirana.” (1 Pet. 4:10) Mwina tingamaone kuti zimene timachita mumpingo ndi zazing’ono. Koma zinthu zing’onozing’ono zimene timachita polimbikitsa mgwirizano zili ngati ulusi wosokera umene umathandiza kuti chovala chilumikizane. Choncho tiyeni tonse tizichita khama kuchotsa maganizo alionse a mpikisano amene tingakhale nawo. Tiyeninso titsimikize mtima kuchita zonse zomwe tingathe polimbikitsa mtendere komanso mgwirizano mumpingo.—Aef. 4:3.
NYIMBO NA. 80 “Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova ndi Wabwino”
^ ndime 5 Mofanana ndi timing’alu tomwe tingachititse kuti mphika wadothi ukhale wosalimba, mtima wampikisano ungachititse kuti mpingo ugawikane. Ngati mpingo si wolimba ndipo anthu sakugwirizana, sungakhale malo a mtendere olambiriramo Mulungu. Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake tiyenera kupewa mtima wampikisano komanso zimene tingachite kuti tizilimbikitsa mtendere mumpingo.
^ ndime 4 Mayina asinthidwa.