Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 29

Muzisangalala Ndi Zimene Mukuchita Potumikira Yehova

Muzisangalala Ndi Zimene Mukuchita Potumikira Yehova

“Aliyense payekha . . . adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”—AGAL. 6:4.

NYIMBO NA. 34 Kuyenda ndi Mtima Wosagawanika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani Yehova satiyerekezera ndi anthu ena?

YEHOVA amakonda zinthu zosiyanasiyana ndipo sayembekezera kuti zonse zizikhala zofanana. Umboni wa zimenezi ndi wakuti iye analenga mitundu yosiyanasiyana ya zinthu, kuphatikizapo anthu. Munthu aliyense ndi wosiyana ndi mnzake. Choncho Yehova samakuyerekezerani ndi anthu ena. Iye amafufuza mmene mtima wanu ulili. (1 Sam. 16:7) Amaganiziranso zinthu zimene mumachita bwino, zofooka zanu komanso mmene munaleredwera. Ndipo sayembekezera kuti muzichita zimene simungakwanitse. Tiyenera kutsanzira Yehova pomadziona ngati mmene iye amationera. Tikatero tidzasonyeza kuti ndife “munthu woganiza bwino,” osati kumadziona kuti ndife munthu wapamwamba kapena wolephera.​—Aroma 12:3.

2. N’chifukwa chiyani si bwino kumadziyerekezera ndi ena?

2 N’zoona kuti tingapindule kwambiri tikamachita chidwi ndi zimene m’bale kapena mlongo wina wokhulupirika amachita pa nkhani yolalikira. (Aheb. 13:7) Tikutero chifukwa tikhoza kuphunzira njira zolalikirira zimene zingatithandize kuti ifenso tizichita bwino mu utumiki. (Afil. 3:17) Koma pali kusiyana pakati pa kutengera chitsanzo chabwino cha munthu wina, ndi kudziyerekezera ndi munthuyo. Ngati mutayamba kudziyerekezera ndi munthu wina, mukhoza kuyamba kumuchitira nsanje, kufooka komanso kumadziona ngati wachabechabe. Monga tinaphunzirira munkhani yapita ija, kuchita zinthu mopikisana ndi ena mumpingo, kukhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho Yehova amatiuza mwachikondi kuti: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.”​—Agal. 6:4.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene mwakwanitsa kuchita potumikira Yehova zomwe zimakuchitsani kukhala osangalala?

3 Yehova amafuna kuti muzisangalala ndi zimene mukuchita pomutumikira. Ngati munabatizidwa, muyenera kuti mumasangalala kuti munakwaniritsa cholinga chimenecho. Ndipo munasankha nokha kuchita zimenezi chifukwa chakuti mumakonda Mulungu. Ndiye taganizirani zimene mwakwanitsa kuchita kuchokera nthawi imeneyo. Mwachitsanzo, kodi panopa mumakonda kwambiri kuwerenga komanso kuphunzira Baibulo? Kodi mapemphero anu ayamba kukhala ochokera pansi pa mtima kuposa kale? (Sal. 141:2) Kodi panopa mumayamba kukambirana mosavuta ndi anthu komanso kugwiritsa ntchito mwaluso zinthu zophunzitsira? Komanso ngati muli ndi banja, kodi Yehova wakuthandizani kuti mukhale mwamuna, mkazi komanso kholo labwino? Muyenera kuti mumasangalala komanso kukhala wokhutira chifukwa cha zimene mwakwanitsa kuchita pa zinthu zimenezi.

4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Tingathandize anthu ena kuti azisangalala ndi zimene akukwanitsa kuchita potumikira Yehova. Tingawathandizenso kuti azipewa kudziyerekezera ndi ena. Munkhaniyi, tiona zimene makolo angachite kuti azithandiza ana awo, zimene anthu okwatirana angachite kuti azithandizana komanso mmene akulu ndi anthu ena mumpingo angathandizire abale ndi alongo awo. Pomaliza, tikambirana mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize kukhala ndi zolinga zimene tingazikwaniritse mogwirizana ndi luso lathu komanso mmene zinthu zilili pa moyo wathu.

ZIMENE MAKOLO KOMANSO ANTHU OKWATIRANA ANGACHITE

Makolo, muziyamikira zinthu zabwino zimene mwana wanu aliyense amachita (Onani ndime 5-6) *

5. Mogwirizana ndi Aefeso 6:4, kodi makolo ayenera kupewa kuchita chiyani?

5 Makolo ayenera kukhala osamala kuti asamayerekezere mwana wina ndi mnzake komanso asamayembekezere kuti mwana azichita zimene sangakwanitse. Ngati makolo atamachita zimenezi akhoza kufooketsa mwanayo. (Werengani Aefeso 6:4.) Mlongo wina dzina lake Sachiko * ananena kuti: “Aphunzitsi anga ankayembekezera kuti ndizichita bwino m’kalasi kuposa ana ena. Kuwonjezera pamenepo, mayi anga ankafuna kuti ndizikhoza bwino n’cholinga choti ndizilalikira bwino kwa aphunzitsi anga komanso bambo anga omwe si a Mboni. Ndipotu mayi anga ankafuna kuti ndizikhoza zonse pa mayeso, zomwe ndinkaona kuti n’zosatheka. Ngakhale kuti ndinamaliza sukulu zaka zambiri m’mbuyomo, nthawi zina ndimakayikira ngati Yehova amasangalala ndi zimene ndimachita pomutumikira.”

6. Kodi makolo angaphunzire chiyani pa Salimo 131:1, 2?

6 Makolo angapeze phunziro lina labwino pa Salimo 131:1, 2. (Werengani.) Mfumu Davide ananena kuti ‘sanafunefune zinthu zapamwamba kwambiri,’ kapena zinthu zimene sakanazikwanitsa. Kudzichepetsa kunamuthandiza kuti ‘adzitonthoze ndiponso kukhazika mtima wake pansi.’ Kodi makolo angaphunzire chiyani pa mawu a Davidewa? Makolo angakhale odzichepetsa, osati pokhapokha akamapewa kuganizira kwambiri zokhudza iwowo, koma akamapewanso kuyembekezera zambiri kuchokera kwa ana awo. Iwo angalimbikitse ana awo akamazindikira zimene anawo angakwanitse ndi zimene sangakwanitse, n’kumawathandiza kukhala ndi zolinga zimene angazikwaniritse. Mlongo wina dzina lake Marina ananena kuti: “Mayi anga sankandiyerekezera ndi abale anga kapena ana ena. Iwo anandiphunzitsa kuti aliyense ali ndi luso losiyana ndi mnzake komanso kuti tonsefe ndi amtengo wapatali kwa Yehova. Ndimawathakoza chifukwa zimenezi zinandithandiza kuti ndisamadziyerekezere ndi ena.”

7-8. Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amalemekeza mkazi wake?

7 Mwamuna wa Chikhristu ayenera kumalemekeza mkazi wake. (1 Pet. 3:7) Kulemekeza munthu kumaphatikizapo kumuganizira komanso kumupatsa ulemu. Mwachitsanzo, mwamuna angasonyeze kuti amalemekeza mkazi wake akamamuona kuti ndi wofunika kwambiri. Iye samauza mkazi wake kuti achite zimene sangakwanitse ndipo samamuyerekezera ndi akazi ena. Kodi pangakhale mavuto otani ngati mwamuna amayerekezera mkazi wake ndi akazi ena? Mlongo wina dzina lake Rosa yemwe mwamuna wake si wa Mboni, nthawi zambiri amamuyerekezera ndi akazi ena. Mawu onyoza amene mwamuna wake amamulankhula amachititsa Rosa kuti asamamve bwino komanso azikayikira ngati pali anthu ena amene amamukonda. Iye ananena kuti: “Ndimafunika kuti pafupipafupi ena azindikumbutsa kuti Yehova amandikonda.” Mosiyana ndi zimenezi, mwamuna wa Chikhristu amalemekeza mkazi wake. Iye amadziwa kuti zimenezi zingathandize kuti azigwirizana ndi mkazi wake komanso akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. *

8 Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake amalankhula zinthu zabwino zokhudza mkazi wakeyo, kumutsimikizira kuti amamukonda komanso kumuyamikira. (Miy. 31:28) Zimenezi ndi zimene mwamuna wa Katerina, amene tamutchula munkhani yapita ija, amachita ndipo zathandiza mkazi wakeyo kuti asamadzione ngati wopanda pake. Ali mwana, mayi ake ankamunyoza ndipo ankakonda kumuyerekezera ndi atsikana ena, kuphatikizaponso anzake. Izi zinachititsa kuti Katerina azidziyerekezera ndi ena ngakhale pambuyo poti waphunzira choonadi. Komabe, mwamuna wake wamuthandiza kuti athe kulimbana ndi maganizo amenewa n’kumadziona moyenera. Katerina ananena kuti: “Mwamuna wanga amandikonda, kundiyamikira ndikachita bwino zinthu komanso amandipempherera. Iye amandikumbutsanso makhalidwe abwino amene Yehova ali nawo ndipo amandithandiza ndikayamba kukhala ndi maganizo olakwika.”

ZIMENE AKULU ACHIKONDI KOMANSO ENA MUMPINGO ANGACHITE

9-10. Kodi akulu achikondi anathandiza bwanji mlongo wina yemwe ankadziona kuti ndi wosafunika akadziyerekezera ndi ena?

9 Kodi akulu angathandize bwanji anthu amene amakonda kudziyerekezera ndi ena? Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Hanuni yemwe sankayamikiridwa ali mwana. Iye ananena kuti: “Ndinali wamanyazi ndipo ndinkaona ngati ana ena amachita bwino zinthu kuposa ineyo. Ndinayamba kudziyerekezera ndi ena kuyambira kale ndili mwana.” Ngakhale pambuyo pophunzira choonadi, Hanuni anapitirizabe kumadziyerekezera ndi ena. Chifukwa cha zimenezi, iye ankaziona ngati wosafunika mumpingo. Koma panopa, Hanuni akusangalala kuchita upainiya. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kusintha mmene amadzionera?

10 Hanuni ananena kuti akulu achikondi ndi amene anamuthandiza. Iwo ankasonyeza kuti amamudalira ndipo ankamuyamikira chifukwa cha kukhulupirika kwake. Iye analemba kuti: “Nthawi zina akulu ankandipempha kuti ndilimbikitse alongo ena omwe ankafunika kulimbikitsidwa. Zimenezi zinandithandiza kuti ndizidziona kukhala wofunika. Ndimakumbukira nthawi ina pamene akulu anandiyamikira chifukwa cholimbikitsa alongo ena achitsikana. Iwo anandiwerengera lemba la 1 Atesalonika 1:2, 3. Zimenezi zinandilimbikitsa kwambiri. Ndimayamikira kwambiri abusa abwino amenewa, chifukwa tsopano ndimaona kuti ndine wofunika kwambiri m’gulu la Yehova.”

11. Kodi tingathandize bwanji anthu ‘opsinjika ndi a mtima wodzichepetsa,’ monga mmene lafotokozera lemba la Yesaya 57:15?

11 Werengani Yesaya 57:15. Yehova amakonda kwambiri anthu ‘opsinjika ndi a mtima wodzichepetsa.’ Tonsefe, osati akulu okha, tingalimbikitse abale ndi alongo okondedwa amenewa. Njira imodzi imene tingawalimbikitsire ndi kuwasonyeza kuti timawaganizira. Yehova amafuna kuti tiziwasonyeza kuti iye amawakonda komanso kuti ndi nkhosa zake zamtengo wapatali. (Miy. 19:17) Tingalimbikitsenso abale ndi alongowa tikamachita zinthu modzichepetsa. Sitiyenera kuchititsa ena kuti azingoganizira za ifeyo, zomwe zingachititse kuti ayambe kukhala ndi mtima wansanje. M’malomwake tiyenera kugwiritsa ntchito luso limene tili nawo komanso zimene timadziwa polimbikitsa abale athu.​—1 Pet. 4:10, 11.

Ophunzira a Yesu ankamukonda chifukwa sankadziona kukhala wapamwamba kuposa ena. Iye ankasangalala kucheza ndi anzake (Onani ndime 12)

12. N’chifukwa chiyani anthu wamba ankakonda kubwera kwa Yesu? (Onani chithunzi chapachikuto.)

12 Kuganizira mmene Yesu ankachitira zinthu ndi otsatira ake kungatithandize kudziwa mmene tingachitire zinthu ndi anthu ena. Iye anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Koma anali “wofatsa ndi wodzichepetsa.” (Mat. 11:28-30) Iye sankadzionetsera kuti ndi wanzeru kwambiri kapena amadziwa zinthu zambiri. Ankagwiritsa ntchito mawu komanso zitsanzo zosavuta kumva, zomwe zinkafika pamtima anthu odzichepetsa. (Luka 10:21) Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo omwe anali onyada, Yesu sankachititsa anthu ena kuti azidziona ngati osafunika kwa Mulungu. (Yoh. 6:37) M’malomwake, iye ankalemekeza anthu wamba.

13. Kodi mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake zinasonyeza bwanji kuti anali wokoma mtima komanso wachikondi?

13 Mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake, zinkasonyeza kuti ndi wokoma mtima komanso wachikondi. Iye ankadziwa kuti ophunzirawo anali ndi luso losiyana komanso zinthu pa moyo wawo zinali zosiyana. Choncho sizikanatheka kuti akhale ndi maudindo ofanana komanso azichita zofanana pa ntchito yolalikira. Komabe Yesu ankayamikira ophunzirawo chifukwa aliyense ankachita zinthu ndi mtima wake wonse. Yesu anasonyeza kuti ankamvetsa ophunzira ake pamene anafotokoza fanizo la matalente. M’fanizoli, mbuye anapereka ntchito kwa kapolo aliyense “malinga ndi luso lake.” Mmodzi wa akapolo awiri akhama, anapeza phindu lalikulu kuposa mnzake. Koma mbuyeyo anayamikira onsewa ndi mawu ofanana akuti, “Wachita bwino kwambiri, kapolo wabwino ndi wokhulupirika iwe!”​—Mat. 25:14-23.

14. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikamachita zinthu ndi ena?

14 Yesu amachita nafe zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi. Iye amadziwa kuti tili ndi maluso osiyana komanso zinthu ndi zosiyana pa moyo. Ndipo amasangalala ndi zimene timayesetsa kuchita potumikira Mulungu. Tingachite bwino kutengera chitsanzo cha Yesu tikamachita zinthu ndi ena. Sitiyenera kuchititsa Mkhristu mnzathu kuti azidziona ngati wosafunika kapena kumuchititsa manyazi chifukwa chakuti sangathe kuchita zambiri ngati ena. M’malomwake, tiyenera kumapeza mipata yoti tiziyamikira abale ndi alongo athu chifukwa choyesetsa kuchita zonse zomwe angathe potumikira Yehova.

MUZIKHALA NDI ZOLINGA ZIMENE MUNGAZIKWANIRITSE

Kukhala ndi zolinga zimene mungazikwaniritse kungakuthandizeni kuti muzisangalala (Onani ndime 15-16) *

15-16. Kodi mlongo wina anapindula bwanji chifukwa chodziikira zolinga zomwe angakwaniritse?

15 Kukhala ndi zolinga potumikira Yehova kungatithandize kukhala ndi moyo wokhutiritsa komanso watanthauzo. Chinsinsi chagona pa kukhala ndi zolinga zimene tingazikwaniritse malinga ndi luso komanso mmene zinthu zilili pa moyo wathu, osati mmene zilili pa moyo wa anthu ena. Zimenezi zingathandize kuti tisadzakhumudwe kapena kufooka. (Luka 14:28) Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina yemwe ndi mpainiya dzina lake Midori.

16 Midori ali mwana, bambo ake omwe si a Mboni, ankamuchititsa manyazi pomamuyerekezera ndi abale ake komanso anzake a m’kalasi. Iye anati: “Ndinkangodziona ngati wachabechabe.” Komabe atakula anasiya kudzikayikira. Ananenanso kuti: “Ndinkawerenga Baibulo tsiku lililonse n’cholinga choti ndikhale ndi mtendere wamumtima komanso ndiziona kuti Yehova amandikonda.” Kuwonjezera pamenepo, iye anadziikira zolinga zimene angazikwaniritse ndipo ankapempha Mulungu kuti amuthandize kukwaniritsa zolingazo. Zimenezi zinamuthandiza kuti azisangalala ndi zimene ankakwanitsa kuchita potumikira Yehova.

PITIRIZANI KUCHITA ZIMENE MUNGATHE POTUMIKIRA YEHOVA

17. Kodi tingatani kuti tipitirize ‘kukhala atsopano mumphamvu yoyendetsa maganizo athu,’ ndipo zotsatirapo zake zingakhale zotani?

17 Pangatenge nthawi kuti tisinthe maganizo athu komanso mmene timadzionera. Choncho Yehova amatiuza kuti: “Munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.” (Aef. 4:23, 24) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kumapemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kuganizira mozama zimene taphunzirazo. Nthawi zonse muzichita zimenezi ndipo muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu. Mzimu wake woyera udzakuthandizani kuchotsa maganizo alionse odziyerekezera ndi ena. Iye adzakuthandizani kuti mudziwe ngati mwayamba kukhala ndi mtima wansanje kapena wonyada ndipo adzakuthandizani kuti musinthe mwamsanga.

18. Kodi mawu a pa 2 Mbiri 6:29, 30, angatilimbikitse bwanji?

18 Werengani 2 Mbiri 6:29, 30. Yehova amadziwa mtima wathu. Iye amadziwanso mavuto amene timalimbana nawo monga zinthu zoipa za m’dzikoli zimene zingatisokoneze komanso zimene timalakwitsa chifukwa chakuti si ife angwiro. Yehova akamaona zimene timachita poyesetsa kulimbana ndi mavuto amenewa, amayamba kutikonda kwambiri.

19. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito chitsanzo chotani potithandiza kudziwa kuti amatikonda kwambiri?

19 Pofuna kutithandiza kumvetsa kuti amatikonda kwambiri, Yehova anagwiritsa ntchito chitsanzo cha chikondi chimene chimakhalapo pakati pa mayi ndi mwana wake. (Yes. 49:15) Taganizirani chitsanzo cha mayi wina dzina lake Rachel. Iye analemba kuti: “Mwana wanga Stephanie anabadwa masiku osakwana. Nditamuona koyamba ankaoneka wamng’ono kwambiri komanso womvetsa chisoni. Komabe adokotala ankandilola kuti ndizimunyamula tsiku lililonse m’mwezi woyamba pamene ankakhala m’mashini omuthandiza kuti akhalebe ndi moyo. Nthawi imeneyo inathandiza kuti ine ndi mwana wangayo tizikondana kwambiri. Panopa ali ndi zaka 6 ndipo amaoneka wamng’ono kuyerekeza ndi anzake amene anabadwa naye nthawi imodzi. Koma ndimam’konda kwambiri mwana wangayu chifukwa analimbana ndi mavuto aakulu kuti akhalebe ndi moyo, ndipo ndimasangalala ndikamamuona.” N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri chonchi akationa tikuyesetsa kulimbana ndi mavuto n’cholinga choti tizimutumikira ndi mtima wonse.

20. Monga mtumiki wodzipereka wa Yehova, kodi muli ndi chifukwa chiti chokhalira wosangalala?

20 Monga mtumiki wa Yehova, dziwani kuti iye amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali komanso wapadera m’banja lake. Sikuti Yehova anakukokerani kwa iye chifukwa choti anaona kuti ndinu wabwino kwambiri kuposa ena. Iye anakukokani chifukwa anaona mtima wanu kuti ndinu munthu wofatsa komanso wophunzitsika, yemwe akhoza kumuumba. (Sal. 25:9) Dziwani kuti iye amayamikira mukamachita zonse zomwe mungathe pomutumikira. Kupirira komanso kukhulupirika kwanu, ndi umboni wakuti muli ndi “mtima woona komanso wabwino.” (Luka 8:15) Choncho pitirizani kutumikira Yehova ndi mtima wanu wonse. Mukatero mudzakhala ndi chifukwa chosangalalira ‘ndi ntchito yanu.’

NYIMBO NA. 38 Mulungu Adzakulimbitsa

^ ndime 5 Yehova satiyerekezera ndi anthu ena. Koma enafe tikhoza kumadziyerekezera ndi ena, kenako n’kumaona kuti ndife olephera. Munkhaniyi, tikambirana chifukwa chake kuchita zimenezi kuli koopsa. Tionanso zimene tingachite kuti tizithandiza anthu a m’banja lathu komanso ena mumpingo kuti azidziona mmene Yehova amawaonera.

^ ndime 5 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 7 Ngakhale kuti mfundozi zikufotokoza za mwamuna, zingathandizenso kwambiri mkazi.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pa nthawi ya kulambira kwa pabanja, makolo akusonyeza kuti akusangalala ndi zimene mwana aliyense akuchita pokonza chingalawa cha Nowa.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo yemwe akulera yekha mwana amene sanayambe kupita kusukulu, akukonza ndandanda yochitira upainiya wothandiza ndipo akusangalala kuti wakwaniritsa cholinga chakechi.