Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
N’chifukwa chiyani Mulungu ankalola kuti Aisiraeli azimenya nkhondo?
Yehova ndi Mulungu wachikondi. Koma nthawi zina, ankalola kuti anthu ake amenye nkhondo akaona kuti akuponderezedwa ndiponso pakuchitika zinthu zoipa. Mulungu ndi amene ankasankha anthu oti akamenye nkhondo komanso nthawi yake.—w15 11/1, tsamba 4-5.
Kodi makolo angatani kuti athandize ana awo achinyamata kuti azitumikira Yehova?
Makolo ayenera kukonda ana awo achinyamata ndipo ayenera kuwasonyeza kuti iwo ndi odzichepetsa. Ayeneranso kukhala ozindikira ndipo aziyesetsa kuwamvetsa ana awowo.—w15 11/15, tsamba 9-11.
Kodi papa ndi wolowa m’malo mwa Petulo?
Lemba la Mateyu 16:17, 18 silinanene kuti mtumwi Petulo adzakhala mutu wampingo wachikhristu. Baibulo limasonyeza kuti Yesu ndiye mwala wapakona wa maziko a mpingo. (1 Pet. 2:4-8)—w15 12/1, tsamba 12-14.
Kodi tiyenera kuganizira zinthu ziti tisanayambe kulankhula?
Kuti tizigwiritsa ntchito bwino lilime lathu, tiyenera kuganizira (1) nthawi yolankhula (Mlal. 3:7), (2) zimene tingalankhule (Miy. 12:18) komanso (3) mmene tingalankhulire (Miy. 25:15).—w15 12/15, tsamba 19-22.
Kodi Akhristu ayenera kupewa zinthu ziti kuti akhale oona mtima?
Akhristu ayenera kupewa kunama komanso miseche. Sayeneranso kuba, kuchita chinyengo kapena kulankhula nkhani yabodza imene ingapweteketse ena.—wp16.1, tsamba 5.
Kodi “ansembe aakulu” amene amatchulidwa m’Baibulo anali ndani?
“Ansembe aakulu” anali anthu omwe ankayang’anira magulu a ansembe ena ndipo m’gululi munkakhalanso anthu ena omwe anachotsedwa pa udindo wawo ngati mkulu wa ansembe.—wp16.1, tsamba 10.
Kodi tizichita bwanji zinthu ndi anthu amene amadya zizindikiro pa Chikumbutso?
Akhristu sapereka ulemu wapadera kwa anthu amene amadya zizindikiro. Ndipotu odzozedwa enieni safuna kuti tiziwachitira zimenezi. Iwo saonanso kuti zimenezi ndi zotchukira. (Mat. 23:8-12)—w16.01, tsamba 23-24.
Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Abulahamu anachita kuti akhale bwenzi la Mulungu?
Abulahamu ayenera kuti anamva za Mulungu kuchokera kwa Semu. Zimene Mulungu anamuchitira iyeyo komanso banja lake zinachititsa kuti amudziwe bwino n’kumamukonda. Nafenso tiyenera kudziwa bwino Mulungu n’kumamukonda.—w16.02, tsamba 9-10.
Kodi ndani amene anagawa machaputala ndi mavesi a m’Baibulo?
Okopera mabuku achiyuda anagawa Baibulo lachiheberi m’mavesi. M’zaka za m’ma 1200 C.E., Stephen Langton anagawa Baibulo m’machaputala. Ndipo cha m’ma 1500 C.E., Robert Estienne anagawanso Malemba Achigiriki m’mavesi.—wp16.2, tsamba. 14-15.
Kodi Satana anapitadi ndi Yesu kukachisi kuti akamuyese?
Sitikudziwa. Mawu a pa Mateyu 4:5 ndi pa Luka 4:9 angatanthauze kuti Yesu anangoonetsedwa masomphenya kapena anapitadi pamalo ena okwera apakachisipo.—w16.03, tsamba 31-32.
Kodi utumiki wathu ungafanane bwanji ndi mame?
Mame amagwa pang’onopang’ono, amasangalatsa komanso amathandiza kuti zomera zisafe. Mame ndi madalitso ochokera kwa Yehova. (Deut. 33:13) Ndi mmene zililinso ndi utumiki umene anthu a Mulungu amachita.—w16.04, tsamba 4.