NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) June 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa August 5–September 1, 2019

‘Samalani Kuti Wina Angakugwireni’

Satana ndi katswiri pa nkhani yopusitsa anthu. Kodi amayesetsa bwanji kutipusitsa kuti tisiye kukonda Yehova?

Tizichotsa Maganizo Alionse Otsutsana ndi Kudziwa Mulungu

Maganizo athu amaumbidwa ndi kumene tinakulira, chikhalidwe chathu komanso maphunziro athu. Kodi tingachotse bwanji maganizo olakwika omwe ali ngati “zinthu zozikika molimba”?

Tizidalira Yehova Tikakhala ndi Nkhawa

Tikamada nkhawa kwa nthawi yaitali tikhoza kudwala kapena kusokonezeka maganizo. Tingaphunzire zambiri tikaganizira zimene Yehova anachita pothandiza atumiki ake akale kuti athane ndi nkhawa.

Tizithandiza Anthu Amene Ali ndi Nkhawa

Loti, Yobu ndi Naomi ankatumikira Yehova mokhulupirika koma nthawi zina ankada nkhawa. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinawachitikira?

Msampha Wina wa Satana

Anthu ambiri akodwa mumsampha woonera zolaula. Kodi tingapewe bwanji khalidwe loipali?

Akwanitsa Kuwerenga Mpukutu Wakale

Mu 1970, asayansi anafukula mpukutu wakupsa ku Ein Gedi m’dziko la Israel ndipo akwanitsa kuona mkati mwake pogwiritsa ntchito njira yamakono yochitira sikani zinthu. Kodi mumpukutuwu mwapezeka zotani?