Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akwanitsa Kuwerenga Mpukutu Wakale

Akwanitsa Kuwerenga Mpukutu Wakale

Zinali zosatheka kuwerenga mawu apachidutswa cha mpukutu wakupsa chimene chinapezeka ku Ein Gedi mu 1970. Koma njira yatsopano yochitira sikani zinthu yathandiza kudziwa kuti muli mavesi a Levitiko komanso dzina la Mulungu

MU 1970, asayansi anafukula mpukutu wakupsa ku Ein Gedi m’dziko la Israel chakumadzulo kwa Nyanja Yakufa. Mpukutuwu anaupeza pofukula sunagoge amene anawotchedwa pa nthawi imene mudzi wina wam’deralo unawonongedwa, mwina m’zaka za pakati pa 500 ndi 550 C.E. Mpukutuwu unapsa kwambiri moti zinali zosatheka kuutambasula komanso kuuwerenga. Koma panopa asayansi akwanitsa kuona zimene zili mkati mwake pogwiritsa ntchito njira yamakono yochitira sikani zinthu. Iwo akwanitsa kuwerenga zimene zinalembedwa mumpukutuwu pogwiritsa ntchito pulogalamu yatsopano yapakompyuta.

Kodi mumpukutuwu mwapezeka zotani? Apeza kuti mumpukutuwu muli malemba ena a m’Baibulo. Kachidutswa kamene kanatsala kakusonyeza mavesi ena akumayambiriro kwa buku la Levitiko. M’mavesi amenewa mukupezekanso zilembo zinayi zachiheberi zoimira dzina la Mulungu. Zikuoneka kuti mpukutuwu unalembedwa m’zaka zapakati pa 50 ndi 400 C.E. Choncho umenewu ndi mpukutu wakale kwambiri wa Malemba Achiheberi womwe wapezeka pambuyo pa mipukutu imene inapezeka pafupi ndi Nyanja Yakufa. Munthu wina dzina lake Gil Zohar analemba munyuzipepala ina (The Jerusalem Post) kuti: “Mpukutu wokhala ndi mavesi a m’buku la Levitikowu usanapezeke, mipukutu yakale imene inalipo inali yomwe inapezeka pafupi ndi Nyanja Yakufa komanso wina wotchedwa Aleppo Codex. Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inalembedwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo cha m’ma 100 B.C.E. Pomwe wotchedwa Aleppo Codex unalembedwa cha m’ma 930 C.E. Choncho tingati pakati pake panadutsa zaka 1,000. Koma panopa tili ndi mpukutu wina wakale womwe unapezeka ku Ein Gedi uja.” Akatswiri ena akunena kuti mpukutuwu ukusonyeza kuti uthenga wa m’mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo sunasinthe ngakhale kuti panapita zaka zoposa 1,000 ndipo Amasoreti sanakopere Baibulo molakwika.