Kodi Tingathandize Bwanji Ana a Anthu Ochokera M’mayiko Ena?
“Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.”—3 YOH. 4.
NYIMBO: 88, 41
1, 2. (a) Kodi ana a anthu amene asamukira m’dziko lina, amakumana ndi mavuto otani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?
M’BALE wina dzina lake Joshua anati: “Kuyambira ndili wamng’ono kwambiri, ndinkalankhula chilankhulo cha makolo anga kunyumba komanso kumpingo. Koma nditayamba sukulu, ndinayamba kukonda kulankhula chilankhulo cha dziko limene tinasamukira. Patangopita zaka zochepa zokha, ndinayamba kukonda kwambiri chilankhulo chimenecho. Ndinkavutika kumvetsa zimene zinkanenedwa kumisonkhano komanso ndinasiya kumvetsa zinthu zokhudza chikhalidwe cha makolo anga.” Zimene zinachitikira Joshua n’zimene zimachitikiranso ana ambiri amene asamukira m’dziko lina.
2 Masiku ano, anthu oposa 240,000,000 amakhala m’dziko limene anachita kusamukiramo. Ngati muli ndi ana ndipo mwasamukira m’dziko lina, kodi mungatani kuti muzithandiza ana anu kukonda Yehova ndiponso ‘kuyendabe m’choonadi’? (3 Yoh. 4) Nanga kodi anthu ena angathandize bwanji?
MUZIPEREKA CHITSANZO CHABWINO KWA ANA ANU
3, 4. (a) Kodi makolo angapereke bwanji chitsanzo chabwino kwa ana awo? (b) Kodi makolo sayenera kukhala ndi maganizo ati?
3 Chitsanzo chanu chabwino chingathandize kwambiri ana anu kuti ayambe kuyenda panjira yopita ku moyo wosatha. Ana anu akamaona kuti ‘mukufunafuna ufumu choyamba’ nawonso amayamba kudalira Yehova kuti aziwathandiza kupeza zinthu zofunika. (Mat. 6:33, 34) Choncho ndi bwino kukhala moyo wosalira zambiri ndipo muzipewa ngongole. Muziika zinthu zokhudza kutumikira Yehova pamalo oyamba, osati chuma. Muziyesetsa kusangalatsa Yehova. Mukatero ndiye kuti mukufunafuna “chuma kumwamba” osati chuma cha m’dzikoli kapena “ulemerero wa anthu.”—Werengani Maliko 10:21, 22; Yoh. 12:43.
4 Musamatanganidwe kwambiri mpaka kusowa nthawi yocheza ndi ana anu. Muziwauza kuti mumawayamikira akamaika Yehova pamalo oyamba m’malo mofunafuna ndalama zambiri kapena zinthu zimene zingachititse kuti iwowo kapena banja lanu litchuke. Musamakhale ndi maganizo oti ana ayenera kufunafuna ndalama n’cholinga choti inuyo mudzakhale ndi moyo wawofuwofu. Muzikumbukira mfundo yakuti, “ana sayenera kusunga chuma kuti chidzathandize makolo awo m’tsogolo, koma makolo ndi amene ayenera kusungira ana awo.”—2 Akor. 12:14.
MUZIYESETSA KUPHUNZITSA ANA ANU M’CHILANKHULO CHIMENE AMACHIDZIWA BWINO
5. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kulankhula ndi ana awo zokhudza Yehova?
5 Mogwirizana ndi zimene Baibulo linanena, anthu “ochokera m’zilankhulo zonse za anthu” akulowa m’gulu la Yehova. (Zek. 8:23) Koma ngati ana sadziwa bwino chilankhulo chanu, zingakhale zovuta kuwaphunzitsa za Yehova. Ana anu ndi ofunika kuwaphunzitsa Baibulo kuposa munthu wina aliyense ndipo zimenezi zingawathandize kuti adzapeze moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Kuti ana anu aphunzire mfundo za Yehova, muyenera kulankhula nawo pafupipafupi.—Werengani Deuteronomo 6:6, 7.
6. Kodi kuphunzira chilankhulo chanu kungathandize bwanji ana anu? (Onani chithunzi choyambirira.)
6 Ana anu angaphunzire chilankhulo cha dziko limene mukukhala akamapita kusukulu komanso kucheza ndi anthu a m’deralo. Koma angaphunzire chilankhulo chanu mukamacheza nawo nthawi zonse. Ana anu akadziwa chilankhulo chanu mukhoza kumacheza nawo momasuka kwambiri. Komanso kudziwa zilankhulo ziwiri kungathandize ana anu kukhala anzeru ndiponso kuti azitha kucheza ndi anthu osiyanasiyana. Kungawathandizenso kuti akhale ndi mwayi wochita zambiri potumikira Yehova. Mtsikana wina dzina lake Carolina, yemwe makolo ake amachokera m’dziko lina, anati: “Kutumikira mumpingo wachilankhulo china ndiponso kumene kukufunika ofalitsa ambiri n’kosangalatsa kwambiri.”
7. Kodi mungatani ngati mwana wanu sadziwa bwino chilankhulo chanu?
7 Komabe ana ena akayamba kuzolowera chikhalidwe ndiponso chilankhulo cha dziko limene asamukira, angasiye kuchita chidwi ndi chilankhulo cha makolo awo. Akhozanso kuiwala chilankhulocho mpaka kuvutika kwambiri kuti achilankhule. Ngati zili choncho ndi ana anu, mungachite bwino kuphunzira chilankhulo cha dziko limene mwasamukiralo. Mukachita zimenezi mudzatha kuphunzitsa bwino ana anu kuti akhale Akhristu. Zili choncho chifukwa mudzatha kumvetsa bwino zimene amalankhula, zimene amakonda ndiponso zimene akuphunzira kusukulu. Mudzathanso kulankhulana bwinobwino ndi aphunzitsi awo. N’zoona kuti kuphunzira chilankhulo china kumafuna nthawi, khama komanso kudzichepetsa. Koma tiyerekeze kuti mwana wanu wasiya kumva, kodi simungayesetse kuti muphunzire chinenero chamanja n’cholinga choti muzilankhulana naye? Ngati zili choncho, muyeneranso kuchita zomwezo kuti muthandize mwana amene sakudziwa bwino chilankhulo chanu. *
8. Kodi mungathandize bwanji ana anu ngati simukudziwa bwino chilankhulo chimene amalankhula?
2 Tim. 3:15) Ngati muli ndi vutoli, mukhozabe kuthandiza ana anu kuti adziwe Yehova ndiponso kumukonda. Mkulu wina dzina lake Shan anati: “Mayi athu ankatilera okha ndipo sankadziwa bwino chilankhulo chimene ine ndi azichemwali anga tinkalankhula. Komanso ifeyo sitinkalankhula bwino chilankhulo chawo. Komabe iwo ankaphunzira Baibulo, kupemphera komanso kuyesetsa kuti azichita nafe kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse. Zimenezi zinatithandiza kuzindikira kuti kudziwa bwino Yehova n’kofunika kwambiri.”
8 Komabe mwina sizingatheke kuti makolo aphunzire mpaka kudziwa bwinobwino chilankhulo chimene ana awo amalankhula bwino. Izi zingachititse kuti makolowo azivutika pothandiza ana awo kuti adziwe bwino “malemba oyera.” (9. Kodi makolo angathandize bwanji ana amene amafunika kuphunzira za Yehova m’zilankhulo ziwiri?
9 Ana ena amafunika kuphunzira za Yehova m’zilankhulo ziwiri, chimene amalankhula kusukulu komanso chimene amalankhula kunyumba. Choncho makolo ena amagwiritsa ntchito mabuku, magazini, zinthu zongomvetsera komanso mavidiyo a m’zilankhulo zonse ziwiri pophunzitsa ana awo. Apa zikuonekeratu kuti pamafunika khama komanso nthawi yambiri kuti makolo amene asamukira m’dziko lina azithandiza ana awo kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.
KODI MUYENERA KUKHALA MUMPINGO WACHILANKHULO CHITI?
10. (a) Kodi ndi ndani ayenera kusankha mpingo umene muyenera kusonkhana? (b) Kodi ayenera kuchita chiyani asanasankhe zochita pa nkhaniyi?
10 Ngati anthu asamukira m’dziko lina ndipo mulibe mpingo wachilankhulo chawo, ayenera kusonkhana mumpingo wachilankhulo cha dzikolo. (Sal. 146:9) Koma ngati mpingo wachilankhulo chanu ukupezeka, ndi bwino kudzifunsa kuti: Kodi tiyenera kukhala mumpingo wachilankhulo chiti? M’bale asanasankhe zochita, ayenera kuiganizira bwino nkhaniyi, kuipempherera komanso kukambirana ndi banja lake lonse. (1 Akor. 11:3) Kodi ndi mfundo ziti zimene ayenera kuziganizira? Tiyeni tikambirane zimenezi.
11, 12. (a) Kodi n’chiyani chingathandize ana kuphunzira zambiri kumisonkhano? (b) N’chiyani chingachititse kuti ana ena asafune kuphunzira chilankhulo cha makolo awo?
11 Makolo ayenera kuganizira bwino zimene ana awo akufunikira. N’zoona kuti mwana sangaphunzire mokwanira zokhudza Yehova pa nthawi yochepa imene amakhala pamisonkhano mlungu uliwonse. Komabe ana akamapita kumisonkhano imene imachitika m’chilankhulo chimene amachidziwa bwino akhoza kuphunzira zambiri, mwina kuposa zimene makolo awo angaganizire. Izi sizingachitike ngati ana sakudziwa bwino chilankhulo cha mpingo umene amasonkhana. (Werengani 1 Akorinto 14:9, 11.) Mwina chilankhulo chimene mwana anaphunzira ali wamng’ono kwambiri sichingakhalenso chilankhulo chimene amamvetsa bwino kapena chomwe chimamufika pamtima. Ana akhoza kumayankha pamisonkhano, kuchita zitsanzo komanso kukamba nkhani m’chilankhulo cha makolo awo koma nthawi zina zimene amanenazo sizichokera mumtima.
12 Mtima wa mwana ukhoza kukhudzidwa ndi zinthu zambiri osati chilankhulo chokha. Umu ndi mmene zinalili ndi Joshua yemwe tamutchula kale uja. Mchemwali wake dzina lake Esther anati: “Ana amaona kuti chilankhulo, chikhalidwe ndiponso chipembedzo cha makolo awo n’zogwirizana.” Choncho ngati ana samvetsa bwino chikhalidwe cha makolo awo mwina sangafune kuphunzira chilankhulo chawo komanso zimene amakhulupirira. Kodi anthu amene asamukira m’dziko lina angathandize bwanji ana awo pa nkhaniyi?
13, 14. (a) N’chifukwa chiyani banja lina linasankha kusamukira mumpingo wachilankhulo cha dziko limene ankakhala? (b) Kodi n’chiyani chinathandiza makolowo kuti akhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?
13 Makolo ayenera kuchita zimene zingathandize ana awo kuti azitumikira Yehova osati zongosangalatsa iwowo. (1 Akor. 10:24) Bambo a Joshua ndi Esther dzina lawo a Samuel anati: “Ine ndi mkazi wanga tinkachita chidwi kuti tidziwe chilankhulo chimene chingathandize ana athu kuti azitumikira bwino Mulungu ndipo tinapemphera kuti Mulungu atipatse nzeru. Zimene tinapeza si zimene zinkatisangalatsa. Koma titaona kuti ana athu sankamvetsa bwino misonkhano m’chilankhulo chathu, tinasankha zosamukira mumpingo wachilankhulo cha dziko limene tinkakhala. Nthawi zonse tinkapita limodzi ndi ana athu kumisonkhano komanso mu utumiki. Tinkaitananso anthu amumpingowo kuti adzadye nafe kunyumba kwathu komanso kuti apite nafe kwinakwake kukacheza. Zonsezi zinathandiza ana athu kuti adziwane ndi abale ndi alongo. Zinawathandizanso kudziwa bwino Yehova n’kumamuona kuti ndi Mulungu wawo, Atate wawo komanso Mnzawo wapamtima. Tinaona kuti zimenezi n’zofunika kwambiri kuposa kudziwa bwino chilankhulo chathu.”
14 A Samuel ananenanso kuti: “Koma kuti ine ndi mkazi wanga tipitirize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova tinkapitanso kumisonkhano ya m’chilankhulo chathu. N’zoona kuti tinkatanganidwa kwambiri komanso tinkakhala otopa. Koma tikuyamikira Yehova chifukwa chodalitsa khama lathu komanso kudzipereka kwathu. Ana athu onse atatu akuchita utumiki wa nthawi zonse.”
ZIMENE ACHINYAMATA ANGACHITE
15. N’chifukwa chiyani Kristina anaona kuti ndi bwino kusamukira mumpingo wachilankhulo cha m’dziko limene ankakhala?
15 Mwina achinyamata angaone kuti akhoza kutumikira bwino Yehova mumpingo wachilankhulo chimene amachidziwa bwino. Iwo akasankha kuchita zimenezi, makolo sayenera kuona kuti ana awo sakufuna kuchita nawo zinthu limodzi. Mlongo wina dzina lake Kristina anati: “Ndinkadziwa chilankhulo cha makolo anga, koma mawu ambiri amene anthu ankalankhula kumisonkhano sindinkawadziwa bwino. Koma ndili ndi zaka 12, ndinapita kumsonkhano wachilankhulo chimene tinkalankhula kusukulu. Aka kanali koyamba kumvetsa kuti zimene ndinkaphunzira zinalidi choonadi. Zinthu zinasinthanso pamene ndinayamba kupemphera m’chilankhulocho chifukwa ndinkatha kulankhula ndi Yehova kuchokera pansi pa mtima.” (Mac. 2:11, 41) Kristina atakulirapo, anakambirana ndi makolo ake ndipo anasankha kuti asamukire mumpingo wachilankhulo chimenecho. Iye anati: “Kuphunzira za Yehova m’chilankhulochi kunandilimbikitsa kuchita zambiri potumikira Yehova.” Pasanapite nthawi yaitali, Kristina anayamba kuchita upainiya wokhazikika.
16. N’chifukwa chiyani Nadia akusangalala kuti anakhalabe mumpingo wachilankhulo cha makolo ake?
16 Kodi achinyamatanu mumaona kuti mungakonde kukhala mumpingo wachilankhulo cha m’dziko limene mukukhala? Ngati zili choncho, dzifunseni chifukwa chimene mukufunira zimenezi. Kodi kukhala mumpingo umenewu kungakuthandizeni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova? (Yak. 4:8) Kapena kodi mukufuna kusamukira mumpingowo chifukwa chongofuna ufulu wambiri? Mlongo wina dzina lake Nadia, yemwe akutumikira ku Beteli, anati: “Ine ndi azichemwali anga komanso mchimwene wanga titakulirapo tinkafuna kusamukira mumpingo wachilankhulo cha m’dzikolo.” Koma makolo ake ankadziwa kuti zimenezi sizingathandize ana awowo kuti azitumikira bwino Mulungu. Nadia ananenanso kuti: “Panopa timayamikira kuti makolo athu ankayesetsa kuti atiphunzitse chilankhulo chawo komanso kuti tikhalebe mumpingo wachilankhulocho. Zimenezi zinatithandiza kudziwa zambiri komanso kukhala ndi mwayi waukulu wothandiza anthu kudziwa Yehova.”
KODI ANTHU ENA ANGATHANDIZE BWANJI?
17. (a) Kodi Yehova wapatsa ndani udindo wolera ana? (b) Kodi makolo angapemphe ndani kuti awathandize kuphunzitsa ana awo za Yehova?
17 Yehova wapatsa makolo, osati agogo kapena anthu ena, udindo wophunzitsa ana awo Mawu ake. (Werengani Miyambo 1:8; 31:10, 27, 28.) Komabe makolo amene sadziwa chilankhulo cha dziko limene asamukiralo mwina angafune kuti anthu ena aziwathandiza kuphunzitsa ana awo mogwira mtima. Izi sizikutanthauza kuti makolo azingosiyira anthu ena udindo wophunzitsa ana awo. Anthu enawo ndi ongothandiza makolowo pa udindo umene ali nawo ‘wolera ana awo m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.’ (Aef. 6:4) Mwachitsanzo, makolo angapemphe akulu mumpingo kuti awapatse malangizo okhudza mmene angachitire kulambira kwa pabanja komanso kuti athandize ana awo kupeza anzawo abwino.
18, 19. (a) Kodi abale ndi alongo achitsanzo chabwino angathandize bwanji achinyamata? (b) Kodi makolo ayenera kuchita chiyani?
18 Nthawi zina makolo angachitenso bwino kuitana mabanja ena kuti achite nawo kulambira kwa pabanja. Achinyamata angathandizidwenso ndi abale ndi alongo achitsanzo chabwino akamayenda nawo mu utumiki kapena kuchitira nawo limodzi zosangalatsa. (Miy. 27:17) Shan amene tamutchula kale uja ananena kuti: “Sindingaiwale abale amene ankandithandiza kwambiri. Ndinkaphunzira zambiri akamandithandiza kukonzekera nkhani. Ndinkamva bwinonso pamene tinkachitira limodzi zosangalatsa.”
19 Anthu amene apemphedwa ndi makolo kuti azithandiza ana awo ayenera kunena zinthu zabwino zokhudza makolowo akamalankhula ndi anawo. Izi zingathandize kuti anawo azilemekeza makolo awo. Komanso anthuwo sayenera kuona kuti apatsidwa udindo wa makolowo. Iwo ayeneranso kupewa kuchita zinthu zomwe zingapangitse anthu amumpingo kapena amene si Mboni kukayikira zolinga zawo. (1 Pet. 2:12) Nawonso makolowo sayenera kungosiyira anthu enawo udindo wophunzitsa ana awo za Yehova. M’malomwake ayenera kuchita chidwi ndi zimene anthuwo akuchita ndi ana awo komanso ayenera kupitiriza kuwaphunzitsa okha.
20. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale atumiki odalirika a Yehova?
20 Ngati ndinu makolo, muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni komanso kuchita zonse zimene mungathe pophunzitsa ana anu. (Werengani 2 Mbiri 15:7.) Muziona kuti udindo wothandiza ana anu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova ndi wofunika kwambiri kuposa zofuna zanu. Muziyesetsa kwambiri kuti mufike ana anu pamtima ndi Mawu a Mulungu. Musamakayikire kuti mwana wanu akhoza kukhala mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Ana anu akamatsatira Mawu a Mulungu komanso chitsanzo chanu, mudzamva ngati mmene Yohane ankamvera akaganizira za anthu amene anawaphunzitsa. Iye anati: “Palibe chimene chimandisangalatsa kwambiri kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.”—3 Yoh. 4.
^ ndime 7 Onani nkhani yakuti “Mungathe Kuphunzira Chinenero China!” mu Galamukani! ya March 2007, tsamba 10-12.