NKHANI YOPHUNZIRA 19
Tizisonyeza Chikondi ndi Chilungamo M’dziko Loipali
“Inu sindinu Mulungu wokondwera ndi zoipa, palibe munthu woipa amene angakhale ndi inu.”—SAL. 5:4.
NYIMBO NA. 142 Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-3. (a) Malinga ndi Salimo 5:4-6, kodi Yehova amamva bwanji akaona zoipa? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kugwirira mwana n’kosemphana kwambiri ndi “chilamulo cha Khristu”?
YEHOVA MULUNGU amadana ndi chinthu chilichonse choipa. (Werengani Salimo 5:4-6.) Ndiye mukuganiza kuti amamva bwanji munthu akachita tchimo loipa kwambiri logwirira mwana? Popeza timatsanzira Yehova, a Mboni za Yehovafe timadananso kwambiri ndi kugwirira ana moti nkhani imeneyi ikachitika mumpingo sitiilekerera.—Aroma 12:9; Aheb. 12:15, 16.
2 Kugwirira mwana ndi kosemphana kwambiri ndi “chilamulo cha Khristu.” (Agal. 6:2) N’chifukwa chiyani tikutero? Munkhani yapita ija tinaona kuti chilamulo cha Khristu chimatanthauza zinthu zonse zimene Yesu anaphunzitsa m’mawu ndi zochita zake. Tinaonanso kuti chilamulochi chinapangidwa chifukwa cha chikondi ndipo chimalimbikitsa chilungamo. Popeza Akhristu amatsatira lamulo limeneli, amathandiza ana kuti azimva kuti ndi otetezeka komanso amakondedwa. Koma munthu amene wagwirira mwana amasonyeza kuti ndi wodzikonda komanso wopanda chilungamo. Amachititsanso mwanayo kumva kuti si wotetezeka komanso sakondedwa.
3 N’zomvetsa chisoni kuti nkhani yogwirira ana ikufala kwambiri padziko lonse ndipo ngakhale Akhristu oona akhudzidwa ndi nkhaniyi. N’chifukwa chiyani zafika pamenepa? Masiku ano, anthu oipa akuchuluka ndipo ena amafuna kulowa mumpingo. (2 Tim. 3:13) Anthu enanso amene anali mumpingo amatengeka ndi zilakolako zoipa moti afika pogwirira ana. Tiyeni tikambirane chifukwa chake tikunena kuti kugwirira mwana ndi tchimo loipa kwambiri. Kenako tikambirana zimene akulu ayenera kuchita ngati munthu wina wachita tchimo lalikulu monga kugwirira mwana. Pomaliza, tikambirana mmene makolo angatetezere ana awo. *
TCHIMO LALIKULU
4-5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu amachimwira mwana ngati wamugwirira?
4 Kugwirira mwana kumasokoneza anthu kwa nthawi yaitali. Anthu amene agwiriridwa, achibale awo komanso abale ndi alongo mumpingo amakhudzidwa kwambiri. Choncho tinganene kuti kugwirira mwana ndi tchimo lalikulu kwambiri.
5 Amachimwira mwana amene wamugwirirayo. Kupweteka munthu wina mopanda chilungamo n’kuchimwa. Munkhani yotsatira tidzaona kuti munthu amene wagwirira mwana amapweteka mwanayo koopsa. Iye amachititsa mwanayo kumva kuti si wotetezeka ndiponso kuti asamakhulupirire anthu. Choncho ana ayenera kutetezedwa kuti zoipazi zisawachitikire ndipo anthu amene agwiriridwa amafunika kulimbikitsidwa komanso kuthandizidwa.—1 Ates. 5:14.
6-7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu akagwirira mwana amachimwira mpingo komanso boma?
6 Amachimwira mpingo. Ngati munthu wamumpingo wagwirira mwana, amaipitsa mbiri ya mpingo. (Mat. 5:16; 1 Pet. 2:12) Amakhala kuti wachitira zinthu zopanda chilungamo Akhristu okhulupirika mamiliyoni ambiri, omwe akuyesetsa “kumenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro.” (Yuda 3) Sitimalekerera anthu amene aipitsa mbiri yabwino ya mpingo chifukwa chochita tchimo lalikulu ndipo sanalape.
7 Amachimwira boma. Akhristu ayenera ‘kumvera olamulira akuluakulu.’ (Aroma 13:1) Timakhala omvera tikamatsatira malamulo a dziko limene tikukhala. Munthu wamumpingo akaphwanya lamulo la dziko pochita zinthu monga kugwirira mwana ndiye kuti wachimwira boma. (Yerekezerani ndi Machitidwe 25:8.) Ngakhale kuti si udindo wa akulu kuimba munthu mlandu chifukwa chophwanya malamulo a boma, sateteza munthu yemwe wagwirira mwana kuti asaimbidwe mlandu ndi bomalo. (Aroma 13:4) Munthu wolakwayo amakolola zimene wafesa.—Agal. 6:7.
8. Kodi Yehova amamva bwanji ngati munthu wachimwira munthu mnzake?
8 Koposa zonse, amachimwira Mulungu. (Sal. 51:4) Munthu akachimwira munthu mnzake amakhala kuti wachimwiranso Yehova. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Chilamulochi chinkanena kuti munthu amene wabera mnzake ‘wachita mosakhulupirika kwa Yehova.’ (Lev. 6:2-4) Munthu wamumpingo amene wagwirira mwana amachititsa kuti mwanayo azimva kuti ndi wosatetezeka. Choncho tinganene kuti wachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova. Munthuyo amaipitsa kwambiri dzina la Yehova. N’chifukwa chake tinganene kuti munthu amene wagwirira mwana amachimwira kwambiri Mulungu.
9. Kodi gulu la Yehova lakhala likupereka malangizo ati, nanga n’chifukwa chiyani limachita zimenezi?
9 Gulu la Yehova lakhala likupereka malangizo ambiri ochokera m’Malemba othandiza pa nkhani yogwirira mwana. Mwachitsanzo, nkhani za mu Nsanja ya Olonda komanso
Galamukani! zafotokoza zimene zingathandize anthu omwe agwiriridwa kuti mtima wawo ukhale m’malo, mmene anthu ena angawalimbikitsire komanso zimene makolo angachite kuti ateteze ana awo. Akulu aphunzitsidwanso mfundo zambiri zokhudza zimene angachite ngati munthu wagwirira mwana. Ndipotu gulu likupitiriza kuonanso zimene mipingo iyenera kuchita munthu akagwirira mwana. Zili choncho chifukwa limafuna kutsimikizira kuti zimene mipingo imachita n’zogwirizana ndi chilamulo cha Khristu.ZIMENE AKULU AYENERA KUCHITA MUNTHU AKACHITA TCHIMO LALIKULU
10-12. (a) Kodi akulu ayenera kukumbukira mfundo iti akamasamalira nkhani zokhudza machimo akuluakulu, nanga ayenera kuganizira za chiyani? (b) Malinga ndi Yakobo 5:14, 15, kodi akulu ayenera kuyesetsa kuchita chiyani?
10 Kodi akulu ayenera kukumbukira mfundo iti akamasamalira nkhani zokhudza machimo akuluakulu? Ayenera kukumbukira kuti chilamulo cha Khristu chimafuna kuti akuluwo azisamalira nkhosa mwachikondi. Chimafunanso kuti azichita zinthu zimene Mulungu amaona kuti ndi zoyenera komanso zachilungamo. Choncho akulu akamva kuti munthu wina wachita tchimo lalikulu ayenera kuganizira mfundo zambiri. Akulu amaganizira kwambiri zimene angachite kuti dzina la Mulungu lisadetsedwe. (Lev. 22:31, 32; Mat. 6:9) Iwo amaganiziranso zoteteza abale ndi alongo mwauzimu ndiponso amayesetsa kuthandiza aliyense amene walakwiridwa.
11 Ngati wochimwayo ndi munthu wamumpingo, akulu amaganiziranso zomuthandiza kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova, ngati n’zotheka. (Werengani Yakobo 5:14, 15.) Mkhristu amene amatengeka ndi zilakolako zoipa mpaka kufika pochita tchimo lalikulu, amakhala kuti akudwala mwauzimu. Apa tikutanthauza kuti munthuyo salinso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. * Ndiyeno akulu amakhala ngati madokotala amene amayesetsa ‘kuchiritsa wodwalayo.’ Ngati munthuyo walapa kuchokera mumtima, malangizo awo ochokera m’Malemba angamuthandize kuti akonze ubwenzi wake ndi Mulungu.—Mac. 3:19; 2 Akor. 2:5-10.
12 Apa zikuonekeratu kuti akulu ali ndi udindo waukulu kwambiri. Iwo amakonda kwambiri nkhosa zimene Mulungu wawapatsa kuti aziziyang’anira. (1 Pet. 5:1-3) Amafuna kuti abale ndi alongo azimva kuti ndi otetezeka mumpingo. Choncho akulu akamva kuti munthu wina wachita tchimo lalikulu monga kugwirira mwana, amasamalira nkhaniyo mwamsanga. Kuti mudziwe zimene amachita, onani mayankho a mafunso amene ali mundime 13, 15 ndi 17.
13-14. Kodi akulu amatsatira lamulo lokanena ku boma ngati wina akuganiziridwa kuti wagwirira mwana? Fotokozani.
13 Kodi akulu ayenera kutsatira lamulo lokanena ku boma ngati wina akuganiziridwa kuti wagwirira mwana? Inde. M’mayiko kumene kuli lamulo loti anthu azikanena ku boma ngati wina akuganiziridwa kuti wagwirira mwana, akulu amayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi lamuloli. (Aroma 13:1) Zili choncho chifukwa malamulo ngati amenewa sasemphana ndi malamulo a Mulungu. (Mac. 5:28, 29) Choncho akulu akangomva kuti munthu wina wagwirira mwana, amapempha malangizo ku ofesi ya nthambi n’cholinga choti achite zinthu mogwirizana ndi malamulo a boma.
14 Akulu amauzanso ana amene agwiriridwa, makolo awo kapena anthu ena amene akudziwa
za nkhaniyi kuti akhoza kukanena nkhaniyo ku boma. Koma tiyerekeze kuti munthu amene akuganiziridwa kuti wagwirira mwana ndi wamumpingo. Ndiyeno Mkhristu wina anakanena nkhaniyo ku boma ndipo zachititsa kuti anthu ambiri a m’deralo aidziwe. Kodi Mkhristu ameneyu ayenera kuganiza kuti waipitsa dzina la Mulungu? Ayi. Zili choncho chifukwa chakuti wogwirirayo ndi amene waipitsa dzina la Mulungu.15-16. (a) Malinga ndi 1 Timoteyo 5:19, n’chifukwa chiyani pamafunika mboni ziwiri akulu asanakonze zoweruza nkhani? (b) Kodi akulu ayenera kuchita chiyani akangomva zoti munthu wina wagwirira mwana?
15 N’chifukwa chiyani payenera kukhala mboni ziwiri akulu asanakonze zoweruza nkhani kumpingo? Zimenezi zimagwirizana ndi mfundo zachilungamo zopezeka m’Baibulo. Ngati munthu sakuvomereza kuti wachita tchimo, payenera kukhala mboni ziwiri kuti akulu akonze zoweruza nkhaniyo. (Deut. 19:15; Mat. 18:16; werengani 1 Timoteyo 5:19.) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti munthu asanakanene ku boma ayeneranso kukhala ndi mboni ziwiri? Ayi. Pa nkhani yokanena ku boma za mlandu ngati umenewu, akulu kapena anthu ena sayenera kudikira kuti papezeke mboni ziwiri.
16 Zikangomveka kuti munthu wina mumpingo wagwirira mwana, akulu ayenera kutsatira malamulo a boma okhudza kukanena nkhaniyi, kenako ayenera kutsatira njira za m’Malemba zofufuzira nkhaniyo. Munthu woganiziridwayo akakana nkhaniyi, akulu ayenera kumva zimene mboni zina zikunena. Ngati pali mboni ziwiri, akulu akhoza kukonza komiti yoweruza. Mboni yoyamba ikhoza kukhala munthu amene wanena za nkhaniyi ndipo yachiwiri ikhoza kukhala munthu amene anaonanso zimenezi zikuchitika kapena kuona munthuyo akuchitanso zofananazo nthawi ina. * Koma ngati palibe mboni yachiwiri sizitanthauza kuti mboni yoyambayo sikunena zoona. Ngakhale zitakhala kuti mboni yachiwiri palibe, akulu ayenera kuzindikira kuti mwina munthuyo wachitadi tchimo lalikulu lomwe likupweteka kwambiri anthu ena. Choncho akulu ayenera kupitiriza kulimbikitsa anthu onse amene apwetekedwa ndi nkhaniyo. Ayeneranso kukhala tcheru ndi munthu amene akuganiziridwayo n’cholinga choti ateteze mpingo.—Mac. 20:28.
17-18. Kodi udindo wa komiti yoweruza umakhala wotani?
17 Kodi akulu amene ali mu komiti yoweruza ayenera kuchita chiyani? Mawu oti komiti yoweruza satanthauza kuti akulu amaweruza ngati munthu amene akuganiziridwayo ndi woyenera kulangidwa ndi boma kapena ayi. Akulu salowerera nkhani zokhudza malamulo a boma koma amalola kuti akuluakulu a boma asamalire nkhani ngati zimenezi. (Aroma 13:2-4; Tito 3:1) Akuluwo amaweruza ngati munthuyo ndi woyenera kukhalabe mumpingo kapena ayi.
18 Udindo wa akulu amene ali mu komiti yoweruza umakhala wokhudza ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova komanso mpingo. Iwo amagwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba kuti aweruze ngati munthu wolakwayo ali ndi mtima wolapa kapena ayi. Ngati munthuyo sanalape, amachotsedwa ndipo chilengezo chimaperekedwa kumpingo. (1 Akor. 5:11-13) Koma ngati walapa ndi mtima wonse akhoza kukhalabe mumpingo. Koma akuluwo ayenera kumuuza kuti sangapatsidwe ntchito kapena udindo uliwonse mumpingo kwa zaka zambiri kapenanso kwa moyo wake wonse. Pofuna kuteteza ana, akulu akhoza kuchenjeza makolo mwachinsinsi kuti azionetsetsa mmene ana awo akuchezera ndi munthuyo. Koma poteteza anawo, akulu ayenera kusamala kuti asaulule anthu amene anagwiriridwa.
ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZITETEZA ANA ANU
19-22. Kodi makolo angateteze bwanji ana awo? (Onani chithunzi patsamba loyamba la magaziniyi.)
19 Makolo ndi amene ali ndi udindo waukulu woteteza ana awo. * Paja Baibulo limati ana ndi “cholowa chochokera kwa Yehova,” kapena kuti mphatso imene iye wawapatsa. (Sal. 127:3) Choncho ndi udindo wa makolo kuteteza anawo. Kodi mungateteze bwanji ana anu kuti asagwiriridwe?
20 Choyamba, muyenera kudziwa zambiri zokhudza anthu ogwirira ana. Muyenera kudziwa za anthu amene amagwirira ana komanso zimene amachita pofuna kuwanyengerera. Nthawi zonse muyenera kukhala tcheru kuti muzindikire ngati ana anu angakhale pa ngozi. (Miy. 22:3; 24:3) Muzikumbukira kuti nthawi zambiri ana amagwiriridwa ndi munthu amene akumudziwa komanso kumukhulupirira.
21 Chachiwiri, muzicheza ndi ana anu momasuka. (Deut. 6:6, 7) Kuti muchite zimenezi, muyenera kumvetsera bwino ana anu akamalankhula. (Yak. 1:19) Muyenera kukumbukira kuti ana amene agwiriridwa amaopa kuuza anthu ena. Mwina amaganiza kuti anthu sangawakhulupirire, apo ayi munthu amene wawagwirirayo akhoza kuwaopseza kuti asaulule. Ngati mukukayikira kuti mwina zinazake zachitika, muyenera kuwafunsa mafunso mokoma mtima ndipo muziwamvetsera moleza mtima akamafotokoza.
22 Chachitatu, muziphunzitsa ana anu. Muziwafotokozera nkhani zokhudza kugonana zogwirizana ndi msinkhu wawo. Muziwaphunzitsa zimene anganene komanso kuchita ngati munthu wina akufuna kuwagwira mosayenera. Powaphunzitsa, muzigwiritsa ntchito malangizo amene gulu la Yehova lapereka pa nkhani yoteteza ana.—Onani bokosi lakuti “ Muziphunzira Komanso Kuphunzitsa Ana Anu.”
23. Kodi nkhani yogwirira ana timaiona bwanji, nanga tidzakambirana funso liti munkhani yotsatira?
23 A Mboni za Yehovafe timaona kuti kugwirira ana ndi tchimo lalikulu komanso loipa kwambiri. Popeza timatsatira chilamulo cha Khristu, mipingo yathu siteteza anthu amene agwirira ana kuti asalangidwe. Koma kodi tingathandize bwanji anthu amene anagwiriridwa? Tidzakambirana yankho la funso limeneli munkhani yotsatira.
NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso za Amuna
^ ndime 5 Munkhaniyi tikambirana mmene tingatetezere ana kuti asagwiriridwe. Tiona zimene akulu angachite poteteza mpingo komanso mmene makolo angatetezere ana awo.
^ ndime 3 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kugwirira mwana kumatanthauza zinthu zimene munthu wamkulu angachite kwa mwana n’cholinga choti akhutiritse chilakolako chake cha kugonana. Apa tikutanthauza zinthu monga kugona mwanayo kwenikweni, kumugona mkamwa kapena kumatako, kumuseweretsa maliseche, mabere kapena matako. Tizikumbukira kuti mwana akagwiriridwa amakhala kuti wachitiridwa nkhanza kwambiri ndipo iyeyo ndi wosalakwa. N’zoona kuti amene amagwiriridwa kawirikawiri ndi atsikana koma anyamata ambiri amagwiriridwanso. Nthawi zambiri amuna ndi amene amagwirira ana koma akazi ena amachitanso zimenezi.
^ ndime 11 Ngakhale munthu atachita tchimo chifukwa choti akudwala mwauzimu amakhala kuti wapalamulabe mlandu. Amafunika kuyankha mlanduwo kwa Yehova chifukwa chosankha zinthu mopanda nzeru komanso kuchita zinthu zoipa.—Aroma 14:12.
^ ndime 16 Akulu sayenera kupempha kuti mwana amene wagwiriridwa akhalepo pamene akulankhula ndi munthu amene wamugwirirayo. Ndi bwino kuti makolo kapena munthu wina amene mwanayo amamudalira afotokozere akulu zimene mwanayo akunena. Izi zingathandize kuti maganizo a mwanayo asapitirize kusokonezeka.
^ ndime 19 Malangizowa ndi othandizanso kwa anthu amene si makolo koma ali ndi udindo wosamalira ana.