NKHANI YOPHUNZIRA 20
Tizilimbikitsa Anthu Amene Achitiridwa Zoipa
“Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 AKOR. 1:3, 4.
NYIMBO NA. 134 Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti anthu amafuna kulimbikitsidwa komanso ali ndi luso lolimbikitsa anzawo. (b) Kodi ana ena amapwetekedwa bwanji?
MWACHIBADWA, anthu amafuna kulimbikitsidwa komanso amakhala ndi luso lolimbikitsa anzawo. Mwachitsanzo, mwana akagwa n’kuvulala pamene akusewera, amathamangira mayi kapena bambo ake uku akulira. N’zoona kuti makolowo sangapoletse bala koma akhoza kutonthoza mwanayo. Akhoza kumufunsa zimene zachitika, kumupukuta misozi, kumutonthoza, mwinanso kumupaka mankhwala kapena kumumanga bandeji. Pasanathe nthawi yaitali, mwanayo amatonthola ndipo amakaseweranso. Pakapita nthawi, balalo limapola.
2 Koma nthawi zina ana amapwetekedwa kwambiri. Mwachitsanzo, ena amagwiriridwa. Zimenezi zikhoza kuchitika kamodzi kapena mobwerezabwereza kwa zaka zambiri. Kaya zinachitika kangati, mfundo ndi yakuti kugwiriridwa kumasokoneza munthu kwa nthawi yaitali. Nthawi zina, wogwirira amagwidwa n’kulangidwa, pomwe ena salangidwa. Koma ngakhale wogwirirayo atalangidwa mwachilungamo, mwana amene wagwiriridwa akhoza kuvutika kwa zaka zambiri.
3. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 1:3, 4, kodi Yehova amafuna chiyani, nanga tikambirana mafunso ati?
3 Ngati Mkhristu amene anagwiriridwa ali mwana akuvutikabe, kodi angathandizidwe bwanji? (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) N’zosachita kufunsa kuti Yehova amafuna kuti anthu ake azikondedwa komanso kulimbikitsidwa kwambiri. Choncho tiyeni tikambirane mafunso atatu awa: (1) N’chifukwa chiyani anthu amene anagwiriridwa ali ana amafunika kulimbikitsidwa? (2) Kodi ndi ndani amene angawalimbikitse? (3) Kodi tingawalimbikitse bwanji?
N’CHIFUKWA CHIYANI AMAFUNIKA KULIMBIKITSIDWA?
4-5. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuzindikira kuti ana amasiyana ndi anthu akuluakulu? (b) Kodi kugwiriridwa kungakhudze bwanji mwana pa nkhani yokhulupirira anthu ena?
4 Anthu ena amene anagwiriridwa ali ana angafunike kulimbikitsidwa ngakhale kuti padutsa zaka zambiri. Kuti timvetse chifukwa chake, tiyenera kuzindikira kuti ana amasiyana kwambiri ndi anthu akuluakulu. Mwana akachitiridwa zoipa amakhudzidwa mosiyana kwambiri ndi munthu wamkulu. Tiyeni tikambirane zitsanzo zina pa nkhaniyi.
5 Ana amafunika kudalira komanso kugwirizana kwambiri ndi anthu amene akuwasamalira. Zimenezi zimathandiza kuti anawo azimva kuti ndi otetezeka ndipo savutika kukhulupirira anthu ena amene amawakonda. (Sal. 22:9) N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri mwana amagwiriridwa ali kunyumba ndipo amene amamugwirirayo amakhala wa m’banja lake kapena mnzawo wa anthu a m’banjalo. Mwana akasiya kukhulupirira anthu a m’banja lake, zimamuvuta kuti azikhulupirira anthu ena ngakhale patadutsa zaka zambiri.
6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kugwirira mwana ndi nkhanza kwambiri?
6 Ana sangathe kudziteteza ndipo kuwagwirira ndi nkhanza kwambiri. Kugwirira mwana kungamusokoneze kwambiri chifukwa choti amakhala asanafike msinkhu woti angalowe m’banja n’kuyamba kugonana. Kungamuchititse kuti akhale ndi maganizo olakwika okhudza kugonana, azidziona kuti ndi wachabechabe komanso azikayikira aliyense amene akufuna kugwirizana naye.
7. (a) N’chifukwa chiyani munthu wogwirira sangavutike kunyengerera mwana, nanga angamuchititse kukhulupirira mabodza ati? (b) Kodi mabodza oterewa angakhudze bwanji mwana?
7 Ana amakhala asanafike poganiza bwinobwino kapena pozindikira zinthu zoopsa n’kumazipewa. (1 Akor. 13:11) Choncho anthu ogwirira savutika kunyengerera ana. Anthuwo amachititsa ana kukhulupirira mabodza oopsa. Mwachitsanzo, mwanayo angakhulupirire kuti iyeyo ndi amene wachititsa kuti agwiriridwe. Angakhulupirirenso kuti sayenera kuulula zimene zachitika ndipo akaulula palibe munthu amene angazisamale kapena kukhulupirira. Akhoza kukhulupiriranso kuti palibe vuto ngati akuluakulu agonana ndi ana chifukwa ndi njira yongosonyezera chikondi. Mabodza oterewa angasokoneze maganizo a mwana kwa zaka zambiri. Mwanayo akhoza kumaganiza kuti ndi woipa komanso wosayenera kukondedwa kapena kulimbikitsidwa.
8. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova akhoza kulimbikitsa anthu amene achitiridwa zoipa?
8 Apa zikuonekeratu kuti mwana akagwiriridwa amavutika kwa zaka zambiri. Choncho tinganene kuti tchimo limeneli ndi loipa kwambiri. Kufala kwa zoipa ngati zimenezi ndi umboni wamphamvu wakuti tikukhala m’masiku otsiriza pamene anthu ambiri ndi “osakonda achibale awo” ndipo ‘anthu oipa ndi onyenga akuipiraipirabe.’ (2 Tim. 3:1-5, 13) Zochita za Satana ndi zoipa kwambiri ndipo zimakhala zomvetsa chisoni anthu akamachita zofuna zake. Koma Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana komanso aliyense amene amachita zofuna za Satanayo. Yehova amadziwa chilichonse chimene Satana amachita. Iye amadziwanso mmene tikuvutikira ndipo amatilimbikitsa m’njira yoyenera. Ndi mwayi waukulu kutumikira “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse, kuti tithe kutonthoza amene ali m’masautso amtundu uliwonse, chifukwa nafenso tatonthozedwa ndi Mulungu.” (2 Akor. 1:3, 4) Koma kodi Yehova amagwiritsa ntchito ndani kuti alimbikitse anthu?
KODI NDI NDANI AMENE ANGAWALIMBIKITSE?
9. Malinga ndi mawu a Mfumu Davide pa Salimo 27:10, kodi Yehova adzachitira chiyani anthu amene asiyidwa ndi makolo kapena achibale awo?
9 Anthu amene makolo awo sanawateteze kapena amene anagwiriridwa ndi a m’banja lawo angafunike kulimbikitsidwa kwambiri. Davide ankadziwa kuti Yehova ndi amene angalimbikitse munthu nthawi zonse. (Werengani Salimo 27:10.) Iye sankakayikira kuti Yehova angasamalire anthu amene asiyidwa ndi makolo kapena achibale awo. Koma kodi Mulungu amachita bwanji zimenezi? Iye amagwiritsa ntchito atumiki ake okhulupirika. Akhristu anzathu ali ngati anthu a m’banja lathu. Mwachitsanzo, Yesu ankaona kuti anthu amene ankamutsatira polambira Yehova anali abale, alongo ndi amayi ake.—Mat. 12:48-50.
10. Kodi mtumwi Paulo anafotokoza bwanji zimene ankachita monga mkulu?
10 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Paulo. Iye anali mkulu ndipo ankagwira ntchito mwakhama mumpingo. Paulo ankachita bwino zinthu chifukwa ankatsanzira Khristu ndipo Mulungu anamuuzira kulemba kuti anthu ena azimutsanzira. (1 Akor. 11:1) Pofotokoza zimene iyeyo ankachita monga mkulu, analemba kuti: “Tinakhala odekha pakati panu monga mmene mayi woyamwitsa amasamalirira ana ake.” (1 Ates. 2:7) Masiku anonso, akulu ayenera kukhala odekha komanso kusankha bwino mawu akamalimbikitsa anthu pogwiritsa ntchito Malemba.
11. N’chiyani chikusonyeza kuti si akulu okha amene angalimbikitse anthu ena?
11 Kodi ndi akulu okha amene angalimbikitse anthu amene anagwiriridwa? Ayi. Tonsefe tili ndi udindo woti ‘tizilimbikitsana.’ (1 Ates. 4:18) Alongo olimba mwauzimu angalimbikitse kwambiri alongo ena amene akuvutika. M’pake kuti Yehova Mulungu ananena kuti iye ali ngati mayi amene amatonthoza mwana wake. (Yes. 66:13) M’Baibulo muli zitsanzo za akazi amene analimbikitsa anzawo. (Yobu 42:11) Yehova amasangalala kwambiri akamaona alongo amene amalimbikitsa alongo anzawo omwe akuda nkhawa. Nthawi zina, akulu angapemphe mwachinsinsi mlongo wina wolimba mwauzimu kuti athandize mlongo amene akuvutika maganizo. *
KODI TINGAWALIMBIKITSE BWANJI?
12. Kodi si bwino kuchita chiyani?
12 Tonsefe timadziwa kuti si bwino kulowerera nkhani zimene Mkhristu wina safuna kuti ena azidziwe. (1 Ates. 4:11) Koma kodi tingatani ngati anthu ena akufuna kuthandizidwa komanso kulimbikitsidwa? Tiyeni tikambirane njira 5 za m’Malemba zomwe tingatsatire powalimbikitsa.
13. Malinga ndi 1 Mafumu 19:5-8, kodi mngelo wa Yehova anathandiza bwanji Eliya, nanga ife tingamutsanzire bwanji?
13 Tizichita zinthu zowathandiza. Pamene Eliya ankathawa, anavutika kwambiri maganizo moti ankaona kuti bola kungofa. Ndiyeno Yehova anatumiza mngelo kwa mneneriyu ndipo mngeloyo anachita zinthu zomuthandiza. Iye anapatsa Eliya chakudya chotentha bwino n’kumuuza kuti adye. (Werengani 1 Mafumu 19:5-8.) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Nthawi zina, kungochita zinthu zochepa kungathandize kwambiri munthu. M’bale kapena mlongo amene akuvutika maganizo akhoza kulimbikitsidwa kwambiri ngati titangomuchitira zinthu monga kumukonzera chakudya, kumupatsa kamphatso kapena kumulembera kakhadi. Ngati timavutika kukambirana ndi anthu nkhani yachinsinsi kapena imene ikuwapweteka kwambiri, tikhoza kuchita zinthu zothandiza ngati zimenezi.
14. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Eliya?
14 Tizithandiza anthu amene akuvutika kuti azimasuka komanso kuona kuti ndi otetezeka. Pali mfundo inanso imene tingaphunzire pa nkhani ya Eliya. Yehova anamupatsa mphamvu zodabwitsa kuti athe kuyenda mtunda wautali mpaka kukafika kuphiri la Horebe. N’kutheka kuti Eliya anamva kuti ndi wotetezeka atafika paphirili, pomwe Yehova m’mbuyomo anachita pangano ndi anthu ake. Mwina ankaona kuti pamene wafikapo adani ake sangamupezenso. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Ngati tikufuna kulimbikitsa anthu amene anachitiridwa nkhanza, choyamba tiyenera kuwathandiza kuzindikira kuti ndi otetezeka. Mwachitsanzo, akulu ayenera kukumbukira kuti mlongo wina amene akuvutika maganizo akhoza kukhala womasuka ngati ali kunyumba kwawo osati ku Nyumba ya Ufumu. Koma wina angamasuke ngati atakhala ku Nyumba ya Ufumu.
15-16. Kodi munthu womvetsera bwino amatani?
15 Tizimvetsera bwino. Baibulo limatilangiza momveka bwino kuti: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.” (Yak. 1:19) Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimamvetsera bwino?’ Mwina tingaganize kuti kumvetsera kumangotanthauza kukhala phee n’kumayang’ana munthu amene akulankhulayo popanda kuyankha chilichonse. Koma kumvetsera bwino kumatanthauza zambiri. Mwachitsanzo, pamene Eliya ankafotokoza zimene zinkamudetsa nkhawa, Yehova anamvetsera bwinobwino. Iye anazindikira kuti Eliya ali ndi mantha, akumva kuti ali yekhayekha komanso akuona kuti ntchito yonse imene anagwira yapita pachabe. Ndiyeno Yehova anamuthandiza pa mavuto onsewa. Apa anasonyeza kuti ankamvetseradi zimene Eliya ankafotokoza.—1 Maf. 19:9-11, 15-18.
16 Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife achifundo komanso tikumvera munthu chisoni pa nthawi imene tikumumvetsera? Nthawi zina, mawu ochepa koma osankhidwa bwino angasonyeze mmene tikumvera mumtima mwathu. Mwina tinganene kuti, “Iii pepani kwambiri 1 Akor. 13:4, 7.
kuti zimenezo zinakuchitikirani! Si bwino kuti mwana azichitiridwa zinthu ngati zimenezo.” Tikhoza kufunsanso funso limodzi kapena awiri otithandiza kumvetsa bwino zimene munthuyo akutanthauza. Mwina tinganene kuti, “Ndikufuna ndingomvetsa zimene mukutanthauza pamene mwanena kuti . . . ?” Apo ayi, tinganene kuti, “Pamene mwanena zakutizakuti ndikumva ngati mukutanthauza kuti . . . , kaya ndamva bwino?” Mawu ngati amenewa, angathandize munthu kutsimikizira kuti tikumvetseradi ndipo tikufuna kudziwa zolondola.—17. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima komanso ‘odekha polankhula’?
17 Koma tiyenera kukhala ‘odekha polankhula.’ Si bwino kudula munthu mawu n’cholinga choti timupatse malangizo kapena timuthandize kusintha maganizo olakwika. Tiyenera kukhala oleza mtima. Pamene Eliya ankafotokozera Yehova zimene zinkamudetsa nkhawa analankhula mowawidwa mtima kwambiri. Ngakhale pamene Yehova anamulimbikitsa, iye analankhulanso mawu omwewo. (1 Maf. 19:9, 10, 13, 14) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Nthawi zina, munthu amene akuda nkhawa angafotokoze zimene zili mumtima mwake mobwerezabwereza. Choncho tiyenera kutsanzira Yehova n’kumamvetsera moleza mtima. M’malo mofulumira kupereka malangizo, tiyenera kusonyeza chifundo chachikulu.—1 Pet. 3:8.
18. Kodi tingatani kuti mapemphero athu alimbikitse munthu amene akuda nkhawa?
18 Tizipemphera nawo kuchokera mumtima. Anthu amene akuda nkhawa angavutike kupemphera. Mwina angaganize kuti si oyenera kulankhula ndi Yehova. Kuti tiwalimbikitse, tikhoza kupemphera nawo ndipo tizitchula dzina lawo m’pempherolo. Popempherapo tinganene mawu osonyeza kuti ifeyo komanso abale ndi alongo mumpingo amakonda kwambiri munthuyo. Tingapemphe Yehova kuti alimbikitse komanso kutonthoza mtumiki Yak. 5:16.
wake wamtengo wapataliyo. Mapemphero ngati amenewa angalimbikitse kwambiri munthuyo.—19. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tilimbikitse munthu?
19 Tizisankha mawu olimbikitsa. Tiyenera kuganiza tisanalankhule. Tikamalankhula tisanaganize, mawu athu akhoza kukhala opweteka. Koma tikamalankhula mokoma mtima, anthu amalimbikitsidwa. (Miy. 12:18) Choncho tizipempha Yehova kuti atithandize kusankha bwino mawu n’cholinga choti tilankhule mokoma mtima komanso molimbikitsa. Tizikumbukira kuti mawu a Yehova omwe ali m’Baibulo ndi amphamvu kuposa mawu ena alionse.—Aheb. 4:12.
20. Kodi anthu amene anagwiriridwa angakhale ndi maganizo ati, nanga tingawathandize bwanji?
20 Munthu amene anagwiriridwa akhoza kumaganiza kuti ndi wachabechabe, sakondedwa ndipo mwina sangakondedwenso. Koma limeneli ndi bodza lenileni. Choncho tizigwiritsa ntchito Malemba pothandiza munthuyo kudziwa kuti ndi wamtengo wapatali kwa Yehova. (Onani bokosi lakuti “ Malemba Olimbikitsa.”) Tizikumbukira mmene mngelo analimbikitsira Danieli pa nthawi imene anafooka. Yehova ankafuna kuti mneneriyu adziwe kuti amakondedwa kwambiri. (Dan. 10:2, 11, 19) Yehova amakondanso abale ndi alongo amene akuvutika maganizo.
21. Kodi anthu amene amachita zoipa ndipo salapa zidzawathera bwanji, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani panopa?
21 Tikamalimbikitsa anthu, timawathandiza kuzindikira kuti Yehova amawakonda. Tisamaiwalenso kuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo. Iye amaona nkhanza zilizonse zimene munthu angachitiridwe. Yehova adzaonetsetsa kuti munthu aliyense amene anachita nkhanza ndipo sanalape alangidwe. (Num. 14:18) Koma panopa tiyeni tizichita zonse zimene tingathe polimbikitsa anthu amene anagwiriridwa. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova adzathandiza anthu kuti asadzavutikenso maganizo chifukwa cha mavuto onse amene anakumana nawo m’dziko la Satanali. Posachedwapa, mavuto onsewa sadzabweranso m’maganizo kapena m’mitima yathu.—Yes. 65:17.
NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima
^ ndime 5 Anthu amene anagwiriridwa ali ana amavutikabe ngakhale patapita zaka zambiri. Nkhaniyi itithandiza kumvetsa chifukwa chake zili choncho. Tikambirananso kuti ndi ndani amene angalimbikitse anthu amenewa. Pomaliza, tikambirana zimene tingachite kuti tiwalimbikitse.
^ ndime 11 Munthu amene akuvutika maganizo chifukwa choti anagwiriridwa ayenera kusankha yekha ngati angafune kupita kuchipatala kapena ayi.
^ ndime 76 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wolimba mwauzimu akulimbikitsa mlongo amene ali ndi nkhawa
^ ndime 78 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI : Akulu awiri apita kukaona mlongo amene akuda nkhawa ndipo mlongoyo waitananso mlongo amene anamulimbikitsa uja