Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi ntchito za mtumiki woyang’anira nyumba zinali zotani?

KALE, mtumiki woyang’anira nyumba anali ndi udindo woyang’anira malo kapena zinthu zonse za m’nyumba ya mbuye wake.

Pamene Yosefe, mwana wa Yakobo, anali kapolo ku Iguputo anakhala mtumiki woyang’anira nyumba ya mbuye wake. Baibulo limanena kuti mbuye wakeyo “anasiya zinthu zake zonse m’manja mwa Yosefe.” (Gen. 39:2-6) Nayenso Yosefe atakhala wolamulira wamphamvu m’dziko la Iguputo, anali ndi mtumiki woyang’anira nyumba yake.​—Gen. 44:4.

Munthawi ya Yesu, mabwana ankakhala m’mizinda yakutali ndi minda yawo. Choncho mabwanawo ankasankha mtumiki amene ankayang’anira zochitika za tsiku ndi tsiku zakumindayo.

Kodi ndi ndani ankayenera kukhala mtumiki woyang’anira nyumba? Wolemba mbiri wina wachiroma dzina lake Columella, yemwe anakhalapo m’nthawi ya atumwi, ananena kuti munthu amene ankayenera kukhala mtumiki woyang’anira nyumba ankayenera kukhala munthu “wodziwa bwino ntchito.” Ankayeneranso kukhala munthu amene “angayang’anire ena popanda kuwalekerera kapena kuwachitira nkhanza.” Ananenanso kuti: “Chofunika kwambiri n’chakuti munthuyo sankayenera kumaganiza kuti amadziwa zonse, koma ankafunika kukhala wakhama pophunzira zinthu zatsopano.”

Baibulo limagwiritsa ntchito mawu amene anamasuliridwa kuti mtumiki woyang’anira nyumba pofotokoza za zinthu zina zimene zimachitika mumpingo. Mwachitsanzo, mtumwi Petulo analimbikitsa Akhristu kuti azigwiritsa ntchito mphatso zimene Mulungu anawapatsa “potumikirana monga oyang’anira [kapena kuti atumiki oyang’anira nyumba] abwino amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.”​—1 Pet. 4:10.

Yesu nayenso anagwiritsa ntchito mawu akuti mtumiki woyang’anira nyumba mufanizo la pa Luka 16:1-8. Komanso mu ulosi wonena za kukhalapo kwake monga Mfumu, Yesu anauza otsatira ake kuti adzasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kapena kuti “mtumiki woyang’anira nyumba.” Udindo waukulu wa mtumiki woyang’anira nyumba ameneyu ndi wopereka chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera kwa otsatira a Khristu munthawi ya mapeto. (Mat. 24:45-47; Luka 12:42) Timayamikira kukhala m’gulu la anthu amene amalandira chakudya chauzimu cholimbitsa chikhulupiriro chimene mtumiki woyang’anira nyumbayu amakonza komanso kupereka padziko lonse.