Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 42

Kodi Yehova Adzakuthandizani Kuchita Chiyani?

Kodi Yehova Adzakuthandizani Kuchita Chiyani?

“Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.”​AFIL. 2:13.

NYIMBO NA. 104 Mzimu Woyera Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova angachite zinthu ziti pofuna kukwaniritsa cholinga chake?

YEHOVA akhoza kukhala chilichonse chimene akufuna kuti akwaniritse cholinga chake. Mwachitsanzo, iye amatha kukhala Mphunzitsi, Wotonthoza ndiponso Mlaliki. (Yes. 48:17; 2 Akor. 7:6; Agal. 3:8) Ngakhale zili choncho, nthawi zambiri amagwiritsa ntchito anthu kuti akwaniritse cholinga chake. (Mat. 24:14; 28:19, 20; 2 Akor. 1:3, 4) Yehova angatipatsenso nzeru ndi mphamvu kuti tikwanitse kuchita zimene iye akufuna. Zonsezi zikugwirizana ndi zimene akatswiri ambiri amanena pofotokoza tanthauzo la dzina lake lakuti Yehova.

2. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatichititse kukayikira kuti Yehova angatigwiritse ntchito? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Tonsefe timafuna kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova koma ena amakayikira ngati iye angawagwiritse ntchito. Amatero chifukwa chakuti amaona kuti ndi achikulire, alibe luso kapena zinthu sizili bwino pa moyo wawo. Ndiye pali anthu ena amene amaona kuti zimene akuchita n’zokwanira ndipo palibe chifukwa choti aziyesetsa kuchita zambiri. Munkhaniyi tikambirana mmene Yehova angatithandizire kuti tichite zinthu pokwaniritsa cholinga chake. Kenako tikambirana nkhani za m’Baibulo za amuna ndi akazi amene Yehova anawapatsa mtima wofuna kuchita zambiri komanso mphamvu zochitira zinthuzo. Pomaliza tiona zimene tingachite kuti Yehova azitigwiritsa ntchito.

KODI YEHOVA AMATITHANDIZA BWANJI?

3. Malinga ndi Afilipi 2:13, kodi Yehova angatipatse bwanji mtima wofuna kuchita zinthu zinazake?

3 Werengani Afilipi 2:13. * Yehova angatipatse mtima wofuna kuchita zinthu zinazake. Kodi angachite bwanji zimenezi? Mwina tikhoza kumva kuti pali zinthu zina zimene zikufunika mumpingo. Kapena akulu angawerenge kalata yochokera ku ofesi ya nthambi yofotokoza zimene zikufunika kwina. Ndiye mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndingathandize bwanji?’ Kapena mwina tingapatsidwe utumiki wovuta n’kumakayikira ngati tingauchite bwino. Mwinanso pambuyo powerenga mavesi ena a m’Baibulo tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji mavesiwa pothandiza ena?’ Yehova sadzatikakamiza kuchita chilichonse. Koma akaona kuti tikuganizira zoti tichite zinazake, iye angatipatse mtima wofuna kuchita zomwe tikuganizazo.

4. Kodi Yehova angatipatse bwanji mphamvu zochitira zinthu zimene amafuna?

4 Yehova angatipatsenso mphamvu zochitira zinthu zimene amafuna. (Yes. 40:29) Iye angagwiritse ntchito mzimu woyera kuti awonjezere luso limene tili nalo kale. (Eks. 35:30-35) Yehova angagwiritsenso ntchito gulu lake kutiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito inayake. Ngati simukudziwa mmene mungagwirire ntchito imene mwapatsidwa, muzipempha ena kuti akuthandizeni. Komanso muzipempha Atate wathu wakumwamba kuti akupatseni “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akor. 4:7; Luka 11:13) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za amuna komanso akazi amene Yehova anawathandiza kukhala ndi mtima wofuna kuchita zinthu komanso mphamvu zochitira zinthuzo. Tikamakambirana zitsanzo za anthuwa, yesetsani kuganizira njira zimene Yehova angakugwiritsireni ntchito.

ZIMENE YEHOVA ANATHANDIZA AMUNA ENA KUCHITA

5. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa njira imene Yehova anagwiritsira ntchito Mose komanso nthawi imene anachitira zimenezi?

5 Yehova anathandiza Mose kuti apulumutse Aisiraeli. Koma kodi anamugwiritsa ntchito pa nthawi iti? Kodi ndi pa nthawi imene Mose ankaona kuti angagwire bwino ntchitoyi pambuyo ‘pophunzira nzeru zonse za Aiguputo’? (Mac. 7:22-25) Ayi, koma Yehova anamugwiritsa ntchito atamuphunzitsa kuti akhale wodzichepetsa komanso wofatsa. (Mac. 7:30, 34-36) Yehova anathandiza Mose kuti alimbe mtima n’kukalankhula ndi wolamulira wamphamvu kwambiri wa ku Iguputo. (Eks. 9:13-19) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa njira komanso nthawi imene Yehova anagwiritsira ntchito Mose? Yehova amagwiritsa ntchito anthu amene amatsanzira makhalidwe ake komanso kumudalira.​—Afil. 4:13.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachita pogwiritsa ntchito Barizilai kuti athandize Mfumu Davide?

6 Patapita zaka zambiri, Yehova anagwiritsa ntchito Barizilai kuti athandize Mfumu Davide. Davide ndi anthu ake ankathawa Abisalomu ndipo ‘anali ndi njala, anatopa komanso anali ndi ludzu.’ Barizilai, yemwe anali wachikulire, limodzi ndi anthu ena anaika moyo wawo pa ngozi kuti athandize Davide ndi anthu ake. Iye sankaona kuti Yehova sangamugwiritse ntchito chifukwa chokhala wachikulire. Koma Barizilai anagwiritsa ntchito mowolowa manja zinthu zake kuti athandize atumiki a Mulungu. (2 Sam. 17:27-29) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngakhale kuti ndife achikulire, Yehova angatigwiritse ntchito pothandiza Akhristu anzathu amene akusowa zofunika pa moyo, kaya m’dera lathu kapena kumayiko ena. (Miy. 3:27, 28; 19:17) Mwina sitingawathandize mwachindunji, koma tingapereke ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse zomwe zingagwiritsidwe ntchito pothandiza anthu amene akuvutika.​—2 Akor. 8:14, 15; 9:11.

7. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji Simiyoni, nanga tikuphunzirapo chiyani?

7 Yehova analonjeza Simiyoni, yemwe anali bambo wachikulire ku Yerusalemu, kuti sadzamwalira asanaone Mesiya. Simiyoni ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi lonjezoli chifukwa anali atadikira kwa zaka zambiri kuti Mesiya afike. Iye anadalitsidwa chifukwa chopirira komanso kukhala ndi chikhulupiriro. Tsiku lina, Simiyoni analowa m’kachisi “motsogoleredwa ndi mzimu.” Atalowa anaona Yesu ndipo Yehova anagwiritsa ntchito Simiyoniyo kuti anene ulosi wokhudza mwanayo, yemwe anadzakhala Khristu. (Luka 2:25-35) Simiyoni ayenera kuti anamwalira Yesu asanayambe utumiki wake padzikoli, koma iye anayamikira mwayi wakewu ndipo adzadalitsidwa kwambiri m’tsogolo. M’dziko latsopano, munthu wokhulupirikayu adzaona madalitso amene anthu onse padzikoli adzapeza chifukwa cha ulamuliro wa Yesu. (Gen. 22:18) Nafenso tiyenera kuyamikira mwayi uliwonse umene timakhala nawo potumikira Yehova.

8. Kodi Yehova angatigwiritse ntchito bwanji ngati mmene anachitira ndi Baranaba?

8 M’nthawi ya atumwi, munthu wina wamtima wopatsa dzina lake Yosefe analola Yehova kuti amugwiritse ntchito. (Mac. 4:36, 37) Zikuoneka kuti atumwi anamupatsa dzina loti Baranaba, kutanthauza “Mwana wa Chitonthozo,” chifukwa ankalimbikitsa kwambiri anthu ena. Mwachitsanzo, Saulo atakhala Mkhristu abale ambiri ankamuopa chifukwa choti anali ndi mbiri yoti ankazunza Akhristu. Koma Baranaba anamuchitira chifundo ndipo anamuthandiza. Saulo ayenera kuti ankayamikira kwambiri zimenezi. (Mac. 9:21, 26-28) Pa nthawi ina, akulu a ku Yerusalemu ankafuna kulimbikitsa abale amene ankakhala kutali ku Antiokeya wa ku Siriya. Ndiye kodi anasankha kutumiza ndani? Iwo anasankha bwino kwambiri chifukwa anatumiza Baranaba. Baibulo limanena kuti Baranaba “anayamba kulimbikitsa onse kuti apitirize kukhala okhulupirika kwa Ambuye motsimikiza mtima.” (Mac. 11:22-24) Yehova angatithandizenso ifeyo kuti tikhale ngati Baranaba potonthoza Akhristu anzathu. Mwachitsanzo, angatigwiritse ntchito kutonthoza anthu amene aferedwa. Apo ayi, angatilimbikitse kuti tikaone kapena kuimbira foni munthu amene akudwala kapena akuvutika maganizo. Kodi inunso mudzalola kuti Yehova azikugwiritsani ntchito ngati mmene anachitira ndi Baranaba?​—1 Ates. 5:14.

9. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachita kuti athandize Vasily kukhala m’busa wabwino?

9 Yehova anathandiza m’bale wina dzina lake Vasily kuti akhale m’busa wabwino kwambiri. Vasily anaikidwa kukhala mkulu ali ndi zaka 26 ndipo ankaopa kuti sangakwanitse kuthandiza bwinobwino mpingo, makamaka anthu amene ankakumana ndi mavuto. Koma anaphunzira zambiri kwa abale amene anali atakhala akulu kwa nthawi yaitali komanso pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Vasily anayesetsa kuti akhale m’busa wabwino. Mwachitsanzo, analemba zolinga zing’onozing’ono ndipo akakwaniritsa cholinga chilichonse mantha ake ankachepa. Iye anati: “Zimene ndinkaopa pa nthawiyo, panopa zimandisangalatsa kwambiri. Yehova akandithandiza kupeza lemba loyenera loti ndilimbikitsire m’bale kapena mlongo ndimasangalala kwambiri.” Ngati ndinu m’bale ndipo mukulolanso kuti Yehova azikugwiritsani ntchito, iye angakupatseni luso loti muzichita zinthu zambiri mumpingo.

ZIMENE YEHOVA ANATHANDIZA AKAZI ENA KUCHITA

10. Kodi Abigayeli anachita zotani, nanga tikuphunzirapo chiyani?

10 Davide ndi anzake ankafuna thandizo pa nthawi imene ankathawa Mfumu Sauli. Amuna amene anali ndi Davide anakapempha chakudya kwa munthu wina wolemera dzina lake Nabala. Iwo sanaope kukapempha chifukwa choti anali atathandiza kuteteza ziweto zake m’chipululu. Koma Nabala anali wodzikonda ndipo anakana kuwapatsa chilichonse. Zitatero, Davide anakwiya kwambiri ndipo ankafuna kupha Nabala komanso mwamuna aliyense wa m’nyumba yake. (1 Sam. 25:3-13, 22) Koma mkazi wa Nabala, dzina lake Abigayeli, yemwe anali wokongola kwambiri analinso wanzeru. Iye analimba mtima n’kukagwada pamaso pa Davide ndipo anamuchonderera kuti asabwezere zoipazo n’kupalamula mlandu wa magazi. Iye anauza Davide mwaulemu kuti angosiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Kudzichepetsa komanso nzeru za Abigayeli zinathandiza kwambiri Davide. Iye anafika poona kuti Yehova ndi amene anamutuma. (1 Sam. 25:23-28, 32-34) Abigayeli anali ndi makhalidwe amene anathandiza kuti agwiritsidwe ntchito ndi Yehova. Masiku anonso, alongo amene amachita zinthu mwanzeru akhoza kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova kuti alimbikitse anthu a m’banja lawo komanso amumpingo.​—Miy. 24:3; Tito 2:3-5.

11. Kodi ana aakazi a Salumu anachita zotani, nanga ndi ndani akuchitanso chimodzimodzi masiku ano?

11 Patapita zaka zambiri, ana aakazi a Salumu anathandiza nawo pa ntchito yokonza mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:20; 3:12) Ngakhale kuti bambo awo anali kalonga, iwo anadzipereka kugwira nawo ntchito yovuta komanso yoopsa imeneyi. (Neh. 4:15-18) Zimene anachitazi zinali zosiyana ndi zimene anthu otchuka pakati pa Atekowa anachita. Anthu otchukawo sanali odzichepetsa ndipo anakana kugwira nawo ntchitoyi. (Neh. 3:5) Ana aakazi a Salumu ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona kuti ntchitoyo yatha patangopita masiku 52 okha. (Neh. 6:15) Masiku anonso, alongo ena amadzipereka kuti atumikire Yehova pa ntchito zomangamanga kapena kukonza malo amene anaperekedwa kwa Yehova. Luso lawo, khama lawo komanso kukhulupirika kwawo zimathandiza kwambiri kuti ntchitozi ziziyenda bwino.

12. Kodi Yehova angatigwiritse ntchito bwanji mofanana ndi Tabita?

12 Yehova analimbikitsanso Tabita kuti azigwira “ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso zachifundo” makamaka pothandiza akazi amasiye. (Mac. 9:36) Popeza anali wokoma mtima komanso wopatsa, anthu ambiri analira atamwalira. Koma anasangalala kwambiri Petulo atamuukitsa. (Mac. 9:39-41) Kodi tikuphunzira chiyani kwa Tabita? Kaya ndife aang’ono kapena achikulire, amuna kapena akazi, tonse tikhoza kuchita zinthu zina pothandiza abale ndi alongo athu.​—Aheb. 13:16.

13. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito bwanji mlongo wina wamanyazi dzina lake Ruth, nanga iye ananena kuti chiyani?

13 Mlongo wina dzina lake Ruth ankafuna kukhala mmishonale koma anali wamanyazi. Iye ali wamng’ono ankayenda mofulumira kwambiri n’kumakapereka timapepala kunyumba ndi nyumba. Iye anati, “Zimenezi zinkandisangalatsa kwambiri.” Koma zinkamuvuta kwambiri kulankhula ndi anthu n’kumawafotokozera za Ufumu wa Mulungu. Ngakhale kuti mlongoyu anali wamanyazi, iye anayamba upainiya ali ndi zaka 18. Mu 1946, anapita ku Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo ndipo anakatumikira ku Hawaii ndi ku Japan. Yehova anamugwiritsa ntchito kwambiri kuti alalikire uthenga wabwino m’madera amenewa. Ruth atatumikira Yehova kwa zaka pafupifupi 80 ananena kuti: “Yehova wakhala akundipatsa mphamvu kwambiri. Wandithandiza kuti ndithane ndi vuto la manyazi. Sindikukayikira kuti munthu aliyense amene amadalira Yehova akhoza kugwiritsidwa ntchito.”

LOLANI KUTI YEHOVA AZIKUGWIRITSANI NTCHITO

14. Malinga ndi Akolose 1:29, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova azitigwiritsa ntchito?

14 Kuyambira kale, Yehova wakhala akuthandiza atumiki ake kuti azichita zinthu zosiyanasiyana. Nanga kodi inuyo adzakuthandizani kuchita chiyani? Yankho lake lingadalire zimene inuyo mungadzipereke kuchita. (Werengani Akolose 1:29.) Mukadzipereka, Yehova angakuthandizeni kukhala munthu wolalikira mwakhama, wophunzitsa mwaluso, wotonthoza ena, wogwira ntchito mwaluso, wothandiza ena kapenanso wochita chilichonse chimene iye akufuna kuti akwaniritse cholinga chake.

15. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 4:12, 15, kodi abale achinyamata ayenera kupempha Yehova kuti awathandize kuchita chiyani?

15 Ngati ndinu m’bale wachinyamata, kodi mungachite chiyani? M’gulu la Yehova mukufunika abale ambiri akhama kuti akhale atumiki othandiza. M’mipingo yambiri, akulu amakhala ambiri poyerekezera ndi atumiki othandiza. Ndiye kodi mungayesetse kukhala ndi mtima wofuna kuchita zambiri mumpingo? Nthawi zina, abale ena amanena kuti, “Ine ndimangofuna kukhala wofalitsa basi.” Ngati ndi mmene mumamvera, mungachite bwino kupempha Yehova kuti akupatseni mtima wofuna kukhala mtumiki wothandiza komanso mphamvu zochitira zonse zimene mungathe pomutumikira. (Mlal. 12:1) Dziwani kuti timafuna thandizo lanu.​—Werengani 1 Timoteyo 4:12, 15.

16. Kodi tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse chiyani? Perekani chifukwa.

16 Yehova angakuthandizeni kuchita chilichonse chimene chingafunike kuti akwaniritse cholinga chake. Choncho muyenera kumupempha kuti akupatseni mtima wofuna kugwira ntchito yake kenako n’kumupemphanso kuti akupatseni mphamvu zogwirira ntchitoyo. Kaya ndinu achinyamata kapena achikulire, muzigwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso zinthu zanu polemekeza Yehova panopa. (Mlal. 9:10) Musamalole mantha kapena kudzikayikira kukulepheretsani kuti mukhale ndi mwayi wochita zambiri potumikira Yehova. Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kuchita chilichonse pothandiza kuti Atate wathu wachikondi azilandira ulemu womuyenera.

NYIMBO NA. 127 Mtundu wa Munthu Amene Ndiyenera Kukhala

^ ndime 5 Kodi mumaona kuti simukuchita zambiri potumikira Yehova? Kodi mumakayikira zoti Mulungu angakugwiritseni ntchito? Kapena kodi mumaona kuti simukufunika kulola kuti Yehova azikugwiritsani ntchito mmene akufunira? Munkhaniyi tiona njira zimene Yehova angatithandizire kuti tikhale ndi mtima wofuna kuchita zinthu zogwirizana ndi cholinga chake komanso mphamvu zochitira zinthuzo.

^ ndime 3 Ngakhale kuti Paulo analembera kalatayi Akhristu a mu nthawi ya atumwi, mfundo zake zingathandize atumiki onse a Yehova.