Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 43

Musafooke

Musafooke

“Tisaleke kuchita zabwino.”​—AGAL. 6:9.

NYIMBO NA. 68 Tizifesa Mbewu za Ufumu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi mwayi waukulu uti umene tili nawo?

 TIMASANGALALA komanso timaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala a Mboni za Yehova. Timadziwika ndi dzina la Mulungu ndipo timachita zinthu mogwirizana ndi dzinali tikamagwira nawo ntchito yolalikira komanso kuthandiza anthu kudziwa za iye. Timasangalala tikathandiza munthu ‘amene ali ndi maganizo abwino omwe angamuthandize kukapeza moyo wosatha’ kuti akhale wokhulupirira. (Mac. 13:48) Timamva ngati mmene Yesu anamvera pamene “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera,” ophunzira ake atamufotokozera zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo polalikira.​—Luka 10:1, 17, 21.

2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri?

2 Timaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: “Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.” Anawonjezeranso kuti: “Ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.” (1 Tim. 4:16) Choncho ntchito yolalikira imapulumutsa miyoyo ya anthu. Timasamala ndi zimene timachita chifukwa ndife nzika za Ufumu wa Mulungu. Nthawi zonse timafuna kuchita zinthu m’njira imene imachititsa kuti Yehova alemekezedwe komanso mogwirizana ndi uthenga wabwino umene timalalikira. (Afil. 1:27) Timasonyeza kuti ‘timasamala ndi zimene timaphunzitsa’ tikamakonzekera bwino komanso tikamapempha Yehova kuti atithandize pamene tikukalalikira.

3. Kodi ndi anthu onse amene amamvetsera uthenga wa Ufumu? Perekani chitsanzo.

3 Ngakhale titachita zonse zomwe tingathe, mwina anthu ambiri m’gawo lathu sangamvetsere uthenga wa Ufumu. Taganizirani zimene zinachitikira M’bale Georg Lindal, yemwe ankalalikira yekhayekha ku Iceland kuchokera mu 1929 mpaka mu 1947. Iye anagawira mabuku ambiri, koma palibe ngakhale m’modzi amene anakhala wa Mboni. Iye anati: “Ena ankatsutsa choonadi, komanso ambiri sankasonyeza chidwi n’komwe.” Ngakhale kuti ku Iceland kunafika amishonale omwe analowa Sukulu ya Giliyadi kuti adzathandize pa ntchito yolalikira, panadutsa zaka 9 popanda aliyense amene anadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa.

4. Kodi tingamamve bwanji anthu akamakana kumvetsera uthenga wabwino?

4 Timakhumudwa anthu akamapanda kumvetsera uthenga wabwino. Tingamamve ngati mmene Paulo ankamvera, yemwe anali ndi ‘chisoni chachikulu ndiponso mtima unkamupweteka nthawi zonse’ chifukwa Ayuda ankakana kukhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya. (Aroma 9:1-3) Bwanji ngati mumayesetsa kuthandiza munthu amene mukuphunzira naye Baibulo komanso kumupempherera koma iye sakupita patsogolo ndipo mukufunika kusiya kuphunzira naye? Kapenanso bwanji ngati simunaphunzirepo ndi munthu wina mpaka kufika pobatizidwa? Kodi muyenera kumadziimba mlandu, mwina n’kumaganiza kuti Yehova sakudalitsa utumiki wanu? Munkhaniyi, tikambirana mafunso awiri awa: (1) Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti zinthu zikutiyendera bwino pa utumiki wathu? (2) Kodi tiyenera kuyembekezera chiyani tikamagwira ntchito yolalikira?

KODI N’CHIYANI CHIMASONYEZA KUTI ZINTHU ZIKUTIYENDERA BWINO PA UTUMIKI WATHU?

5. N’chifukwa chiyani nthawi zina zomwe timachita potumikira Yehova sizikhala ndi zotsatira zomwe timayembekezera?

5 Ponena za munthu amene amachita chifuniro cha Mulungu, Baibulo limati: “Zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.” (Sal. 1:3) Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti chilichonse chomwe timachita potumikira Yehova chingachitike mmene tikufunira. Moyo wathu ndi “wodzaza ndi masautso” chifukwa choti tonsefe si angwiro. (Yobu 14:1) Kuwonjezera pamenepa, nthawi zina anthu amene amatitsutsa akhoza kukwanitsa kutilepheretsa kuti tizigwira ntchito yolalikira mwaufulu. (1 Akor. 16:9; 1 Ates. 2:18) Ndiye kodi n’chiyani chimachititsa Yehova kuona kuti ntchito yathu yolalikira ikuyenda bwino? Tiyeni tione mfundo zina za m’Baibulo zomwe zingatithandize kupeza yankho la funso limeneli.

Yehova amayamikira zonse zomwe timachita kaya tikulalikira khomo ndi khomo, kulemba kalata kapenanso pafoni (Onani ndime 6)

6. Kodi Yehova amaona kuti utumiki wathu wayenda bwino potengera chiyani?

6 Yehova amaona khama komanso kupirira kwathu. Ngakhale ena asamvetsere uthenga wathu, Yehova amasangalala tikamagwira ntchito yolalikira mwakhama komanso chifukwa chomukonda. Paulo analemba kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikira oyera ndipo mukupitiriza kuwatumikira.” (Aheb. 6:10) Iye amakumbukira khama lathu komanso chikondi chathu ngakhale sitinapeze munthu yemwe taphunzira naye Baibulo mpaka kubatizidwa. Choncho zimene Paulo anauza Akhristu a ku Korinto zingagwirenso ntchito kwa inu. Iye anati: “Zonse zimene mukuchita mu ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe,” kaya ntchitoyo yakhala ndi zotsatira zimene mumayembekezera kapena ayi.​—1 Akor. 15:58.

7. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene mtumwi Paulo anafotokoza zokhudza utumiki wake?

7 Mtumwi Paulo anali mmishonale waluso ndipo anakhazikitsa mipingo yambirimbiri m’mizinda yosiyanasiyana. Koma anthu atayamba kumunena kuti sanali mphunzitsi wabwino, iye sanatchule za kuchuluka kwa anthu omwe anawathandiza kuti akhale Akhristu. M’malomwake, potsutsa anthu omwe ankadzikuzawo, iye analemba kuti anagwira ‘ntchito zovuta mowirikiza koposa.’ (2 Akor. 11:23) Mofanana ndi Paulo, muzikumbukira kuti Yehova amaona kuti chofunika kwambiri ndi khama komanso kupirira kwanu.

8. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani yokhudza utumiki wathu?

8 Yehova amasangalala ndi utumiki wathu. Yesu anatumiza ophunzira 70 kukalalikira uthenga wa Ufumu ndipo atamaliza kugwira ntchitoyo “anabwerera ali osangalala.” N’chifukwa chiyani anasangalala? Iwo anati: “Ngakhale ziwanda zinatigonjera pamene tinagwiritsa ntchito dzina lanu.” Komabe Yesu anawathandiza kukhala ndi maganizo oyenera powauza kuti: “Musakondwere ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.” (Luka 10:17-20) Yesu ankadziwa kuti si nthawi zonse pamene ophunzirawo azidzakumana ndi zosangalatsa mu utumiki. Ndipotu sitikudziwa kuti ndi anthu angati amene anamvetsera ophunzirawo omwe anakhala okhulupirira. Sikuti ophunzirawo ankangofunika kukhala osangalala chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita, koma makamaka chifukwa choti Yehova ankasangalala ndi khama lawo.

9. Mogwirizana ndi Agalatiya 6:7-9, kodi padzakhala zotsatira zotani ngati tikupirira pa ntchito yathu yolalikira?

9 Tikamapirira pa ntchito yathu yolalikira, tidzapeza moyo wosatha. Tikamachita zonse zomwe tingathe pofesa komanso kusamalira mbewu za choonadi cha Ufumu, timakhalanso kuti ‘tikutsatira mzimu wa Mulungu’ polola kuti mzimuwo uzigwira ntchito mwaufulu pa moyo wathu. Ngati sitingafooke kapena “kutopa,” Yehova akulonjeza kuti adzatipatsa moyo wosatha ngakhale ngati sitinathandizepo munthu wina mpaka kufika pobatizidwa.​—Werengani Agalatiya 6:7-9.

KODI TIYENERA KUYEMBEKEZERA CHIYANI TIKAMAGWIRA NTCHITO YOLALIKIRA?

10. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu amvetsere kapena asamvetsere uthenga wathu?

10 Kuti anthu amvetsere, zimadalira mtima wawo. Yesu anafotokoza mfundo ya choonadi imeneyi mufanizo lake la wofesa mbewu yemwe anazifesa pa nthaka zosiyanasiyana, koma imodzi yokha ndi yomwe inabala zipatso. (Luka 8:5-8) Iye ananena kuti nthaka zosiyanasiyana zikuimira anthu amene mitima yawo imakhudzidwa mosiyana akamva “mawu a Mulungu.” (Luka 8:11-15) Mofanana ndi wofesa mbewu, sitingachititse kuti mbewu za choonadi zikule m’mitima ya anthu omwe tawalalikira. Udindo wathu ndi kupitiriza kufesa mbewu zabwino za uthenga wa Ufumu. Malinga ndi zimene Paulo ananena, “aliyense payekha adzalandira mphoto yake mogwirizana ndi ntchito yake,” osati zotsatira za ntchitoyo.​—1 Akor. 3:8.

Ngakhale kuti Nowa analalikira mokhulupirika kwa zaka zambiri, palibe amene analowa m’chingalawa kupatulapo iye ndi anthu a m’banja lake. Ngakhale zinali choncho, Nowa ankamverabe Mulungu (Onani ndime 11)

11. N’chifukwa chiyani Yehova anasangalala ndi Nowa n’kumamuona kuti anali “mlaliki wa chilungamo”? (Onani chithunzi chapachikuto.)

11 Atumiki akale a Yehova ankakumananso ndi anthu omwe sankamvetsera uthenga wawo. Mwachitsanzo, Nowa anali “mlaliki wa chilungamo,” mwina kwa zaka pafupifupi 40 kapena 50. (2 Pet. 2:5) N’zosakayikitsa kuti iye ankayembekezera kuti anthu ambiri amvetsera uthenga wake, koma Yehova sanamuuze kuti zimenezi ndi zomwe zidzachitike. M’malomwake, pouza Nowa kuti amange chingalawa, Mulungu anati: “Iweyo udzalowe m’chingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.” (Gen. 6:18) Komanso poganizira kukula kwa chingalawa chomwe Mulungu anamuuza kuti amange, Nowa ayenera kuti anazindikira kuti ndi anthu ochepa okha omwe adzamvetsere uthenga wake. (Gen. 6:15) Ndipotu n’zimene zinachitikadi. Palibe ngakhale munthu mmodzi amene anamvetsera uthenga wa Nowa. (Gen. 7:7) Ndiye kodi Yehova anaona kuti Nowa sanagwire bwino ntchito yolalikira? Ayi. Yehova anasangalala ndi Nowa chifukwa anachita mokhulupirika zimene anamuuza.​—Gen. 6:22.

12. N’chiyani chinathandiza Yeremiya kuti azisangalalabe ngakhale kuti anthu sankamumvetsera komanso ankamutsutsa?

12 Mneneri Yeremiya nayenso analalikira kwa zaka zoposa 40 ngakhale kuti anthu sankamumvetsera komanso ankamutsutsa. Iye anafooka chifukwa ‘chonyozedwa ndi kutonzedwa’ ndi anthu omwe ankamutsutsa moti anaganiza zongosiya utumiki wake. (Yer. 20:8, 9) Komabe Yeremiya sanasiye utumikiwo. Ndiye n’chiyani chinamuthandiza kuti apitirizebe n’kumakhala wosangalala? Iye ankaganizira mfundo ziwiri zofunika kwambiri. Choyamba, uthenga wa Mulungu umene Yeremiya ankauza anthu ukanawapatsa “chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.” (Yer. 29:11) Chachiwiri, Yehova anasankha Yeremiya kuti azimulankhulira pouza anthu uthenga wake. (Yer. 15:16) Ifenso timauza anthu uthenga wa chiyembekezo m’dziko lamavutoli ndiponso timadziwika ndi dzina la Yehova monga Mboni zake. Tikamaganizira mfundo ziwiri zofunika kwambirizi, tikhoza kumasangalala kaya anthu amvetsera uthenga wathu kapena ayi.

13. Kodi tikuphunzira chiyani mufanizo la Yesu lopezeka pa Maliko 4:26-29?

13 Pamatenga nthawi kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro. Yesu anaphunzitsa mfundo ya choonadiyi mufanizo lake la wofesa mbewu amene anagona. (Werengani Maliko 4:26-29.) Iye atafesa mbewuzo, zinkakula pang’onopang’ono ndipo palibe chomwe akanachita kuti zikule mofulumira. Mwina ifenso tingafunike kudikira kwa kanthawi ndithu kuti tiyambe kuona ophunzira Baibulo akugwiritsa ntchito zimene akuphunzira. Ndipo mofanana wofesayo, sitingachititse wophunzira Baibulo wathu kukhala ndi chikhulupiriro mofulumira mmene ifeyo tikufunira. Choncho musamafooke kapena kutaya mtima ngati akuoneka kuti sakupita patsogolo mwamsanga ngati mmene inuyo mumayembekezera. Mofanana ndi ulimi, ntchito yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu imafunika kuleza mtima.​—Yak. 5:7, 8.

14. Kodi ndi chitsanzo chiti chomwe chikusonyeza kuti pangatenge nthawi kuti zotsatira za ntchito yathu ziyambe kuonekera?

14 M’madera ena, pangatenge zaka zambiri kuti zotsatirapo za ntchito yathu yolalikira zionekere. Taganizirani chitsanzo cha alongo awiri apachibale, Gladys ndi Ruby Allen, omwe mu 1959 anatumizidwa monga apainiya okhazikika m’chigawo cha Quebec ku Canada. * Chifukwa choopa anthu oyandikana nawo komanso Tchalitchi cha Katolika, anthu sankamvetsera uthenga wa Ufumu womwe alongowa ankalalikira. Gladys anati: “Kwa maola 8 patsiku, tinkayenda khomo ndi khomo kwa zaka ziwiri koma panalibe amene ankafuna kulankhula nafe. Anthu akatsegula chitseko n’kuona kuti ndi ife, ankangotseka chitsekocho. Koma sitinafooke.” Pang’ono ndi pang’ono anthu anayamba kusintha ndipo ankamvetsera. Panopa m’tawuni imeneyi muli mipingo itatu.​—Yes. 60:22.

15. Kodi lemba la 1 Akorinto 3:6, 7, limatithandiza kudziwa chiyani zokhudza ntchito yophunzitsa anthu?

15 Tonse timathandizapo. Pa ntchito yophunzitsa munthu, timadziwa kuti aliyense mumpingo amathandizapo kuti wophunzira Baibulo afike pobatizidwa. (Werengani 1 Akorinto 3:6, 7.) Mwachitsanzo, wofalitsa angagawire kapepala kapena magazini kwa munthu wachidwi. Kenako wofalitsayo akuona kuti nthawi yake siikumulola kuti abwererekonso kwa munthuyo, ndiye akupempha wofalitsa wina kuti akachite ulendo wobwereza. Wofalitsa winayo wakwanitsa kuyambitsa phunziro la Baibulo. Kenako iye akumatenga abale ndi alongo osiyanasiyana kuphunzirolo omwe akulimbikitsa wophunzirayo m’njira zosiyanasiyana. M’bale kapena mlongo aliyense amene wakumana ndi wophunzirayo amathandiza kuthirira mbewu ya choonadi. Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, onse omwe anachita khama pothandiza wophunzirayo amasangalala iye akabatizidwa.​—Yoh. 4:35-38.

16. N’chifukwa chiyani mungamasangalale ndi utumiki wanu ngakhale kuti thanzi lanu ndi lofooka kapena mulibe mphamvu zambiri?

16 Bwanji ngati simungathe kuchita zambiri pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino chifukwa cha kufooka kwa thanzi kapena kuchepa kwa mphamvu zanu? Mukhoza kumasangalalabe ndi zimene mukukwanitsa kuchita pa ntchito yokolola. Taganizirani zimene zinachitika pamene Mfumu Davide ndi amuna omwe anali nawo anakapulumutsa mabanja awo ndi katundu wawo kwa Aamaleki. Amuna 200 anali atatopa kwambiri moti sakanatha kumenya nkhondo, choncho anatsala n’kumalondera katundu. Atapambana pa nkhondoyo, Davide analamula kuti onse agawane mofanana zinthu zomwe anafunkha kwa Aamaleki. (1 Sam. 30:21-25) Zimenezi ndi zofanana ndi zimene zimachitika pa ntchito yathu yophunzitsa anthu. Onse omwe achita zomwe angathe pa ntchitoyi, amasangalala mofanana munthu wina akathandizidwa n’kuyamba kuyenda panjira yopita kumoyo.

17. Kodi timathokoza Yehova chifukwa chiyani?

17 Timathokoza Yehova chifukwa cha mmene amaonera utumiki wathu. Amadziwa kuti sitingachititse anthu kuti azimvetsera uthenga wathu kapena kuti ayambe kumulambira. Komabe iye amaona khama ndi zolinga zathu zabwino ndipo amadalitsa ntchito yathu. Amatiphunzitsanso zimene tingachite kuti tizisangalala ndi zomwe timachita pa ntchito yaikulu yokololayi. (Yoh. 14:12) Tingatsimikize kuti Yehova akusangalala ndi zomwe tikuchita ngati sitingafooke.

NYIMBO NA. 67 “Lalikira Mawu”

^ ndime 5 Timasangalala anthu akamafuna kumvetsera uthenga wabwino, koma timakhumudwa ngati sakutero. Koma bwanji ngati munthu amene mukuphunzira naye Baibulo sakupita patsogolo? Kapena bwanji ngati simunathandizepo winawake mpaka kufika pobatizidwa? Kodi muyenera kuganiza kuti mwalephera pa ntchito yophunzitsa anthu? Munkhaniyi, tiona zimene tingachite kuti tizichita zambiri mu utumiki n’kumasangalala kaya anthu akumvetsera kapena ayi.

^ ndime 14 Onani mbiri ya moyo wa Gladys Allen pamutu wakuti, “Sindingasinthe Kanthu!,” mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2002.