‘Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu’
“Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”—AHEB. 4:12.
NYIMBO: 114, 113
1. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti Mawu a Mulungu ndi amphamvu? (Onani chithunzi choyambirira.)
ANTHU a Mulungufe sitikayikira zoti mawu amene Mulungu amatiuza “ndi amoyo ndi amphamvu.” (Aheb. 4:12) Ambirife mphamvu ya Baibulo yatithandiza kusintha kwambiri moyo wathu. Abale ndi alongo ena m’mbuyomo anali akuba, ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo ena anali achiwerewere. Anthu ena ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino m’dzikoli koma mumtima mwawo ankaona kuti akusowa chinachake. (Mlal. 2:3-11) Mphamvu ya Baibulo yathandiza anthu ambiri amene anataya mtima kuti ayambe kuyenda panjira ya ku moyo. Mwina inuyo mwawerengapo za anthu amene anasintha kwambiri moyo wawo munkhani za mu Nsanja ya Olonda zakuti “Baibulo Limasintha Anthu.” Mwaonanso kuti Malemba amathandizabe Akhristu amene anabatizidwa kuti apitirize kusintha moyo wawo.
2. Kodi Mawu a Mulungu anathandiza bwanji Akhristu mu nthawi ya atumwi?
2 Kodi tiyenera kudabwa tikaona anthu akusintha kwambiri chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu? Ayi. Paja ngakhale mu nthawi ya atumwi, abale ndi alongo omwe anali ndi chiyembekezo chopita kumwamba, anali atasinthanso. (Werengani 1 Akorinto 6:9-11.) Mtumwi Paulo atatchula anthu osiyanasiyana amene sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu ananena kuti: “Ena mwa inu munali otero.” Iwo anasintha chifukwa chothandizidwa ndi Malemba komanso mzimu woyera wa Mulungu. Ena analinso ndi mavuto aakulu ngakhale pambuyo polowa mumpingo wachikhristu. Mwachitsanzo, Baibulo limatchula za Mkhristu wina amene anachotsedwa koma patapita nthawi anabwezeretsedwa. (1 Akor. 5:1-5; 2 Akor. 2:5-8) Timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira mavuto amene Akhristu anzathu anali nawo n’kuona mmene Mawu a Mulungu anawathandizira kuti asinthe.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Popeza tili ndi Mawu a Mulungu omwe ndi amphamvu, tiyenera kuwagwiritsa ntchito bwino kwambiri. (2 Tim. 2:15) Munkhaniyi tiona zimene tingachite kuti tiziwagwiritsa ntchito bwino (1) pa moyo wathu, (2) mu utumiki komanso (3) pophunzitsa pamisonkhano. Kukambirana mfundo zimenezi kungatithandize kuti tizisonyeza kuti timakonda komanso kuthokoza Atate wathu wakumwamba amene amatiphunzitsa kuti zinthu zizitiyendera bwino.—Yes. 48:17.
PA MOYO WATHU
4. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mawu a Mulungu azitithandiza? (b) Kodi mumatani kuti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse?
4 Kuti Mawu a Mulungu azitithandiza tiyenera kuwawerenga tsiku lililonse ngati n’zotheka. (Yos. 1:8) N’zoona kuti ambirife timatanganidwa kwambiri. Komabe sitiyenera kulola chilichonse, ngakhale chimene tikuona kuti n’chofunika, kuti chitilepheretse kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. (Werengani Aefeso 5:15, 16.) Atumiki ambiri a Yehova amayesetsa kupeza nthawi yoti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse. Ena amaliwerenga m’mawa pomwe ena amachita zimenezi asanakagone. Iwo amakhala ndi maganizo ofanana ndi a wolemba masalimo amene ananena kuti: “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.”—Sal. 119:97.
5, 6. (a) Kodi n’chifukwa chiyani kusinkhasinkha n’kofunika kwambiri? (b) Kodi tingatani kuti tizisinkhasinkha? (c) Kodi inuyo mwathandizidwa bwanji chifukwa chowerenga Mawu a Mulungu ndiponso kuwasinkhasinkha?
5 Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo tiyeneranso kusinkhasinkha zimene tawerengazo. (Sal. 1:1-3) Tikamachita zimenezi tidzatha kugwiritsa ntchito bwino nzeru za Mulungu pa moyo wathu. Kaya timagwiritsa ntchito Baibulo lenileni kapena timaliwerenga pachipangizo chamakono, tiyenera kukhala ndi cholinga choti mawuwo azitifika pamtima.
6 Kodi tingatani kuti tizisinkhasinkha? Anthu ambiri amakonda kuima kaye atawerenga malemba angapo n’kumadzifunsa kuti: 2 Akor. 10:4, 5.
‘Kodi malembawa akundiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova? Kodi ineyo ndikutsatira bwanji mfundo ya pa malembawa pa moyo wanga? Nanga ndiyenera kusintha zinthu ziti kuti ndizitsatira mfundoyi kwambiri?’ Tikamasinkhasinkha Mawu a Mulungu komanso kupemphera timakhala ndi mtima wofunitsitsa kutsatira kwambiri malangizo ake. Tikamachita zimenezi tidzatha kugwiritsa ntchito bwino Baibulo pa moyo wathu.—MU UTUMIKI
7. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu mu utumiki?
7 Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu mu utumiki? Choyamba, tizikonda kuwawerenga tikamalalikira kapena kuphunzitsa anthu. Pa nkhani imeneyi, m’bale wina ananena kuti: “Tiyerekeze kuti inuyo mukulalikira kunyumba ndi nyumba limodzi ndi Yehova. Kodi mungamalankhule nokha kapena mungamupatse mpata kuti alankhulenso?” Apatu ankatanthauza kuti tikamawerenga Mawu a Mulungu mu utumiki timakhala ngati tikupatsa Yehova mpata woti alankhule ndi munthuyo. Lemba losankhidwa bwino likhoza kuthandiza kwambiri munthu kuposa mawu alionse amene ifeyo tingalankhule. (1 Ates. 2:13) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayesetsa kuwerengera Baibulo anthu amene ndimawalalikira?’
8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kungowerengera munthu lemba si kokwanira?
8 Komabe, kungowerengera munthu lemba si kokwanira. Tikutero chifukwa chakuti anthu ambiri salimvetsa bwino Baibulo. Vuto limeneli linalipo nthawi ya atumwi ndipo liliponso masiku ano. (Aroma 10:2) Choncho tisamaganize kuti tikangowerengera munthu lemba ndiye kuti adzamvetsa tanthauzo lake. Tiyenera kusankha mawu ofunika kwambiri palembalo, mwina n’kuwawerenganso kenako n’kufotokoza tanthauzo lake. Tikatero tidzathandiza kuti uthenga wa m’Baibulo ufike m’maganizo komanso mumtima mwa anthu amene tikukambirana nawo.—Werengani Luka 24:32.
9. Kodi tingatchule bwanji malemba kuti tithandize munthu kulemekeza Baibulo?
9 Tiyeneranso kutchula malemba m’njira yothandiza munthu kuti azilemekeza Baibulo. Mwachitsanzo tinganene kuti, “Tiyeni tione zimene Mlengi wathu akunena pa nkhaniyi.” Tikamakambirana ndi munthu yemwe si Mkhristu tinganene kuti, “Taonani zimene Malemba Oyera akunena pa nkhaniyi.” Ngati munthu amene tikukambirana nayeyo sakonda za Mawu a Mulungu tinganene kuti, “Kodi mwambi uwu munaumvapo?” Mwachidule tingati tiyenera kusintha ulaliki wathu kuti ugwirizane ndi munthu aliyense amene tikukambirana naye.—1 Akor. 9:22, 23.
10. (a) Fotokozani zimene zinachitikira m’bale wina mu utumiki. (b) Fotokozani zimene zinakuchitikirani mu utumiki zomwe zikusonyeza kuti Mawu a Mulungu ndi amphamvu.
10 Akhristu ambiri amaona kuti kuwerenga Baibulo mu utumiki kumathandiza kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina amene anachita ulendo wobwereza kwa munthu wina wachikulire. Munthuyo anali atawerenga magazini athu kwa zaka zambiri. M’malo mongomupatsa Nsanja ya Olonda yatsopano, m’baleyo anaganiza zomuwerengera lemba limene linali m’magaziniyo. Anamuwerengera lemba la 2 Akorinto 1:3, 4 lomwe limanena kuti: “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.” Wachikulireyo analikonda kwambiri lembali moti anapempha m’baleyo kuti aliwerengenso. Kenako ananena kuti iye ndi mkazi wake ankafunitsitsa kutonthozedwa. Zimenezi zinachititsa kuti afune kuphunzira zambiri. Uwutu ndi umboni wakuti Mawu a Mulungu amakhala amphamvu tikamawagwiritsa ntchito mu utumiki.—Mac. 19:20.
POPHUNZITSA PAMISONKHANO
11. Kodi abale amene amaphunzitsa pamisonkhano ayenera kuchita chiyani?
11 Tonsefe timasangalala kupezeka pamisonkhano yathu yampingo komanso ikuluikulu. Cholinga chathu chachikulu popezeka pamisonkhano ndi kulambira Yehova. Koma kumisonkhano timalandiranso malangizo othandiza kwambiri. Abale amene amaphunzitsa pamisonkhanoyi ali ndi mwayi waukulu. Komabe iwo ayenera kuzindikiranso kuti umenewu ndi udindo waukulu kwambiri. (Yak. 3:1) Choncho ayenera kutsimikizira kuti zimene akuphunzitsa ndi zochokera m’Mawu a Mulungu. Ngati mumaphunzitsa pamisonkhano, kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito bwino Baibulo?
12. Kodi m’bale angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino Malemba pokamba nkhani?
12 Muyenera kuonetsetsa kuti mukugwiritsa ntchito bwino Malemba pokamba nkhani yanu. (Yoh. 7:16) Kodi mungachite bwanji zimenezi? Choyamba, muziyesetsa kuti anthu aziganizira kwambiri malemba amene mukugwiritsa ntchito m’malo moganizira kwambiri zitsanzo zanu, mafanizo kapenanso kalankhulidwe kanu. Muzikumbukiranso kuti kungowerenga malemba sikutanthauza kuti mukugwiritsa ntchito bwino malembawo pophunzitsa. Komanso kugwiritsa ntchito malemba ambiri kungachititse kuti anthu asawakumbukire. Choncho muyenera kusankha bwino malemba anu n’cholinga choti muthe kuwawerenga, kuwafotokoza, kupereka fanizo komanso kusonyeza mmene malembawo angathandizire anthu. (Neh. 8:8) Ngati nkhani imene mukufuna kukamba ndi yochokera mu autilaini yokonzedwa ndi gulu, muyenera kuikonzekera bwino n’kuona malemba onse. Yesetsani kuti muone kugwirizana pakati pa mfundo za pa autilaini ndi malemba ake. Kenako muyenera kusankha malemba amene angakuthandizeni kuphunzitsa mfundo za mu autilainiyo. (Mukhoza kupeza mfundo zothandiza pa phunziro 21 mpaka 23 m’buku lakuti Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.) Koma chofunika kwambiri ndi kupempha Yehova kuti akuthandizeni kufotokoza bwino mfundo zofunika za m’Mawu ake.—Werengani Ezara 7:10; Miyambo 3:13, 14.
13. (a) Kodi mlongo wina anakhudzidwa bwanji ndi lemba limene linagwiritsidwa ntchito pamisonkhano? (b) Kodi inuyo mwathandizidwa bwanji ndi malemba amene anagwiritsidwa ntchito pamisonkhano?
13 Mlongo wina wa ku Australia anakhudzidwa kwambiri ndi malemba ena amene anagwiritsidwa ntchito pamisonkhano. Iye anakumana ndi mavuto aakulu ali mwana koma anaphunzira Baibulo ndipo anadzipereka kwa Yehova. Ngakhale zinali choncho, zinkamuvuta kukhulupirira kuti Yehova amamukonda. Koma patapita nthawi, anamva lemba lina pamisonkhano ndipo analiganizira kwambiri n’kuligwirizanitsa ndi malemba ena. * Zimenezi zinamuthandiza kuti ayambe kuona kuti Yehova amamukonda. Kodi inunso munakhudzidwapo ndi malemba amene anagwiritsidwa ntchito pa misonkhano yampingo kapena ikuluikulu?—Neh. 8:12.
14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira Baibulo?
14 Tonsefe timathokoza kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa Mawu ake. Iye anatipatsa Baibulo chifukwa chotikonda ndipo wakwaniritsa lonjezo lake lakuti Mawu akewo adzakhalapo mpaka kalekale. (1 Pet. 1:24, 25) Tingachite bwino kuwerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse ndiponso kuwagwiritsa ntchito pa moyo wathu komanso pothandiza anthu ena. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti timayamikira Baibulo. Koma chofunika kwambiri n’chakuti timasonyeza kuti timakonda kwambiri Yehova Mulungu amene anatipatsa Baibulolo.
^ ndime 13 Onani bokosi lakuti “ Maganizo Anga Anasintha.”