“Mawu a Mulungu Wathu Adzakhala Mpaka Kalekale”
“Udzu wobiriwirawo wauma. Maluwawo afota. Koma mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”—YES. 40:8.
NYIMBO: 116, 115
1, 2. (a) Kodi moyo wathu ukanakhala wotani zikanakhala kuti kulibe Baibulo? (b) N’chiyani chimafunika kuti Baibulo lizitithandiza?
KODI mukuganiza kuti moyo wanu ukanakhala wotani zikanakhala kuti kulibe Baibulo? Simukanakhala ndi malangizo okuthandizani tsiku lililonse. Simukanapezanso mayankho a mafunso okhudza Mulungu, moyo komanso zimene zidzachitike m’tsogolo. Komanso simukanadziwa zimene Mulungu anachitira anthu m’mbuyomu.
2 Koma chosangalatsa n’chakuti Yehova watipatsa Baibulo lomwe ndi Mawu ake. Ndipo iye amatitsimikizira kuti uthenga umene uli m’Baibulo udzakhalapo mpaka kalekale. M’kalata yake, mtumwi Petulo analemba mawu amene amapezeka pa Yesaya 40:8. N’zoona kuti mawuwo si ofotokoza za Baibulo limene tili nalo panopa koma mfundo yake imagwiranso ntchito ponena za uthenga wa m’Baibulo. (Werengani 1 Petulo 1:24, 25.) Baibulo likhoza kutithandiza makamaka ngati tikuliwerenga m’chilankhulo chimene timamva bwino. Anthu okonda Mawu a Mulungu anazindikira mfundo imeneyi kalekale. Choncho kwa zaka zambiri, anthu ena amtima wabwino akhala akugwira ntchito yomasulira Malemba komanso kuwafalitsa mwakhama ngakhale kuti sizinali zophweka. Zimene ankachitazi zinali zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu choti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”—1 Tim. 2:3, 4.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi? (Onani chithunzi choyambirira.)
3 Munkhaniyi, tikambirana chifukwa chake Mawu a Mulungu akupezekabe ngakhale kuti (1) zilankhulo zimasintha, (2) ulamuliro ukasintha chilankhulo chachikulu chinkasinthanso (3) anthu ena ankaletsa kumasulira Baibulo. Kukambirana mfundo zimenezi kungatithandize kuti tiziyamikira kwambiri Mawu a Mulungu. Kungatithandizenso kuti tizikonda kwambiri Yehova amene analemba Baibulo n’kutipatsa.—Mika 4:2; Aroma 15:4.
ZILANKHULO ZIMASINTHA
4. (a) Kodi zilankhulo zimasintha bwanji pakapita nthawi? (b) N’chiyani chimasonyeza kuti Mulungu sakondera chilankhulo chinachake, nanga kudziwa zimenezi kumakulimbikitsani kuchita chiyani?
4 Pakapita nthawi, zilankhulo zimasintha moti matanthauzo a mawu ena amasinthiratu. Mwina mwaona zimenezi m’chilankhulo china chimene mumachidziwa. Umu ndi mmene zilili ndi Chiheberi komanso Chigiriki. Pafupifupi Baibulo lonse linalembedwa m’zilankhulo ziwirizi. Koma zilankhulo zimenezi zasintha kwambiri masiku ano tikayerekeza ndi mmene zinalili pamene Baibulo linkalembedwa. Choncho anthu ambiri, ngakhale amene amalankhula Chiheberi kapena Chigiriki cha masiku ano, ayenera kuwerenga Baibulo limene linachita kumasuliridwa kuti alimvetse bwino. Anthu ena amaganiza kuti ayenera kuphunzira Chiheberi ndi Chigiriki chakale n’cholinga choti aziwerenga Baibulo m’chilankhulo chimene linalembedwa. Koma zimenezi sizingawathandize kwenikweni. * Chosangalatsa n’chakuti panopa Baibulo lathunthu kapena mbali zake zina zamasuliridwa m’zilankhulo zoposa 3,000. Apa zikuonekeratu kuti Yehova amafuna kuti Mawu ake azithandiza anthu ochokera ‘kudziko lililonse, fuko lililonse komanso chinenero chilichonse.’ (Werengani Chivumbulutso 14:6.) Kudziwa zimenezi kumatilimbikitsa kukonda kwambiri Mulungu wathu yemwe ndi wopanda tsankho.—Mac. 10:34.
5. Kodi Baibulo la King James Version linali losiyana bwanji ndi Mabaibulo ena?
5 Komatu si Chiheberi ndi Chigiriki chokha chimene chasintha. Zilankhulo zina zimene Baibulo linamasuliridwa zimasinthanso pakapita nthawi. Choncho Baibulo limene poyamba linkathandiza kwambiri anthu pakapita nthawi limakhala losathandiza chifukwa cha kusintha kwa chilankhulo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Baibulo lina limene linamasuliridwa m’Chingelezi. Baibulo lake ndi la King James Version lomwe linatuluka mu 1611. Anthu ambiri ankakonda Baibuloli ndipo mawu ake ena okuluwika anayamba kugwiritsidwa ntchito kwambiri m’Chingelezi. * Koma m’Baibuloli dzina la Mulungu limangopezeka m’mavesi ochepa. M’mavesi ena amene dzina la Yehova linkapezeka mu Malemba Achiheberi oyambirira, m’Baibuloli anangoikamo mawu oti Ambuye olembedwa m’zilembo zazikulu. Patapita nthawi, mawu oti Ambuye olembedwa m’zilembo zazikulu anayamba kuwaikanso m’mavesi ena a Malemba Achigiriki. Zimenezi zikusonyeza kuti ofalitsa Baibuloli ankazindikira kuti dzina la Mulungu liyenera kupezekanso m’Malemba Achigiriki, omwe anthu ambiri amati Chipangano Chatsopano.
6. N’chifukwa chiyani timayamikira kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano?
6 Koma patapita nthawi, mawu ambiri a m’Baibulo limeneli anayamba kumveka achikale. Umu ndi mmenenso zilili ndi Mabaibulo amene Sal. 119:97) Chosangalatsa kwambiri ndi Baibuloli n’chakuti dzina la Mulungu linabwezeretsedwa m’malo ake onse.
anamasuliridwa m’zilankhulo zina. N’chifukwa chake tikuyamikira kwambiri kuti tili ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lomasuliridwa m’chilankhulo chamakono. Baibulo limeneli likupezeka lonse kapena mbali zake m’zilankhulo zoposa 150. Choncho anthu ambiri padziko lonse akhoza kulipeza. Popeza kuti mawu ake ndi osavuta kumva, uthenga wake umafika anthu pamtima. (ULAMULIRO UKASINTHA CHILANKHULO CHACHIKULU CHINKASINTHANSO
7, 8. (a) N’chifukwa chiyani Ayuda ambiri ankavutika kumva Malemba Achiheberi m’ma 200 B.C.E.? (b) Kodi mungalifotokoze bwanji Baibulo la Septuagint?
7 Chilankhulo chachikulu chimasintha mogwirizana ndi ulamuliro umene ulipo pa nthawiyo. Koma Yehova waonetsetsa kuti kusintha kumeneku kusalepheretse anthu kumva Mawu ake. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mabuku 39 oyambirira a m’Baibulo omwe analembedwa ndi Aisiraeli kapena kuti Ayuda. Paja Baibulo limanena kuti poyamba “mawu opatulika a Mulungu anaikidwa m’manja mwa Ayuda.” (Aroma 3:1, 2) Koma pofika m’ma 200 B.C.E., Ayuda ambiri sankamva Chiheberi. Zinali choncho chifukwa choti ulamuliro wa Agiriki unafalikira m’madera ambiri nthawi ya Alekizanda Wamkulu. (Dan. 8:5-7, 20, 21) Zimenezi zinachititsa kuti Chigiriki chikhale chilankhulo chodziwika ndi anthu ambiri, kuphatikizapo Ayuda amene ankakhala m’madera amenewa. Ayuda ambiri atayamba kulankhula Chigiriki ankavutika kumva Malemba Achiheberi. Kodi vuto limeneli linatha bwanji?
8 Cha m’ma 250 B.C.E., mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo anali atamasuliridwa m’Chigiriki. Pofika m’ma 100 B.C.E., mabuku ena amene anatsala m’Malemba Achiheberi anali atamasuliridwanso m’Chigiriki. Ataphatikiza mabuku onse a Malemba Achiheberi omasuliridwa m’Chigiriki, anapanga Baibulo lomwe limadziwika kuti Septuagint. Limeneli linali Baibulo loyamba kumasulira Malemba onse Achiheberi m’Chigiriki.
9. (a) Kodi Baibulo la Septuagint komanso Mabaibulo a zilankhulo zina anathandiza bwanji anthu? (b) Kodi inuyo mumakonda kwambiri mavesi ati a m’Malemba Achiheberi?
9 Baibulo limeneli linathandiza Ayuda komanso anthu ena olankhula Chigiriki kuti azimva bwinobwino Malemba Achiheberi. Anthu amenewa ayenera kuti anasangalala kwambiri kumva Mawu a Mulungu m’chilankhulo chimene ankachidziwa bwino. Patapita nthawi, mabuku ena a m’Baibulo anamasuliridwanso m’zilankhulo zina za pa nthawiyo monga Chisiriya, Chigoti ndi Chilatini. Anthu atayamba kuwerenga Mawu a Mulungu m’zilankhulo zimene ankazidziwa bwino, ayenera kuti anali ndi mavesi ena amene ankawakonda kwambiri. (Werengani Salimo 119:162-165.) Zonsezi zikusonyeza kuti Mawu a Mulungu akhalapobe ngakhale kuti zilankhulo zodziwika ndi anthu ambiri zakhala zikusintha mogwirizana ndi ulamuliro umene ulipo.
ANTHU ENA ANKALETSA KUMASULIRA BAIBULO
10. N’chifukwa chiyani anthu ambiri sankatha kuwerenga Baibulo m’zaka za m’ma 1300 C.E.?
10 Anthu ena monga atsogoleri achipembedzo akhala akuletsa kuti anthu wamba akhale ndi Baibulo. Koma anthu ena amtima wabwino sanagwirizane ndi zimenezi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi katswiri wamaphunziro a Baibulo dzina lake John Wycliffe, yemwe anakhalapo m’zaka za m’ma 1300 C.E. Iye ankakhulupirira kuti munthu aliyense ayenera kuwerenga ndiponso kumvetsa bwino Mawu a Mulungu. Koma pa nthawiyo, anthu wamba a ku England sankatha kuwerenga Baibulo. Zinali choncho chifukwa anthu ambiri sankakwanitsa kuligula. Nthawi Miy. 2:1-5.
imeneyo Mabaibulo ankakoperedwa pamanja ndipo anali odula kwambiri. Vuto lina n’lakuti anthu ambiri sankadziwa kuwerenga. Mwina ankamva mavesi akuwerengedwa kutchalitchi, koma n’kutheka kuti sankawamvetsa. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limene linkagwiritsidwa ntchito m’matchalitchi linali lachilatini, koma anthu wamba sankadziwa Chilatini. Ndiye kodi anthuwo anathandizidwa bwanji?—11. Kodi Baibulo la Wycliffe linathandiza bwanji anthu?
11 Mu 1382, Baibulo lachingelezi limene linkadziwika kuti Baibulo la Wycliffe linatulutsidwa. Anthu amene ankatsatira Wycliffe ankalikonda kwambiri. Anthu ena amene ankafuna kuti anthu wamba adziwe bwino Mawu a Mulungu ankayenda m’midzi m’dziko lonse la England n’kumalalikira. Iwo ankawerenga mavesi ena a m’Baibulo la Wycliffe kwa anthu amene ankakumana nawo ndipo ankakhala ndi mapepala oti anakoperapo mavesiwo n’kumapereka kwa anthu. Zimene ankachitazi zinathandiza kwambiri kuti anthu ayambe kukondanso Mawu a Mulungu.
12. Kodi atsogoleri achipembedzo anachita chiyani Wycliffe atatulutsa Baibulo lake?
12 Kodi atsogoleri achipembedzo anachita chiyani? Iwo anayamba kudana kwambiri ndi Wycliffe, Baibulo lake komanso otsatira ake. Atsogoleriwa anayamba kuzunza kwambiri anthu amene ankatsatira Wycliffe aja ndipo ankasakasaka Mabaibulo ake n’kumawawononga. Wycliffe atamwalira, atsogoleriwa ankamuonabe ngati wampatuko. Popeza zinali zosatheka kuti amulange atamwalira, iwo anakafukula mafupa ake n’kuwawotcha ndipo phulusa lake anakalitaya mumtsinje wa Swift. Koma anthu ambiri ankafunitsitsa kuwerenga Mawu a Mulungu ndiponso kuwamvetsa moti atsogoleri achipembedzowa analephera kuwaletsa. M’zaka zotsatira, anthu ambiri ku Europe ndiponso kumadera ena anayamba kulimbikitsa kuti Baibulo lizimasuliridwa ndiponso kufalitsidwa m’zilankhulo zimene anthu wamba amalankhula.
“NDIMAKUPHUNZITSANI KUTI ZINTHU ZIKUYENDERENI BWINO”
13. Kodi Mabaibulo amene afalitsidwa amapereka umboni wotani, nanga zimatitsimikizira za chiyani?
13 Akhristu sayenera kuona kuti ntchito yomasulira Baibulo la Septuagint, la Wycliffe komanso la King James Version inkatsogoleredwa ndi mzimu woyera ngati mmene zinalili ndi Baibulo loyambirira. Komabe tikaganizira Yos. 23:14.
za Mabaibulo amenewa komanso Mabaibulo ena ambiri amene afalitsidwa, timaona umboni wakuti Mawu a Yehova adzakhalapobe mpaka kalekale ngati mmene iye analonjezera. Zimenezi zimatitsimikizira kuti malonjezo ena onse a Yehova adzakwaniritsidwa.—14. Kodi kuganizira chifukwa chake tili ndi Mawu a Mulungu kumatithandiza bwanji?
14 Tikamaganizira kuti Baibulo likupezekabe masiku ano, timalimbikitsidwanso kukonda kwambiri Yehova. * Koma kodi n’chifukwa chiyani Yehova anatipatsa Mawu ake? Nanga n’chifukwa chiyani anatitsimikizira kuti Mawu ake adzakhalapobe mpaka kalekale? Iye anachita zonsezi chifukwa chakuti amatikonda ndipo amafuna kutiphunzitsa kuti zinthu zizitiyendera bwino. (Werengani Yesaya 48:17, 18.) Popeza Yehova wasonyeza kuti amatikonda, ifenso tiyenera kumukonda ndiponso kumvera malamulo ake.—1 Yoh. 4:19; 5:3.
15. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
15 Ngati timaona kuti Mawu a Mulungu ndi ofunika, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti mawuwa azitithandiza pa moyo wathu. Ndiye kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri tikamawerenga Baibulo? N’chiyani chingatithandize kuti tiziligwiritsa ntchito kwambiri tikamalalikira? Nanga anthu amene amaphunzitsa mumpingo angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino Baibulo? Tidzakambirana mafunso amenewa munkhani yotsatira.
^ ndime 4 Onani nkhani yakuti “Kodi Muyenera Kuphunzira Chiheberi ndi Chigiriki?” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2009.
^ ndime 5 Mawu ena okuluwika amene anayamba kuwagwiritsa ntchito m’Chingelezi ndi akuti: “anagwa nkhope yake pansi,” “khungu la mano anga” ndiponso “khuthulani za mumtima mwanu.”—Num. 22:31; Yobu 19:20; Sal. 62:8.
^ ndime 14 Onani bokosi lakuti “ Bwerani Mudzaone!”