Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 38

“Bwerani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”

“Bwerani kwa Ine . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”

“Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani.”​—MAT. 11:28.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yesu analonjeza chiyani pa Mateyu 11:28-30?

YESU analonjeza anthu amene ankamumvetsera zinthu zabwino kwambiri. Iye ananena kuti: ‘Bwerani kwa ine ndipo ndidzakutsitsimutsani.’ (Werengani Mateyu 11:28-30.) Apatu Yesu analonjeza zinthu zimene angazikwaniritsedi. Mwachitsanzo, taganizirani zimene anachitira mayi wina yemwe ankavutika kwambiri ndi matenda ake.

2. Kodi Yesu anathandiza bwanji mayi amene ankadwala?

2 Mayi ameneyu ankafuna kwambiri kuthandizidwa. Iye anadwala kwa zaka 12, ndipo anali atapita kwa madokotala osiyanasiyana koma sanamuchiritse. Mogwirizana ndi Chilamulo, mayiyu anali wodetsedwa. (Lev. 15:25) Kenako anamva kuti Yesu akhoza kuchiritsa anthu odwala ndipo anapita kwa iye. Atamupeza n’kugwira chovala chake, anachira nthawi yomweyo. Apatu Yesu anamuthandiza kuti achire komanso kuti azimva kuti amakondedwa ndiponso kulemekezedwa. Mwachitsanzo, polankhula naye anagwiritsa ntchito mawu akuti “mwanawe,” omwe m’chilankhulo chawo ankasonyeza ulemu komanso chikondi. N’zosachita kufunsa kuti mayiyu analimbikitsidwa kwambiri.​—Luka 8:43-48.

3. Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Nkhaniyi imati mayiyo ndi amene anapita kwa Yesu osati anangokhala n’kumamudikira. Ndi mmene zililinso masiku ano. Tiyenera kuyesetsa kuti tipite kwa Yesu. N’zoona kuti panopa, Yesu sachiritsa matenda enieni a anthu amene apita kwa iye. Koma akuitanabe anthu kuti: ‘Bwerani kwa ine ndipo ndidzakutsitsimutsani.’ Munkhaniyi tikambirana mafunso 5 awa: Kodi tingapite bwanji kwa Yesu? Kodi iye ankatanthauza chiyani ponena kuti: “Senzani goli langa”? Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yesu? Nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito imene watipatsa imatitsitsimula? Kodi tingatani kuti tipitirize kutsitsimulidwa posenza goli lake?

“BWERANI KWA INE”

4-5. Kodi ndi njira ziti zimene zingatithandize kuti tipite kwa Yesu?

4 Njira imodzi imene ingatithandize kuti tipite kwa Yesu ndi kuyesetsa kuphunzira zimene anachita komanso kunena. (Luka 1:1-4) Ndi udindo wathu kuphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza Yesu ndipo palibe amene angatichitire zimenezi. Timapitanso kwa Yesu ngati tasankha kubatizidwa n’kukhala wotsatira wake.

5 Njira ina imene ingatithandize kuti tipite kwa Yesu ndi kupempha akulu kuti azitithandiza tikakumana ndi mavuto. Akulu ndi “mphatso za amuna” zimene Yesu amagwiritsa ntchito posamalira nkhosa zake. (Aef. 4:7, 8, 11; Yoh. 21:16; 1 Pet. 5:1-3) Choncho ifeyo tiyenera kupempha akulu kuti azitithandiza. Tisamayembekezere kuti akulu akhoza kudziwa okha zimene tikuganiza kapena tikufunikira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Julian. Iye anati: “Ndinkafunika kusiya kutumikira ku Beteli chifukwa cha matenda ndipo mnzanga wina anandiuza kuti ndingachite bwino kupempha ulendo waubusa. Poyamba ndinkaganiza kuti sindikufunikira zimenezi. Koma kenako ndinapempha kuti akulu andithandize ndipo ulendo waubusa umene anachita unali ngati mphatso yabwino kwambiri kuposa zonse zimene ndinalandirapo.” Akulu okhulupirika ngati amene anathandiza Julian angatithandize kudziwa “maganizo a Khristu.” Apa tikutanthauza kuti angatithandize kumvetsa bwino mmene Yesu amaganizira ndiponso kutengera chitsanzo chake. (1 Akor. 2:16; 1 Pet. 2:21) Imeneyi ndi mphatso yabwino kwambiri yomwe angatipatse.

“SENZANI GOLI LANGA”

6. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Senzani goli langa”?

6 Pamene Yesu ananena kuti: “Senzani goli langa,” mwina ankatanthauza kuti “Muzigonjera ulamuliro wanga.” Apo ayi, ankatanthauza kuti “Bwerani tisenze limodzi goli langa ndipo tithandizane kugwira ntchito ya Yehova.” Kaya ankatanthauza chiyani, mawu akuti goli akusonyeza kuti pali ntchito imene tiyenera kugwira.

7. Malinga ndi Mateyu 28:18-20, kodi tapatsidwa ntchito iti, nanga sitiyenera kukayikira chiyani?

7 Timamvera mawu a Yesu amenewa tikadzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa. Yesu akuitana anthu onse ndipo sangakane munthu aliyense amene akufunitsitsa kutumikira Mulungu. (Yoh. 6:37, 38) Anthu onse amene amatsatira Khristu apatsidwa mwayi wogwira nawo ntchito imene Yehova anapatsa Yesu. Tisamakayikire kuti Yesu azitithandiza nthawi zonse kugwira ntchito imeneyi.​—Werengani Mateyu 28:18-20.

“PHUNZIRANI KWA INE”

Tizitsitsimula ena ngati Yesu (Onani ndime 8-11) *

8-9. N’chifukwa chiyani anthu ooneka ngati onyozeka ankakonda kupita kwa Yesu, nanga tingadzifunse mafunso ati?

8 Anthu odzichepetsa ankakonda kupita kwa Yesu. (Mat. 19:13, 14; Luka 7:37, 38) Tingamvetse chifukwa chake tikaganizira kusiyana pakati pa Yesu ndi Afarisi. Tikutero chifukwa chakuti Afarisi anali onyada komanso opanda chikondi. (Mat. 12:9-14) Koma Yesu anali wachikondi ndiponso wodzichepetsa. Afarisi ankafuna kutchuka komanso ankakonda maudindo. Pomwe Yesu ankalimbikitsa ophunzira ake kuti azipewa mtima wokonda udindo komanso kuti azikhala odzichepetsa n’kumatumikira ena. (Mat. 23:2, 6-11) Afarisi ankakonda kuopseza ndiponso kupondereza anthu ena. (Yoh. 9:13, 22) Koma Yesu ankalimbikitsa anthu ena powachitira zinthu mwachikondi komanso kuwalankhula mokoma mtima.

9 Kodi inuyo mumatsanzira Yesu? Kuti muyankhe funsoli, mungadzifunse kuti: ‘Kodi anthu ena amaona kuti ndine wofatsa komanso wodzichepetsa? Kodi ndimalolera kuchita zinthu zooneka ngati zonyozeka pothandiza ena? Nanga ndimachita zinthu mokoma mtima?

10. Kodi Yesu ankagwira ntchito bwanji ndi anzake?

10 Yesu ankagwira ntchito ndi anzake mwamtendere ndipo ankasangalala powaphunzitsa. (Luka 10:1, 19-21) Iye ankalimbikitsa ophunzira ake kuti azifunsa mafunso ndipo ankakonda kumva maganizo awo. (Mat. 16:13-16) Ophunzira ake anali ngati maluwa osamaliridwa bwino. Iwo ankamvetsa bwino zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ankabala zipatso kapena kuti ankachita zinthu zabwino.

Tizikhala Ochezeka

Tizikhala Akhama

Tizidzichepetsa N’Kumalimbikira Ntchito *

11. Kodi tingadzifunse mafunso ati?

11 Kodi inuyo mumayang’anira anthu ena? Ngati ndi choncho, muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimachita bwanji zinthu ndi ena kuntchito kapena kunyumba? Kodi ndimalimbikitsa mtendere? Nanga ndimalimbikitsa ena kuti azindifunsa mafunso? Kodi ndimakonda kumvetsera maganizo awo?’ Akhristufe sitifuna ngakhale pang’ono kufanana ndi Afarisi omwe sankakonda kufunsidwa mafunso ndipo ankazunza anthu omwe anali ndi maganizo osiyana ndi awo.​—Maliko 3:1-6; Yoh. 9:29-34.

“MUDZATSITSIMULIDWA”

12-14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito imene Yesu anatipatsa imatitsitsimula?

12 Kodi ntchito imene Yesu anatipatsa imatitsitsimula bwanji? Pali njira zingapo, koma tiyeni tingokambirana njira zochepa.

13 Tili ndi oyang’anira abwino kwambiri. Woyang’anira wathu wamkulu ndi Yehova ndipo iye si wosayamika kapena wankhanza. Koma amayamikira ntchito imene timagwira. (Aheb. 6:10) Amatipatsanso mphamvu kuti tigwire bwino ntchito yathu. (2 Akor. 4:7; Agal. 6:5) Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu, amapereka chitsanzo chabwino kwambiri. (Yoh. 13:15) Nawonso akulu amene amatiyang’anira amayesetsa kutsanzira Yesu yemwe ndi “m’busa wamkulu.” (Aheb. 13:20; 1 Pet. 5:2) Iwo amatidyetsa komanso kutiteteza. Pochita zimenezi amayesetsa kukhala olimbikitsa, okoma mtima komanso olimba mtima.

14 Tili ndi anzathu abwino kwambiri. Palibenso anthu ena amene ali ndi anzawo achikondi amene angagwire nawo ntchito mogwirizana ngati mmene zilili ndi ifeyo. Tangoganizani: Tili ndi mwayi wogwira ntchito limodzi ndi anthu amakhalidwe abwino kwambiri koma omwe sadziona ngati apamwamba. Anzathuwo ndi aluso kwambiri koma amadzichepetsa n’kumaona kuti anthu ena ndi owaposa. Iwo amationa ngati anzawo apamtima osati anthu ongogwira nawo ntchito. Iwo amatikonda kwambiri moti angalolere kutifera.

15. Kodi tiyenera kumva bwanji tikaganizira za ntchito yathu?

15 Tili ndi ntchito yabwino kwambiri. Timaphunzitsa anthu mfundo zoona zokhudza Yehova komanso timawathandiza kuzindikira mabodza a Mdyerekezi. (Yoh. 8:44) Satana amasenzetsa anthu katundu amene sangakwanitse kumunyamula. Mwachitsanzo, amafuna kuti tiziganiza kuti Yehova sangatikhululukire ndipo palibe amene angatikonde. Limeneli ndi bodza lamkunkhuniza komanso katundu wolemera koopsa. Anthufe tikapita kwa Khristu machimo athu amakhululukidwa. Ndipo zoona zake n’zakuti Yehova amatikonda kwambiri tonsefe. (Aroma 8:32, 38, 39) Ndi mwayi waukulu kwambiri kuthandiza anthu kuti ayambe kudalira Yehova n’kumasintha moyo wawo kuti akhale osangalala.

PITIRIZANI KUTSITSIMULIDWA POSENZA GOLI LA YESU

16. Kodi katundu amene Yesu watiuza kuti timusenze ndi wosiyana bwanji ndi katundu wina amene timanyamula?

16 Katundu amene Yesu watiuza kuti timusenze ndi wosiyana kwambiri ndi katundu amene timanyamula nthawi zonse. Mwachitsanzo, pambuyo pogwira ntchito zina, anthu ambiri amakhala atatopa komanso osasangalala. Koma tikagwira ntchito kwa nthawi yaitali potumikira Yehova ndi Khristu timakhala osangalala. Mwina tikhoza kuweruka kuntchito titatopa kwambiri n’kudzikakamiza kupita kumisonkhano. Ndipo nthawi zambiri timabwera titalimbikitsidwa komanso tikusangalala. Zimenezi zimachitikanso tikamalalikira komanso kuphunzira patokha. N’zoona kuti tiyenera kuchita khama kwambiri kuti tichite zinthu zimenezi koma madalitso amene timapeza ndi ambiri.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kuzindikira malire athu komanso kukhala osamala?

17 Tiyenera kuzindikira kuti mphamvu zathu zili ndi malire. Choncho tizisamala kuti tisamachite zinthu zambiri kuposa zimene tingakwanitse. Mwachitsanzo, tikhoza kumatanganidwa kwambiri poyesetsa kupeza chuma. Koma ndi bwino kukumbukira zimene Yesu anauza mnyamata wina wachuma amene anamufunsa kuti: “Ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?” Mnyamatayo ankamvera Chilamulo ndipo ayenera kuti anali munthu wabwino. Tikutero chifukwa chakuti buku la Maliko limanena kuti Yesu “anam’konda.” Yesu anauza mnyamatayo kuti: ‘Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndipo ubwere udzakhale wotsatira wanga.’ Munthuyo ankafuna kuchita zimenezi koma zikuoneka kuti sankafuna kuluza ‘katundu wake wambiri.’ (Maliko 10:17-22) Choncho anakana goli la Yesu ndipo anapitiriza kukhala kapolo wa “Chuma.” (Mat. 6:24) Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?

18. Kodi nthawi zina tiyenera kuchita chiyani? Perekani chifukwa.

18 Nthawi zina tiyenera kudzifufuza kuti tidziwe zimene tikuika pamalo oyamba. Zimenezi zingatithandize kutsimikizira kuti tikugwiritsa ntchito mwanzeru mphamvu zathu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mnyamata wina dzina lake Mark. Iye anati: “Kwa zaka zambiri, ndinkaganiza kuti ndikukhala moyo wosalira zambiri. Ngakhale kuti ndinkachita upainiya, ndinkangokhalira kuganizira za ndalama komanso zokhala ndi moyo wabwino. Koma ndinadabwa kuti ndinkakhala wopanikizika. Kenako ndinazindikira kuti ndinkaika zofuna zanga pamalo oyamba n’kumagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zimene zatsala kuti ndizitumikira Yehova.” Mark anasintha maganizo ake komanso moyo wake kuti ayambe kuchita zambiri potumikira Yehova. Iye ananena kuti: “Nthawi zina ndimada nkhawa koma Yehova komanso Yesu amandithandiza kuthana ndi mavuto anga.”

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona zinthu moyenera?

19 Kuti tipitirize kutsitsimulidwa posenza goli la Yesu, tiyenera kuchita zinthu zitatu. Choyamba, tiziona zinthu moyenera. Ntchito imene timagwira ndi ya Yehova choncho tiyenera kuigwira m’njira imene iye akufuna. Paja ife ndife antchito ndipo Yehova ndi Ambuye wathu. (Luka 17:10) Tikamagwira ntchitoyi m’njira yathuyathu tidzapeza kuti tikuvutika kusenza golilo. Ngakhale ng’ombe yamphamvu kwambiri ikhoza kutopa komanso kudzipweteka ngati nthawi zonse ikulimbana ndi goli chifukwa sikufuna kupita kumene mwiniwake akufuna. Koma tikamatsatira malangizo a Yehova tikhoza kuchita zinthu zikuluzikulu komanso kuthana ndi vuto lililonse. Tisaiwale kuti palibe amene angalepheretse Yehova kukwaniritsa zimene akufuna.​—Aroma 8:31; 1 Yoh. 4:4.

20. Kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chotani tikamasenza goli la Yesu?

20 Chachiwiri, tizichita zinthu ndi cholinga chabwino. Cholinga chathu ndi kulemekeza Atate wathu wachikondi, Yehova. Yesu ali padzikoli, anthu amene anali ndi cholinga chadyera kapena ankangofuna kupeza zinazake sanapitirize kukhala osangalala ndipo anasiya kusenza goli lake. (Yoh. 6:25-27, 51, 60, 66; Afil. 3:18, 19) Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene sanali odzikonda koma ankakonda Mulungu ndi anzawo ankasenza golili kwa moyo wawo wonse ndipo ankayembekezera kukatumikira ndi Khristu kumwamba. Nafenso tikamachita zinthu ndi cholinga chabwino tikhoza kusenza goli la Yesu mosangalala.

21. Malinga ndi Mateyu 6:31-33, kodi tiziyembekezera kuti Yehova angachite chiyani?

21 Chachitatu, tiziyembekezera kuti Yehova angatithandize. Akhristufe tinasankha moyo wodzimana zinthu zina komanso wogwira ntchito mwakhama. Yesu anatichenjezanso kuti tidzazunzidwa. Koma tiyenera kuyembekezera kuti Yehova adzatipatsa mphamvu kuti tipirire vuto lililonse. Ndipo tikamapirira kwambiri m’pamene timakhalanso olimba kwambiri. (Yak. 1:2-4) Tisamakayikire kuti Yehova azitipatsa zimene tikufunikira, Yesu azititsogolera ngati m’busa wabwino komanso abale ndi alongo athu azitilimbikitsa. (Werengani Mateyu 6:31-33; Yoh. 10:14; 1 Ates. 5:11) Apatu tingati tili ndi zonse zimene tingafunikire.

22. Kodi tiyenera kuyamikira chiyani?

22 Mayi wodwala uja anatsitsimulidwa pa tsiku limene Yesu anamuchiritsa. Koma kuti apitirize kutsitsimulidwa mpaka kalekale, anafunika kukhala wophunzira wokhulupirika wa Khristu. Kodi inuyo mukuganiza kuti mayiyu anatani? Ngati anasankha kusenza goli la Yesu, ndiye kuti anali ndi mwayi wokatumikira ndi Yesuyo kumwamba. Chilichonse chimene analolera kudzimana kuti azitsatira Khristu n’chaching’ono kwambiri poyerekezera ndi madalitso amenewa. Kaya tikuyembekezera moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli, tiyenera kuyamikira kuti tinavomera pamene Yesu anatiuza kuti: “Bwerani kwa ine.”

NYIMBO NA. 13 Khristu Ndi Chitsanzo Chathu

^ ndime 5 Yesu akutiitana kuti tipite kwa iye. Kodi tingapite bwanji kwa iye? Nkhaniyi iyankha funso limeneli komanso isonyeza zimene tingachite kuti titsitsimulidwe pogwira ntchito ndi Khristu.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Yesu ankatsitsimula anthu m’njira zosiyanasiyana.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mofanana ndi Yesu, m’bale wina akuyesetsanso kuchita zinthu zosiyanasiyana zimene zingalimbikitse ena