Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 39

“Ndinaona Khamu Lalikulu la Anthu”

“Ndinaona Khamu Lalikulu la Anthu”

“Ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga . . . Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.”—CHIV. 7:9.

NYIMBO NA. 60 Akamvera Adzapeza Moyo

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi zinthu zinali bwanji pa moyo wa mtumwi Yohane cha m’ma 95 C.E.?

CHA M’MA 95 C. E., mtumwi Yohane anali atakalamba komanso anali m’ndende pachilumba cha Patimo. Pa nthawiyi, atumwi ena onse anali atamwalira. (Chiv. 1:9) Yohane ankadziwa kuti m’mipingo munali otsutsa amene ankasocheretsa anthu komanso kusokoneza mgwirizano. Zinkaoneka ngati mipingo yachikhristu sipitirira kukhalapo.​—Yuda 4; Chiv. 2:15, 20; 3:1, 17.

Mtumwi Yohane anaona a “khamu lalikulu” atavala mikanjo yoyera ndiponso atanyamula nthambi zakanjedza m’manja mwawo (Onani nkhani yophunzira 39, ndime 2)

2. Malinga ndi Chivumbulutso 7:9-14, kodi Yohane anaona masomphenya ati? (Onani chithunzi patsamba loyamba la magaziniyi.)

2 Pa nthawi yovutayi, Mulungu anaonetsa Yohane masomphenya a zinthu zosangalatsa zimene zidzachitike m’tsogolo. M’masomphenyawo, angelo anauzidwa kuti agwire mphepo zowononga za chisautso chachikulu kufikira akapolo ena atadindidwa chidindo chomaliza. (Chiv. 7:1-3) Akapolowo ndi anthu okwana 144,000 omwe adzalamulire ndi Yesu kumwamba. (Luka 12:32; Chiv. 7:4) Kenako Yohane anatchulanso za gulu lina lalikulu kwambiri moti ananena kuti: “Ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse. Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Werengani Chivumbulutso 7:9-14.) Yohane ayenera kuti anasangalala kwambiri atadziwa kuti m’tsogolo anthu ambirimbiri azidzalambira Mulungu woona.

3. (a) N’chifukwa chiyani masomphenya a Yohane angalimbitse chikhulupiriro chathu? (b) Kodi tiphunzira chiyani munkhaniyi?

3 N’zosakayikitsa kuti chikhulupiriro cha Yohane chinalimba ataona masomphenyawa. Masomphenyawa akhoza kulimbitsa kwambiri chikhulupiriro chathu chifukwa tikukhala mu nthawi imene akukwaniritsidwa. Masiku ano anthu ambirimbiri akusonkhanitsidwa ndipo akuyembekezera kupulumuka pa chisautso chachikulu n’kudzakhala padzikoli mpaka kalekale. Munkhaniyi, tiphunzira mmene Yehova anathandizira anthu ake zaka zoposa 80 zapitazo kudziwa bwino khamu lalikululi. Kenako tikambirana zinthu ziwiri zokhudza khamuli. Zinthu zake ndi (1) kukula kwake komanso (2) anthu ake ndi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana. Zimenezi zilimbitsa chikhulupiriro cha anthu onse amene ali m’gulu limeneli.

KODI KHAMU LALIKULU LIDZAKHALA KUTI?

4. Kodi ndi mfundo iti ya m’Malemba imene matchalitchi saimvetsa, nanga zikusiyana bwanji ndi zimene Ophunzira Baibulo ankakhulupirira?

4 Matchalitchi amene amati ndi achikhristu saphunzitsa mfundo ya m’Malemba yakuti anthu omvera Mulungu adzakhala ndi moyo wosatha padzikoli. (2 Akor. 4:3, 4) Masiku ano, zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti anthu onse abwino akamwalira amapita kumwamba. Koma Ophunzira Baibulo ochepa, amene ankafalitsa Nsanja ya Olonda kuyambira mu 1879, sankaphunzitsa zimenezi. Iwo ankakhulupirira kuti Mulungu adzabwezeretsa Paradaiso padzikoli ndipo anthu omvera Mulungu ambirimbiri adzakhala padzikoli osati kumwamba. Koma zinawatengera nthawi kuti azindikire kuti anthu omverawo ndi ndani.​—Mat. 6:10.

5. Kodi Ophunzira Baibulo ankakhulupirira zotani zokhudza a 144,000?

5 Ophunzira Baibulo anazindikiranso kuti Malemba amaphunzitsa kuti anthu ena ‘adzagulidwa kuchokera padziko lapansi’ kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. (Chiv. 14:3) Anthu amenewa ndi Akhristu okwana 144,000 omwe amatumikira Mulungu mokhulupirika pa nthawi imene ali padzikoli. Koma kodi Ophunzira Baibulo ankakhulupirira zotani zokhudza khamu lalikulu?

6. Kodi Ophunzira Baibulo ankakhulupirira zotani zokhudza khamu lalikulu?

6 M’masomphenyawa, Yohane anaona anthu a m’gululo “ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:9) Mawu amenewa anachititsa Ophunzira Baibulo kuganiza kuti anthu a m’khamu lalikululo adzapitanso kumwamba. Zikanakhala kuti magulu onse awiriwa, a 144,000 komanso khamu lalikulu, adzapita kumwamba, kodi maguluwa akanasiyana bwanji? Ophunzira Baibulo ankaganiza kuti khamu lalikulu ndi la Akhristu omwe sanamvere Mulungu pa zinthu zina ali padzikoli. Ankaona kuti ngakhale anthu amakhalidwe abwino omwe anali adakali m’matchalitchi, analinso m’khamu lalikulu. Ophunzira Baibulo ankakhulupirira kuti a khamu lalikulu ankakhala ndi khama ndithu koma osati lokwanira kuti akalamulire ndi Yesu. Ankaganiza kuti popeza anthu a khamu lalikululi sankakonda Mulungu mokwanira, anali oyenera kupita kumwamba n’kuimirira pamaso pa mpando wachifumu koma osati kukhala m’mipando yachifumu.

7. Kodi Ophunzira Baibulo ankaganiza kuti ndi ndani amene adzakhale padzikoli mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, nanga ankakhulupirira chiyani zokhudza anthu okhulupirika akale?

7 Ndiye kodi Ophunzira Baibulowa ankakhulupirira kuti ndi ndani adzakhale padzikoli? Iwo ankakhulupirira kuti anthu 144,000 komanso a khamu lalikulu akadzapita kumwamba, anthu mamiliyoni ambiri adzapatsidwa moyo padzikoli kuti adzapeze madalitso mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Ophunzira Baibulo ankaganiza kuti anthu mamiliyoniwo sadzayamba kutumikira Yehova Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu usanayambe. Koma ankaganiza kuti anthuwa adzaphunzitsidwa njira za Yehova pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000. Kenako anthu amene adzatsatire mfundo za Yehova adzapatsidwa moyo wosatha padziko lapansi, pomwe amene sadzamvera adzawonongedwa. Ophunzira Baibulo ankakhulupiriranso kuti mwina anthu ena omwe adzakhala “akalonga” padzikoli adzapita kumwamba Ulamuliro wa Zaka 1,000 ukadzatha. Ndipo ankaona kuti ena mwa akalongawa adzakhala anthu okhulupirika akale amene adzaukitsidwe.​—Sal. 45:16.

8. Kodi Ophunzira Baibulo ankaganiza kuti pali magulu atatu ati?

8 Choncho Ophunzira Baibulo ankakhulupirira kuti pali magulu atatu awa: (1) Anthu 144,000 omwe adzalamulire ndi Yesu kumwamba, (2) khamu lalikulu la anthu omwe sanali akhama mokwanira ndipo adzapita kumwamba n’kukaimirira “pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa” komanso (3) anthu mamiliyoni ambiri omwe adzaphunzitsidwe njira za Yehova pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. * Koma pa nthawi imene Yehova anaona kuti ndi yoyenera, choonadi chinayamba kuwala kwambiri pa nkhaniyi.​—Miy. 4:18.

KUWALA KWA CHOONADI KUNAWONJEZEREKA

Pamsonkhano wa mu 1935 anthu ambiri oyembekezera kudzakhala padzikoli anabatizidwa (Onani ndime 9)

9. (a) Kodi khamu lalikulu lingaimirire bwanji “pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa”? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kufotokoza lemba la Chivumbulutso 7:9 m’njira imeneyi n’komveka?

9 Mu 1935, a Mboni za Yehova anamvetsa bwino za khamu lalikulu limene Yohane anaona m’masomphenya. Iwo anazindikira kuti khamu lalikululi silidzafunika kupita kumwamba kwenikweni kuti likaimirire “pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” Anazindikira kuti mawu amenewa ndi ophiphiritsa. Zikungotanthauza kuti ngakhale kuti khamuli ndi lapadziko lapansi, limaimirira “pamaso pa mpando wachifumu” chifukwa limazindikira kuti Yehova ndi woyenera kulamulira komanso limagonjera ulamuliro wake. (Yes. 66:1) Khamuli limaimiriranso “pamaso pa Mwanawankhosa” chifukwa limasonyeza kuti limakhulupirira nsembe ya Yesu. Mfundoyi ndi yofanana ndi ya pa Mateyu 25:31, 32 pamene pamati “mitundu yonse ya anthu,” kuphatikizapo anthu oipa, “idzasonkhanitsidwa kwa” Yesu atakhala pampando wake wachifumu waulemerero. Apa n’zodziwikiratu kuti mitundu yonse ya anthuyi idzakhala padziko lapansi osati kumwamba. Zimene a Mboni anazindikira pa nkhani ya khamu lalikulu n’zomveka. Zikusonyeza chifukwa chake Baibulo silinena kuti khamu lalikulu lidzapita kumwamba. Pali gulu limodzi lokha limene lalonjezedwa kupita kumwamba. Gulu lake ndi la 144,000 lomwe likakhala “mafumu olamulira dziko lapansi” limodzi ndi Yesu.​—Chiv. 5:10.

10. N’chifukwa chiyani khamu lalikulu liyenera kuphunzitsidwa njira za Yehova Ulamuliro wa Zaka 1,000 usanayambe?

10 Kuyambira mu 1935, a Mboni za Yehova akhala akukhulupirira kuti khamu lalikulu limene Yohane anaona m’masomphenya ndi la Akhristu okhulupirika amene akuyembekezera moyo wosatha padzikoli. Kuti khamuli lidzapulumuke chisautso chachikulu, liyenera kuphunzitsidwa njira za Yehova Ulamuliro wa Zaka 1,000 usanayambe. Iwo afunika kusonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro cholimba kuti adzathe ‘kuthawa zinthu zonse zimene zikuyembekezeka kuchitika’ Ulamuliro wa Zaka 1,000 usanayambe.​—Luka 21:34-36.

11. Kodi mwina Ophunzira Baibulo ena ankakhulupirira kuti anthu ena adzapita kumwamba pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 pa chifukwa chiti?

11 Nanga bwanji za mfundo imene ankakhulupirira yakuti anthu ena abwino adzapita kumwamba pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000? Mfundo imeneyi inafotokozedwa kalekale mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1913. Mwina inafotokozedwa chonchi chifukwa choganiza kuti: ‘Zingatheke bwanji kuti anthu okhulupirika kwambiri akale angopatsidwa moyo padziko lapansi koma anthu amene sanali okhulupirika kwambiri apatsidwe mwayi wopita kumwamba?’ Anthu ankaganiza zimenezi chifukwa cha mfundo ziwiri zolakwika zokhudza khamu lalikulu zimene ankakhulupirira. Mfundo zake ndi zakuti: (1) khamu lalikulu lidzapita kumwamba ndiponso (2) khamu lalikulu ndi la Akhristu omwe sanali okhulupirika kwambiri.

12-13. Kodi odzozedwa komanso a khamu lalikulu amadziwa kuti adzalandira mphoto yawo pa chifukwa chiti?

12 Malinga ndi zimene takambirana, kuyambira mu 1935, a Mboni za Yehova akhala akukhulupirira kuti khamu lalikulu limene Yohane anaona ndi la anthu amene adzapulumuke pa Aramagedo. Iwo ‘adzatuluka m’chisautso chachikulu’ padziko lomweli ndipo adzapitiriza “kufuula ndi mawu okweza, kuti: ‘Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’” (Chiv. 7:10, 14) Malemba amasonyezanso kuti anthu amene adzapite kumwamba adzalandira “chinthu chabwino kwambiri” kuposa anthu okhulupirika akale. (Aheb. 11:40) Abale athu atamvetsa zimenezi, anayamba kugwira ntchito mwakhama pothandiza anthu kuti ayambe kutumikira Yehova n’cholinga choti adzapeze moyo wosatha padziko lapansi.

13 A khamu lalikulu amasangalala kwambiri akaganizira zimene akuyembekezera. Iwo amazindikira kuti Yehova ndi amene amasankha malo oti anthu ake okhulupirika amutumikire, kaya ndi kumwamba kapena padziko lapansi. Odzozedwa komanso a khamu lalikulu amadziwa kuti adzalandira mphoto yawo chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kumene anakusonyeza popereka dipo la Yesu Khristu.​—Aroma 3:24.

KHAMULI NDI LALIKULU KWAMBIRI

14. Pambuyo pa 1935, kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri sankadziwa mmene ulosi wokhudza khamu lalikulu udzakwaniritsidwire?

14 Anthu a Yehova atayamba kumvetsa bwino nkhani ya khamu lalikulu mu 1935, ambiri ankadzifunsa kuti, ‘Zingatheke bwanji kuti anthu oyembekezera kudzakhala padzikoli achuluke mpaka kufika pokhala khamu lalikulu?’ Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Ronald Parkin, yemwe anali ndi zaka 12 pa nthawi imeneyo. Iye ananena kuti: “Pa nthawiyo panali ofalitsa okwana 56,000 okha padziko lonse ndipo mwina ambiri mwa iwo anali odzozedwa. Choncho tinganene kuti khamu lalikulu linali lisanafike pokhala lalikulu kwenikweni.”

15. Kodi chachitika n’chiyani pa nkhani yosonkhanitsa khamu lalikulu?

15 Koma pa zaka zotsatira, amishonale ankatumizidwa kumayiko ambiri ndipo izi zinathandiza kuti chiwerengero cha Mboni za Yehova chipitirize kuwonjezereka. Kenako mu 1968, a Mboni anayamba kugwiritsa ntchito buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya pophunzira Baibulo ndi anthu. Bukuli linkafotokoza mfundo za m’Baibulo momveka bwino ndipo linathandiza anthu ambiri ofatsa kuti ayambe kutumikira Yehova. Zaka 4 zisanathe, anthu oposa 500,000 anabatizidwa. Kenako Tchalitchi cha Katolika chinayamba kuchepa mphamvu kumayiko a ku Latin America ndipo ntchito yathu inavomerezedwa kumayiko ena a ku Eastern Europe ndi ku Africa. Izi zinathandiza kuti anthu enanso mamiliyoni abatizidwe. (Yes. 60:22) M’zaka za posachedwapa, gulu la Yehova latulutsa zinthu zina zambiri zothandiza anthu kuphunzira Baibulo. Zikuonekeratu kuti panopa khamuli ndi lalikulu chifukwa anthu oposa 8 miliyoni asonkhanitsidwa.

KHAMU LALIKULU LA ANTHU OSIYANASIYANA

16. Kodi khamu lalikulu ndi lochokera kuti?

16 Yohane analemba kuti khamu lalikululi ndi lochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” Iye asanalembe zimenezi, mneneri Zekariya anali ataloseranso kuti: “M’masiku amenewo, amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’”​—Zek. 8:23.

17. N’chiyani chikuchitika pothandiza anthu amitundu yonse komanso azilankhulo zonse?

17 A Mboni za Yehova amadziwa kuti anthu ochokera m’zilankhulo zonse akhoza kusonkhanitsidwa pokhapokha ngati uthenga wabwino ukulalikidwa m’zilankhulo zambiri. Takhala tikumasulira mabuku ophunzirira Baibulo kwa zaka zoposa 130, koma masiku ano mabuku athu akumasuliridwa m’zilankhulo zambiri kuposa m’mbuyo monsemu. Tingati Yehova akuchita zinthu zodabwitsa kwambiri posonkhanitsa khamu lalikulu lochokera m’mitundu yonse. Popeza mabuku ophunzirira Baibulo akupezeka m’zilankhulo zambirimbiri, khamu lalikulu la anthu ochokera kosiyanasiyana likulambira Yehova mogwirizana. Ndipo anthu ake amadziwika chifukwa cha kulalikira mwakhama komanso kukondana. Kunena zoona, zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri.​—Mat. 24:14; Yoh. 13:35.

KODI MASOMPHENYA AMENEWA AMATIKHUDZA BWANJI?

18. (a) Malinga ndi Yesaya 46:10, 11, n’chifukwa chiyani sitikudabwa kuti Yehova wakwaniritsa ulosi wokhudza khamu lalikulu modabwitsa kwambiri? (b) N’chifukwa chiyani anthu amene adzakhale padzikoli saganiza kuti akumanidwa zinazake?

18 Kunena zoona ulosi wokhudza khamu lalikulu ndi wosangalatsa. Sitikudabwa kuti Yehova wakwaniritsa ulosi umenewu modabwitsa kwambiri. (Werengani Yesaya 46:10, 11.) A khamu lalikulu amayamikira zimene Yehova wawalonjeza. Iwo saganiza kuti akumanidwa zinthu zina chifukwa choti sanadzozedwe ndi mzimu wa Mulungu kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. Malemba amafotokoza za amuna ndi akazi okhulupirika ambiri amene ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera koma sanali m’gulu la 144,000. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yohane M’batizi. (Mat. 11:11) Chitsanzo china ndi Davide. (Mac. 2:34) Iwo limodzi ndi anthu ena ambirimbiri adzaukitsidwa kuti akhale padziko lapansi. Onsewa limodzi ndi a khamu lalikulu adzapatsidwa mwayi wosonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova komanso ulamuliro wake.

19. Kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi wokhudza khamu lalikulu kumasonyeza bwanji kuti tiyenera kulalikira mwakhama?

19 Aka n’koyamba kuti Mulungu agwirizanitse anthu mamiliyoni ambiri ochokera m’mitundu yonse. Kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kukhala padzikoli, tiyenera kuthandiza anthu onse amene tingathe kuti akhale m’gulu la khamu lalikulu la “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Posachedwapa, chisautso chachikulu chidzayamba ndipo Yehova adzawononga maboma komanso zipembedzo zomwe zakhala zikuzunza anthu. A khamu lalikulu akuyembekezera mwayi waukulu kwambiri wodzatumikira Yehova padziko lapansi mpaka kalekale.​—Chiv. 7:14.

NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

^ ndime 5 Munkhaniyi tikambirana za masomphenya a Yohane onena za kusonkhanitsidwa kwa “khamu lalikulu la anthu.” Mosakayikira, nkhaniyi ilimbitsa chikhulupiriro cha anthu onse amene ali m’gulu limeneli.

^ ndime 8 Onani buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulira, tsamba 52, ndime 14-15 komanso Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 159-163.