Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 35

Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali

Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali

“Yehova . . . amaona wodzichepetsa.”​—SAL. 138:6.

NYIMBO NA. 48 Tiziyenda ndi Yehova Tsiku Lililonse

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova amaona bwanji anthu odzichepetsa? Fotokozani.

YEHOVA amakonda kwambiri anthu odzichepetsa. Ndipo anthu odzichepetsa okha ndi amene angakhale naye pa ubwenzi wolimba. Koma munthu “wodzikuza samuyandikira.” (Sal. 138:6) Tonsefe timafuna kuti tizisangalatsa Yehova komanso kuti iye azitikonda. Choncho tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Munkhaniyi tikambirana mafunso atatu awa: (1) Kodi kudzichepetsa n’kutani? (2) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala odzichepetsa? (3) Kodi tingavutike kukhala odzichepetsa pa nthawi iti? Tiona kuti tikamayesetsa kukhala odzichepetsa timasangalatsa Yehova komanso zimatithandiza ifeyo.​—Miy. 27:11; Yes. 48:17.

KODI KUDZICHEPETSA N’KUTANI?

3. Kodi kudzichepetsa n’kutani?

3 Kudzichepetsa kumatanthauza kukhala ndi mtima wosadzikweza kapena wosanyada. Baibulo limasonyeza kuti munthu wodzichepetsa amakhala ndi maganizo oyenera podziyerekezera ndi Yehova Mulungu komanso anzake. Iye amazindikira kuti munthu aliyense amamuposa m’njira inayake.​—Afil. 2:3, 4.

4-5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti maonekedwe a munthu sangasonyeze ngati alidi wodzichepetsa?

4 Anthu ena amaoneka ngati odzichepetsa chifukwa choti ndi aphee. Apo ayi, amasonyeza ulemu chifukwa cha chikhalidwe chawo kapena mmene makolo awo anawalerera. Koma pansi pa mtima akhoza kukhala anthu odzikuza kwambiri. Ndipo zinthu zina zikachitika khalidwe lawo lenileni limaonekera.​—Luka 6:45.

5 Ndiye pali anthu ena amene amaoneka omasuka kwambiri kapena osadzikayikira koma sikuti amakhala odzikuza. (Yoh. 1:46, 47) Anthu oterewa ayenera kusamala kuti asayambe kudzidalira. Kaya ndife omasuka kapena ayi, tonsefe tiyenera kuyesetsa kukhala ndi mtima wodzichepetsa.

Mtumwi Paulo anali wodzichepetsa ndipo sankadziona kuti ndi wapamwamba (Onani ndime 6) *

6. Malinga ndi 1 Akorinto 15:10, kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha mtumwi Paulo?

6 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Paulo. Yehova anamugwiritsa ntchito kwambiri pokhazikitsa mipingo m’mizinda yosiyanasiyana. N’kutheka kuti iye anachita zambiri mu utumiki kuposa atumwi ena onse a Yesu Khristu. Koma Paulo sankadziona ngati wapamwamba. Iye ananena modzichepetsa kuti: “Ineyo ndine wamng’ono kwambiri mwa atumwi onse, ndipo si ine woyenera kutchedwa mtumwi, chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu.” (1 Akor. 15:9) Iye ananena kuti anali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulunguyo osati chifukwa cha makhalidwe ake kapena ntchito zake. (Werengani 1 Akorinto 15:10.) Kalata ya Paulo yopita kwa Akorinto imasonyeza kuti iye anali wodzichepetsa kwambiri. Izi zimaonekera bwino tikaganizira zoti sankalimbana ndi anthu ena mumpingowo amene ankapikisana naye.​—2 Akor. 10:10.

Karl F. Klein anali m’Bungwe Lolamulira ndipo anali wodzichepetsa (Onani ndime 7)

7. Kodi m’bale wina wodziwika bwino anasonyeza bwanji kudzichepetsa?

7 Anthu a Yehova ambiri akhala akulimbikitsidwa ndi mbiri ya moyo wa M’bale Karl F. Klein, yemwe anatumikira m’Bungwe Lolamulira. Munkhani yakeyo, iye ananena mosabisa zinthu zina zimene analakwitsa komanso mavuto ena amene anakumana nawo. Mwachitsanzo, cha m’ma 1920 iye ankaona kuti ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba ndi yovuta kwambiri moti atangopita kamodzi kokha anakhala zaka ziwiri osapitanso. Nthawi ina ali ku Beteli, anakwiyira m’bale wina chifukwa choti anamupatsa malangizo. Ananenanso kuti pa nthawi ina anadwala matenda amaganizo koma kenako anapeza bwino. Ngakhale zinali choncho, iye anali ndi maudindo osiyanasiyana m’gulu la Yehova. Kunena zoona, panafunika kudzichepetsa kwambiri kuti m’bale wodziwika chonchi aulule mavuto ake komanso zimene analakwitsa. Abale ndi alongo ambiri saiwala M’bale Klein ndi mbiri ya moyo wake yomwe anaifotokoza moona mtima kwambiri. *

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHALA ODZICHEPETSA?

8. Kodi lemba la 1 Petulo 5:6 limasonyeza bwanji kuti Yehova amasangalala ndi anthu odzichepetsa?

8 Chifukwa chachikulu chotichititsa kukhala odzichepetsa n’chakuti Yehova amasangalala ndi khalidweli. Mtumwi Petulo anasonyeza mfundo imeneyi momveka bwino. (Werengani 1 Petulo 5:6.) Pofotokoza zimene Petulo ananena, buku lakuti ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’ limanena kuti: “Kudzikuza kuli ngati poizoni, ndipo kumawononga zinthu kwambiri. Munthu amene ali ndi luso lotha kuchita bwino zinthu zosiyanasiyana angakhale wachabechabe m’maso mwa Mulungu ngati wayamba kudzikuza. Koma munthu wodzichepetsa, ngakhale atakhala wooneka ngati wonyozeka, amakhala wamtengo wapatali kwa Yehova. . . . [Yehovayo] adzasangalala kukupatsani inunso mphoto chifukwa cha kudzichepetsa kwanu.” * Kunena zoona, palibe chinthu china chabwino kuposa kusangalatsa mtima wa Yehova.​—Miy. 23:15.

9. N’chifukwa chiyani anthu amakonda kucheza ndi anthu odzichepetsa?

9 Kuwonjezera pa kusangalatsa Yehova, timadalitsidwa kwambiri tikamayesetsa kukhala odzichepetsa. Tikakhala odzichepetsa anthu ambiri amafuna kukhala anzathu. Inunso muyenera kuti mumasangalala kucheza ndi anthu odzichepetsa. (Mat. 7:12) Ambirife sitisangalala ndi anthu amene nthawi zonse amakakamira maganizo awo ndipo safuna kumva za ena. Koma timasangalala kuchita zinthu ndi abale ndi alongo ‘omvera ena chisoni, okonda abale, achifundo chachikulu ndiponso amaganizo odzichepetsa.’ (1 Pet. 3:8) Popeza timasangalala ndi anthu odzichepetsa, iwonso angasangalale nafe ngati tili odzichepetsa.

10. Kodi kudzichepetsa kumathandiza bwanji kuti tisamavutike kwambiri ndi zinthu?

10 Kudzichepetsa kumathandizanso kuti zinthu zisamatisowetse mtendere. Kunena zoona, anthufe timakumana ndi zinthu zina zimene zimaoneka kuti si zachilungamo. Mwachitsanzo, Solomo yemwe anali mfumu yanzeru ananena kuti: “Ndaonapo antchito atakwera pamahatchi, koma akalonga akuyenda pansi ngati antchito.” (Mlal. 10:7) Nthawi zina anthu aluso kwambiri sayamikiridwa pomwe amene ali ndi luso lochepa ndi amene amalemekezedwa. Koma Solomo ananena kuti ndi nzeru kungovomereza mmene zinthu zilili m’malo molimbana nazo. (Mlal. 6:9) Tikakhala odzichepetsa, sitingavutike kuvomereza mmene zinthu zilili m’malo mokakamira kuti zisinthe.

KODI TINGAVUTIKE KUKHALA ODZICHEPETSA PA NTHAWI ITI?

N’chifukwa chiyani tingavutike kukhala odzichepetsa zinthu ngati zimenezi zikachitika? (Onani ndime 11-12) *

11. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikapatsidwa malangizo?

11 Tsiku lililonse timakumana ndi zinthu zimene zimachititsa kuti tizivutika kudzichepetsa. Tiyeni tikambirane zinthu zingapo. Tikapatsidwa malangizo. Tizikumbukira kuti ngati munthu wafika potipatsa malangizo, ndiye kuti talakwitsa kwambiri kuposa mmene tikuganizira. Mwina poyamba tingaganize kuti sitikufunikira malangizowo. Ndipo tingayambe kupezera zifukwa munthu amene watipatsa malangizowo kapena mmene anawaperekera. Koma ngati ndife odzichepetsa tingayesetse kuona zinthu moyenera.

12. Mogwirizana ndi Miyambo 27:5, 6, n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira ngati munthu watipatsa malangizo? Perekani chitsanzo.

12 Munthu wodzichepetsa amayamikira akapatsidwa malangizo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti muli kumisonkhano. Ndiye mutacheza ndi abale ndi alongo angapo, munthu wina akukutengerani pambali n’kukuuzani kuti kachakudya kenakake katsalira m’mano. N’zosachita kufunsa kuti mungachite manyazi. Koma mungayamikire kuti wakuuzani zimenezo ndipo mwina mukanakonda ngati wina akanakuuzani mwamsanga. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kudzichepetsa n’kumayamikira ngati Mkhristu mnzathu walimba mtima n’kutipatsa malangizo. Tiyenera kuona kuti munthuyo ndi mnzathu osati mdani wathu.​—Werengani Miyambo 27:5, 6; Agal. 4:16.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala odzichepetsa anthu ena akapatsidwa utumiki winawake? (Onani ndime 13-14) *

13. Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa anthu ena akalandira utumiki winawake?

13 Ena akapatsidwa utumiki winawake. Mkulu wina dzina lake Jason ananena kuti: “Ndikaona anthu ena atapatsidwa udindo winawake, nthawi zina ndimadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani sanandipatse ineyo?’” Kodi zoterezi zinakuchitikiraninso inuyo? Si kulakwa ‘kuyesetsa’ kuti muyenerere udindo winawake potumikira Yehova. (1 Tim. 3:1) Koma tiyenera kukhala osamala pa nkhaniyi. Tikapanda kusamala tikhoza kuyamba mtima wodzikuza. Mwachitsanzo, m’bale angayambe kuganiza kuti iye ndi amene ali woyenera kwambiri kupatsidwa ntchito inayake. Apo ayi, mlongo angaganize kuti mwamuna wake angachite bwino zinthu zina kuposa abale ena. Koma ngati ndifedi odzichepetsa tidzapewa mtima wodzikuza umenewu.

14. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mose anachita anthu ena atapatsidwa udindo?

14 Tingachite bwino kutsanzira zimene Mose anachita anthu ena atalandira udindo. Iye ankaona kuti ntchito yake yotsogolera Aisiraeli inali yamtengo wapatali. Koma kodi Mose anatani Yehova atalola anthu ena kuti azigwira naye ntchito? Iye sanachite nsanje. (Num. 11:24-29) Mose anali wodzichepetsa ndipo analola kuti anthu ena azimuthandiza pa ntchito yoweruza Aisiraeli. (Eks. 18:13-24) Chifukwa cha zimenezi, Aisiraeli ankatha kuthandizidwa mofulumira kuposa kale. Choncho Mose ankaika zofuna za ena pamalo oyamba osati kuganizira kwambiri za udindo wake. Chitsanzo chimenechi ndi chabwino kwambiri kwa ife. Kuti Yehova azitigwiritsa ntchito, chofunika kwambiri ndi kukhala odzichepetsa osati kukhala ndi luso linalake. Ngakhale kuti “Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa.”​—Sal. 138:6.

15. Kodi zinthu zinasintha bwanji pa moyo wa abale ndi alongo ena?

15 Zinthu zikasintha pa moyo wathu. Pa zaka zaposachedwapa, utumiki wa abale ndi alongo ambiri amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali unasintha. Mwachitsanzo, mu 2014 oyang’anira chigawo ndi akazi awo anauzidwa kuti ayambe utumiki wina wa nthawi zonse. Kungoyambira chaka chimenecho, oyang’anira madera amafunika kusiya utumiki wawo akakwanitsa zaka 70. Komanso abale amene akwanitsa zaka 80 sangapitirize kukhala ogwirizanitsa ntchito za akulu. Kuwonjezera pamenepa, anthu ambiri amene ankatumikira pa Beteli anapemphedwa kuti akachite upainiya. Ndiye palinso anthu ena amene anayenera kusiya utumiki wawo chifukwa cha matenda, udindo wina wa m’banja kapena mavuto ena.

16. Kodi abale ndi alongo ena asonyeza bwanji kudzichepetsa utumiki wawo utasintha?

16 Ambiri mwa abale ndi alongowa anavutika moyo wawo utasintha. N’zosakayikitsa kuti ankakonda utumiki wawo ndipo mwina anali atauchita kwa zaka zambiri. Ena anadandaula kwambiri ndipo zinawatengera nthawi kuti azolowere utumiki watsopano. Koma kenako anazolowera. Chimene chinawathandiza kwambiri ndi kukonda Yehova. Iwo ankadziwa kuti anadzipereka kwa Mulungu osati ku ntchito kapena udindo winawake. (Akol. 3:23) Abale ndi alongowa amasangalala kutumikira Yehova modzichepetsa m’njira iliyonse imene angathe. Iwo ‘amamutulira nkhawa zawo zonse, podziwa kuti amawadera nkhawa.’​—1 Pet. 5:6, 7.

17. N’chifukwa chiyani timayamikira kuti Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala odzichepetsa?

17 Timayamikira kwambiri kuti Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tikhale odzichepetsa. Tikamayesetsa kukhala odzichepetsa zimathandiza ifeyo komanso anthu ena. Zimatithandiza kuti tisamavutike kupirira mavuto. Koma kuposa zonse, zimatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba. Timasangalala kudziwa kuti ngakhale kuti Yehova ndi “Wapamwamba ndi Wokwezeka” amakonda atumiki ake odzichepetsa ndipo amawaona kuti ndi amtengo wapatali.​—Yes. 57:15.

NYIMBO NA. 45 Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

^ ndime 5 Khalidwe lina lofunika limene tiyenera kukhala nalo ndi kudzichepetsa. Kodi kudzichepetsa n’kutani? N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala odzichepetsa? Nanga n’chifukwa chiyani tingavutike kukhala odzichepetsa zinthu zikasintha pa moyo wathu? Munkhaniyi tikambirana mafunso amenewa.

^ ndime 7 Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya October 1, 1984 pamutu wakuti “Jehovah Has Dealt Rewardingly With Me.”

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mtumwi Paulo ali kunyumba kwa m’bale wina ndipo akusonyeza kudzichepetsa pocheza ndi anthu ena, ngakhale ana.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale wina akulandira malangizo ochokera m’Baibulo amene m’bale wachinyamata akumupatsa.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale wachikulire sakuchitira nsanje m’bale wachinyamata amene ali ndi udindo winawake mumpingo.