NKHANI YOPHUNZIRA 14
Kodi Mukukwaniritsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?
“Gwira ntchito ya mlaliki, ndipo ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.”—2 TIM. 4:5.
NYIMBO NA. 57 Tizilalikira kwa Anthu a Mitundu Yonse
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi tonsefe timafunika kugwira ntchito iti, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuigwira? (Onani chithunzi patsamba loyamba.)
KHRISTU YESU analamula otsatira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.” (Mat. 28:19) Choncho mtumiki wa Mulungu aliyense wokhulupirika amafuna kudziwa zimene angachite kuti ‘akwaniritse’ utumiki umene wapatsidwa. (2 Tim. 4:5) Ndipotu ntchito imene tapatsidwa ndi yothandiza kwambiri komanso yofunika kugwiridwa mwamsanga kuposa ntchito ina iliyonse. Koma nthawi zina sizitheka kupeza nthawi yokwanira yoti tigwire ntchitoyi mmene timafunira.
2. Kodi ndi mavuto ati amene timakumana nawo?
2 Anthufe timakhala ndi zinthu zina zofunika zimene timayenera kuchita. Mwachitsanzo, ena amafunika kugwira ntchito maola ambiri kuti apeze zofunika pa moyo wawo kapena wa banja lawo. M’banja lathu mukhoza kukhalanso anthu amene akukumana ndi mavuto monga matenda, kuvutika maganizo kapena ukalamba. Ndiye kodi tingatani kuti tizikwaniritsa utumiki wathu ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto ngati amenewa?
3. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu a pa Mateyu 13:23?
3 Sitiyenera kudziimba mlandu ngati mavuto ena amachititsa kuti tizingopeza nthawi yochepa yochitira utumiki. Ngakhale Yesu ankadziwa kuti anthufe sitingachite zinthu mofanana. (Werengani Mateyu 13:23.) Yehova amayamikira kwambiri zimene timachita pomutumikira ngati tikuyesetsa kuchita zonse zimene tingathe. (Aheb. 6:10-12) Koma mwina timaona kuti tikhoza kuchita zambiri kuposa zimene tikuchita panopa. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tiziika utumiki pamalo oyamba, tizikhala moyo wosalira zambiri komanso tiziwonjezera luso lathu polalikira ndi kuphunzitsa anthu. Koma choyamba, tiyeni tikambirane tanthauzo la kukwaniritsa mbali zonse za utumiki wathu.
4. Kodi kukwaniritsa utumiki wathu kumatanthauza chiyani?
4 Mwachidule, mawu oti kukwaniritsa utumiki wathu amatanthauza kuchita zonse zimene tingathe pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Koma chofunika si kungopeza nthawi yambiri yogwira ntchitoyi. Yehova amaona kuti cholinga chathu chogwirira ntchitoyo n’chofunikanso. Akhristufe timachita utumiki * wathu chifukwa chokonda Yehova ndi anzathu. (Maliko 12:30, 31; Akol. 3:23) Kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse kumatanthauza kugwiritsa ntchito mphamvu ndi luso lathu modzipereka pomutumikira. Munthu akamaona kuti ntchito yolalikira ndi yamtengo wapatali, amayesetsa kulalikira kwa anthu ambiri.
5-6. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti munthu akhoza kuika pamalo oyamba ntchito yolalikira ngakhale kuti sapeza nthawi yambiri.
5 Kuti timvetse nkhaniyi, tiyeni tiganizire za munthu amene amadziwa kuimba gitala ndipo amaikonda kwambiri. Kenako munthuyo akulembedwa ntchito yoti aziimba gitalayo Loweruka ndi Lamlungu pamalo ena. Koma ndalama zimene amalandira n’zosakwanira kuti azipeza zofunika pa moyo wake. Ndiye akupezanso ntchito ina yogulitsa musitolo kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu. Ngakhale kuti nthawi yambiri amakhala ali musitolo, chimene amakonda kwambiri ndi kuimba. Akufunitsitsa kukulitsa luso loimba n’cholinga choti m’tsogolo ntchito yake idzangokhala yoimba basi. Ngati ndi choncho, akhoza kumayesetsa kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti aziimba gitalayo.
6 Mofanana ndi munthu woimbayu, timakonda kwambiri ntchito yolalikira koma mwina nthawi imene timapeza kuti tiigwire imakhala
yochepa. Timayesetsa kukulitsa luso lathu n’cholinga choti tiziwafika anthu pamtima ndi uthenga wabwino. Popeza timatanganidwa kwambiri, mwina tingamadzifunse kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ntchito yolalikira izikhala pamalo oyamba?’KODI MUNGATANI KUTI MUZIIKA UTUMIKI PAMALO OYAMBA?
7-8. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pochita utumiki wathu?
7 Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Ntchito yofunika kwambiri pa moyo wake inali youza anthu za Ufumu wa Mulungu. (Yoh. 4:34, 35) Iye ankayenda mitunda italiitali kuti akalalikire kwa anthu ambiri. Ankagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti alalikire kwa anthu m’nyumba zawo komanso m’malo opezeka anthu ambiri. Mwachidule tingati utumiki unali wofunika kwambiri pa moyo wa Yesu.
8 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu? Tiyenera kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti tiuze anthu uthenga wabwino. Tiyenera kuchita zimenezi ngakhale pa nthawi yomwe zinthu sizili bwino kwenikweni pa moyo wathu. (Maliko 6:31-34; 1 Pet. 2:21) Abale ndi alongo ena amatha kuchita upainiya wapadera, wokhazikika kapena wothandiza. Ena amaphunzira chinenero china kapena kusamukira kudera limene kukufunika anthu ambiri olalikira. Ngakhale zili choncho, ntchito yaikulu yolalikira imagwiridwa ndi ofalitsa akhama amene amachita zonse zimene angathe potumikira Mulungu. Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tizikumbukira kuti Yehova satipempha kuchita zinthu zimene sitingathe. Iye amafuna kuti tonsefe tizimutumikira mosangalala pamene tikulengeza ‘uthenga wabwino waulemerero wochokera kwa Mulungu wachimwemwe.’—1 Tim. 1:11; Deut. 30:11.
9. (a) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankaika ntchito yolalikira patsogolo ngakhale kuti ankagwira ntchito ina? (b) Kodi lemba la Machitidwe 28:16, 30, 31 limasonyeza kuti Paulo ankaona bwanji utumiki wake?
9 Nayenso mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino poika utumiki pamalo oyamba. Pamene anafika ku Korinto pa ulendo wake wachiwiri waumishonale, ndalama zinamuthera ndipo anafunika kugwira ntchito yokonza matenti. Koma sikuti iye ankaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri. Iye ankagwira ntchitoyi n’cholinga choti azipeza zofunika uku akuchita utumiki. Paulo sankafuna kuti Akhristu a ku Korinto ataye ndalama zawo pomusamalira. (2 Akor. 11:7) Ngakhale kuti Paulo ankafunika kugwira ntchito ina, iye ankaonabe kuti utumiki ndi wofunika kwambiri moti ankalalikira pa tsiku la Sabata lililonse. Zinthu zitasintha pa moyo wake, Paulo anatha kuchita zambiri mu utumiki kuposa kale. Iye “anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu. Iye anali kuchitira umboni kwa Ayuda ndi kuwatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.” (Mac. 18:3-5; 2 Akor. 11:9) Patapita nthawi, Paulo anamangidwa ku Roma kwa zaka ziwiri, koma ankalalikira anthu amene ankabwera kudzamuona komanso ankalemba makalata. (Werengani Machitidwe 28:16, 30, 31.) Paulo ankaonetsetsa kuti china chilichonse chisasokoneze utumiki wake. Iye analemba kuti: “Popeza tili ndi utumiki umenewu . . . , sitikubwerera m’mbuyo.” (2 Akor. 4:1) Mofanana ndi Paulo, n’zotheka kuika utumiki pamalo oyamba ngakhale kuti tili pa ntchito ina.
10-11. Kodi tingakwaniritse bwanji utumiki wathu ngakhale pamene tikuvutika ndi matenda kapena ukalamba?
10 Ngati tikuvutika ndi matenda kapena ukalamba moti sitingathe kulalikira kunyumba ndi nyumba, tikhoza kumalalikira m’njira zina. Akhristu oyambirira ankalalikira paliponse pamene papezeka anthu. Iwo ankalalikira kunyumba ndi nyumba, m’malo opezeka anthu Mac. 17:17; 20:20) Ngati nafenso sitingathe kuyenda kwambiri, tikhoza kungokhala pamalo opezeka anthu ambiri n’kumalalikira kwa anthu odutsa. Apo ayi, tikhoza kumangolalikira mwamwayi, kulemba makalata kapena kulalikira pa foni. Abale ndi alongo ambiri amene sangachite zambiri mu utumiki chifukwa cha mavuto awo, amasangalala kulalikira pogwiritsa ntchito njira ngati zimenezi.
ambiri komanso paliponse pamene mpata wapezeka. (11 Kaya mukudwala kapena ndinu okalamba, mukhoza kukwaniritsa utumiki wanu. Taganiziraninso chitsanzo cha Paulo. Iye ananena kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Paulo anafunika mphamvu zimenezi atadwala pa ulendo wina waumishonale. Iye anauza Akhristu a ku Galatiya kuti: ‘Mukudziwa kuti nthawi yoyamba ndinalengeza uthenga wabwino kwa inu chifukwa chakuti ndinali kudwala.’ (Agal. 4:13) Ifenso tikadwala tikhoza kulalikira uthenga wabwino kwa madokotala, manesi komanso anthu ena amene akutithandiza. Ambiri mwa anthu amenewa salalikiridwa kunyumba zawo chifukwa choti amakhala ali kuntchito.
ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUKHALE NDI MOYO WOSALIRA ZAMBIRI
12. Kodi kukhala ndi ‘diso lolunjika pa chinthu chimodzi’ kumatanthauza chiyani?
12 Yesu ananena kuti: “Nyale ya thupi ndi diso. Chotero ngati diso lako lili lolunjika pa chinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala.” (Mat. 6:22) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Ankatanthauza kuti tiyenera kukhala ndi moyo wosalira zambiri, wokhala ndi cholinga chimodzi ndipo tisamalole kusokonezedwa. Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yoika utumiki pamalo oyamba ndipo anauza ophunzira ake kuti maganizo awo onse azikhala pa utumiki komanso Ufumu wa Yehova. Tiyenera kutsanzira Yesu poika utumiki pamalo oyamba komanso “kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo” cha Mulungu.—Mat. 6:33.
13. N’chiyani chingatithandize kuti tiziika utumiki pamalo oyamba?
13 Njira imodzi imene ingatithandize kuti tiziika utumiki pamalo oyamba ndi kukhala moyo wosalira zambiri. * Izi zimathandiza kuti tizikhala ndi nthawi yambiri yothandiza anthu kudziwa Yehova komanso kumukonda. Mwachitsanzo, kodi tingachepetse nthawi imene timagwira ntchito zina n’cholinga choti tizikhala ndi nthawi yambiri yolalikira mkati mwa mlungu? Nanga tingapewe zosangalatsa zina zomwe zimatiwonongera nthawi yambiri?
14. Kodi banja lina linachita zotani kuti lizipeza nthawi yambiri yolalikira?
14 M’bale wina dzina lake Elias ndi mkazi wake anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. M’baleyu ndi mkulu ndipo anati: “Sitikanatha kuyamba upainiya nthawi imene tinaganiza zoika utumiki pamalo oyamba koma tinaona kuti pali zina zimene tingachite. Choncho tinayamba pang’onopang’ono kuwonjezera nthawi imene tinkalalikira. Mwachitsanzo, tinachepetsa zinthu zimene tinkagula. Tinasiyanso kuchita zosangalatsa zina zimene zinkatiwonongera nthawi. Komanso tinapempha mabwana athu kuti tizigwira ntchito nthawi yochepa n’cholinga choti tizilalikira. Izi zinathandiza kuti tizilalikira madzulo, tizichititsa maphunziro ambiri komanso tizilalikira nawo mkati mwa mlungu kawiri pa mwezi. Tinasangalala kwambiri kuchita zimenezi.”
KODI MUNGATANI KUTI MUWONJEZERE LUSO LOLALIKIRA KOMANSO KUPHUNZITSA?
15-16. Malinga ndi lemba la 1 Timoteyo 4:13, 15, kodi tingawonjezere bwanji luso lathu? (Onani bokosi lakuti “ Zolinga Zimene Zingandithandize Kukwaniritsa Utumiki Wanga.”)
15 Kuwonjezera luso lathu pa ntchito yolalikira kumathandizanso kuti tizikwaniritsa utumiki wathu. M’dzikoli, anthu amene amagwira ntchito zosiyanasiyana amaphunzitsidwabe zina ndi zina kuti awonjezere luso lawo pa ntchitoyo. Ndi mmene zililinso ndi ntchito yolalikira. Tiyenera kuphunzira kuti tiwonjezere luso lathu mu utumiki.—Miy. 1:5; werengani 1 Timoteyo 4:13, 15.
16 Koma kodi tingawonjezere bwanji luso lathu? Tiyenera kumvetsera mwatcheru malangizo amene timalandira mlungu uliwonse pa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu. Zimene timaphunzira pa msonkhano umenewu zingatithandize kwambiri kuti tiwonjezere luso lathu polalikira. Mwachitsanzo, tcheyamani akapereka malangizo kwa anthu amene apatsidwa nkhani timaphunzirapo zimene tingachite kuti tiziphunzitsa bwino. Ndiyeno tikakhala mu utumiki tiyenera kugwiritsa ntchito zimene taphunzirazo. Njira ina yothandiza ndi kupempha woyang’anira kagulu kathu kuti atithandize kapena tiyende naye mu utumiki. Apo ayi, tikhoza kupempha thandizoli kwa wofalitsa waluso, mpainiya kapena woyang’anira dera. Tikamawonjezera luso lathu pogwiritsa ntchito Zinthu Zophunzitsira, utumiki umakhala wosangalatsa kwambiri.
17. Kodi chingachitike n’chiyani tikamayesetsa kukwaniritsa utumiki wathu?
17 Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kukhala “antchito anzake” a Yehova. (1 Akor. 3:9) Tikamayesetsa ‘kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti’ komanso kuika utumiki pamalo oyamba, utumiki wathu udzakhala wosangalatsa kwambiri. (Afil. 1:10; Sal. 100:2) Kaya mavuto anu ndi aakulu bwanji, simuyenera kukayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova adzakupatsani mphamvu kuti mukwaniritse utumiki wanu. (2 Akor. 4:1, 7; 6:4) Tikamachita zonse zimene tingathe potumikira Mulungu, ngakhale zitakhala zochepa, tikhoza ‘kukhala ndi zifukwa zosangalalira.’ (Agal. 6:4) Tikamakwaniritsa utumiki wathu timasonyeza kuti timakonda Yehova komanso anzathu. Ndipo tikamachita zimenezi ‘tidzadzipulumutsa tokha komanso anthu otimvera.’—1 Tim. 4:16.
NYIMBO NA. 58 Kufufuza Anthu Okonda Mtendere
^ ndime 5 Akhristufe tapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu komanso kuphunzitsa anthu. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tikwaniritse mbali zonse za utumiki wathu ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto. Tikambirananso zimene tingachite kuti tizilalikira mogwira mtima komanso mosangalala.
^ ndime 4 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Utumiki wathu umaphatikizapo zinthu monga kulalikira, kuphunzitsa, ntchito zomangamanga, kukonza malo olambirira komanso kuthandiza anthu amene akumana ndi ngozi zadzidzidzi.—2 Akor. 5:18, 19; 8:4.
^ ndime 13 Onani mfundo 7 zimene zili m’bokosi lakuti “Zimene Mungachite Kuti Muzikhala Moyo Wosalira Zambiri” mu Nsanja ya Olonda ya July 2016, tsamba 10.
^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo akuchita chitsanzo cha ulendo wobwereza pamisonkhano. Pambuyo pake, tcheyamani akumupatsa malangizo ndipo mlongoyo akulemba malangizowo m’kabuku kakuti Kuphunzitsa. Kumapeto kwa mlungu, mlongoyu ali mu utumiki ndipo akugwiritsa ntchito zimene anaphunzira kumisonkhano.