NKHANI YOPHUNZIRA 33
Muzisangalala ndi Utumiki Wanu
“Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.”—MLAL. 6:9.
NYIMBO NA. 111 Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi anthu ambiri akuchita chiyani potumikira Yehova?
TILI ndi ntchito yambiri yoti tigwire pamene mapeto a dzikoli akuyandikira. (Mat. 24:14; Luka 10:2; 1 Pet. 5:2) Tonsefe timafunitsitsa kutumikira Yehova mmene tingathere. Ambiri akuwonjezera utumiki wawo. Ena amafuna atachita upainiya ndipo enanso amafuna kutumikira pa Beteli kapena kuchita utumiki wa zomangamanga. Komanso abale ambiri akuyesetsa kuti azitumikira monga atumiki othandiza kapena akulu. (1 Tim. 3:1, 8) Yehova amasangalala poona zimene atumiki ake akuyesetsa kuchita pomutumikira.—Sal. 110:3; Yes. 6:8.
2. Kodi tingamve bwanji chifukwa choona kuti zolinga zathu zina sizikukwaniritsidwa?
2 Mwina tikhoza kukhumudwa ngati titaona kuti padutsa nthawi yaitali tisanakwaniritse zolinga zathu zauzimu. Tikhozanso kufooka poona kuti sitingathe kuchita mautumiki ena chifukwa cha msinkhu wathu kapenanso mmene zinthu zilili pa moyo wathu. (Miy. 13:12) Zimenezi ndi zimene zinachitikira Melissa. * Iye ankafuna atatumikira pa Beteli kapena kukalowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu koma ananena kuti: “Panopa zimenezi sizingatheke chifukwa cha msinkhu wanga, moti nthawi zina ndimakhumudwa.”
3. Kodi ndi zinthu ziti zimene ena ayenera kuchita kuti ayenerere kupatsidwa mautumiki osiyanasiyana.
3 Ena akhoza kukhala achinyamata komanso athanzi. Komabe kuti apatsidwe maudindo ena owonjezereka ayenera kukulitsa komanso kusonyeza makhalidwe ena ofunika. Iwo akhoza kukhala anzeru, otsimikiza ndiponso ofunitsitsa kuchita zinthu, komabe
angafunike kuphunzira kukhala oleza mtima, adongosolo komanso aulemu. Mukamachita khama kukulitsa makhalidwe ofunikawa, mungathe kupatsidwa mwayi wautumiki winawake pa nthawi imene simukuyembekezera. Taganizirani zimene zinachitikira Nick. Ali ndi zaka 20, iye anakhumudwa kwambiri chifukwa choona kuti sanaikidwe kukhala mtumiki wothandiza. Iye anati: “Ndinkaona ngati pali zinazake zimene ndikulakwitsa.” Komabe Nick sanataye mtima. M’malomwake, iye ankachita khama kugwira ntchito zina zampingo komanso kulalikira. Panopa Nick akutumikira m’Komiti ya Nthambi.4. Kodi tikambirana mfundo ziti munkhaniyi?
4 Kodi inuyo ndinu wokhumudwa chifukwa chakuti simukukwaniritsa cholinga chinachake chauzimu? Ngati ndi choncho, muzifotokozera Yehova m’pemphero mmene mukumvera. (Sal. 37:5-7) Komanso muzipempha abale amene ndi olimba mwauzimu kuti akupatseni malangizo amene angakuthandizeni kuti muzichita bwino zinthu potumikira Mulungu, ndipo muziyesetsa kugwiritsa ntchito malangizo amene akupatsaniwo. Mukamachita zimenezi mungathe kupatsidwa utumiki umene mukufuna kapena kukwaniritsa cholinga chanu. Koma mofanana ndi Melissa yemwe tamutchula kale uja, n’kutheka kuti panopa sizingatheke kuti muchite utumiki umene mukufuna. Zikatere kodi mungatani kuti muzikhalabe osangalala? Kuti tiyankhe funso limeneli, munkhaniyi tikambirana (1) zimene zingatithandize kukhala osangalala, (2) zimene tingachite kuti tizisangalala kwambiri komanso (3) zolinga zimene tingakhale nazo zomwe zingatithandize kuwonjezera chimwemwe chathu.
ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUKHALA OSANGALALA
5. Kodi tiyenera kumaganizira kwambiri chiyani kuti tikhale osangalala? (Mlaliki 6:9)
5 Lemba la Mlaliki 6:9, limafotokoza zimene zingatithandize kukhala osangalala. (Werengani.) Munthu amene amasangalala ndi zimene ‘waona ndi maso ake,’ amayamikira zimene ali nazo ndipo amakhala wokhutira ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake. Koma mosiyana ndi zimenezi, munthu amene amalakalaka ndi mtima wake, amafunitsitsa kukhala ndi zinthu zimene sangathe kuzipeza. Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Kuti tizisangalala, tiziganizira kwambiri zimene tili nazo komanso tizikhala ndi zolinga zimene tingazikwaniritse.
6. Kodi tsopano tikambirana fanizo liti, nanga tiphunzira chiyani mufanizoli?
6 Mwachibadwa, anthufe timafuna kuchita zinthu zina zatsopano. Ndiye kodi n’zothekadi kumakhutira ndi zimene tili nazo? Inde n’zotheka. Tikhoza kumasangalala ndi zinthu zimene tili nazo panopa, zimene ‘tikuona ndi maso’ athu. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Kuti tipeze yankho, tiyeni tione zimene Yesu ananena mufanizo lake la matalente, lomwe lili pa Mateyu 25:14-30. Tikambirana kwambiri mmene fanizoli lingatithandizire kuti tizisangalala komanso zimene tingachite kuti tiwonjezere chimwemwe chathucho mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu.
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZISANGALALA KWAMBIRI
7. Fotokozani mwachidule fanizo la Yesu lonena za matalente.
7 Mufanizo lina, Yesu anatchula za munthu amene ankafuna kupita kudziko lina. Asananyamuke, iye anaitana akapolo ake n’kuwapatsa matalente kuti achite nawo malonda. * Poganizira zimene kapolo aliyense angakwanitse, munthuyo anapereka matalente 5 kwa kapolo woyamba, matalente awiri kwa kapolo wina ndipo wachitatu anam’patsa talente imodzi. Akapolo awiri oyambawo, anagwiritsa ntchito bwino matalente amene anapatsidwa. Koma kapolo wachitatu uja sanachite chilichonse ndi talente imene anapatsidwa, ndipo mbuye wake anamuchotsa ntchito.
8. Kodi n’chiyani chikanachititsa kuti kapolo woyamba uja asangalale?
8 Kapolo woyambayo ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona kuti mbuye wake wamupatsa matalente 5. Imeneyitu inali ndalama yambiri ndipo izi zikusonyeza kuti mbuye wake ankamukhulupirira kwambiri. Koma nanga bwanji kapolo wachiwiri uja. Iye akanatha kukhumudwa chifukwa chakuti sanalandire matalente ambiri ngati kapolo woyamba uja. Ndiye kodi iye anatani?
9. Kodi Yesu sananene kuti kapolo wachiwiriyu anachita zinthu ziti? (Mateyu 25:22, 23)
9 Werengani Mateyu 25:22, 23. Yesu sananene kuti kapolo wachiwiriyo anakhumudwa kapena kukwiya chifukwa chakuti analandira matalente awiri okha. Iye sananene kuti kapoloyo anayamba kudandaula n’kumanena kuti: ‘Ndangopatsidwa zomwezi basi? Inenso ndimagwira ntchito mwakhama ngati kapolo walandira matalente 5 uja. Ngati mbuye wanga sayamikira zimene ndimachita, kuli bwino inenso ndikangokwirira matalentewa n’kumachita zofuna zanga.’
10. Kodi kapolo wachiwiri anatani ndi matalente amene anapatsidwa?
10 Mofanana ndi kapolo woyambayo, kapolo wachiwiri anaona kuti wapatsidwa udindo wofunika kwambiri ndipo anachita khama kutumikira mbuye wake. Iye anawonjezera matalente ena awiri pa matalente amene mbuye wake anamupatsa. Kapoloyu anapatsidwa mphoto chifukwa cha khama komanso luso lake. Kuwonjezera pa kusangalala ndi zimene anachita, mbuye wake anamuwonjezeranso zochita zina.
11. Kodi tingatani kuti tizisangalala kwambiri?
Mac. 18:5; Aheb. 10:24, 25) Muzikonzekera bwino misonkhano n’cholinga choti muzikapereka ndemanga zolimbikitsa. Muzikonzekeranso bwino mukapatsidwa nkhani za ophunzira pamisonkhano ya mkati mwa mlungu. Mukapemphedwa kuti mugwire ntchito inayake mumpingo, muzisunga nthawi komanso muzikhala odalirika. Musamaone kuti zimene mwapemphedwa n’zosafunika kapena kungotaya nthawi. Muziyesetsa kuwonjezera luso lanu. (Miy. 22:29) Mukamadzipereka kwambiri pa utumiki wanu, m’pamenenso mumapita patsogolo mofulumira ndipo mumasangalala. (Agal. 6:4) Zimenezi zingakuthandizeninso kuti muzisangalala ndi ena akapatsidwa utumiki umene inuyo mumaulakalaka.—Aroma 12:15; Agal. 5:26.
11 Mofanana ndi zimenezi, ifenso tingamasangalale kwambiri ngati titakhala akhama pa chilichonse chimene timachita potumikira Yehova. Nthawi zonse ‘tizitanganidwa kwambiri’ ndi ntchito yolalikira ndipo tizidzipereka ndi mtima wonse pogwira ntchito zamumpingo. (12. Kodi n’chiyani chimene a Mboni ena awiri anachita kuti awonjezere chimwemwe chawo?
12 Kodi mwamukumbukira Melissa, mlongo amene ankalakalaka atakatumikira pa Beteli kapena kulowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? Ngakhale kuti sizinatheke kuchita mautumiki amenewa, iye ananena kuti: “Ndimayesetsa kuchita zonse zomwe ndingathe pa utumiki wanga waupainiya komanso kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira. Zimenezi zandithandiza kuti ndizisangalala kwambiri.” Nanga kodi n’chiyani chinathandiza Nick kuti asapitirize kukhala wokhumudwa pa nthawi imene sanaikidwe kukhala mtumiki wothandiza? Iye ananena kuti: “Ndinkaganizira kwambiri mautumiki amene ndikanatha kuchita monga kulalikira komanso kupereka ndemanga zogwira mtima pamisonkhano. Ndinafunsiranso utumiki wa pa Beteli ndipo chaka chotsatira ndinaitanidwa.”
13. Kodi n’chiyani chingachitike ngati titamachita khama pa utumiki umene tikuchita panopa? (Mlaliki 2:24)
13 Ngati mutamachita khama pa utumiki umene mukuchita panopa, kodi mungadzapatsidwe maudindo ena akuluakulu m’tsogolo? Inde n’zotheka, ngati mmene zinakhalira ndi Nick. Koma ngati sizingatheke ngati mmene zinalili ndi Melissa, mukhoza kukhalabe osangalala ndi zimene mukukwanitsa kuchita potumikira Yehova. (Werengani Mlaliki 2:24.) Kuwonjezera pamenepo, n’zosakayikitsa kuti mukhoza kumakhala osangalala podziwa kuti zimene mukuchita zikusangalatsa Mbuye wathu, Yesu Khristu.
ZOLINGA ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUWONJEZERA CHIMWEMWE CHATHU
14. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamadziikira zolinga zimene tikufuna kukwaniritsa?
14 Kodi kukhala wokhutira ndi utumiki umene tikuchita panopa kukutanthauza kuti sitiyenera kuganizira njira zina zowonjezera utumiki wathu kwa Yehova? Ayi si choncho. Tingathe kuchita zambiri ndipo tikhoza kudziikira zolinga zimene zingathandize kuti tizilalikira mwaluso komanso tizithandiza abale ndi alongo athu. Tingakwaniritse zolinga zimenezi tikamachita zinthu mwanzeru komanso modzichepetsa pothandiza ena m’malo momangoganizira zofuna zathu.—Miy. 11:2; Mac. 20:35.
15. Kodi ndi zolinga zina ziti zimene zingakuthandizeni kuwonjezera chimwemwe chanu?
15 Kodi ndi zolinga ziti zimene mungadziikire? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kudziwa zolinga zimene mungazikwaniritse. (Miy. 16:3; Yak. 1:5) Kodi n’zotheka kuti mukhale ndi zolinga zimene zatchulidwa mundime yoyamba munkhaniyi, monga kuchita upainiya wothandiza, kapena wokhazikika, kutumikira pa Beteli kapenanso kuchita nawo utumiki wa zomangamanga? Mukhozanso kuphunzira chinenero china n’cholinga choti muzilalikira uthenga wabwino m’gawo limene amalankhula chinenerocho. Mungadziwe zambiri powerenga mutu 10 m’buku Lochita Chifuniro cha Yehova komanso pokambirana ndi akulu a mumpingo mwanu. lakuti Gulu * Mukamayesetsa kukwaniritsa zolinga zanu, kupita kwanu patsogolo kudzaonekera ndipo mudzawonjezera chimwemwe chanu.
16. Kodi mungatani ngati panopa simungathe kukwaniritsa cholinga chinachake?
16 Koma bwanji ngati n’zosatheka kuti mukwaniritse zolinga zimene zatchulidwazi? Mungachite bwino kudziikira cholinga china chimene mungathe kuchikwaniritsa. Taganizirani zolinga zotsatirazi.
17. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 4:13, 15, kodi m’bale angatani kuti aziphunzitsa mwaluso?
17 Werengani 1 Timoteyo 4:13, 15. Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, mungamachite khama kuti muwonjezere luso lanu lokamba nkhani komanso kuphunzitsa. Chifukwa chiyani? Chifukwa ‘kudzipereka’ kwanu pa kuwerenga, luso lakulankhula komanso kuphunzitsa kungathandize kwambiri anthu okumvetserani. Mukhozanso kudziikira cholinga chakuti muziphunzira komanso kugwiritsa ntchito mfundo zamuphunziro lililonse m’kabuku kakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso. Muziyesa kuphunzira luso limodzi n’kuliyeserera muli kunyumba komanso kugwiritsa ntchito mfundo zake mukamakamba nkhani. Muzipemphanso malangizo kwa mlangizi wothandiza kapena akulu ena omwe “amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” * (1 Tim. 5:17) Mukamakulitsa luso lomwe mwaphunzira mu phunziro linalake, muzithandizanso omvetsera anu kulimbitsa chikhulupiriro chawo kapenanso kuwalimbikitsa kuti azigwiritsa ntchito zimene aphunzira. Mukamachita zimenezi mudzawonjezera chimwemwe chanu komanso chawo.
18. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikwaniritse cholinga chathu pa ntchito yolalikira?
Mat. 28:19, 20; Aroma 10:14) Kodi mukufuna kuwonjezera luso lanu pa ntchito yofunika kwambiri imeneyi? Mukamaphunzira mfundo za m’kabuku ka Kuphunzitsa, muzidziikira zolinga zoti mugwiritse ntchito zimene mwaphunzirazo. Mungapezenso malangizo ena othandiza mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndiponso mavidiyo a zitsanzo za ulaliki omwe amaonetsedwa pamisonkhano ya mkati mwa mlungu. Muziyeserera njira zosiyanasiyana n’kuona imene ili yabwino kwambiri kwa inu. Mukamatsatira malangizo amenewa, mudzakhala mphunzitsi waluso ndipo zimenezi zidzathandiza kuti muzisangalala kwambiri.—2 Tim. 4:5.
18 Tonsefe tinapatsidwa ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa. (19. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzikulitsa makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo?
19 Mukamaganizira zolinga zimene mukufuna kukhala nazo, musamanyalanyaze chinthu chofunika kwambiri chomwe ndi kukulitsa makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo. (Agal. 5:22, 23; Akol. 3:12; 2 Pet. 1:5-8) Kodi mungatani kuti mukhale ndi makhalidwe amenewa? Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukufuna mutakhala ndi chikhulupiriro cholimba. Muyenera kuwerenga m’mabuku athu nkhani zimene zili ndi malangizo amene angakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Mukhozanso kupindula kwambiri ndi mavidiyo a JW Broadcasting® onena za abale ndi alongo ena omwe anasonyeza chikhulupiriro polimbana ndi mayesero osiyanasiyana amene anakumana nawo. Kenako muziganizira njira zimene mungatsanzirire chikhulupiriro chawo pa moyo wanu.
20. Kodi tingatani kuti tiwonjezere chimwemwe chathu ndipo tisamakhumudwe kwambiri?
20 Mosakayikira, tonsefe timafuna titachita zambiri potumikira Yehova. M’dziko latsopano, tidzakhala ndi mwayi waukulu womutumikira mmene tingathere. Koma panopa tikamagwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene wapezeka, tikhoza kuwonjezera chimwemwe chathu ndipo sitingamadandaule kwambiri. Tikamachita zimenezi, tikhoza kulemekeza komanso kutamanda Yehova, ‘Mulungu wathu wachimwemwe.’ (1 Tim. 1:11) Choncho tiyeni tizisangalala ndi zimene tikukwanitsa kuchita potumikira Yehova panopa.
NYIMBO NA. 82 “Onetsani Kuwala Kwanu”
^ ndime 5 Timakonda kwambiri Yehova ndipo timafuna kuchita zonse zomwe tingathe pomutumikira. Chifukwa cha zimenezi, tingafune kuwonjezera utumiki wathu kapena kuyesetsa kuti tizitumikira m’maudindo ena mumpingo. Komabe mwina tingayesetse koma n’kulephera kukwaniritsa zolinga zomwe tili nazo. Ndiye kodi tingatani kuti tipitirize kuchita zambiri potumikira Yehova n’kumakhalabe osangalala? Tingapeze yankho la funso limeneli m’fanizo la Yesu la matalente.
^ ndime 2 Mayina ena asinthidwa.
^ ndime 7 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Talente imodzi inali yofanana ndi ndalama zimene munthu ankalandira akagwira ntchito kwa zaka pafupifupi 20.
^ ndime 15 Abale obatizidwa akulimbikitsidwa kuti azichita khama kuti ayenerere kukhala atumiki othandiza komanso akulu. Kuti mudziwe zimene mungachite kuti muyenerere, onani mutu 5 ndi 6 m’buku lakuti Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova.
^ ndime 17 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mlangizi wothandiza ndi mkulu amene amapatsidwa udindo wopereka malangizo kwa akulu ndi atumiki othandiza omwe akamba nkhani mumpingo.
^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pofuna kukwaniritsa cholinga chake choti aziphunzitsa mwaluso, m’bale akufufuza malangizo othandiza m’mabuku athu.
^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pambuyo podziikira cholinga choti azilalikira mwamwayi, mlongo akugawira kakhadi kodziwitsa anthu za webusaiti yathu kwa woperekera zakudya.
^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chifukwa chofunitsitsa kusonyeza makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo, mlongo akupereka mphatso kwa wolambira mnzake.