Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Lemba la Miyambo 24:16 limati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” Kodi pamenepa akunena za munthu amene amachita machimo mobwerezabwereza koma kenako Mulungu n’kumukhululukira?
Zimenezi si zimene lembali limatanthauza. M’malomwake lembali likutanthauza kuti munthu akakumana ndi mavuto ambiri amakhala ngati wagwa, ndipo akakwanitsa kuwapirira zimakhala ngati wadzukanso.
Tiyeni tionenso nkhaniyi kuchokera mu vesi 15 mpaka 17: “ Mofanana ndi munthu woipa, usamabisalire munthu wolungama pamalo ake okhala. Usamasakaze malo ake okhala, pakuti wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso. Koma anthu oipa, tsoka lidzawapunthwitsa. Mdani wako akagwa usamasangalale ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere.”—Miy. 24:15-17.
Anthu ena amaganiza kuti vesi 16 limanena za munthu amene wachita tchimo kenako n’kulapa, n’kukhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Atsogoleri awiri achipembedzo a ku Britain analemba kuti, “alaliki akale komanso a masiku ano akhala akufotokoza lembali mwanjira imeneyi.” Atsogoleriwa ananenanso kuti zimenezi zingatanthauze kuti “munthu wabwino akhoza kuchita machimo akuluakulu koma n’kumakondedwabe ndi Mulungu, ndipo nthawi iliyonse imene walapa amakhala kuti wadzukanso.” Mfundo imeneyi ingakhale yosangalatsa kwa munthu amene safuna kusiya kuchita machimo. Iye angamaganize kuti ngakhale atachimwa mobwerezabwereza Mulungu azimukhululukirabe.
Koma zimenezi si zimene vesi 16 likutanthauza.
Mawu a Chiheberi amene anamasuliridwa kuti “kugwa” komanso “akagwa” mu vesi 16 ndi 17, angagwiritsidwe ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mawuwa angatanthauze kugwa kwenikweni. Mwachitsanzo, ng’ombe yagwa pamsewu, munthu wagwa kuchokera padenga, mwala wagwera pansi. (Deut. 22:4, 8; Amosi 9:9) Mawuwa angakhalenso ndi tanthauzo lina ngati mmene zilili pa lemba lotsatirali: “Yehova walimbitsa mapazi a munthu wamphamvu zake. Ndipo Mulungu amakondwera ndi njira zake. Ngakhale atapunthwa, sadzagweratu, pakuti Yehova wamugwira dzanja.”—Sal. 37:23, 24; Miy. 11:5; 13:17; 17:20.
Komabe taonani mfundo imene pulofesa wina dzina lake Edward H Plumptre analemba. Iye anati: “Mawu a Chiheberi amene anamasuliridwa kuti ‘kugwa’ sanagwiritsidwepo ntchito ponena za kuchita tchimo.” Komanso katswiri wina wa Baibulo anafotokoza vesili kuti: “Kuzunza anthu a Mulungu n’kosathandiza chifukwa nthawi zonse amapambana, koma anthu oipa sangapambane.”
Choncho zonsezi zikusonyeza kuti lemba la Miyambo 24:16, silikunena za kuchita tchimo koma likunena za kukumana ndi mavuto mobwerezabwereza. M’dziko loipali munthu wolungama angakumane ndi mavuto a thanzi, kapenanso mavuto ena. Akhozanso kuzunzidwa ndi boma chifukwa cha chikhulupiriro chake. Koma amakhulupirira kuti Mulungu angamuthandize kuti athe kupirira komanso kuti zinthu zimuyendere bwino. Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi sindimaona kuti nthawi zambiri atumiki a Mulungu zinthu zimawayendera bwino?’ N’zolimbikitsa kuti “Yehova amachirikiza amene ali pafupi kugwa, ndipo amaweramutsa onse amene awerama chifukwa cha masautso.”—Sal. 41:1-3; 145:14-19.
“Munthu wolungama” sasangalala anthu ena akamakumana ndi mavuto. M’malomwake amalimbikitsidwa podziwa kuti “anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino, chifukwa chakuti anali kumuopa.”—Mlal. 8:11-13; Yobu 31:3-6; Sal. 27:5, 6.