Chikumbutso Chimatithandiza Kukhala Ogwirizana
‘Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri kukhala pamodzi mogwirizana!’—SAL. 133:1.
1, 2. N’chiyani chidzathandize anthu kukhala ogwirizana mu 2018, ndipo n’chifukwa chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)
PA March 31, 2018, anthu a Mulungu komanso anthu ena oitanidwa adzasonkhana pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Mwambo wokumbukira imfa ya Khristuwu udzachitika padziko lonse dzuwa litalowa ndipo anthu mamiliyoni ambiri adzapezekapo. Chaka chilichonse, mwambo umenewu umathandiza kwambiri kuti anthu padziko lonse achite zinthu mogwirizana.
2 Popeza dzuwa limalowa nthawi yosiyanasiyana padzikoli, Yehova ndi Yesu ayenera kuti amasangalala kwambiri kuona anthu padziko lonse akuchita mwambowu pafupifupi ola lililonse mpaka tsiku la Chikumbutsoli litatha. Baibulo linaneneratu kuti “khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene [angathe] kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse” lidzafuula kuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:9, 10) N’zosangalatsa kwambiri kuti Yehova ndi Yesu amalemekezedwa kwambiri chaka chilichonse pa nthawi ya Chikumbutso.
3. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?
3 Munkhaniyi tikambirana mafunso angapo amene anthu amafunsa okhudza Chikumbutso. Mafunso ake ndi akuti: (1) Kodi tingakonzekere bwanji kuti tidzapindule ndi Chikumbutso? (2) Kodi Chikumbutso chimathandiza bwanji anthu a Mulungu kuti azigwirizana? (3) Kodi aliyense payekha angathandize bwanji kuti tizigwirizana? (4) Kodi tidzasiya kuchita mwambowu? Ngati ndi choncho, tidzasiya liti?
KODI TINGAKONZEKERE BWANJI KUTI TIPINDULE NDI CHIKUMBUTSO?
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizipezeka pa Chikumbutso?
4 Tiyenera kuganizira kufunika kopezeka pa Chikumbutso. Tizikumbukira kuti tikamasonkhana timakhala kuti tikulambira Yehova. Choncho Yehova ndi Yesu ayenera kuti amayamikira anthu amene amayesetsa kuti afike pamsonkhano wofunika kwambiri wa Chikumbutso. Timafuna kuti iwo aone kuti timayesetsa kupezeka pamsonkhanowu kupatulapo ngati pali mavuto aakulu. Tiyenera kusonyeza kuti timaona kuti misonkhano yathu ndi yofunika kwambiri. Izi zimathandiza kuti Yehova asunge dzina lathu ‘m’buku la chikumbutso’ kapena kuti “m’buku la moyo.” Bukuli ndi limene iye amalembamo mayina a anthu amene adzapeze moyo wosatha.—Mal. 3:16; Chiv. 20:15.
5. Chikumbutso chikamayandikira, kodi tingadziyese bwanji kuti ‘tione ngati tidakali olimba m’chikhulupiriro’?
5 Chikumbutso chikamayandikira, tingachite bwino kupeza nthawi yoti tizipemphera komanso kuganizira bwinobwino za ubwenzi wathu ndi Yehova. (Werengani 2 Akorinto 13:5.) Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera ‘kudziyesa kuti tione ngati tidakali olimba m’chikhulupiriro.’ Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti ndili m’gulu lokhalo limene Yehova akuligwiritsa ntchito kuti akwaniritse cholinga chake? Kodi ndikuchita zonse zimene ndingathe polalikira ndiponso kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu? Kodi zochita zanga zimasonyeza kuti ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti tili m’masiku otsiriza ndipo ulamuliro wa Satana watsala pang’ono kuwonongedwa? Kodi ndimakhulupirira kwambiri Yehova ndi Yesu ngati mmene ndinkachitira pamene ndinadzipereka kwa Yehova Mulungu?’ (Mat. 24:14; 2 Tim. 3:1; Aheb. 3:14) Kuganizira mafunso oterewa kungatithandize kudziyesa kuti tidziwe kuti ndife otani.
6. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzapeze moyo wosatha? (b) Kodi m’bale wina amakonzekera bwanji Chikumbutso, nanga mungamutsanzire bwanji?
6 Tiyenera kuwerenga ndiponso kusinkhasinkha nkhani za m’Baibulo zimene zimafotokoza kufunika kwa Chikumbutso. (Werengani Yohane 3:16; 17:3.) Popanda ‘kuphunzira ndi kudziwa’ Yehova komanso kukhulupirira Mwana wake Yesu, sitingadzapeze moyo wosatha. Choncho pokonzekera Chikumbutso, mungachite bwino kuphunzira nkhani zimene zingakuthandizeni kukonda kwambiri Yehova ndi Yesu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina amene wakhala mkulu kwa zaka zambiri. Iye wakhala akusonkhanitsa nkhani za mu Nsanja ya Olonda zimene zimafotokoza za Chikumbutso komanso chikondi chimene Yehova ndi Yesu anatisonyeza. Milungu ingapo Chikumbutso chisanachitike, iye amawerenga nkhanizi n’kumasinkhasinkha kufunika kwa mwambowu. Nthawi zina, amawonjezeramo nkhani imodzi kapena ziwiri zatsopano. M’baleyu waona kuti akamawerenga nkhanizi ndiponso kutsatira ndandanda ya kuwerenga Baibulo pa nthawi ya Chikumbutso amaphunzira mfundo zatsopano chaka chilichonse. Koma chofunika kwambiri n’chakuti amaona kuti chikondi chake pa Yehova ndi Yesu chimawonjezeka chaka chilichonse. Nanunso mukamachita zimenezi mudzayamba kukonda kwambiri Yehova ndi Yesu komanso kuwayamikira ndipo mudzapindula kwambiri ndi Chikumbutso.
CHIKUMBUTSO CHIMATHANDIZA KUTI TIZIGWIRIZANA
7. (a) Kodi Yesu anapempherera nkhani iti pa tsiku limene anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye? (b) N’chiyani chimasonyeza kuti Yehova wayankha pemphero la Yesu?
7 Usiku umene Yesu anayambitsa mwambowu, anapemphera kuti otsatira ake akhale ogwirizana ngati mmene zilili pakati pa iyeyo ndi Atate wake. (Werengani Yohane 17:20, 21.) Yehova wayankhadi pemphero la Mwana wakeli moti panopa anthu mamiliyoni ambiri akukhulupirira kuti Yesu anatumidwa ndi Yehova. Umboni wakuti a Mboni za Yehovafe ndi ogwirizana umaonekera kwambiri pa Chikumbutso kuposa pamisonkhano yonse imene timakhala nayo. Pa tsiku la mwambowu, anthu a mitundu yosiyanasiyana amasonkhana padziko lonse. Izi n’zochititsa chidwi chifukwa kumadera ena, anthu a mitundu yosiyana sachitira limodzi misonkhano yachipembedzo ndipo amanyoza anthu amene amachita zimenezi. Koma Yehova ndi Yesu amasangalala kwambiri kuona anthu osiyana akusonkhana pamodzi mogwirizana.
8. Kodi Yehova anapatsa Ezekieli uthenga uti wokhudza mgwirizano?
8 Anthu a Yehovafe sitidabwa ndi mgwirizano wathu. Paja Yehova ananeneratu kuti tidzakhala ogwirizana. Mwachitsanzo, anapatsa mneneri Ezekieli uthenga wonena za kuika ndodo ziwiri pamodzi kuti zikhale ndodo imodzi. Ndodo ina inali “ya Yuda” ndipo ina inali “ya Yosefe.” (Werengani Ezekieli 37:15-17.) Mu Nsanja ya Olonda ya July 2016 muli nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” yomwe inanena kuti: “Kudzera mwa Ezekieli, Yehova ananeneratu kuti Aisiraeli adzakhalanso ogwirizana m’Dziko Lolonjezedwa. Ulosiwu unkanenanso za atumiki a Mulungu a m’masiku otsiriza ano kuti adzakhala ogwirizana.”
9. Kodi mgwirizano umene Ezekieli analosera umaonekera bwanji pa Chikumbutso?
9 Kuyambira mu 1919, Yehova wakhala akugwirizanitsa odzozedwa omwe akuimiridwa ndi ndodo “ya Yuda.” Kenako anthu ambiri amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, omwe akuimiridwa ndi ndodo “ya Yosefe,” anagwirizana ndi odzozedwa n’kukhala “gulu limodzi” la nkhosa. (Yoh. 10:16; Zek. 8:23) Yehova analonjeza kuti adzaphatikiza ndodo ziwiri n’kukhala ndodo imodzi m’dzanja lake. (Ezek. 37:19) Panopa, magulu awiriwa akutumikira mogwirizana ndipo amamvera Mfumu Yesu Khristu yemwe Mulungu amamutchulanso kuti “Davide mtumiki wanga.” (Ezek. 37:24, 25) Mgwirizano umene Ezekieli anaufotokoza umaonekera kwambiri chaka chilichonse pamene odzozedwa ndi a “nkhosa zina” amakumbukira limodzi imfa ya Khristu. Koma kodi aliyense payekha angachite chiyani kuti tizigwirizana kwambiri?
ZIMENE ALIYENSE ANGACHITE KUTI TIZIGWIRIZANA
10. Kodi tingalimbitse bwanji mgwirizano m’gulu la Yehova?
10 Chinthu chimodzi chimene chingathandize kuti tizigwirizana ndi kukhala ndi mtima wodzichepetsa. Yesu ali padzikoli anauza ophunzira ake kuti ayenera kukhala odzichepetsa. (Mat. 23:12) Munthu wodzichepetsa satengera mzimu wa m’dzikoli wodziona ngati wapamwamba. Mtima wodzichepetsa ungatithandize kuti tizigonjera amene akutitsogolera ndipo zimenezi n’zimene zimathandiza kuti mpingo uzikhala wogwirizana. Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikakhala odzichepetsa timasangalatsa Mulungu. Paja Baibulo limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”—1 Pet. 5:5.
11. Kodi kuganizira zimene zizindikiro za pa Chikumbutso zimaimira kungatithandize bwanji?
11 Chinthu chachiwiri chimene chingatithandize kuti tizigwirizana ndi kuganizira zimene zizindikiro za pa Chikumbutso zimaimira. Tsiku la mwambowu lisanafike komanso pa tsikulo, tiyenera kuganizira kwambiri kufunika kwa zimene 1 Akor. 11:23-25) Mkate umaimira thupi la Yesu lopanda uchimo limene linaperekedwa nsembe ndipo vinyo amaimira magazi ake. Koma chofunika si kungodziwa kuti chizindikiro ichi chimaimira chakuti, ichi chimaimira chakuti. Tizikumbukira kuti dipo ndi njira imene Yehova ndi Yesu anasonyezera chikondi kuposa munthu wina aliyense. Yehova anasonyeza chikondi popereka Mwana wake kuti adzatifere ndipo Yesu anasonyeza chikondi pololera kupereka moyo wake chifukwa cha ifeyo. Kuganizira chikondi chimenechi kungatilimbikitse kuti nafe tiziwakonda. Ndipo chikondi chimene aliyense wa ife ali nacho kwa Yehova chili ngati chingwe chimene chimatimangirira pamodzi kuti tizikhala ogwirizana kwambiri.
mkate wopanda chofufumitsa komanso vinyo wofiira zimaimira. (12. Kodi Yesu anapereka fanizo liti posonyeza kuti Yehova amafuna kuti tizikhululukira anzathu?
12 Chinthu chachitatu chimene chingatithandize kuti tizigwirizana ndi kukhala ndi mtima wokhululukira ena. Tikamakhululukira anzathu, timasonyeza kuti timayamikira nsembe ya dipo imene Khristu anapereka yomwe imathandiza kuti nafenso machimo athu akhululukidwe. Taganizirani fanizo limene Yesu ananena pa Mateyu 18:23-34. Ndiye ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimayesetsa kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa? Kodi ndimamvetsa Akhristu anzanga komanso kuwalezera mtima? Kodi ndine wokonzeka kukhululukira munthu aliyense amene angandilakwire?’ N’zoona kuti machimo ena amakhala aakulu moti zingavute kuti munthu yemwe si wangwiro awaiwale. Koma fanizoli likutithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani yokhululukayi. (Werengani Mateyu 18:35.) Pa lembali, Yesu ananena momveka bwino kuti Yehova sadzatikhululukira ngati ifeyo timakana kukhululukira anzathu pamene pali zifukwa zowakhululukira. Mfundo imeneyitu ndi yofunika kuiganizira kwambiri. Tikamayesetsa kutsatira malangizo a Yesu akuti tizikhululukira anzathu timathandiza kuti tizigwirizana kwambiri.
13. Kodi kukhala okonda mtendere kumathandiza bwanji kuti tizigwirizana?
13 Tikamakhululukira anzathu timasonyeza kuti ndife okonda mtendere. Tizikumbukira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu Aef. 4:3) Choncho tsiku la Chikumbutso likamayandikira komanso likafika, tiyenera kuganizira mmene timachitira zinthu ndi anzathu. Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimasonyeza kuti sindisungira anthu zifukwa? Kodi anthu amadziwa kuti ndimachita zonse zimene ndingathe polimbikitsa mtendere komanso mgwirizano?’ Mafunso amenewa ndi ofunika kuwaganizira kwambiri pa nyengo ya Chikumbutso.
pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chotigwirizanitsa. Umodziwo timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera.” (14. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘timalolerana m’chikondi’?
14 Chinthu cha nambala 4 chimene chingatithandize kuti tizigwirizana ndi kutsanzira Yehova pa nkhani yosonyeza chikondi. Tizikumbukira kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi. (1 Yoh. 4:8) Si nzeru kumanena Mkhristu mnzathu kuti, “N’zoona kuti ndiyenera kumukonda koma kungoti sandisangalatsa.” Maganizo amenewa ndi osiyana ndi malangizo a Paulo akuti ‘tizilolerana m’chikondi.’ (Aef. 4:2) Chochititsa chidwi n’chakuti Paulo sanangonena kuti ‘tizilolerana,’ koma ananena kuti ‘tizilolerana m’chikondi.’ Kungololerana n’kosiyana ndi kulolerana m’chikondi. Tikutero chifukwa chakuti Yehova amakokera mumpingo wake anthu a mitundu yosiyanasiyana. (Yoh. 6:44) Iye akamakokera munthu m’gulu lake amakhala ataona makhalidwe enaake abwino mwa munthuyo ndipo amamukonda. Ndiye kodi ndi nzeru ifeyo kuganiza kuti munthu wina mumpingo si woyenera kumukonda? Si bwino kukana kukonda anthu amene Yehova watilamula kuti tiziwakonda.—1 Yoh. 4:20, 21.
KODI CHIKUMBUTSO CHOMALIZA CHIDZACHITIKA LITI?
15. Kodi tikudziwa bwanji kuti padzakhala Chikumbutso chomaliza?
15 Tsiku lina tidzachita Chikumbutso chomaliza. N’chifukwa chiyani tikutero? M’kalata yoyamba imene Paulo analembera Akhristu odzozedwa a ku Korinto, ananena kuti akamakumbukira imfa ya Yesu amalengeza “imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.” (1 Akor. 11:26) Palembali, mawu oti “adzafike” akunena za nthawi ya kubwera kwake imene Yesu anaifotokoza mu ulosi wonena za masiku otsiriza. Pofotokoza za chisautso chachikulu chimene chatsala pang’ono kufika anati: “Chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaonekera kumwamba. Ndiyeno mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni, ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. [Yesu] adzatumiza angelo ake ndi kulira kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera kumphepo zinayi, kuchokera kumalekezero a m’mlengalenga mpaka kumalekezero ena.” (Mat. 24:29-31) Mawu oti “adzasonkhanitsa osankhidwa ake” akunena za nthawi imene odzozedwa onse amene adzatsale ndi moyo padzikoli adzatengedwe kukalandira mphoto yawo kumwamba. Zimenezi zidzachitika mbali yoyamba ya chisautso chachikulu ikadzadutsa koma nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Kenako a 144,000 onse adzathandiza Yesu kuti agonjetse mafumu a dzikoli. (Chiv. 17:12-14) Choncho Chikumbutso chimene chidzachitike odzozedwawa atatsala pang’ono kutengedwa kupita kumwamba chidzakhala chomaliza chifukwa Yesu adzakhala atabwera.
16. N’chifukwa chiyani mukufunitsitsa kupezeka pa Chikumbutso cha chaka chino?
16 Tiyeni tonse tichite zimene tingathe pokonzekera kuti tidzapindule ndi Chikumbutso cha pa 31 March 2018. Tizipemphanso Yehova kuti atithandize kulimbikitsa mgwirizano m’gulu lake. (Werengani Salimo 133:1.) Tizikumbukira kuti tsiku lina tidzachita Chikumbutso chomaliza. Choncho tiyeni panopa tiziyesetsa kukonzekera kuti tidzapezeke pa Chikumbutso ndipo tiziyamikira mgwirizano umene umaoneka pa mwambo umenewu.