NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) July 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa September 3-30, 2018.

ANADZIPEREKA NDI MTIMA WONSE

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Myanmar

Kodi n’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova ambiri achoka kwawo kuti akathandize pa ntchito yolalikira ku Myanmar?

Kodi Mumafuna Kukhala Wodziwika kwa Ndani?

Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mulungu amachita posonyeza kuti amadziwa komanso kuyamikira atumiki ake okhulupirika?

Kodi Maso Anu Amayang’ana kwa Ndani?

Tingaphunzire mfundo yofunika kwambiri pa zimene Mose analakwitsa.

“Ndani Ali Kumbali ya Yehova?”

Nkhani za m’Baibulo zokhudza Kaini, Solomo, Mose ndi Aroni zimasonyeza kuti ndi nzeru kukhala kumbali ya Yehova.

Ndife Anthu a Yehova

Kodi tingathokoze bwanji Yehova chifukwa chotipatsa mwayi wokhala naye pa ubwenzi?

Muzichitira Chifundo Anthu “Kaya Akhale a Mtundu Wotani”

Tizitsanzira Yehova pa nkhani yokhala achifundo ndipo tiziyesetsa kuona mavuto amene anthu ali nawo n’kuwathandiza ngati zingatheke.

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Ngati mwamuna ndi mkazi amene sali pa banja atakhala limodzi usiku wonse popanda zifukwa zomveka, kodi tingati achita tchimo lalikulu?