Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 26

“Bwererani Kwa Ine”

“Bwererani Kwa Ine”

“Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu.”​—MAL. 3:7.

NYIMBO NA. 102 “Muthandize Ofookawo”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova amamva bwanji nkhosa yake yomwe inasochera ikapezeka?

MONGA tinaphunzirira munkhani yapitayi, Yehova amadziyerekezera ndi m’busa wabwino amene amasamalira mwachikondi nkhosa yake iliyonse. Ndipo amafufuza imene yasochera. Yehova anauza Aisiraeli omwe anasiya kumutumikira kuti: “Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu.” Tikudziwa kuti umu ndi mmene amamverabe masiku ano chifukwa iye amati: “Sindinasinthe.” (Mal. 3:6, 7) Yesu ananena kuti Yehova komanso angelo amasangalala kwambiri mtumiki Wake amene anasochera akabwerera kwa Iye, ngakhale atakhala mmodzi yekha.​—Luka 15:10, 32.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Tiyeni tikambirane mafanizo atatu a Yesu omwe amasonyeza mmene tingathandizire anthu amene anasiya kutumikira Yehova. Tikambirananso makhalidwe amene timafunika kukhala nawo pothandiza nkhosa zimene zinasochera kuti zibwererenso kwa Yehova. Tionanso mmene timamvera tikachita khama pothandiza munthu amene anali wofooka.

KUFUFUZA KHOBIDI LOTAYIKA

3-4. N’chifukwa chiyani mayi wotchulidwa pa Luka 15:8-10, anafufuza mosamala khobidi lake ladalakima limene linatayika?

3 Pamafunika khama kuti tipeze anthu omwe akufuna kubwerera kwa Yehova. Mufanizo lina lopezeka mu Uthenga Wabwino wa Luka, Yesu anafotokoza mmene mayi wina anafufuzira khobidi lake ladalakima limene linasowa. Mfundo yofunika m’fanizoli ndi khama limene mayiyu anasonyeza pofufuza khobidilo.​—Werengani Luka 15:8-10.

4 Yesu anafotokozanso mmene mayiyo anamvera atapeza khobidi lomwe linasowalo. Zikuoneka kuti m’nthawi ya Yesu, azimayi ena achiyuda ankapatsa ana awo aakazi makobidi 10 adalakima patsiku la ukwati wawo. Ndiyeno mwina khobidilo linali lapadera kwa mayiyo chifukwa choti linali limodzi mwa makobidi 10 omwe mayi ake anamupatsa. Mayiyo anaganiza kuti ndalama yake yagwera pansi m’nyumba mwake momwemo. Choncho anayatsa nyale n’kuyamba kufufuza koma sanaipeze. Mwina kuwala kwa nyaleyo sikunali kokwanira kuti aone khobidilo. Kenako, anasesa mosamala m’nyumba monsemo. Ndiyeno akuwola fumbi, anangoona khobidi lija likunyezimira ndi kuwala kwa nyale. Apatu anasangalala kwambiri. Iye anaitana anzake komanso oyandikana nawo nyumba n’kuwafotokozera nkhani yabwinoyi.

5. N’chifukwa chiyani pamafunika khama kuti tipeze anthu amene anasiya kusonkhana?

5 Monga taonera mufanizo la Yesuli, pamafunika khama kuti munthu apeze chinthu chake chomwe chatayika. Zimenezi zikufanana ndi zomwe timafunika kuchita kuti tipeze anthu omwe anasiya kusonkhana. N’kutheka kuti padutsa zaka zambiri kuchokera pamene anasiya kusonkhana. Mwinanso anasamukira kudera lina kumene abale akumeneko sawadziwa. Koma sitikukayikira kuti panopa, ena mwa anthuwa akufuna atabwerera kwa Yehova. Akufuna atamatumikiranso Yehova limodzi ndi abale ndi alongo awo, koma amafunika thandizo lathu.

6. Kodi anthu onse mumpingo angagwire nawo bwanji ntchito yofufuza anthu amene anasiya kusonkhana?

6 Kodi ndi ndani angagwire nawo ntchito yofufuza anthu amene anasiya kusonkhana? Aliyense angagwire nawo ntchitoyi, kaya ndi akulu, apainiya, achibale a munthuyo komanso ofalitsa onse mumpingo. Ndiye kodi muli ndi mnzanu kapena wachibale amene anasiya kusonkhana? Kodi mungachite chiyani ngati mwakumana ndi munthu amene anasiya kusonkhana pamene mukulalikira kunyumba ndi nyumba kapena m’malo opezeka anthu ambiri? Mungamufotokozere kuti ngati angakonde kuti akulu a mumpingo wanu amuyendere, mukhoza kukawapatsa nambala yafoni kapena adiresi yake.

7. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene mkulu wina dzina lake Thomas ananena?

7 Kodi akulu angachite chiyani kuti akwanitse udindo wawo waukulu wofufuza anthu amene akufuna kubwerera kwa Yehova? Mkulu wina wa ku Spain dzina lake Thomas, * anathandiza anthu oposa 40 kuti ayambirenso kusonkhana. Iye anati: “Choyamba ndimafunsa abale ndi alongo osiyanasiyana ngati akudziwa kumene anthuwo akukhala panopa. Apo ayi ndimafunsa ofalitsa ngati akukumbukira anthu ena amene sakufikanso pamisonkhano. Ambiri mumpingo amakhala okonzeka kuthandiza chifukwa amadzimva kuti akugwira nawo ntchito yofufuzayi. Ndiyeno ndikayendera abale ndi alongo amene anasiya kusonkhanawo, ndimafunsa za ana komanso achibale awo ena. Ena mwa abale ndi alongowa ankabwera ndi ana komanso achibale awo ena kumisonkhano, omwe mwinanso anali ofalitsa. Amenewanso tingawathandize kuti abwerere kwa Yehova.”

TIZITHANDIZA ANTHU KUTI ABWERERE KWA YEHOVA

8. Mufanizo la mwana wolowerera lopezeka pa Luka 15:17-24, kodi bambo anachitira chiyani mwana wawo amene anasonyeza kuti walapa?

8 Kodi tiyenera kukhala ndi makhalidwe ati kuti tithandize anthu kubwerera kwa Yehova? Tiyeni tione zimene tikuphunzira mufanizo la Yesu la mwana wolowerera amene anachoka pakhomo pa makolo ake. (Werengani Luka 15:17-24.) Yesu anafotokoza kuti mwanayo pambuyo pake anazindikira kuti sanaganize bwino ndipo anasankha zobwereranso kwawo. Bambo ataona mwana wawoyo anamuthamangira ndi kumukumbatira mwachikondi. Mwanayo ankadziimba mlandu ndipo ankaona kuti sakuyeneranso kutchedwa mwana wa bambowo. Koma atawafotokozera mmene ankamvera, anamumvera chisoni. Kenako anachita zinthu zimene zinatsimikizira mwanayo kuti amulandira ngati mwana wawo wokondedwa osati ngati wantchito. Pofuna kusonyeza zimenezi, bambowo anakonza phwando komanso anapatsa mwana wawoyo zovala zabwino.

9. Kodi tiyenera kukhala ndi makhalidwe ati kuti tithandize anthu amene anasiya kusonkhana kuti abwererenso kwa Yehova? (Onani bokosi lakuti “Mmene Tingathandizire Anthu Amene Akufuna Kubwerera kwa Yehova.”)

9 Yehova ali ngati bambo a mufanizoli. Iye amakonda kwambiri abale ndi alongo athu amene anasiya kusonkhana ndipo amafuna kuti abwererenso kwa iye. Tikamatsanzira Yehova tingawathandize kuti abwerere. Kuti tichite zimenezi tiyenera kukhala oleza mtima, achifundo komanso achikondi. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi makhalidwewa nanga tingawasonyeze bwanji?

10. Kodi kuleza mtima n’kofunika bwanji pothandiza munthu kuti abwerere kwa Yehova?

10 Timafunika kukhala oleza mtima chifukwa pamatenga nthawi kuti munthu abwerere kwa Yehova. Anthu ena amene anasiya kusonkhana m’mbuyomu anafotokoza kuti anayambiranso kusonkhana akulu ndi Akhristu ena atawayendera mobwerezabwereza. Mlongo wina wa ku Asia, dzina lake Nancy ananena kuti: “Mnzanga wina wamumpingo anandithandiza kwambiri. Ankandikonda kwambiri ngati mkulu wake. Anandikumbutsa zinthu zabwino zimene tinachitirapo limodzi. Ankandimvetsera moleza mtima ndikamafotokoza mmene ndikumvera ndipo sankazengereza kundipatsa malangizo. Analidi mnzanga weniweni ndipo anali wokonzeka kundithandiza nthawi iliyonse.”

11. Kodi kuchitira chifundo munthu amene anakhumudwa n’kothandiza bwanji?

11 Kuchitira ena chifundo kuli ngati mankhwala othandiza munthu amene wakhumudwa. Ena anasiya kusonkhana chifukwa choti anakhumudwitsidwa ndi munthu wina mumpingo. Ngakhale kuti panadutsa nthawi yaitali, zimawapwetekabe ndipo zimawavuta kuti abwererenso kwa Yehova. Enanso amaona kuti sanachitiridwe zachilungamo. Ndiye amafuna munthu amene angawamvetsere komanso kuwamvetsa. (Yak. 1:19) Mlongo wina dzina lake María, yemwe nthawi ina anasiya kutumikira Yehova anati: “Chomwe ndinkafunikira ndi munthu amene akanandimvetsera, kunditonthoza komanso kundipatsa malangizo.”

12. Fotokozani chitsanzo chosonyeza mmene chikondi cha Yehova chimathandizira anthu kuti abwererenso kwa iye.

12 Baibulo limafotokoza kuti chikondi cha Yehova chili ngati chingwe. N’chifukwa chiyani chikondi cha Mulungu chimayerekezeredwa ndi chingwe? Taganizirani izi: Yerekezerani kuti mukumira ndipo wina wakuponyerani chovala chokuthandizani kuti muziyandama. N’zosakayikitsa kuti mungamuyamikire kwambiri. Koma ngati madziwo ndi ozizira kwambiri, chovalacho sichingakuthandizeni kuti mukhalebe ndi moyo. Ndiye mungafunike kuti wina akuponyereni chingwe n’kukukokerani m’boti. Ponena za Aisiraeli omwe anasochera, Yehova anati: “Ndinali kuwakoka mokoma mtima ndi mwachikondi.” (Hos. 11:4) Umu ndi mmene Mulungu amachitiranso ndi anthu amene anasiya kumutumikira komanso akukumana ndi mavuto ambiri omwe amawadetsa nkhawa. Iye amafuna kuti anthuwo adziwe kuti amawakonda komanso amafuna kuwathandiza kuti abwerere kwa iye. Ndipo Yehova akhoza kugwiritsa ntchito inuyo powathandiza kuti aone chikondi chake.

13. Kodi kusonyeza ena chikondi n’kofunika bwanji? Perekani chitsanzo.

13 Tizitsimikizira anthu amene anasiya kusonkhana kuti Yehova amawakonda kwambiri komanso tiziwasonyeza kuti nafenso timawakonda. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika? Pablo, yemwe tinamutchula munkhani yapita ija, anasiya kutumikira Yehova kwa zaka zoposa 30. Iye anati: “Tsiku lina m’mawa, ndikunyamuka pakhomo, ndinakumana ndi mlongo wina wachikulire ndipo anandilankhula mwachikondi. Ndinayamba kulira ngati mwana. Ndipo ndinamuuza kuti zikuoneka kuti ndi Yehova amene anamutuma kuti adzandilankhule. Kuyambira pamenepo ndinaganiza zobwerera kwa Yehova.”

TIZITHANDIZA MWACHIKONDI ANTHU AMENE ANAFOOKA

14. Mogwirizana ndi fanizo lopezeka pa Luka 15:4, 5, kodi m’busa anatani atapeza nkhosa imene inasochera?

14 Tifunika kupitirizabe kuthandiza anthu amene anafooka. Mofanana ndi mwana wolowerera wa mufanizo la Yesu, anthuwa akhoza kumavutika maganizo. Komanso n’kutheka kuti zimene akumana nazo m’dziko la Satanali zachititsa kuti asakhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Choncho tiyenera kuwathandiza kuti alimbitsenso chikhulupiriro chawo. Mufanizo la nkhosa imene inasochera, Yesu anafotokoza kuti m’busa ananyamula nkhosayo paphewa pake ndi kupita nayo komwe kunali zinzake. M’busayo anali atathera nthawi yaitali komanso mphamvu zake poifufuza. Komabe ataipeza anaona kuti ikufunika kunyamulidwa chifukwa inalibe mphamvu zoti n’kubwerera payokha.​—Werengani Luka 15:4, 5.

15. Kodi tingathandize bwanji anthu amene anafooka omwe akufuna kuyambiranso kutumikira Yehova? (Onani bokosi lakuti “Kabuku Kothandiza Kwambiri.”)

15 Timafunika kugwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zathu pothandiza anthu amene anafooka kuti akwanitse kulimbana ndi mavuto amene angawalepheretse kuyambiranso kutumikira Yehova. Koma mzimu wa Yehova, Mawu ake ndiponso mabuku amene timalandira zingatithandize polimbikitsa anthuwa kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. (Aroma 15:1) Kodi tingachite bwanji zimenezi? M’bale wina amene watumikira ngati mkulu kwa nthawi yaitali anati: “Anthu ambiri omwe anafooka akafuna kubwereranso kwa Yehova, amafunika ayambirenso kuphunzira Baibulo.” * Ndiye ngati mwapemphedwa kuti muziphunzira ndi munthu amene anafooka, muziona kuti ndi mwayi wanu. Mkuluyu ananenanso kuti: “Wofalitsa amene akuchititsa phunziroli ayenera kukhala munthu amene wofookayo angamasuke naye kumamufotokozera zakukhosi kwake.”

KUMAKHALA CHISANGALALO KUMWAMBA KOMANSO PADZIKO LAPANSI

16. Kodi tikudziwa bwanji kuti angelo amatithandiza tikamafufuza anthu amene akufuna kubwerera kwa Yehova?

16 Pali zitsanzo zambiri zomwe zimasonyeza kuti angelo amatithandiza tikamafufuza anthu amene akufuna kubwerera kwa Yehova. (Chiv. 14:6) Mwachitsanzo, m’bale wina wa ku Ecuador dzina lake Silvio, ankapemphera kwa Yehova kuti amuthandize kubwerera kwa iye. Asanamalize kupemphera, akulu awiri anafika pakhomo pake. Akuluwo anamufotokozera zimene angachite ndipo anali ofunitsitsa kumuthandiza.

17. Kodi timamva bwanji tikathandiza ofooka kubwereranso kwa Yehova?

17 Tikamathandiza anthu amene anafooka, timakhala osangalala kwambiri. Mpainiya wina dzina lake Salvador, amayesetsa kuthandiza anthu amene anafooka. Iye anati: “Ndikamaganizira za ofalitsa ena ofooka amene anabwerera kwa Yehova, ndimasangalala kwambiri moti nthawi zina ndimagwetsa misozi. Zimandisangalatsa kuona kuti Yehova wapulumutsa nkhosa yake kuchokera kudziko la Satanali ndipo ndinali ndi mwayi wothandiza nawo kuti zimenezi zitheke.”​—Mac. 20:35.

18. Kodi anthu amene anasiya kusonkhana ayenera kudziwa chiyani?

18 Ngati munasiya kupezeka pamisonkhano, muyenera kudziwa kuti Yehova amakukondanibe. Amafuna kuti mubwererenso kwa iye. Ndiye mukufunika kuyesetsa kuti mubwerere. Mofanana ndi bambo a mufanizo la Yesu, Yehova akuyembekezera kuti mubwerere kwa iye, ndipo adzakulandirani ndi manja awiri.

NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso za Amuna

^ ndime 5 Yehova akufuna kuti anthu amene anasiya kusonkhana komanso kulalikira abwererenso kwa iye. Yehova akuwauza kuti: “Bwererani kwa ine.” Pali zambiri zomwe tingachite kuti tiwathandize. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite powathandiza kuti abwerere.

^ ndime 7 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 15 Tingathandize anthu ena amene anafooka pophunzira nawo mitu ina ya m’buku lakuti Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani? Kapenanso mitu ina m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova. Abale a m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo ndi amene amasankha munthu woyenerera woti azichititsa phunziroli.

^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Abale atatu akuthandiza m’bale amene akufuna kubwerera kwa Yehova. M’bale wina akuchita zimenezi poimbira foni wofookayo, wina akuchita zinthu zosonyeza kuti amamukonda ndipo wina akuyesetsa kumumvetsera ndi kusonyeza kuti akumumvetsa.