Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudziletsa​—N’kofunika Kuti Yehova Azisangalala Nafe

Kudziletsa​—N’kofunika Kuti Yehova Azisangalala Nafe

M’bale wina dzina lake Paul, anati: “M’bale wanga atandiputa ndinamukanyanga pakhosi. Ndinkafuna kungomupha basi.”

M’bale winanso dzina lake Marco, anati: “Sindinkachedwa kupsa mtima, ngakhale pazinthu zazing’ono. Ndiye ndikakwiya, ndinkaphwanya chilichonse chomwe chandiyandikira.”

Mwina ifeyo sitingachite kufika pamenepa. Komabe nthawi zina tonsefe zimativuta kuti tikhale odziletsa. Izi zili choncho chifukwa tinatengera uchimo kuchokera kwa Adamu. (Aroma 5:12) Mofanana ndi Paul komanso Marco omwe tawatchula pamwambapa, anthu ena zimawavuta kudziletsa komanso kulamulira maganizo awo. Mwachitsanzo, iwo amangoganizira zinthu zimene zimawachititsa mantha kapena kuwafooketsa. Pomwe ena amavutika kudziletsa kuti asachite chiwerewere, kumwa mowa mwauchidakwa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Anthu amene salamulira maganizo, zilakolako komanso zochita zawo, amakumana ndi mavuto ambiri. Komatu kudziletsa kungatithandize kupewa mavuto amenewa. Ndiye kodi tingatani kuti tikhale odziletsa? Tiyeni tikambirane mafunso atatu awa: (1) Kodi munthu wodziletsa amatani? (2) N’chifukwa chiyani kudziletsa n’kofunika? (3) Kodi tingatani kuti tikhale ndi khalidweli lomwe ndi limodzi mwa “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa”? (Agal. 5:22, 23) Kenako tikambirana zimene aliyense payekha angachite ngati nthawi zina zimavuta kukhala odziletsa.

KODI MUNTHU WODZILETSA AMATANI?

Munthu wodziletsa sachita zinthu mopupuluma. M’malomwake amadzigwira kuti asalankhule kapena kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse Mulungu.

Yesu anasonyeza bwino zimene kudziletsa kumatanthauza

Yesu anasonyeza bwino zimene kudziletsa kumatanthauza. Baibulo limati: “Pamene anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” (1 Pet. 2:23) Yesu ali pamtengo wozunzikirapo, anasonyeza kudziletsa pamene adani ake ankamunyoza. (Mat. 27:39-44) Anasonyezanso kuti anali wodziletsa kwambiri pamene atsogoleri achipembedzo ankamufunsa mafunso ongofuna kumukola mawu. (Mat. 22:15-22) Anaperekanso chitsanzo chabwino pa nkhani ya kudziletsa pamene Ayuda ena anatola miyala kuti amugende. M’malo mobwezera, “Yesu anabisala ndi kutuluka m’kachisimo.”​—Yoh. 8:57-59.

Kodi n’zotheka kutsanzira Yesu pankhaniyi? Inde, ngakhale kuti sitingamutsanzire ndendende. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.” (1 Pet. 2:21) Ngakhale kuti siife angwiro, tikhoza kutsanzira mosamala kwambiri chitsanzo cha Yesu cha kudziletsa. Kodi n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kofunika?

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZILETSA N’KOFUNIKA?

Tiyenera kukhala odziletsa ngati tikufuna kuti Yehova azisangalala nafe. Ngakhale titatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri, tikhoza kuwononga ubwenzi wathu ndi iye ngati sitidziletsa pa zochita kapena zolankhula zathu.

Chitsanzo pankhaniyi ndi Mose, yemwe panthawiyo anali “munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:3) Kwa zaka zambiri, Mose ankamvetsera moleza mtima Aisiraeli akamadandaula. Koma tsiku lina analephera kudziletsa. Iye anakwiya pamene Aisiraeli anadandaula kachiwiri kuti analibe madzi. Mose anawalankhula mwaukali, kuti: “Tsopano tamverani anthu opanduka inu! Kodi tichite kukutulutsirani madzi m’thanthweli?”​—Num. 20:2-11.

Pamenepa Mose analephera kudziletsa. Iye sanapereke ulemu kwa Yehova amene anachititsa madzi kutuluka m’thanthwelo. (Sal. 106:32, 33) Chifukwa cha zimenezi, Yehova sanamulole kuti akalowe m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 20:12) Mose ayenera kuti anadandaula kwa moyo wake wonse chifukwa cholephera kudziletsa panthawiyi.​—Deut. 3:23-27.

Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ngakhale titakhala m’choonadi kwa nthawi yaitali, tiyenera kupewa kulankhula mopanda ulemu kwa anthu amene atikwiyitsa kapena amene akufunika kulangizidwa. (Aef. 4:32; Akol. 3:12) N’zoona kuti nthawi zina munthu akamakalamba, amavutika kukhala woleza mtima. Koma tizikumbukira zimene zinachitikira Mose. Tatumikira Yehova mokhulupirika kwa nthawi yaitali ndiye sitingafune kuwononga mbiri imeneyi chifukwa cholephera kudziletsa. Koma kodi tingatani kuti tikhale ndi khalidwe lofunikali?

KODI TINGATANI KUTI TIKHALE ODZILETSA?

Tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera. Kuchita zimenezi n’kofunika chifukwa paja kudziletsa ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa ndipo Yehova amapereka mzimu wakewo kwa amene amamupempha. (Luka 11:13) Yehova angagwiritse ntchito mzimuwu potipatsa mphamvu zoti tithe kukhala odziletsa. (Afil. 4:13) Angatithandizenso kuti tikhale ndi makhalidwe ena amene mzimu umatulutsa monga chikondi, chomwe chingachititse kuti tisamavutike kukhala odziletsa.​—1 Akor. 13:5.

Tizipewa chilichonse chimene chingachititse kuti tizivutika kudziletsa

Tizipewa chilichonse chimene chingachititse kuti tizivutika kudziletsa. Mwachitsanzo, tiyenera kupewa mawebusaiti ndi zosangalatsa zimene zimasonyeza makhalidwe oipa. (Aef. 5:3, 4) Ndipotu tiyenera kupewa chilichonse chimene chingatikope kuti tichite zoipa. (Miy. 22:3; 1 Akor. 6:12) Mwachitsanzo, munthu amene sachedwa kukopeka kuti achite chiwerewere, angafunike kupeweratu mabuku kapena mafilimu okhudza zachikondi.

Mwina tingaone kuti kutsatira malangizo amenewa ndi kovuta. Komabe tikamachita khama, Yehova adzatipatsa mphamvu zimene tikufunikira kuti tikhale odziletsa. (2 Pet. 1:5-8) Iye adzatithandiza kuti tizidziletsa pa zoganiza, zolankhula komanso zochita zathu. Chitsanzo cha Paul ndi Marco, omwe tawatchula kale aja, chikutsimikizira zimenezi chifukwa onse anaphunzira kudziletsa ndipo anasiya kupsa mtima msanga. Chitsanzo chinanso ndi cha m’bale wina yemwe nthawi zambiri ankapsa mtima akamayendetsa galimoto, mpaka ankafika pomakangana ndi anthu ena pamsewu. Ndiye kodi anatani? Iye anati: “Tsiku lililonse ndinkapemphera kuchokera pansi pamtima. Ndinkaphunziranso nkhani zokhudza kudziletsa ndipo ndinaloweza mavesi ena a m’Baibulo. Ngakhale kuti ndakhala ndikuchita zimenezi kwa zaka, ndimafunikabe kudzikumbutsa m’mawa uliwonse kuti patsikulo ndikwaniritse cholinga changa chokhalabe wodekha. Ndipo ndimayesetsa kunyamuka nthawi yabwino kuti ndisamaone kuti ena akundichedwetsa.”

TIKALEPHERA KUSONYEZA KUDZILETSA

Nthawi zina timalephera kusonyeza kudziletsa. Zikatero, mwina tingachite manyazi kupemphera kwa Yehova. Koma nthawiyi ndi yomwe timafunika kwambiri kupemphera kwa iye. Choncho tizipemphera nthawi yomweyo. Tiyenera tizimupempha kuti atikhululukire komanso atithandize, ndipo tiziyesetsa kuti tisadzachitenso zimene tinalakwitsazo. (Sal. 51:9-11) Yehova sanganyalanyaze pemphero lathu lomupempha kuti atichitire chifundo. (Sal. 102:17) Mtumwi Yohane anatikumbutsa kuti magazi a Mwana wa Mulungu ‘amatiyeretsa ku uchimo wonse.’ (1 Yoh. 1:7; 2:1; Sal. 86:5) Tizikumbukiranso kuti Yehova amauza atumiki ake kuti azikhululukira ena mobwerezabwereza. Choncho tisamakayikire kuti nayenso adzachita chimodzimodzi ndi ife.​—Mat. 18:21, 22; Akol. 3:13.

Yehova sanasangalale Mose atalephera kudziletsa. Komabe, iye anamukhululukira. Ndipo Mawu a Mulungu amanena kuti Mose ndi chitsanzo cha munthu wokhulupirika. (Deut. 34:10; Aheb. 11:24-28) Yehova sanalole kuti Mose alowe m’Dziko Lolonjezedwa koma adzamulola kukhala m’Paradaiso padzikoli ndipo adzamupatsa mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Ifenso tikhoza kukhala ndi mwayi ngati umenewu tikamayesetsa kusonyeza khalidwe lofunika kwambiri la kudziletsa.​—1 Akor. 9:25.