Mafunso Ochokera Kwa Owerenga
Kodi makhalidwe amene “mzimu woyera umatulutsa,” ndi okhawo amene atchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23?
Mavesi amenewa amatchula makhalidwe okwana 9. Mavesiwa amati: “Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.” Koma amenewa si makhalidwe onse amene mzimu woyera ungatithandize kukhala nawo.
Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Asanatchule makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ntchito za thupi . . . ndizo dama, zinthu zodetsa, khalidwe lotayirira, kupembedza mafano, kuchita zamizimu, udani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, kaduka, kumwa mwauchidakwa, maphwando aphokoso, ndi zina zotero.” (Agal. 5:19-21) Apa Paulo anamaliza ndi mawu akuti “ndi zina zotero,” kusonyeza kuti sanatchule zinthu zonse zomwe zili m’gulu la “ntchito za thupi” zomwe zinatchulidwanso pa Akolose 3:5. Mofanana ndi zimenezi, atamaliza kutchula makhalidwe 9 amene mzimu umatulutsa analemba kuti: “Palibe lamulo loletsa zinthu zoterezi.” Choncho Paulo sanatchule makhalidwe onse abwino amene mzimu woyera ungatithandize kuti tikhale nawo.
Zimenezi zikuonekera bwino tikayerekezera makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsawa ndi zimene Paulo analembera Akhristu a mumpingo wa Efeso. Iye analemba kuti: “Zipatso za kuwala ndizo chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama ndi choona.” (Aef. 5:8, 9) Lembali likusonyeza kuti “ubwino” kuphatikizapo chilungamo ndi choonadi ndi zina mwa “zipatso za kuwala” komansotu paja limeneli ndi limodzi mwa “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.”
Komanso tingamvetse bwino zimenezi tikayekezera makhalidwe amene mzimu umatulutsa ndi makhalidwe 6 amene Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti ayenera kukhala nawo. Iye anamuuza kuti: “Tsatira chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro ndi kufatsa.” (1 Tim. 6:11) Pa makhalidwewa ndi atatu okha amene akutchulidwanso pa makhalidwe amene “mzimu woyera umatulutsa.” Makhalidwe ake ndi chikhulupiriro, chikondi ndi kufatsa. Koma Timoteyo ankafunika kuthandizidwanso ndi mzimu woyera kuti akhale ndi makhalidwe enanso amene atchulidwa monga chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu ndi chipiriro.—Yerekezerani Akolose 3:12; 2 Petulo 1:5-7.
Choncho lemba la Agalatiya 5:22, 23, silinatchule makhalidwe onse amene Akhristu ayenera kukhala nawo. N’zoona kuti mzimu wa Mulungu ungatithandize kuti tikhale ndi makhalidwe 9 omwe atchulidwa kuti ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” Koma pali makhalidwe enanso ambiri amene tiyenera kukhala nawo kuti tikule mwauzimu komanso kuti tivale “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.”—Aef. 4:24