NKHANI YOPHUNZIRA 14
Akulu, Pitirizani Kutsanzira Mtumwi Paulo
“Muzitsanzira ine.”—1 AKOR. 11:1.
NYIMBO NA. 99 Khamu la Abale
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. Kodi chitsanzo cha mtumwi Paulo chingathandize bwanji akulu masiku ano?
MTUMWI Paulo ankakonda abale ake ndipo ankagwira ntchito mwakhama kuti awathandize. (Mac. 20:31) Zimenezi zinachititsa kuti abale ndi alongo ake nawonso azimukonda kwambiri. Pa nthawi ina akulu a ku Efeso “analira kwambiri” atamva kuti sadzaonana nayenso. (Mac. 20:37) Akulu odzipereka nawonso amakonda abale ndi alongo awo ndipo amachita zonse zomwe angathe powathandiza. (Afil. 2:16, 17) Koma nthawi zina akulu amakumana ndi mavuto ena. Ndiye kodi n’chiyani chingawathandize kulimbana ndi mavuto amenewa?
2 Akulu akhamawa ayenera kuganizira chitsanzo cha Paulo. (1 Akor. 11:1) Iye sanali munthu wapadera, chifukwa sanali wangwiro ndipo nthawi zina ankavutika kuchita zabwino. (Aroma 7:18-20) Nthawi zinanso ankafunika kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana. Koma zimenezi sizinamuchititse kutaya mtima kapenanso kuti asamasangalale. Akulu akamatsanzira Paulo, angathe kulimbana ndi mavuto amene amakumana nawo n’kupitirizabe kukhala osangalala akamatumikira Yehova. Tiyeni tione mmene angachitire zimenezi.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi, nanga kuchita zimenezi kutithandiza bwanji?
3 Munkhaniyi tikambirana mavuto 4 omwe akulu amakumana nawo nthawi zambiri: (1) kugawa nthawi kuti azitha kugwira nawo ntchito yolalikira komanso ntchito zina, (2) kupeza nthawi yolimbikitsa abale ndi alongo awo, (3) kufooka chifukwa cha zinthu zimene amalakwitsa komanso (4) kuchita zinthu ndi anthu omwe si angwiro. Tionanso zimene Paulo anachita polimbana ndi lililonse mwa mavuto amenewa komanso mmene akulu angamutsanzirire.
KUGAWA NTHAWI KUTI AZILALIKIRA KOMANSO KUGWIRA NTCHITO ZINA
4. N’chifukwa chiyani nthawi zina akulu zingawavute kutsogolera pa ntchito yolalikira?
4 Chifukwa chake kuchita zimenezi kungakhale kovuta. Akulu ali ndi maudindo ambiri kuwonjezera pa kutsogolera pa ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, ambiri amachititsa misonkhano ya mkati mwa mlungu komanso Phunziro la Baibulo la Mpingo. Iwo amakambanso nkhani zina pamisonkhano. Amachita khama kuphunzitsa atumiki othandiza ndipo amasangalala kulimbikitsa abale ndi alongo awo nthawi ndi nthawi. (1 Pet. 5:2) Akulu ena amathandiza pa ntchito yomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu komanso malo ena olambirira. Komabe mofanana ndi onse mumpingo, akulu amakhala patsogolo pogwira ntchito yolalikira uthenga wabwino.—Mat. 28:19, 20.
5. Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yolalikira?
5 Chitsanzo cha Paulo. Mfundo imene inamuthandiza Paulo kuti azigwira bwino ntchito yake, ikupezeka pa Afilipi 1:10, pomwe iye anatilimbikitsa kuti: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” Iye ankatsatira malangizo omwe anaperekawa. Anali atapatsidwa utumiki woti achite ndipo kwa zaka zambiri ankaona utumikiwo monga chinthu chofunika kwambiri. Ankalalikira “poyera komanso kunyumba ndi nyumba.” (Mac. 20:20) Paulo sankangolalikira pa nthawi inayake kapena pa tsiku linalake pa mlungu. M’malomwake ankalalikira pa mpata uliwonse umene wapezeka. Mwachitsanzo, pamene ankayembekezera anzake ku Atene, iye analalikira uthenga wabwino kwa anthu ena otchuka ndipo ena mwa anthuwo anamvetsera uthenga wake. (Mac. 17:16, 17, 34) Ngakhale pamene ‘anamangidwa,’ Paulo ankalalikira kwa anthu amene ankakhala pafupi naye.—Afil. 1:13, 14; Mac. 28:16-24.
6. Kodi Paulo anaphunzitsa ena kuchita chiyani?
6 Paulo ankagwiritsa ntchito bwino nthawi yake. Iye nthawi zambiri ankapempha ena kuti azilalikira naye limodzi. Mwachitsanzo, pa ulendo wake woyamba waumishonale anatenga Yohane Maliko, ndipo pa ulendo wachiwiri anatenga Timoteyo. (Mac. 12:25; 16:1-4) N’zosakayikitsa kuti Paulo anayesetsa kuphunzitsa amunawa mmene angayendetsere zinthu mumpingo, kuchita maulendo aubusa komanso kukhala aphunzitsi abwino.—1 Akor. 4:17.
7. Kodi akulu angatsatire bwanji malangizo a Paulo opezeka pa Aefeso 6:14, 15?
7 Phunziro. Akulu angatsanzire Paulo, osati pongolalikira kunyumba ndi nyumba, koma pokhala okonzeka kulalikiranso pa mpata uliwonse. (Werengani Aefeso 6:14, 15.) Mwachitsanzo, iwo angalalikire pamene apita kogula zinthu kapena kuntchito kwawo. Kapenanso pamene akuthandiza pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, angalalikire kwa anthu okhala pafupi ndi pamalopo komanso ogulitsa malonda. Mofanana ndi Paulo, akulu angagwiritse ntchito nthawi yomwe alowa mu utumiki pophunzitsa ena kuphatikizapo atumiki othandiza.
8. Kodi nthawi zina mkulu angafunike kuchita chiyani?
8 Akulu ayenera kupewa kumatanganidwa kwambiri ndi ntchito zampingo kapena zadera mpaka kufika pomasowa nthawi yolalikira. Kuti azigawa bwino nthawi yawo, nthawi zina angafunike kukana kuchita mautumiki ena. Pambuyo poganizira komanso kupempherera utumiki womwe apatsidwawo, angazindikire kuti ngati atavomera utumikiwo sangakwanitse kusamalira zinthu zina zofunika kwambiri. Zinthu zofunikazi zikuphatikizapo kuchita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse, kugwira nawo mokwanira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa ana awo kulalikira. Ena zimawavuta kukana utumiki womwe apatsidwa. Koma iwo ayenera kukhala otsimikiza kuti Yehova amamvetsa kuti akufuna kugawa bwino nthawi yawo.
KULIMBIKITSA ABALE NDI ALONGO
9. Kodi akulu, omwe amakhala otanganidwa, amakumana ndi vuto liti?
9 Chifukwa chake zingakhale zovuta. Anthu a Yehova akukumana ndi mavuto ambiri. Masiku otsiriza ano, tonsefe timafunika kulimbikitsidwa, kuthandizidwa komanso kutonthozedwa. Nthawi zinanso anthu ena amafunika kuthandizidwa kuti apewe kuchita zoipa. (1 Ates. 5:14) N’zoona kuti akulu sangathetse mavuto onse amene anthu a Yehova amakumana nawo. Ngakhale zili choncho, Yehova amafuna kuti akulu aziyesetsa kulimbikitsa komanso kuteteza nkhosa zake. Ndiye kodi akulu omwe amakhala kale ndi zochita zambiri angapeze bwanji nthawi yothandiza abale ndi alongo?
10. Mogwirizana ndi 1 Atesalonika 2:7, kodi Paulo ankasamalira bwanji anthu a Mulungu?
10 Chitsanzo cha Paulo. Nthawi zonse Paulo ankayesetsa kuyamikira abale ake komanso kuwalimbikitsa. Akulunso angachite bwino kutengera chitsanzo chake pokonda abale komanso kuwakomera mtima. (Werengani 1 Atesalonika 2:7.) Paulo anatsimikizira Akhristu anzake kuti amawakonda komanso kuti Yehova amawakondanso. (2 Akor. 2:4; Aef. 2:4, 5) Ankaona anthu a mumpingo ngati anzake ndipo ankapeza nthawi yocheza nawo. Iye anasonyeza kuti ankawadalira powauza momasuka zimene zinkamudetsa nkhawa komanso zofooka zake. (2 Akor. 7:5; 1 Tim. 1:15) Komabe iye sankangokhalira kuganizira za mavuto ake. M’malomwake ankafuna kuthandiza abale ake.
11. N’chifukwa chiyani Paulo ankapereka malangizo kwa abale ndi alongo ake?
11 Nthawi zina Paulo ankafunika kupereka malangizo kwa abale ndi alongo ake. Koma sankachita zimenezi chifukwa choti wakwiya. Iye ankawapatsa malangizo chifukwa chowakonda, ndipo ankafuna kuwateteza ku zinthu zosiyanasiyana. Ankapereka malangizo omveka bwino ndipo ankafuna kuti anthuwo awalandire. Mwachitsanzo, m’kalata yake imene analembera Akhristu a ku Korinto, Paulo anawapatsa malangizo amphamvu. Pambuyo powalembera kalatayi, anawatumiziranso Tito. Ankafunitsitsa kudziwa mmene anthuwo alandirira malangizo ake. Paulo anasangalalatu kwambiri atadziwa kuti anthuwo analandira malangizowo n’kuwatsatira.—2 Akor. 7:6, 7.
12. Kodi akulu angalimbikitse bwanji Akhristu anzawo?
12 Phunziro. Akulu angatsanzire Paulo popeza nthawi yomacheza ndi Akhristu anzawo. Njira ina imene angachitire zimenezi ndi kufika mofulumira pamisonkhano n’cholinga choti azicheza ndi kulimbikitsa ena. Nthawi zambiri pamangofunika maminitsi ochepa chabe kuti tilankhule zinthu zomwe zingalimbikitse m’bale kapena mlongo. (Aroma 1:12; Aef. 5:16) Mkulu yemwe amatengera chitsanzo cha Paulo, amalimbitsanso chikhulupiriro cha Akhristu anzake pogwiritsa ntchito Baibulo komanso amawatsimikizira kuti Mulungu amawakonda. Kuwonjezera pamenepo, iye amawathandiza kuzindikira kuti amawakonda. Amalankhula nawo pafupipafupi ndipo amayesetsa kuwayamikira. Pamene mkuluyo akufunika kupereka malangizo, amaonetsetsa kuti achokera m’Mawu a Mulungu. Iye amapereka malangizo mosapita m’mbali koma mokoma mtima chifukwa amafuna kuti abale ndi alongowo awalandire.—Agal. 6:1.
KULIMBANA NDI ZIMENE AMALAKWITSA
13. Kodi mkulu angamamve bwanji chifukwa cha zimene amalakwitsa?
13 Chifukwa chake zingakhale zovuta. Akulu si angwiro. Choncho mofanana ndi wina aliyense, nawonso amalakwitsa zinthu. (Aroma 3:23) Nthawi zina zingamawavute kukhala ndi maganizo oyenera pa zimene amalakwitsa. Penanso angafooke chifukwa choganizira kwambiri zimene sangakwanitse kuchita. Enanso angamadzikhululukire pa zimene amalakwitsa, zomwe zingachititse kuti asaone kufunika kosintha zinthu zina pa moyo wawo.
14. Mogwirizana ndi Afilipi 4:13, kodi kudzichepetsa kunathandiza bwanji Paulo kulimbana ndi zimene ankalakwitsa?
14 Chitsanzo cha Paulo. Modzichepetsa, Paulo anazindikira kuti payekha sakanatha kulimbana ndi zofooka zake. Iye ankafunikira mphamvu zimene Mulungu amapereka. Poyamba, iye ankadzipereka kwambiri pozunza Akhristu. Koma kenako anazindikira kulakwa kwake, ndipo anali wofunitsitsa kusintha mmene ankaonera zinthu komanso makhalidwe ake. (1 Tim. 1:12-16) Mothandizidwa ndi Yehova, Paulo anakhala m’busa wachikondi, wachifundo komanso wodzichepetsa. Iye ankadziwa kuti ankalakwitsa zinthu zambiri koma sankangoganizira zimenezo chifukwa ankakhulupirira kuti Yehova amukhululukira. (Aroma 7:21-25) Sankayembekezera kuti azichita zinthu zonse mosalakwitsa. M’malomwake ankayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino ndipo modzichepetsa ankadalira Yehova kuti amuthandize kukwaniritsa utumiki wake.—1 Akor. 9:27; werengani Afilipi 4:13.
15. Kodi akulu angatani kuti aziona moyenera zinthu zomwe amalakwitsa?
15 Phunziro. Akulu saikidwa pa udindo chifukwa choti ndi angwiro. Komabe Yehova amayembekezera kuti iwo azivomereza zimene amalakwitsa n’kumayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. (Aef. 4:23, 24) Mkulu ayenera kudzifufuza pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu n’kusintha pamene akufunika kutero. Akatero Yehova angamuthandize kuti azisangalala komanso azichita bwino utumiki wake.—Yak. 1:25.
KUCHITA ZINTHU NDI ANTHU OMWE SI ANGWIRO
16. Kodi chingachitike n’chiyani ngati mkulu amangoganizira zimene ena amalakwitsa?
16 Chifukwa chake zingakhale zovuta. Akulu angamadziwe zimene abale ndi alongo mumpingo amalakwitsa chifukwa choti nthawi zambiri amachita nawo zinthu limodzi. Ndiye ngati sangasamale akhoza kukhumudwa nawo, kuwachitira zinthu mopanda chifundo kapena kuwaweruza. Paulo anachenjeza Akhristu kuti zimenezi ndi zomwe Satana amafuna kuti iwo azichita.—2 Akor. 2:10, 11.
17. Kodi Paulo ankawaona bwanji abale ndi alongo ake?
17 Chitsanzo cha Paulo. Iye nthawi zonse ankaona moyenera abale ndi alongo ake. Ankadziwa zimene ankalakwitsa, chifukwa nthawi zina zochita zawo zinkamukhumudwitsa. Komabe Paulo ankadziwa kuti munthu akalakwitsa zina zake sizitanthauza kuti ndi woipa. Iye ankawakonda abale ake ndipo ankaganizira kwambiri makhalidwe awo abwino. Iwo akamavutika kuchita zoyenera, iye ankaona kuti zolinga zawo ndi zabwino koma kuti ankangofunika kuthandizidwa.
18. Kodi tikuphunzira chiyani poona mmene Paulo anathandizira Eodiya ndi Suntuke? (Afilipi 4:1-3)
18 Taganizirani mmene Paulo anathandizira alongo awiri a mumpingo wa ku Filipi. (Werengani Afilipi 4:1-3.) Zikuoneka kuti Eodiya ndi Suntuke, analola kuti kusiyana maganizo pa zinthu zina kuwagawanitse. Paulo sanawachitire zinthu mopanda chifundo kapena kuwaweruza. M’malomwake ankaganizira kwambiri makhalidwe awo abwino. Iwo anali alongo okhulupirika omwe anatumikira Yehova kwa nthawi yaitali. Paulo ankadziwa kuti Yehova ankawakonda. Popeza kuti ankawaona moyenera, iye analimbikitsa alongowa kuti athetse kusamvana kwawo. Kuganizira kwambiri makhalidwe abwino a ena, kunamuthandiza kuti azikhala wosangalala komanso azigwirizana kwambiri ndi anthu a mumpingowo.
19. (a) Kodi akulu angatani kuti aziona moyera Akhristu anzawo? (b) Kodi mukuphunzira chiyani pachithunzi chomwe chikusonyeza mkulu akugwira nawo ntchito yoyeretsa m’Nyumba ya Ufumu?
19 Phunziro. Akulu, muziona makhalidwe abwino omwe abale ndi alongo anu ali nawo. Tonsefe si angwiro, komabe aliyense ali ndi makhalidwe enaake abwino. (Afil. 2:3) N’zoona kuti nthawi ndi nthawi akulu amafunika kupereka malangizo kwa m’bale kapena mlongo. Koma mofanana ndi Paulo, iwo ayenera kuyesetsa kuti asamaganizire kwambiri zochita ndi mawu okhumudwitsa amene munthuyo walankhula. M’malomwake iwo angachite bwino kumaganizira kwambiri mmene munthuyo amakondera Yehova, kupirira kwake pomutumikira komanso kuti akhoza kuchita zabwino. Akulu omwe amaona moyenera abale ndi alongo awo, amawathandiza kuona kuti onse mumpingo amawakonda.
PITIRIZANI KUTSANZIRA PAULO
20. Kodi akulu angatani kuti apitirize kupindula ndi chitsanzo cha Paulo?
20 Akulunu, mungapindule kwambiri mukapitiriza kuphunzira zokhudza Paulo. Mwachitsanzo, mu Watch Tower Publications Index mukhoza kufufuza pamutu wakuti “Paul” kenako pakamutu kakuti, “example for elders.” Mukamawerenga magazini ena omwe atchulidwa pamenepo muzidzifunsa kuti: ‘Kodi chitsanzo cha Paulo chingandithandize bwanji kuti ndizisangalalabe pamene ndikukwaniritsa udindo wanga monga mkulu?’
21. Kodi akulu ayenera kumakumbukira chiyani?
21 Akulu, muzikumbukira kuti Yehova sayembekezera kuti mukhale angwiro, koma amafuna kuti mukhale okhulupirika. (1 Akor. 4:2) Yehova ankasangalala ndi Paulo chifukwa choti ankagwira ntchito mwakhama komanso anali wokhulupirika. Inunso musamakayikire kuti Mulungu amasangalala ndi zomwe mukuchita pomutumikira. Yehova sadzaiwala “ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikira oyera ndipo mukupitiriza kuwatumikira.”—Aheb. 6:10.
NYIMBO NA. 87 Bwerani Mudzasangalale
^ ndime 5 Timayamikira kwambiri akulu achikondi chifukwa cha khama lomwe amasonyeza potisamalira. Munkhaniyi tikambirana mavuto 4 omwe akulu amakumana nawo nthawi zambiri. Tionanso mmene chitsanzo cha Paulo chingawathandizire masiku ano polimbana ndi mavuto amenewa. Nkhaniyi itithandiza kuti tiziwamvetsa ndiponso itilimbikitsa kuti tiziwasonyeza chikondi komanso kuwathandiza kuti azigwira ntchito yawo mosavuta.
^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pamene m’bale akuweruka, akulalikira mnzake wogwira naye ntchito.
^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu akulimbikitsa mokoma mtima m’bale yemwe amakonda kukhala payekha.
^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akupereka malangizo othandiza kwa m’bale wina yemwe wakhumudwa chifukwa cha zomwe zachitika.
^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu sakuweruza m’bale yemwe wasokonezedwa ndi zinthu zina n’kusiya ntchito yomwe wadzipereka kugwira.