Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziimba Mosangalala

Tiziimba Mosangalala

“Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda n’kwabwino.”​—SAL. 147:1.

NYIMBO: 9, 138

1. Kodi nyimbo zimatithandiza bwanji?

MUNTHU wina wotchuka amene amapeka nyimbo ananena kuti mawu ongolankhulidwa komanso nyimbo zoimbidwa ndi zida zokha zikhoza kufika munthu pamtima. Koma nyimbo zokhala ndi mawu ndi zimene zimafika kwambiri munthu pamtima. Palibe mawu a m’nyimbo amene tingafune kuti atifike pamtima kuposa mawu amene ali m’nyimbo zotamanda Atate wathu wakumwamba. M’pake kuti kuimba nyimbo patokha kapena ndi mpingo n’kofunika kwambiri polambira Yehova.

2, 3. (a) Kodi anthu ena angaone bwanji kuimba nyimbo mokweza mumpingo? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Koma kodi inuyo mumakonda kuimba mokweza mumpingo, kapena mumachita manyazi? M’zikhalidwe zina, amuna sakonda kuimba pa gulu. Koma ngati anthu amene akutsogolera mumpingo saimba mokweza kapena ngati amatanganidwa ndi zinthu zina pamene nyimbo zikuimbidwa, zimasokoneza mpingo wonse.​—Sal. 30:12.

3 Ngati timaona kuti kuimba nyimbo n’kofunika kwambiri polambira Yehova, tiyenera kuyesetsa kupezeka pa nthawi imene nyimbo zikuimbidwa ndipo tisamatuluke. Choncho tonse tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimakonda kuimba nyimbo pamisonkhano yathu? Nanga ndingatani kuti ndisamachite manyazi kuimba mosangalala komanso kuti ndiziimba ndi mtima wonse?’

KUIMBA NDI KOFUNIKA KWAMBIRI POLAMBIRA YEHOVA

4, 5. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Aisiraeli ankaona kuti kuimba nyimbo n’kofunika kwambiri polambira Yehova?

4 Kuyambira kalekale, atumiki okhulupirika a Yehova akhala akuimba nyimbo pomutamanda. Chochititsa chidwi n’chakuti pamene Aisiraeli ankalambira Yehova mokhulupirika, kuimba nyimbo zotamanda Yehova kunkakhalanso kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, pokonzekera utumiki umene unkachitika kukachisi, Davide anakonza zoti pakhale Alevi 4,000 oimba nyimbo zotamanda Yehova. Ndipo pa anthu amenewa, anthu 288 anali ‘akatswiri ophunzitsidwa kuimbira Yehova.’​—1 Mbiri 23:5; 25:7.

5 Pamwambo wotsegulira kachisi, panaimbidwa nyimbo zambiri. Baibulo limanena kuti: ‘Anthu oimba malipenga ndi oimba pakamwa anayamba kuimba mogwirizana n’kumamveka ngati mawu amodzi otamanda ndi kuthokoza Yehova. Komanso anayamba kuimba ndi malipenga, zinganga, ndi zoimbira zina potamanda Yehova ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu woona.’ Zimenezi ziyenera kuti zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha Aisiraeliwo.​—2 Mbiri 5:13, 14; 7:6.

6. Fotokozani zimene Nehemiya anakonza pa nkhani ya nyimbo pa nthawi imene anali bwanamkubwa ku Yerusalemu.

6 Pa nthawi imene Nehemiya ankatsogolera Aisiraeli okhulupirika pomanga mpanda wa Yerusalemu, anakonza zoti pakhale Alevi oimba nyimbo limodzi ndi zida zosiyanasiyana zoimbira. Pamwambo wotsegulira mpandawu, nyimbo zimene zinaimbidwa zinathandiza kwambiri kuti mwambowu ukhale wosangalatsa. Pamwambowu panali “magulu akuluakulu awiri oimba nyimbo zoyamika.” Maguluwa ankayenda pamwamba pa mpandawu kulowera mbali ziwiri zosiyana ndipo anakumana pafupi ndi kachisi. Iwo ankaimba mokweza kwambiri moti nyimbo zawo zinkamveka kutali. (Neh. 12:27, 28, 31, 38, 40, 43) Yehova ayenera kuti anasangalala kwambiri kumva atumiki ake akumuimbira nyimbo mosangalala.

7. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti kuimba nyimbo n’kofunika polambira Mulungu?

7 Mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa, nyimbo zinalinso zofunika kwambiri polambira Yehova. Pa tsiku lofunika kwambiri m’mbiri ya anthu, lomwe Yesu anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, anaimbanso nyimbo ndi atumwi ake.​—Werengani Mateyu 26:30.

8. Kodi Akhristu oyambirira anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yoimba nyimbo?

8 Akhristu oyambirira ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yoimba nyimbo zotamanda Mulungu. Ngakhale kuti nthawi zambiri ankasonkhana m’nyumba za anthu, ankaimbira Yehova mosangalala kwambiri. Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Pitirizani kuphunzitsana ndi kulangizana mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwira mtima. Pitirizani kuimbira Yehova m’mitima yanu.” (Akol. 3:16) Nyimbo zimene zili m’buku lathu la nyimbo ndi “zauzimu” ndipo tiyenera kuziimba mochokera pansi pa mtima. Nyimbozi ndi mbali ya chakudya chauzimu chimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka.​—Mat. 24:45.

KODI MUNGATANI NGATI MUMACHITA MANYAZI KUIMBA NYIMBO?

9. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zimalepheretsa anthu ena kuimba mosangalala pamisonkhano? (b) Kodi tingatani kuti tiziimba bwino nyimbo zotamanda Yehova, nanga ndani ayenera kutsogolera? (Onani chithunzi choyambirira.)

9 Kodi mungatani ngati anthu achikhalidwe chanu kapena a m’banja lanu sakonda kuimba nyimbo? N’kutheka kuti mumakonda kumvetsera nyimbo zoimbidwa ndi akatswiri, kaya ndi pa wailesi, pa foni kapena pa chipangizo china. Koma mwina mumachita manyazi kapena kudzikayikira mukayerekezera mawu anu ndi mawu a akatswiriwo. Zimenezi siziyenera kukulepheretsani kukwaniritsa udindo wanu wotamanda Yehova pomuimbira nyimbo. Chongofunika ndi kutenga nyimbo yanu n’kuikweza m’mwamba, kudzutsa bwino mutu wanu, n’kumaimba kuchokera pansi pa mtima. (Ezara 3:11; werengani Salimo 147:1.) Masiku ano, m’Nyumba za Ufumu zina mumakhala masikirini osonyeza mawu a nyimbo ndipo izi zimathandiza kuti anthu azikweza bwino mitu yawo poimba. N’zosangalatsanso kuti masiku ano pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu imene akulu amakhala nayo, pamakhalanso nthawi yoimba nyimbo. Zimenezi zikusonyeza kuti akulu ayenera kutsogolera mpingo pa nkhani yoimba.

10. Ngati timaopa kuimba mokweza, kodi tiyenera kukumbukira mfundo iti?

10 Anthu ena saimba mokweza chifukwa cha mantha. Amaopa kuti azimveka kwambiri kapena kuti anthu ena sangasangalale ndi mawu awo. Tizikumbukira kuti “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri” tikamalankhula. (Yak. 3:2) Koma palibe amene amasiya kulankhulako. Choncho si bwino kusiya kutamanda Yehova chifukwa choganiza kuti mawu athu samveka bwino.

11, 12. Tchulani mfundo zina zimene zingatithandize kuti tiziimba bwino.

11 Mwina sitikonda kuimba mokweza chifukwa choganiza kuti sititha kuimba. Koma tikhoza kuphunzira kuimba ngati titatsatira mfundo zingapo. *

12 Kapumidwe kabwino kamathandiza kuti munthu aziimba mokweza komanso mwamphamvu. Mpweya ndi umene umathandiza munthu kuti alankhule kapena kuimba bwino ndipo izi tingaziyerekezere ndi mmene magetsi amathandizira kuti mababu aziwala. Choncho mukamaimba, muzikweza mawu mmene mumalankhulira mwinanso kuposa pamenepo. (Mfundo zina zothandiza mungazipeze m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, tsamba 181 mpaka 184 pakamutu kakuti “Kapumidwe Koyenera.”) Ndipotu malemba ena amatilimbikitsa kuti ‘tizifuula mosangalala’ poimbira Yehova.​—Sal. 33:1-3.

13. Kodi mungachite zinthu zina ziti kuti muzitha kuimba bwino?

13 Tayesani kuchita izi pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja kapena mukakhala panokha: Sankhani nyimbo yomwe imakusangalatsani kwambiri m’buku lathu la nyimbo. Werengani mawu ake mokweza komanso mwamphamvu. Kenako tchulani mawu amumzere winawake ndi mphamvu yomweyo koma popanda kupumira. Kenako imbani mawu amumzerewo mwamphamvu komanso mokweza. (Yes. 24:14) Mukatero mudzatha kuimba mokweza ndipo simuyenera kuchita mantha kapena manyazi.

14. (a) Kodi kutsegula pakamwa mokwanira kumathandiza bwanji poimba? (Onani bokosi lakuti “ Zimene Mungachite Kuti Muziimba Bwino.”) (b) Kodi n’chiyani chimakuthandizani inuyo kuti muziimba bwino?

14 Kuti muzitha kuimba mokweza, muyenera kutsegula pakamwa panu mokwanira. Choncho poimba muyenera kutsegula kwambiri pakamwa kuposa mmene mumachitira polankhula. Nanga kodi mungatani ngati mumaona kuti mawu anu ndi ofooka kapena aang’ono kwambiri? Mfundo zothandiza mungazipeze m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, tsamba 184 pakabokosi kakuti “Kuthana ndi Mavuto Ena.”

TIZIIMBIRA YEHOVA NDI MTIMA WONSE

15. (a) Kodi pamsonkhano wapachaka wa 2016 panali chilengezo chotani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani buku la nyimbo linasinthidwa?

15 Pamsonkhano wapachaka wa mu 2016, anthu anasangalala kwambiri pamene M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira analengeza za buku latsopano la nyimbo. Iye analengeza kuti buku la mutu wakuti Imbirani Yehova Mosangalala lituluka posachedwapa. M’bale Lett anafotokoza kuti buku la nyimbo linasinthidwa n’cholinga choti mawu a nyimbo afanane ndi mawu a mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lokonzedwanso, limene linatuluka mu 2013. Choncho mawu ena amene ankapezeka m’Baibulo lakale anachotsedwa kapena kusinthidwa kuti agwirizane ndi Baibulo lokonzedwanso. Komanso m’bukuli muli nyimbo zatsopano zokhudza ntchito yathu yolalikira ndiponso zosonyeza kuti timayamikira dipo. Popeza kuimba ndi kofunika kwambiri polambira Yehova, Bungwe Lolamulira linkafunanso kuti buku la nyimbo likhale ndi chikuto chofanana ndi Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso.

16, 17. Kodi ndi zinthu ziti zimene zasinthidwa m’buku la nyimbo latsopano?

16 Kuti tisamavutike kupeza nyimbo, m’buku latsopanoli anasanja nyimbo potsatira nkhani zotchulidwa m’nyimbozo. Mwachitsanzo, nyimbo 12 zoyambirira zimanena za Yehova ndipo nyimbo 8 zotsatira zimanena za Yesu komanso dipo. Mulinso mlozera nkhani amene angathandize ngati munthu akufuna kusankha nyimbo yogwirizana ndi nkhani ya onse kapena yoimba pa zochitika zina.

17 Pofuna kuthandiza anthu kuti aziimba mochokera pansi pa mtima, mawu ena asinthidwa kuti akhale osavuta kumva ndipo mawu achikale achotsedwa. Mwachitsanzo, mawu oti “kudza” anawasintha chifukwa sagwiritsidwa ntchito kwambiri masiku ano. Komanso mutu wa nyimbo yakuti “Mgonero wa Ambuye” wasinthidwa kukhala “Chakudya Chamadzulo cha Ambuye” ndipo mawu ena a m’nyimboyi asinthidwanso. Asinthanso mutu wakuti “Tetezani Mtima Wanu” kukhala “Timateteza Mtima Wathu” ndipo mawu ena m’nyimboyi awasinthanso kuti agwirizane ndi mutuwo. Asintha mutuwu chifukwa chakuti pamisonkhano yathu pamakhala anthu atsopano, achidwi, achinyamata ndiponso alongo omwe sangafune kukhala ngati akulangiza anthu ena poimba mawu akuti, “Tetezani mtima wanu.”

Muziyeserera kuimba nyimbo mukamachita Kulambira kwa Pabanja (Onani ndime 18)

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuzidziwa bwino nyimbozi?

18 Nyimbo zambiri za m’buku latsopano lakuti Imbirani Yehova Mosangalala zinalembedwa kuti zikhale ngati mapemphero. Nyimbo zimenezi zikuthandizani kuti muziuza Yehova zimene zili mumtima mwanu. Nyimbo zina ‘zimatilimbikitsa pa chikondi ndi ntchito zabwino.’ (Aheb. 10:24) Tiyenera kuyesetsa kuzidziwa bwino ndipo tikhoza kuchita zimenezi pomvetsera nyimbozi pa jw.org. Tikamayeserera nyimbozi kunyumba, tingathe kumaimba ndi mtima wonse popanda kudzikayikira. *

19. Kodi aliyense mumpingo ayenera kuchita chiyani polambira Yehova?

19 Tisaiwale kuti kuimba ndi kofunika kwambiri polambira Yehova. Zili choncho chifukwa ndi njira yabwino kwambiri yosonyezera kuti timamukonda ndiponso kumuyamikira. (Werengani Yesaya 12:5.) Mukamaimba mosangalala, mudzalimbikitsa anthu ena kuti nawonso aziimba ndi mtima wonse. Aliyense mumpingo, kaya achinyamata, achikulire komanso atsopano akhoza kulambira Yehova pomuimbira nyimbo. Choncho tiyeni tisamachite manyazi poimbira Yehova mosangalala. Tizichita zimenezi pomvera malangizo omveka bwino a wolemba salimo akuti: “Imbirani Yehova.”​—Sal. 96:1.

^ ndime 11 Kuti mudziwe mfundo zambiri zothandiza kuti muziimba bwino, onerani pulogalamu yachingelezi ya JW Broadcasting ya December 2014. (Ikupezeka pamene palembedwa kuti FROM OUR STUDIO.)

^ ndime 18 Pofuna kutithandiza kukhala ndi mtima wofuna kuimba, msonkhano wadera kapena wachigawo umayamba ndi kumvetsera nyimbo kwa 10 minitsi. Nyimbozi zimakonzedwa m’njira yoti zitithandize kukonzekeretsa mitima yathu kuti tipindule ndi nkhani zomwe zikambidwe. Choncho nyimbozi zikangoyamba, tingachite bwino kukhala m’mipando yathu n’kumamvetsera.