Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumathawira kwa Yehova?

Kodi Mumathawira kwa Yehova?

“Yehova amawombola moyo wa atumiki ake. Ndipo palibe aliyense wothawira kwa iye amene adzapezeka wolakwa.”​—SAL. 34:22.

NYIMBO: 8, 54

1. Kodi atumiki a Yehova ambiri amamva bwanji akalakwitsa zinazake?

MTUMWI PAULO anadandaula kuti: “Munthu wovutika ine!” (Aroma 7:24) Pali atumiki a Yehova ambirimbiri amene adandaulapo chonchi. Tonsefe tinatengera uchimo kwa makolo athu ndipo tikachita zinthu zimene tikudziwa kuti Mulungu sangasangalale nazo timavutika kwambiri mumtima. Akhristu ena amene anachita tchimo lalikulu amaganiza kuti Mulungu sangawakhululukirenso.

2. (a) Kodi lemba la Salimo 34:22 limasonyeza bwanji kuti atumiki a Mulungu sayenera kudziimba mlandu mopitirira malire? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi? (Onani bokosi lakuti “ Zimene Tikuphunzirapo Osati Zimene Zikuimira.”)

2 Koma Malemba amatitsimikizira kuti anthu amene amathawira kwa Yehova sayenera kudziimba mlandu mopitirira malire. (Werengani Salimo 34:22.) Koma kodi munthu angathawire bwanji kwa Yehova? Nanga ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuchita kuti Mulungu atichitire chifundo n’kutikhululukira? Kuti tipeze mayankho a mafunsowa, tiyeni tikambirane nkhani ya mizinda yothawirako ya ku Isiraeli. N’zoona kuti mizindayi inakhazikitsidwa potsatira Chilamulo chomwe chinalowedwa m’malo pamwambo wa Pentekosite mu 33 C.E., koma tisaiwale kuti Chilamulocho chinachokera kwa Yehova. Choncho nkhani ya mizinda yothawirako ingatithandize kudziwa mmene Yehova amaonera machimo, anthu ochimwa komanso kulapa. Koma choyamba, tiyeni tikambirane cholinga cha mizindayi komanso mmene ankaigwiritsira ntchito.

“SANKHANI MIZINDA YOTHAWIRAKO”

3. Kodi Aisiraeli ankachita chiyani ngati munthu wapha mnzake mwadala?

3 Yehova amaona kuti kupha munthu ndi mlandu waukulu kwambiri. Pa nthawi ya Aisiraeli, munthu akapha mnzake mwadala nayenso ankaphedwa ndi wachibale wamwamuna wa wophedwayo. Wachibaleyo ankadziwika kuti “Wobwezera magazi.” (Num. 35:19) Kupha munthu wolakwayo kunkathandiza kuti mlandu wopha munthu wosalakwa uphimbidwe. Kuchita zimenezi mwamsanga kunkathandiza kuti Dziko Lolonjezedwa lisaipitsidwe, chifukwa Yehova analamula kuti: ‘Musadetse dziko limene mukukhalamo, chifukwa kukhetsa magazi a anthu n’kumene kumadetsa dziko.’​—Num. 35:33, 34.

4. Kodi Aisiraeli ankachita chiyani ngati munthu wapha mnzake mwangozi?

4 Koma kodi Aisiraeli ankatani ngati munthu wapha mnzake mwangozi? Ngakhale munthu atachita zimenezo mwangozi, ankakhalabe ndi mlandu wopha munthu wosalakwa. (Gen. 9:5) Koma ankachitiridwa chifundo ndipo ankaloledwa kuti athawire kumzinda wothawirako kuti wobwezera magazi asamuphe. Akafika mumzindawo ankakhala wotetezeka ndipo ankafunika kukhalabe mumzindawo mpaka mkulu wa ansembe atafa.​—Num. 35:15, 28.

5. Kodi nkhani ya mizinda yothawirako ingatithandize kumvetsa zinthu ziti zokhudza Yehova?

5 Yehova ndi amene analamula Yoswa kuti asankhe mizinda yoti anthu azithawirako. Iye anamuuza kuti: “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Sankhani mizinda yothawirako.’” Mizindayo inkaonedwa kuti ndi “yopatulika.” (Yos. 20:1, 2, 7, 8) Popeza Yehova ndi amene analamula kuti pakhale mizinda imeneyi, tikhoza kufunsa kuti: Kodi nkhani ya mizinda yothawirako ingatithandize bwanji kumvetsa chifundo cha Yehova? Nanga ingatithandize bwanji kudziwa zimene tingachite kuti tithawire kwa Yehova masiku ano?

“AZIFOTOKOZA NKHANI YAKE KWA AKULU”

6, 7. (a) Kodi akulu ankakhala ndi udindo wotani ngati munthu wapha mnzake mwangozi? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) N’chifukwa chiyani kunali kupanda nzeru ngati munthu wopha mnzake mwangozi atanyalanyaza zopita kwa akulu?

6 Munthu amene wapha mnzake mwangozi akafika pageti lolowera mumzinda wothawirako, ankafunika ‘kufotokoza nkhani yake kwa akulu.’ Ndipo akuluwo ankafunika kumulandira bwino. (Yos. 20:4) Koma pakapita nthawi, ankamubweza kumzinda umene anaphera munthuyo kuti akulu amumzindawo aweruze mlandu wake. (Werengani Numeri 35:24, 25.) Oweruzawo akapeza kuti munthuyo anaphadi mnzake mwangozi ankamulola kuti abwerere kumzinda wothawirako kuja.

7 Kodi n’chifukwa chiyani ankafunika kufotokoza nkhani yake kwa akulu? Izi zinkathandiza kuti dziko la Isiraeli likhale losaipitsidwa komanso kuti munthu wopha mnzake mwangoziyo achitiridwe chifundo ndi Yehova. Katswiri wina wa Baibulo analemba kuti ngati munthu wopalamula mlanduyo sanapite kwa akulu “zinkamuvuta yekha.” Ananenanso kuti: “Ngati ataphedwa, linkakhala vuto lake chifukwa sanachite zonse zofunika kuti Mulungu amuteteze.” N’zoona kuti pankakhala njira yothandizira anthu oterewa koma anthuwo paokha ankafunika kuchitapo kanthu. Akapanda kuthawira kumzinda wothawirako ndiye kuti ankatha kuphedwa ndi wachibale wapafupi wa munthu amene anaphedwayo.

8, 9. N’chifukwa chiyani Mkhristu amene wachita tchimo lalikulu ayenera kufotokozera akulu?

8 Masiku ano, Mkhristu amene wachita tchimo lalikulu ayenera kufotokozera akulu kuti amuthandize. Kodi zimenezi ndi zofunika bwanji? Choyamba, Yehova ndi amene anakonza zoti akulu azitithandiza tikachimwa ndipo izi n’zogwirizana ndi zimene Mawu ake amanena. (Yak. 5:14-16) Chachiwiri, zimenezi zimapereka mwayi kwa wochimwayo kuti athandizidwe ndi Yehova komanso asakhale ndi chizolowezi chochimwa. (Agal. 6:1; Aheb. 12:11) Chachitatu, akulu anapatsidwa udindo komanso anaphunzitsidwa bwino kuti azitha kulimbikitsa munthu wochimwa amene walapa n’cholinga choti asamadziimbe mlandu kwambiri. Yehova ananena kuti akuluwo ali ngati “malo ousapo mvula yamkuntho.” (Yes. 32:1, 2) Kodi inuyo simukuvomereza kuti Mulungu anasonyeza chifundo pokonza zoti ochimwa azithandizidwa ndi akulu?

9 Atumiki a Yehova ambiri amene anachimwa n’kufotokozera akulu anathandizidwa ndipo mtima wawo unakhala m’malo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Daniel. Iye anachita tchimo lalikulu koma panapita miyezi ingapo asanauze akulu. Iye anati: “Pamene nthawi inkapita ndinayamba kuona kuti n’zosathekanso kuti akulu andithandize. Komabe ndinkangokhalira kuganiza za mavuto amene ndidzakumane nawo chifukwa cha zomwe ndinachitazo. Ndipo nthawi zonse ndikamapemphera kwa Yehova ndinkaona kuti ndiyenera kuyamba n’kupepesa kaye pa zomwe ndinalakwitsazo.” Kenako Daniel anauza akulu kuti amuthandize. Iye anati: “Poyamba ndinkaopa kuwafotokozera. Koma nditachita zimenezi ndinamva ngati munthu wina wandilandira chimwala chachikulu chimene ndinasenza. Panopa ndimaona kuti ndili ndi ufulu wonse wolankhula ndi Yehova m’pemphero.” Daniel sadziimbanso mlandu ndipo posachedwapa waikidwa kukhala mtumiki wothandiza.

“AZITHAWIRA KUMZINDA UMODZI MWA MIZINDAYI”

10. Kodi munthu amene wapha mnzake mwangozi ankayenera kuchita chiyani kuti achitiridwe chifundo?

10 Munthu amene wapha mnzake mwangozi ankayenera kuchitapo kanthu kuti achitiridwe chifundo. Iye ankayenera kuthawira kumzinda wothawirako wapafupi. (Werengani Yoswa 20:4.) Wopha mnzake mwangozi ayenera kuti sankanyalanyaza zimenezi chifukwa popanda kuthawira kumzindawu akanatha kuphedwa. Koma panali zinthu zina zimene ankayenera kudzimana kuti apulumuke. Ankayenera kusiya ntchito yake, nyumba yake komanso ufulu wopita kumene akufuna chifukwa ankayenera kukhala mumzindawu mpaka mkulu wa ansembe atafa. * (Num. 35:25) Koma ankalolera kusiya zonsezi chifukwa kuchoka mumzindawu kukanasonyeza kuti sankaona kuti mlandu wake ndi waukulu komanso akanatha kuphedwa.

11. Kodi Mkhristu angasonyeze bwanji kuti amaona moyenera chifundo cha Mulungu?

11 Masiku anonso anthu amene achita tchimo lalikulu ndipo alapa ayeneranso kuchitapo kanthu kuti Mulungu awachitire chifundo. Ayenera kusiyiratu tchimolo komanso kupewa zinthu zimene zingawachititse kuti achite machimo ena akuluakulu. Mtumwi Paulo anafotokoza zimene Akhristu a ku Korinto anachita pambuyo poti alapa. Iye analemba kuti: “Taonani zimene chisoni chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu chimenechi chakuchitirani. Chakuchititsani kukhala akhama kwambiri, chakuchititsani kudziyeretsa, kuipidwa, mantha, kufunitsitsa kulapa, kudzipereka, ndiponso kukonza cholakwacho.” (2 Akor. 7:10, 11) Tikachita zinthu mwamsanga kuti tikonze zimene talakwitsa, Yehova amaona kuti sitikuona nkhaniyo mopepuka komanso sitichita dala machimo poganiza kuti atichitira chifundo.

12. Kodi Mkhristu angafunike kudzimana zinthu ziti ngati akufuna kuti Mulungu azimuchitira chifundo?

12 Kodi Mkhristu angafunike kudzimana zinthu ziti ngati akufuna kuchitiridwa chifundo ndi Mulungu? Nthawi zina ayenera kudzimana zinthu zimene amakonda kwambiri ngati zinthuzo zingamuchimwitse. (Mat. 18:8, 9) Mwachitsanzo, ngati anzanu ena amakulimbikitsani kuchita zinthu zimene Yehova sasangalala nazo, kodi mungapitirize kucheza nawo? Ngati muli ndi vuto pa nkhani ya mowa, kodi mumapeweratu chilichonse chimene chingakuchititseni kumwa mopitirira malire? Ngati zimakuvutani kuti musamalakelake zachiwerewere, kodi mumapewa mafilimu, mawebusaiti kapena zinthu zina zimene zingakuchititseni kuganizira zogonana? Tizikumbukira ubwino wodzimana chilichonse chimene chingatilepheretse kukhala okhulupirika kwa Mulungu. Tikutero chifukwa palibe chinthu chimene chimapweteka kwambiri kuposa kusiyidwa ndi Yehova. Komanso palibe chabwino kwambiri kuposa kudziwa kuti Yehova adzatisonyeza “kukoma mtima kosatha mpaka kalekale.”​—Yes. 54:7, 8.

MIZINDAYO INKATETEZA OPHA MUNTHU MWANGOZI

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu akathawira kumzinda wothawirako ankatha kukhala wotetezeka komanso wosangalala?

13 Munthu akakhala mumzinda wothawirako, ankakhala wotetezeka. Paja Yehova anati: “Mizindayo ntchito yake ikhale yoti wopha munthu mwangozi azithawirako pothawa wobwezera magazi.” (Yos. 20:2, 3) Yehova sankalola kuti munthu aimbidwe mlandu kawiri pa tchimo limodzi komanso kuti wobwezera magazi apite kukapha munthu amene walowa kale mumzinda wothawirako. Izi zinkachititsa munthu amene wathawira mumzindawo kumva kuti ali m’manja mwa Yehova ndipo ndi wotetezeka. Iye sankamva ngati ali kundende. Akakhala mumzindamo ankatha kugwira ntchito, kuthandiza anthu ena komanso kutumikira Yehova mwamtendere. Choncho ankatha kukhalabe ndi moyo wosangalala.

Musamakayikire zoti Yehova amakhululuka (Onani ndime 14-16)

14. Kodi munthu amene walapa sayenera kuopa chiyani?

14 Atumiki a Yehova ena amene anachita machimo akuluakulu n’kulapa, amadziimbabe mlandu moti amamva ngati ali m’ndende ndipo amaona kuti Yehova sangawakhululukire. Ngati mumamva choncho, dziwani kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri moti akakhululuka sadzakuimbaninso mlandu pa nkhaniyo. Daniel amene tamutchula kale uja anatsimikizira mfundo imeneyi. Akulu atamupatsa malangizo n’kumuthandiza kuti akhale ndi chikumbumtima chabwino, ananena kuti: “Kuchokera nthawi imeneyo, ndinayamba kupuma bwino. Nkhaniyi itasamaliridwa ndinasiya kudziimba mlandu. Ndinazindikira kuti ukalapa, zimathera pomwepo. Mogwirizana ndi zimene Yehova ananena, iye amanyamula zolakwa zathu n’kuzitaya kutali kwambiri moti sitidzazionanso.” Munthu akalowa mumzinda wothawirako sankaopanso kuti wobwezera magazi amupeza n’kumupha. Masiku anonso, Yehova akatikhululukira sitiyenera kuopa kuti atikumbutsanso nkhaniyo kapena kutiimbanso mlandu.​—Werengani Salimo 103:8-12.

15, 16. Kodi dipo la Yesu komanso udindo wake monga Mkulu wa Ansembe zingakuthandizeni bwanji kuti musamakayikire zoti Mulungu adzakuchitirani chifundo?

15 Mosiyana ndi Aisiraeli, ife tili ndi chifukwa china chachikulu chotitsimikizira kuti Yehova adzatichitira chifundo. Mtumwi Paulo atadandaula kuti akulephera kumvera Yehova bwinobwino, sanakayikire kuti Mulungu amukhululukira ndipo anati: “Mulungu adzatero kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:25) N’zoona kuti Paulo ankalimbana ndi uchimo ndipo anali atalakwitsapo zinthu n’kulapa, koma sankakayikira kuti Mulungu amukhululukira kudzera mwa Yesu. Dipo la Yesu limathandiza kuti tikhale ndi chikumbumtima choyera komanso mtendere wamumtima. (Aheb. 9:13, 14) Popeza Yesu ndi Mkulu wa Ansembe, “akhoza kupulumutsa kwathunthu anthu amene akufika kwa Mulungu kudzera mwa iye, chifukwa adzakhalabe ndi moyo nthawi zonse ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.” (Aheb. 7:24, 25) Ngati mkulu wa ansembe ankathandiza Aisiraeli kudziwa kuti machimo awo akhululukidwa, ndiye kuli bwanji Yesu? Iye amatitsimikizira kuti ‘adzatichitira chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.’​—Aheb. 4:15, 16.

16 Choncho kuti muthawire kwa Yehova muyenera kukhulupirira nsembe ya Yesu. Sikuti muzingokhulupirira kuti nsembeyi ikhoza kupulumutsa anthu ambirimbiri. Koma muzikhulupirira kuti nsembeyo ikhoza kukuthandizani inuyo panokha. (Agal. 2:20, 21) Muzikhulupirira kuti dipo limathandiza kuti machimo anu akhululukidwe. Muzikhulupiriranso kuti dipo lingakuthandizeni inuyo kuti mudzapeze moyo wosatha. Nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Yehova anakupatsani inuyo.

17. N’chifukwa chiyani inuyo mumafuna kuthawira kwa Yehova?

17 Nkhani ya mizinda yothawirako imasonyeza kuti Yehova ndi wachifundo. Nkhaniyi imasonyeza kuti Yehova amaona kuti moyo ndi wopatulika komanso kuti akulu angatithandize ngati talakwitsa zinazake. Imasonyezanso zimene munthu ayenera kuchita posonyeza kuti walapadi. Nkhaniyi imatithandizanso kuti tisamakayikire kuti Mulungu amakhululuka. Kodi inuyo mumathawira kwa Yehova? Dziwani kuti munthu akathawira kwa Yehova amakhala wotetezeka kuposa kuthawira kwina kulikonse. (Sal. 91:1, 2) M’mutu wotsatira, tiona kuti nkhani ya mizinda yothawirako ingatithandize kutsanzira chilungamo komanso chifundo cha Yehova.

^ ndime 10 Mabuku ena achiyuda amasonyeza kuti banja la munthu amene wapha mnzake mwangozi linkapita kukakhala naye mumzinda wothawirako.