Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Chilungamo ndi Chifundo cha Yehova

Tsanzirani Chilungamo ndi Chifundo cha Yehova

“Muzichita chilungamo chenicheni poweruza milandu. Muzisonyezana kukoma mtima kosatha ndi chifundo.”​—ZEK. 7:9.

NYIMBO: 125, 88

1, 2. (a) Kodi Yesu ankaona bwanji Chilamulo cha Mulungu? (b) Kodi alembi ndi Afarisi ankapotoza bwanji Chilamulo?

YESU ankakonda kwambiri Chilamulo cha Mose. Izi n’zosadabwitsa chifukwa amene anapereka Chilamulocho ndi Atate wake, omwe ndi ofunika kwambiri kuposa aliyense. Lemba la Salimo 40:8 linalosera kuti Yesu azidzakonda malamulo a Mulungu, chifukwa limanena kuti: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.” Zolankhula komanso zochita za Yesu zinkasonyeza kuti iye amaona kuti Chilamulo cha Mulungu ndi changwiro, chothandiza komanso sichingalephere kukwaniritsidwa.​—Mat. 5:17-19.

2 Yesu ayenera kuti zinamuwawa kwambiri kuona alembi ndi Afarisi akupotoza Chilamulo cha Atate wake. Iye ananena kuti iwo ankatsatira tizigawo ting’onoting’ono ta Chilamulocho n’kumanyalanyaza mfundo zofunika kwambiri ndipo anawauza kuti: “Mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti, dilili, ndi chitowe, koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.” (Mat. 23:23) Mosiyana ndi anthu okhwimitsa zinthuwa, Yesu ankadziwa bwino cholinga cha Chilamulo komanso mfundo zokhudza Mulungu zimene tingaphunzire pa lamulo lililonse.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 N’zoona kuti Akhristufe sitiyendera Chilamulo. (Aroma 7:6) Koma Yehova anaonetsetsa kuti Chilamulocho chikhale m’Baibulo kuti tizichiwerenga. Iye safuna kuti tiziganizira kwambiri tinthu ting’onoting’ono ta m’Chilamulo koma tiziganizira “zinthu zofunika” zomwe ndi mfundo zake zikuluzikulu. Mwachitsanzo, kodi ndi mfundo ziti zimene tikuphunzira pa nkhani ya mizinda yopulumukirako? Munkhani yapita ija tinakambirana zimene munthu wopha mnzake mwangozi ankachita komanso zimene tikuphunzirapo. Koma nkhani ya mizinda yothawirako imatiphunzitsanso za Yehova komanso mmene tingamutsanzirire. Choncho munkhaniyi tikambirana mafunso atatu awa: Kodi nkhani ya mizinda yothawirako ikusonyeza bwanji chifundo cha Yehova? Kodi ikusonyeza kuti Yehova amaona bwanji moyo? Nanga ikusonyeza bwanji kuti chilungamo chake n’changwiro? Pamene tikukambirana funso lililonse, muziona zimene mungachite kuti muzitsanzira Atate wanu wakumwamba.​—Werengani Aefeso 5:1.

“MIZINDA YOYENERERA KWA INU”

4, 5. (a) Kodi Aisiraeli ankachita chiyani kuti mizinda yothawirako izikhala yosavuta kufikako, nanga n’chifukwa chiyani ankachita zimenezo? (b) Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wotani?

4 Mizinda 6 yothawirako inali pamalo osavuta kufikako. Yehova anauza Aisiraeli kuti mbali iliyonse ya mtsinje wa Yorodano kukhale mizinda itatu. Anachita zimenezi n’cholinga choti munthu aliyense amene akuthawa azifikako mosavuta n’kutetezeka. (Num. 35:11-14) Misewu yopita kumizinda imeneyi inkalambulidwa bwinobwino. (Deut. 19:3) Malinga ndi zimene olemba mbiri ya Ayuda amanena, pankakhala zikwangwani zosonyeza kumene munthu angalowere kuti akafike kumzinda wothawirako. Kukhala ndi mizinda yothawirako kunkathandiza kuti munthu amene wapha mnzake mwangozi asathawire kudziko lachilendo kumene akhoza kuyesedwa kuti ayambe kulambira milungu yonyenga.

5 Ndiye tangoganizani: Yehova ndi amene analamula kuti wopha mnzake mwadala aziphedwa koma Yehova yemweyo anakonza zoti munthu amene wapha mnzake mwangozi azichitiridwa chifundo komanso kutetezedwa. Pa nkhani imeneyi, katswiri wina ananena kuti Mulungu anasonyeza chifundo chachikulu pokonza zoti zikhale zosavuta kuti munthu athawire kumizindayi. Yehova si woweruza wankhanza amene amasakasaka zifukwa zoti alangire atumiki ake. Koma iye ndi “wachifundo chochuluka.”​—Aef. 2:4.

6. Kodi Afarisi anasonyeza bwanji kuti sankatsanzira chifundo cha Yehova?

6 Koma Afarisi sankakonda kuchitira anthu chifundo. Mwachitsanzo, olemba mbiri ena amanena kuti iwo ankakana kukhululukira munthu ngati wawalakwira pa nkhani yofanana maulendo oposa atatu. Pofuna kusonyeza mmene Afarisi ankaonera anthu olakwa, Yesu anapereka fanizo la Mfarisi amene anapemphera kuti: “Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. Iwo ndi olanda, osalungama ndi achigololo. Sindilinso ngati wokhometsa msonkho uyu.” Pa nthawiyo n’kuti wokhometsa msonkhoyo akupempha Mulungu modzichepetsa kuti amuchitire chifundo. Kodi n’chifukwa chiyani Afarisi sankasonyeza ena chifundo? Baibulo limanena kuti iwo ankaona anthu “ena onse ngati opanda pake.”​—Luka 18:9-14.

Kodi anthu amavutika kupempha kuti muwakhululukire? Muzisonyeza kuti ndinu wokonzeka kukhululuka (Onani ndime 4-8)

7, 8. (a) Kodi tingatsanzire bwanji Yehova ngati munthu wina watilakwira? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti tikamakhululukira anthu timasonyeza kuti ndife odzichepetsa?

7 Ifeyo tiyenera kutsanzira Yehova osati Afarisi. Tiyenera kusonyeza chifundo. (Werengani Akolose 3:13.) Kuti tichite zimenezi, tiyenera kusonyeza kuti ndife okonzeka kukhululukira ena. (Luka 17:3, 4) Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimafulumira kukhululukira anthu amene andilakwira ngakhale mobwerezabwereza? Kodi ndimafunitsitsa kukhazikitsa mtendere ndi munthu amene wandilakwira kapena kundikhumudwitsa?’

8 Tikamakhululukira ena timasonyezanso kuti ndife odzichepetsa. Afarisi ankalephera kuchita zimenezi chifukwa chakuti ankadziona kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena. Koma Akhristufe tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumaona kuti anthu ‘ena ndi otiposa’ komanso oyenera kuwakhululukira. (Afil. 2:3) Kodi inuyo mudzayesetsa kukhala odzichepetsa n’kumatsanzira Yehova? Tinganene kuti tiyenera kukonza mtima wathu kuti tisamavutike kukhululukira anthu komanso anthu asamavutike kupempha kuti tiwakhululukire. Tizikhala ofulumira kuchitira ena chifundo, osati ofulumira kukhumudwa.​—Mlal. 7:8, 9.

MUZILEMEKEZA MOYO KUTI “MUSAKHALE NDI MLANDU WAMAGAZI”

9. Kodi Yehova anathandiza bwanji Aisiraeli kuzindikira kuti moyo wa munthu ndi wamtengo wapatali?

9 Cholinga chachikulu cha mizinda yothawirako chinali kuteteza Aisiraeli kuti asakhale ndi mlandu wamagazi. (Deut. 19:10) Yehova amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali choncho amadana ndi “manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.” (Miy. 6:16, 17) Mulungu ndi wolungama komanso woyera moti sangalekerere mlandu wopha munthu, ngakhale zitachitika mwangozi. N’zoona kuti munthu wopha mnzake mwangozi ankachitiridwa chifundo. Koma iye ankafunika kufotokoza nkhani yake kwa akulu ndipo akapezeka kuti anachitadi mwangozi ankafunika kukhalabe mumzinda wothawirako mpaka mkulu wa ansembe atafa. Mwina izi zinkachititsa kuti munthuyo akhale mumzindawo kwa moyo wake wonse. Zonsezi zinkathandiza Aisiraeli kuona kuti moyo wa munthu ndi wamtengo wapatali. Iwo ankayenera kupewa chilichonse chimene chingaike pa ngozi moyo wawo kapena wa munthu wina. Kuchita zimenezi kukanasonyeza kuti amalemekeza Mlengi wawo.

10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti alembi ndi Afarisi sankalemekeza moyo?

10 Mosiyana ndi Yehova, alembi ndi Afarisi sankalemekeza moyo. N’chifukwa chiyani tikutero? Yesu anawauza kuti: “Munalanda anthu kiyi yowathandiza kudziwa zinthu. Inuyo simunalowemo, ndipo ofuna kulowamo munawatsekereza.” (Luka 11:52) Iwo anali ndi udindo wothandiza anthu kumvetsa Mawu a Mulungu komanso wowathandiza kuti aziyenda pamsewu wopita ku moyo wosatha. Koma m’malo mochita zimenezi, anachititsa kuti anthu asamatsatire “Mtumiki Wamkulu wa moyo,” koma aziyenda pamsewu wopita kukawonongedwa. (Mac. 3:15) Alembi ndi Afarisi anali onyada komanso odzikonda ndipo sankasamala za anthu ena. Iwo anali oipa mtima kwambiri komanso opanda chifundo.

11. (a) Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankaona moyo mmene Mulungu amauonera? (b) N’chiyani chingatithandize kuti tizichita khama mu utumiki ngati mmene Paulo ankachitira?

11 Kodi tingapewe bwanji mtima wa alembi ndi Afarisi n’kumatsanzira Yehova? Tiyenera kulemekeza moyo n’kumaona kuti ndi wamtengo wapatali. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti ankalemekeza moyo chifukwa ankalalikira mwakhama. N’chifukwa chake anatha kunena kuti: “Ndine woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse.” (Werengani Machitidwe 20:26, 27.) Koma sikuti Paulo ankalalikira chifukwa chongoona kuti ndi udindo wake kapena poopa kukhala ndi mlandu. Ankachita zimenezi chifukwa ankakonda anthu ndipo ankaona kuti moyo wawo ndi wamtengo wapatali. (1 Akor. 9:19-23) Nafenso tiyenera kuyesetsa kuti tiziona moyo mmene Mulungu amauonera. Yehova “amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Kodi inunso mumafuna zimenezi? Mukamayesetsa kukhala ndi mtima wachifundo mudzafunitsitsa kulalikira mwakhama komanso mudzasangalala kwambiri pochita zimenezi.

12. N’chifukwa chiyani anthu a Mulungu ayenera kuyesetsa kupewa ngozi?

12 Timasonyezanso kuti timaona moyo mmene Mulungu amauonera tikamayesetsa kupewa ngozi. Tiyenera kuchita zinthu mosamala tikakhala pa ulendo kapena tikamagwira ntchito. Tizichita zimenezi ngakhale pamene tikupita kumalo olambirira, kumanga malowo kapena kuwakonza. Sitiyenera kuika moyo wathu pa ngozi pongofuna kuti ntchito iyende kapena tisawononge ndalama. Tiyenera kuyesetsa kutsanzira Mulungu wathu wolungama amene nthawi zonse amachita zinthu zoyenera m’njira yoyenera. Ndipo akulu ayenera kupereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopewa kuika pa ngozi moyo wawo kapena wa anthu ena. (Miy. 22:3) Choncho ngati mkulu wakukumbutsani malangizo othandiza kupewa ngozi, muyenera kumvera. (Agal. 6:1) Kuona moyo mmene Yehova amauonera kudzakuthandizani kuti “musakhale ndi mlandu wamagazi.”

“AWERUZE . . . MALINGA NDI MALAMULO AMENEWA”

13, 14. Kodi akulu a ku Isiraeli ankayenera kuchita chiyani kuti asonyeze chilungamo cha Yehova?

13 Yehova anauza akulu a ku Isiraeli kuti azitsatira mfundo zake zachilungamo poweruza milandu. Choyamba, ankafunika kumvetsa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo. Kenako ankafunika kuganizira cholinga cha munthu amene wapha mnzake, mtima wake komanso zimene wakhala akuchita. Kuti asonyeze chilungamo cha Mulungu, ankafunika kuona ngati munthuyo anapha mnzake “chifukwa chodana naye” kapena “kuchita kum’bisalira.” (Werengani Numeri 35:20-24.) Popereka umboni wotsimikizira kuti munthuyo anapha mnzake mwadala, umboni wake unkayenera kukhala wa anthu awiri kapena kuposerapo.​—Num. 35:30.

14 Choncho pambuyo pofufuza zimene zinachitika, akulu ankafunika kuganizira munthuyo osati kungoganizira zimene zinachitika. Ankafunika kukhala ozindikira kuti athe kuona nkhani yonseyo bwinobwino, osati kungoiona pamwambamwamba. Koma kuposa zonse, ankafunika kuthandizidwa ndi mzimu woyera kuti athe kutsanzira Yehova posonyeza chifundo, chilungamo komanso kuzindikira.​—Eks. 34:6, 7.

15. Kodi Yesu ankasiyana bwanji ndi Afarisi?

15 Afarisi ankangoona kukula kwa tchimo limene munthu wachita, osati mtima umene munthu wolakwayo anali nawo. Pa nthawi ina ataona kuti Yesu akudya kunyumba kwa Mateyu anafunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?” Yesu atamva zimenezo anayankha kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” (Mat. 9:9-13) Kodi pamenepa tinganene kuti Yesu ankalekerera anthu ochimwa? Ayi sitingatero. Tisaiwale kuti Yesu akamalalikira ankauzanso anthu ochimwa kuti alape. (Mat. 4:17) Koma iye anazindikira kuti anthu ena amene anali ‘okhometsa misonkho komanso ochimwa’ anali ndi mtima wofuna kusintha. Sikuti kunyumba ya Mateyu anthuwo anangopitira kukadya, chifukwa Baibulo limasonyeza kuti ena mwa anthuwo ankafuna kutsatira Yesu. (Maliko 2:15) N’zomvetsa chisoni kuti Afarisi ambiri sankaona anthu ngati amenewo mmene Yesu ankawaonera. Mosiyana ndi Mulungu amene ankanena kuti amamulambira, Afarisiwo ankaona anzawo kuti ndi ochimwa komanso okanika.

16. Kodi akulu amene ali mu komiti yoweruza ayenera kuyesetsa kudziwa chiyani?

16 Masiku ano, akulu ayenera kuyesetsa kutsanzira Yehova amene “amakonda chilungamo.” (Sal. 37:28) Akamva zoti wina wachita tchimo ayenera ‘kufufuza ndi kufunsitsa za nkhaniyo’ kuti atsimikizire ngati n’zoona kapena ayi. Ngati tchimolo lachitikadi, ayenera kuthandiza munthuyo motsatira malangizo a m’Malemba. (Deut. 13:12-14) Akakhala pa komiti yoweruza ayenera kufufuza bwinobwino kuti aone ngati Mkhristu amene wachimwayo ali ndi mtima wolapa. Koma ayenera kukumbukira kuti si zapafupi kuzindikira ngati munthu walapadi. Pamafunika kudziwa maganizo komanso mtima umene munthuyo ali nawo. (Chiv. 3:3) Tikutero chifukwa munthu ayenera kulapa ndi mtima wonse kuti asonyezedwe chifundo. *

17, 18. Kodi akulu angadziwe bwanji ngati munthu walapa ndi mtima wonse? (Onani chithunzi choyambirira.)

17 Mosiyana ndi Yehova ndi Yesu, akulu sangaone mumtima mwa munthu. Ngati ndinu mkulu, kodi mungadziwe bwanji ngati munthu walapa ndi mtima wonse? Choyamba, muyenera kupempha Mulungu kuti akuthandizeni kuchita zinthu mwanzeru ndiponso mozindikira. (1 Maf. 3:9) Chachiwiri, muyenera kufufuza m’Mawu a Mulungu komanso mabuku amene kapolo wokhulupirika watipatsa. Zimenezi zingakuthandizeni kuzindikira ngati munthuyo ali ndi “chisoni cha dziko” kapena walapadi ndipo ali ndi “chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” (2 Akor. 7:10, 11) Muyenera kuona mmene Baibulo limafotokozera anthu olapa ndiponso amene sanalape. Onani mmene limafotokozera mtima wawo, maganizo awo komanso khalidwe lawo.

18 Pomaliza, muyenera kuganizira zinthu zonse zokhudza munthuyo. Muziganizira zimene zachitika pa moyo wake, zolinga zake komanso zimene sangakwanitse kuchita. Ponena za Yesu, yemwe ndi mutu wa mpingo, Baibulo linalosera kuti: “Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.” (Yes. 11:3, 4) Popeza akulu amatsogoleredwa ndi Yesu, iye adzawathandiza kuti aziweruza mmene iye amaweruzira. (Mat. 18:18-20) Timayamikira kwambiri kuti tili ndi akulu achikondi amene amayesetsa kuchita zimenezi. Timathokozanso kwambiri zonse zimene amachita polimbikitsa chifundo ndi chilungamo mumpingo.

19. Pa mfundo zimene taphunzira zokhudza mizinda yothawirako, kodi inuyo mukufuna kutsatira kwambiri mfundo iti?

19 Chilamulo cha Mose chinkathandiza anthu kudziwa choonadi pa nkhani ya Yehova ndiponso mfundo zake zachilungamo. (Aroma 2:20) Mwachitsanzo, nkhani ya mizinda yothawirako imathandiza akulu kuti azichita “chilungamo chenicheni poweruza milandu.” Imatiphunzitsanso tonsefe kuti tiyenera kusonyezana “kukoma mtima kosatha ndi chifundo.” (Zek. 7:9) N’zoona kuti masiku ano sitiyendera Chilamulo cha Mose. Koma Yehova sasintha, choncho amaonabe kuti chilungamo ndi chifundo ndi makhalidwe ofunika kwambiri. Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kulambira Mulungu amene anatilenga m’chifaniziro chake, amene tikhoza kumutsanzira komanso amene tikhoza kuthawira kwa iye.

^ ndime 16 Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2006, tsamba 30.